Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chilipo Chimene Chingagwirizanitse Anthu?

Kodi Chilipo Chimene Chingagwirizanitse Anthu?

Kodi Chilipo Chimene Chingagwirizanitse Anthu?

KAYA mumakhulupirira zotani, mungavomereze kuti pafupifupi m’zipembedzo zonse muli anthu okonda choonadi. Anthu amene amakonda kwambiri choonadi ndiponso amene amachifunafuna angapezeke pa Ahindu, Akatolika, Ayuda, ndi m’zipembedzo zina. Ngakhale zili choncho, chipembedzo chikugawanitsa anthu. Ena amagwiritsa ntchito chipembedzo pa zolinga zoipa. Kodi zidzatheka kuti anthu oona mtima a m’zipembedzo zonse amene amakonda zabwino ndi zoona adzagwirizane? Kodi angadzagwirizane pa cholinga chimodzi?

N’zosautsatu kwambiri kuona kuti chipembedzo chikupitiriza kugaŵanitsa anthu! Taganizani za nkhondo izi. Ahindu anamenyana ndi Abuda ku Sri Lanka. Apulotesitanti, Akatolika, ndi Ayuda apha anthu pankhondo zosiyanasiyana. Anthu amene amati ndi Akristu anamenyana ndi Asilamu ku Bosnia, Chechnya, Indonesia, ndi Kosovo. Ndipo ku Nigeria, anthu 300 anamwalira pamene zipembedzo zinamenyana kwa masiku aŵiri mu March 2000. Inde, kudana kwa zipembedzo kwasonkhezera kwambiri nkhondo zimenezi.

Nthaŵi zambiri anthu oona mtima amakhumudwa kwambiri ndi zoipa zimene zimachitika chifukwa cha chipembedzo. Mwachitsanzo, anthu amene amapita ku tchalitchi amagwidwa nthumazi poona kuti atsogoleri a chipembedzo amene agwirira ana chigololo amawalandira m’matchalitchi ena. Anthu ena okhulupirira amakhumudwa kwambiri chifukwa cha kusiyana maganizo kwa magulu ambiri amene amati ndi achikristu pankhani monga za mathanyula ndi kuchotsa mimba. Ndithudi, chipembedzo sichinagwirizanitse anthu. Komabe, pali anthu okondadi choonadi m’zipembedzo zambiri, monga zitsanzo zotsatirazi zikusonyezera.

Ankafunafuna Choonadi

Fidelia anali munthu wolambira woona mtima ndi wodzipereka mu Tchalitchi cha Akatolika cha San Francisco ku La Paz, Bolivia. Ankagwadira chithunzi cha Maria ndipo ankagula makandulo abwino kwambiri n’kuwaika kutsogolo kwa kolona. Mlungu uliwonse ankapereka chakudya chochuluka kwa wansembe kuti akapatse anthu osauka. Komabe, ana asanu a Fidelia anamwalira asanabatizidwe. Wansembe atamuuza kuti ana ake onsewo anali kuzunzika mumdima wa Limbo, Fidelia ankadzifunsa kuti, ‘Ngati Mulungu ndi wachikondi ndi wachifundo, zimenezi zikutheka bwanji?’

Tara, amene ali dokotala anakulira m’Chihindu ku Kathmandu, Nepal. Ankalambira milungu yake mu akachisi a Chihindu potsatira miyambo yakale ya makolo ake ndipo anali ndi mafano m’nyumba yake. Koma Tara anali kuzunguzika mutu ndi mafunso ngati aŵa: Kodi n’chifukwa chiyani pali mavuto ochuluka chonchi? N’chifukwa chiyani anthu amamwalira? Koma sanapeze mayankho okhutiritsa a mafunso ameneŵa ku chipembedzo chake.

Panya anakulira m’Chibuda, panyumba yapafupi ndi ngalande ku Bangkok, Thailand. Anaphunzira kuti timavutika chifukwa cha zinthu zimene tinachita pamoyo woyamba ndikuti tikhoza kukhalanso pamtendere ngati tikhala osafuna kanthu kalikonse. Monga Abuda ena oona mtima, anaphunzira kulemekeza mawu a amonke ovala mikanjo yachikasu amene ankabwera kunyumba kwake mbandakucha uliwonse kudzapempha zinthu zokapatsa anthu osauka. Ankalambira ndi kusonkhanitsa mafano a Abuda pokhulupirira kuti zimateteza. Panya atachita ngozi yaikulu imene inam’pundula kuyambira m’chiuno mpaka kumiyendo, anapita kunyumba ya amonke ya Abuda akukhulupirira ndi mtima wonse kuti akamuchiritsa mozizwitsa. Sanamuchiritse kapena kum’limbikitsa mwauzimu. M’malo mwake anangodziitanira ziwanda ndipo anayamba kuseŵera nazo.

Virgil anabadwira ku United States ndipo ali ku koleji analoŵa chipembedzo cha Asilamu Achikuda. Anali wolimbikira kugaŵira mabuku awo, amene ankanena kuti mzungu aliyense ndi Mdyerekezi. Kukhulupirira zimenezo kunawapangitsa kuganiza kuti ndicho chifukwa chake azungu anachitira anthu akuda nkhanza zambiri. Ngakhale kuti Virgil anali woona mtima pa zikhulupiriro zake, anali kuvutika maganizo ndi mafunso aŵa: Zingatheke bwanji azungu onse kukhala oipa? Ndipo n’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri ulaliki umakhudza ndalama?

Charo anali Mpulotesitanti woona mtima ngakhale kuti anakulira kudera la South America kumene anthu ambiri anali Akatolika. Ankasangalala kuti sankalambira nawo mafano amene anali otchuka kumeneko. Charo ankakonda kupita ku tchalitchi Lamlungu lililonse kumapemphero otsitsimula mtima, komwe ankafuula kuti “Aleluya!” ndiponso ankaimba nawo ndi kuvina nawo mapemphero akatha. Charo ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti anali wopanda tchimo ndikuti anabadwanso mwatsopano. Ankapereka ku tchalitchi gawo limodzi la magawo khumi a ndalama zimene ankapeza. Ndipo mbusa wolalikira pa TV amene Charo ankamukonda akapempha ndalama zoti akathandizire ana a ku Africa anali kum’patsa. Komano, ankati akawafunsa apasitala ake chifukwa chake Mulungu wachikondi amazunza anthu ku helo, anaona kuti ankalephera kuyankha zomveka. Kenako, anatulukiranso kuti ndalama zimene ankapereka sizinali kupita kukathandiza ana a ku Africa.

Ngakhale kuti anali m’zipembedzo zosiyana, anthu asanu ameneŵa akufanana pamfundo imodzi. Anakonda choonadi ndipo ankafuna ndi mtima wonse mayankho enieni a mafunso awo. Koma kodi angagwirizane m’chipembedzo chimodzi? Nkhani yotsatira iyankha funso limeneli.

[Chithunzi patsamba 4]

Kodi n’zotheka kuti anthu a m’zipembedzo zosiyana agwirizane?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

G.P.O., Jerusalem