Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Madalitso a Yehova Adzakupezani?

Kodi Madalitso a Yehova Adzakupezani?

Kodi Madalitso a Yehova Adzakupezani?

“Madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu.”​—DEUTERONOMO 28:2.

1. Kodi n’chiyani chikanachititsa Aisrayeli kulandira madalitso kapena matemberero?

AISRAYELI anamanga misasa m’Chigwa cha Moabu atatsala pang’ono kumaliza ulendo wawo wa zaka 40 m’chipululu. Anali pafupi ndi Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno Mose analemba buku la Deuteronomo, limene lili ndi madalitso ndi matemberero osiyanasiyana. Aisrayeli ‘akanamvera mawu a Yehova,’ madalitso ‘akanawapeza.’ Yehova anawakonda monga “akeake a paokha” ndipo anafuna kuti asonyeze mphamvu zake m’malo mwawo. Koma ngati sakanamumvera, matemberero akanawapeza.​—Deuteronomo 8:10-14; 26:18; 28:2, 15.

2. Kodi mawu a Chihebri amene anawamasulira kuti “mukadzamvera” ndi “kukupezani” pa Deuteronomo 28:2 amatanthauzanji?

2 Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “mukadzamvera” pa Deuteronomo 28:2 limasonyeza kuti kumverako kuyenera kupitiriza. Anthu a Yehova sayenera kumangomumvera mwa apo ndi apo ayi. Ayenera kumumvera nthaŵi zonse. Akatero m’pamene madalitso a Mulungu adzawapeza. Anthu apeza kuti liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “kukupezani,” ndi liwu losonyeza kufunafuna limene nthaŵi zambiri limatanthauza “kuchipeza chinthu” kapena “kuchifikira.”

3. Kodi tingafanane ndi Yoswa motani ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika kwambiri?

3 Yoswa, mtsogoleri wa Israyeli, anasankha kumvera Yehova ndipo anam’dalitsa. Yoswa ananena kuti: “Mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, . . . koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” Anthu atamva zimenezi anayankha kuti: “Sikungatheke kuti tim’siye Yehova, ndi kutumikira milungu ina.” (Yoswa 24:15, 16) Yoswa anali mmodzi mwa anthu oŵerengeka a mbadwo wake amene anali ndi mwayi woloŵa m’Dziko Lolonjezedwa chifukwa cha mtima wake wabwino. Lerolino, tatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa lalikulu kwambiri​—dziko lapansi la paradaiso kumene anthu omwe Mulungu amakondwera nawo adzakhala ndi madalitso ambiri kuposa a nthaŵi ya Yoswa. Kodi madalitso ameneŵa adzakupezani? Adzatero ngati mudzamvera Yehova. Kuti mukwanitse kuchita zimenezo, ganizirani mbiri ya dziko lakale la Israyeli ndiponso zitsanzo za anthu amene tingatengerepo phunziro.​—Aroma 15:4.

Dalitso Kapena Temberero?

4. Kodi Mulungu anam’patsa chiyani Solomo poyankha pemphero lake, ndipo kodi tiyenera kuganiza bwanji za madalitso ngati amenewo?

4 Pamene Mfumu Solomo anali kulamulira, Aisrayeli analandira madalitso apadera kuchokera kwa Yehova. Anali ndi chitetezo chokwanira ndiponso zinthu zabwino zambiri. (1 Mafumu 4:25) Kulemera kwa Solomo kunamveka ponseponse ngakhale kuti iye sanapemphe chuma kwa Mulungu. M’malo mwake, ali wamng’ono ndiponso asanadziŵe zinthu zambiri, anapempha kuti akhale ndi mtima womvera. Yehova anamva pempho lake ndipo anam’patsa nzeru ndi kuzindikira. Zimenezi zinam’thandiza kuti aweruze bwino anthu ndi kuzindikira chabwino ndi choipa. Ngakhale kuti Mulungu anam’patsanso chuma ndi ulemerero, Solomo monga mnyamata, anazindikira kuti chuma chauzimu n’chimene chili chofunika kwambiri. (1 Mafumu 3:9-13) Kaya ndife olemera kapena ayi, tingayamikiretu kwambiri ngati tili ndi madalitso a Yehova ndi kukhala olemera mwauzimu.

5. Kodi n’chiyani chinachitika pamene Aisrayeli ndi Ayuda analephera kumvera Yehova?

5 Aisrayeli analephera kuyamikira madalitso a Yehova. Popeza sanamumvere, matemberero amene ananeneratu anawapeza. Zimenezi zinachititsa kuti adani awo awagonjetse ndipo nzika za Israyeli ndi Yuda anazitengera kuukapolo. (Deuteronomo 28:36; 2 Mafumu 17:22,23; 2 Mbiri 36:17-20) Kodi anthu a Mulungu anatengapo phunziro pamavuto ameneŵa kuti madalitso a Mulungu amapeza anthu okhawo amene amamvera Yehova? Ayuda otsala amene anabwerera ku dziko lawo mu 537 B.C.E. anali ndi mwayi woti aonetse ngati anapeza “mtima wanzeru” ndipo tsopano anaona kufunika komvera Mulungu.​—Salmo 90:12.

6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anatumiza Hagai ndi Zekariya kuti akalosere kwa anthu ake? (b) Kodi ndi mfundo iti imene uthenga wa Mulungu wonenedwa ndi Hagai unasonyeza?

6 Ayuda amene anabwerera kwawo anamanga guwa la nsembe ndi kuyamba kumanga kachisi mu Yerusalemu. Koma pamene anthu anawatsutsa kwambiri, changu chawo chinazirala ndipo ntchito yomangayo inaima. (Ezara 3:1-3, 10; 4:1-4, 23, 24) Ndiponso anayamba kuika zinthu zosangalatsa zakuthupi patsogolo. Motero, Mulungu anatumiza mneneri Hagai ndi Zekariya kuti akadzutsenso changu cha anthu ake pakulambira koona. Yehova ananena kupyolera mwa Hagai kuti: “Kodi imeneyi ndiyo nthaŵi yakuti inu nokha mukhala m’nyumba zanu zotchingidwa mkatimo, ndi nyumba iyi [yolambiriramo] ikhale yopasuka? . . . Mtima wanu usamalire njira zanu. Mwabzala zambiri, koma mututa pang’ono; mukudya, koma osakhuta; . . . ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m’thumba lobooka.” (Hagai 1:4-6) Kunyalanyaza zinthu zauzimu chifukwa chofunafuna zinthu zakuthupi sikungabweretse madalitso a Yehova.​—Luka 12:15-21.

7. N’chifukwa chiyani Yehova anauza Ayuda kuti: “Mtima wanu usamalire njira zanu”?

7 Ayuda atatanganidwa ndi zofuna zawo za tsiku ndi tsiku, anaiŵala kuti Mulungu angawapatse madalitso a mvula ndi nyengo zabwino ngati akanapitiriza kumumvera, ngakhale ena akuwatsutsa. (Hagai 1:9-11) Choncho, kunalidi koyenera kuwalangiza kuti: “Mtima wanu usamalire njira zanu.” (Hagai 1:7) Kwenikweni, Yehova anali kuwauza kuti: ‘Taganizani! Onani mmene mukugwirira ntchito yopanda phindu m’minda yanu chifukwa cha nyumba yanga yolambiriramo imene ili yabwinja.’ Kenako, mawu ouziridwa a aneneri a Yehova anafika m’mitima ya anthuwo, motero anayambanso kumanga kachisiyo ndi kumaliza mu 515 B.C.E.

8. Kodi Yehova anawapatsa langizo lotani Ayuda a m’nthaŵi ya Malaki, ndipo chifukwa chiyani?

8 Kenaka, m’masiku a mneneri Malaki, Ayuda anaziralanso mwauzimu mpaka kumapereka nsembe zosavomerezeka kwa Mulungu. (Malaki 1:6-8) Motero, Yehova anawalangiza kuti abwere nalo limodzi la magawo khumi a zokolola zawo kunyumba yake yosungiramo kuti amuyese ngati sakanawatsegulira mazenera a kumwamba ndi kuwatsanulira madalitso akuti akanasoŵa malo akuwalandirira. (Malaki 3:10) Ayuda analitu opusa povutikira zinthu zimene Mulungu akanatha kuwapatsa zambirimbiri ngati akanangomvera mawu ake!​—2 Mbiri 31:10.

9. Kodi tipenda nkhani za m’Baibulo za anthu atatu ati?

9 Kuphatikiza pa kufotokoza mbiri ya dziko la Israyeli, Baibulo limafotokozanso za anthu amene analandira madalitso a Yehova ngati anali kumumvera kapena matemberero ngati sanatero. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa anthu atatu okha​—Boazi, Nabala, ndi Hana. Pankhani imeneyi, mungakonde kuŵerenga buku la Rute komanso 1 Samuel 1:1–2:21 ndi 1 Samueli 25:2-42.

Boazi Anamvera Mulungu

10. Kodi Boazi ndi Nabala anali ofanana m’mbali ziti?

10 Ngakhale kuti Boazi ndi Nabala anakhalako nthaŵi zosiyana, panali mbali zina zimene ankafanana. Mwachitsanzo, onse aŵiri anali kukhala m’dziko la Yuda. Anali eni malo olemera, ndipo onse anali ndi mwayi wapadera wosonyeza kukoma mtima kwa anthu osoŵa thandizo. Koma ndi mbali zokhazi zimene anafanana.

11. Kodi Boazi anasonyeza motani kuti anamvera Yehova?

11 Boazi anakhalako m’nthaŵi ya oweruza a Israyeli. Ankalemekeza anthu ena, ndipo amene anali kugwira ntchito yokolola m’munda wake anali kum’lemekeza kwambiri. (Rute 2:4) Pomvera Lamulo, Boazi ankaonetsetsa kuti wasiya khunkha m’munda mwake kuti athandize ovutika ndi osauka. (Levitiko 19:9, 10) Kodi Boazi anachita chiyani atamva za Rute ndi Naomi ndi kuona mmene Rute anachitira khama kupezera mpongozi wake wokalambayo zosoŵa zakuthupi? Anam’chitira chifundo Rute mwapadera ndipo analamula antchito ake kuti am’lole kukunkha m’munda wake. Mwa mawu ake ndi zochita zachikondi, Boazi anasonyeza kuti anali munthu wauzimu amene anamvera Yehova. Motero, Mulungu anakondwera naye ndi kum’dalitsa.​—Levitiko 19:18; Rute 2:5-16.

12, 13. (a) Kodi Boazi anasonyeza motani kuyamikira lamulo la Yehova la kuwombola? (b) Kodi ndi madalitso a Mulungu ati amene anam’peza Boazi?

12 Umboni waukulu kwambiri wakuti Boazi anamvera Yehova ndiwo mmene anachitira mopanda dyera potsatira lamulo la Mulungu la kuwombola. Boazi anachita zonse zimene anatha kuti aonetsetse kuti choloŵa cha mbale wake Elimeleki​—mwamuna wa Naomi amene anamwalira​—chikhalebe ku banja la Elimeleki. Mwa “ukwati wapachilamu,” mkazi wamasiye anayenera kukwatiŵa ndi mbale wa mwamuna wake womwalirayo kuti mwana wamwamuna amene angabadwe adzasunge choloŵacho. (Deuteronomo 25:5-10; Levitiko 25:47-49) Popeza Naomi anapitirira msinkhu woti n’kubereka, Rute anadzipereka kukwatiŵa mmalo mwake. Mbale weniweni wa Elimeleki atasiya kuthandiza Naomi, Boazi anakwatira Rute. Mwana wawo wamwamuna, Obedi, anali kumuona monga mwana wa Naomi ndiponso woloŵa mmalo mwa Elimeleki wovomerezeka.​—Rute 2:19, 20; 4:1, 6, 9, 13-16.

13 Madalitso ochuluka anam’peza Boazi chifukwa chakuti anamvera malamulo a Mulungu mopanda dyera. Mwa mwana wawo Obedi, Boazi ndi Rute anadalitsidwa ndi mwayi wokhala makolo a Yesu Kristu. (Rute 2:12; 4:13, 21, 22; Mateyu 1:1, 5, 6) Zochita za Boazi zopanda dyera zikutiphunzitsa kuti madalitso amapeza anthu amene amakonda ena ndi kuchita mogwirizana ndi zimene Mulungu akufuna.

Nabala Sanamvere

14. Kodi Nabala anali munthu wotani?

14 Mosiyana ndi Boazi, Nabala sanamvere Yehova. Anaphwanya lamulo la Mulungu lakuti: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.” (Levitiko 19:18) Nabala sanasamale zinthu zauzimu. “Anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake.” Anali munthu “woipa” ngakhale kwa antchito ake. Moyenerera, dzina lakelo, Nabala, limatanthauza kuti “wopusa,” kapena “wopanda nzeru.” (1 Samueli 25:3, 17, 25) Kodi Nabala akanachitanji pamene anali ndi mwayi wosonyeza chifundo kwa munthu wosoŵa thandizo​—Davide, wodzozedwa wa Yehova?​—1 Samueli 16:13.

15. Kodi Nabala anam’chitira motani Davide, nanga Abigayeli anasiyana motani ndi mwamuna wake pankhaniyi?

15 Davide ndi anthu ake atamanga misasa pafupi ndi nkhosa za Nabala, anateteza nkhosazo ku magulu a achifwamba popanda kuwauza kuti awalipire. Mmodzi mwa abusa a Nabala anati: “Iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku.” Komabe, amithenga a Davide atam’pempha Nabala chakudya, “iye anawakalipira” ndi kuwabweza opanda kanthu. (1 Samueli 25:2-16) Mkazi wa Nabala, Abigayeli, anapititsa chakudya kwa Davide mwamsanga. Davide anali atapsa mtima kwambiri moti anatsala pang’ono kuti aphe Nabala ndi anthu ake. Choncho, zimene Abigayeli anachita zinapulumutsa miyoyo ya anthu ambiri ndi kuteteza kuti Davide asakhale ndi mlandu wakupha. Komabe umbombo ndi nkhanza za Nabala zinali zazikulu kwambiri. Patapita masiku khumi, “Yehova anam’kantha Nabala, nafa.”​—1 Samueli 25:18-38.

16. Kodi tingatsanzire motani Boazi ndi kupeŵa zimene Nabala anachita?

16 Panalitu kusiyana kwakukulu pakati pa Boazi ndi Nabala. Tiyeni titsanzire chifundo ndi kupanda dyera kwa Boazi ndi kupeŵa dyera ndi nkhanza za Nabala. (Ahebri 13:16) Tingatero mwa kugwiritsa ntchito langizo la Paulo lakuti: “Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pabanja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Lerolino, “nkhosa zina” za Yesu, Akristu amene akuyembekeza kudzakhala padziko lapansi, ali ndi mwayi wochitira zabwino odzozedwa a Yehova, otsalira a 144,000, amene adzalandira moyo wosafa kumwamba. (Yohane 10:16; 1 Akorinto 15:50-53; Chivumbulutso 14:1, 4) Yesu amaona zabwino zimene iwo akuchitazo ngati kuti akum’chitira iye mwini, ndipo Yehova amapereka madalitso ochuluka chifukwa cha zimenezo. (Mateyu 25:34-40; 1 Yohane 3:18)

Chiyeso ndi Madalitso a Hana

17. Kodi Hana anakumana ndi chiyeso chotani, ndipo anaonetsa maganizo otani?

17 Madalitso a Yehova anam’pezanso mkazi wopembedza kwambiri, Hana. Anali kukhala kudera la kumapiri la Efraimu ndi mwamuna wake wachilevi, Elikana. Mogwirizana ndi mmene malamulo analili, Elikana anali ndi mkazi wina​—Penina. Hana anali wosabereka, chinthu chomwe chinali chotonzetsa kwa mkazi wachiisrayeli, pamene Penina anali ndi ana angapo. (1 Samueli 1:1-3; 1 Mbiri 6:16,33,34) Koma mmalo mom’sangalatsa, Penina anam’chitira Hana mopanda chikondi moti zinam’pweteka kwambiri mpaka analira misozi ndi kukana kudya. Choipa kwambiri chinali chakuti Penina ankachita zimenezi “chaka ndi chaka,” nthaŵi iliyonse banjalo likapita ku nyumba ya Yehova ku Silo. (1 Samueli 1:4-8) Ha! Penina analitu wopanda chifundo, ndipo chinalidi chiyeso kwa Hana. Komabe, Hana sanaimbe mlandu Yehova, ndiponso sanaleke kupita ndi mwamuna wake ku Silo. Motero, m’kupita kwanthaŵi, madalitso ochuluka anamupeza.

18. Kodi Hana anapereka chitsanzo chotani?

18 Hana anapereka chitsanzo chabwino kwa anthu a Yehova lerolino, makamaka amene angakhumudwe chifukwa cha kulankhula kopanda chifundo kwa anthu ena. Zimenezo zikachitika, kudzipatula sikungathetse vutolo. (Miyambo 18:1) Hana sanalole kuti chiyeso chake chimulepheretse kukapezeka kumene Mawu a Mulungu ankaphunzitsidwa ndiponso komwe anthu a Mulungu anali kusonkhana kuti amulambire. Motero anakhalabe wolimba mwauzimu. Kuya kwa zomwe ankadziŵa mwauzimu kukuoneka m’pemphero lake labwino kwambiri limene lili pa 1 Samueli 2:1-10. *

19. Kodi tingayamikire motani zinthu zauzimu?

19 Monga atumiki a Yehova amakono, sitimalambira kuchihema. Komabe, tingayamikire zinthu zauzimu, monga mmene Hana anachitira. Mwachitsanzo, tingayamikire mwakuya chuma chauzimu mwa kupezeka nthaŵi zonse pamisonkhano yachikristu, misonkhano yadera ndi yapadera, ndiponso misonkhano yachigawo. Tiyeni tigwiritse ntchito misonkhano imeneyi kulimbikitsana wina ndi mnzake pakulambira koona kwa Yehova amene watipatsa mwayi woti ‘tim’tumikire, mopanda mantha m’chiyero ndi m’chilungamo.’​—Luka 1:74, 75; Ahebri 10:24, 25.

20, 21. Kodi Mulungu anam’dalitsa motani Hana chifukwa cha kudzipereka kwake kwaumulungu?

20 Yehova anaona kudzipereka kwaumulungu kwa Hana ndipo anam’dalitsa kwambiri. Paulendo wina wa chaka ndi chaka wa banjalo wopita ku Silo, Hana anapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova akulira ndi kulonjeza kuti: “Yehova wamakamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiŵala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.” (1 Samueli 1:9-11) Mulungu anamva pemphero la Hana ndi kum’dalitsa ndipo anabala mwana wamwamuna amene anam’patsa dzina lakuti Samueli. Atam’letsa kuyamwa, anapita naye ku Silo kuti akatumikire pa chihema.​—1 Samueli 1:20, 24-28.

21 Hana anaonetsa chikondi kwa Mulungu ndipo anakwaniritsa lonjezo lake kwa Iye lokhudza Samueli. Ndipo tangoganizani madalitso amene iye ndi Elikana anali nawo chifukwa chakuti mwana wawo amene anali kumukonda anali kutumikira pachihema cha Yehova! Makolo achikristu ambiri alinso ndi chimwemwe ndi madalitso ngati amenewo chifukwa ana awo aamuna ndi aakazi akutumikira monga apainiya a nthaŵi zonse, a m’banja la Beteli, kapena mautumiki ena amene amalemekeza Yehova.

Pitirizani Kumvera Yehova!

22, 23. (a) Kodi tingatsimikize za chiyani ngati tipitiriza kumvera mawu a Yehova? (b) Kodi tidzaphunzira chiyani m’nkhani yotsatira?

22 Kodi tingatsimikize za chiyani ngati tipitiriza kumvera Yehova? Tidzalemera mwauzimu ngati tim’konda Mulungu ndi mtima wonse ndi kusonyeza m’moyo wathu kuti ndife atumiki ake amene tadzipatulira kwa iye. Ngakhale kuti tingafunike kupirira ziyeso zoopsa kuti tichite zimenezo, madalitso a Yehova adzatipeza mosakayika​—mwinanso madalitso aakulu kuposa mmene tingaganizire.​—Salmo 37:4; Ahebri 6:10.

23 Mulungu adzapereka madalitso ambiri kwa anthu ake m’tsogolo. Chifukwa cha kumvera Yehova, “khamu lalikulu” lidzapulumuka “chisautso chachikulu” ndipo lidzasangalala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu. (Chivumbulutso 7:9-14; 2 Petro 3:13) M’dziko limenelo, Yehova adzakwaniritsa zikhumbo zolungama za anthu ake onse. (Salmo 145:16) Komabe, monga momwe tidzaonera m’nkhani yotsatira, ngakhale pakalipano anthu amene akupitiriza kumvera mawu a Yehova, akuwadalitsa ndi ‘mphatso zabwino ndi chininkho changwiro zochokera kumwamba.’​—Yakobo 1:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Mawu a Hana akufanana mbali zina ndi mawu amene namwali Mariya analankhula atangodziŵa kumene kuti adzakhala mayi ake a Mesiya.​—Luka 1:46-55.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi mbiri ya Israyeli ingatiphunzitse chiyani za madalitso a Mulungu?

• Kodi Boazi ndi Nabala anali osiyana motani?

• Kodi tingam’tsanzire motani Hana?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kumvera mawu a Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Mfumu Solomo inapempha mtima womvera, ndipo Yehova anam’dalitsa mwa kum’patsa nzeru

[Chithunzi patsamba 12]

Boazi ankalemekeza anthu ndi kuwachitira chifundo

[Chithunzi patsamba 15]

Hana anam’dalitsa kwambiri chifukwa chodalira Yehova