Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Madalitso a Yehova Amatilemeretsa

Madalitso a Yehova Amatilemeretsa

Madalitso a Yehova Amatilemeretsa

“Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”​—MIYAMBO 10:22.

1, 2. N’chifukwa chiyani chuma sichingabweretse chimwemwe?

ANTHU ambiri lerolino atanganidwa ndi kufunafuna chuma. Koma kodi chuma chimawapatsa chimwemwe? Nyuzipepala ina ya ku Australia yotchedwa The Australian Women’s Weekly inanena kuti: “Anthu masiku ano sakusangalala pamoyo wawo monga momwe zinalili kale.” Inapitiriza kuti: “Zimenezi n’zodabwitsa. Tamva kuti dziko la Australia likuchita bwino pankhani ya zachuma kuposa kale lonse. . . . Komabe anthu m’dzikoli akuona kuti zinthu sizikuyenda bwino. Amuna ndi akazi akuona kuti chinachake chikusoŵeka pamoyo wawo koma sakudziŵa kuti chinachakecho n’chiyani.” Malemba amanenatu zoona kuti chuma chimene tili nacho sichingabweretse moyo kapena chimwemwe!​—Mlaliki 5:10; Luka 12:15.

2 Baibulo limaphunzitsa kuti madalitso a Mulungu ndi amene amabweretsa chimwemwe chochuluka. Pankhani imeneyi, Miyambo 10:22 amanena kuti: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.” Kufunafuna chuma mwadyera kumabweretsa chisoni. Mtumwi Paulo anachenjeza moyenerera kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

3. Kodi n’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amakumana ndi mayesero?

3 Koma madalitso omwe sabweretsa chisoni amapeza anthu amene ‘amamvera mawu a Yehova.’ (Deuteronomo 28:2) Komabe, ena angafunse kuti, ‘Ngati madalitso a Yehova sawonjezerapo chisoni, n’chifukwa chiyani atumiki ambiri a Mulungu amavutika?’ Baibulo limavumbula kuti Mulungu walola kuti tikumane ndi mayesero koma mayeserowo amabwera ndi Satana, dziko lake loipali, ndi kupanda ungwiro kwathu. (Genesis 6:5; Deuteronomo 32:4, 5; Yohane 15:19; Yakobo 1:14, 15) Yehova ndiye gwero la “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Choncho, madalitso ake sabweretsa chisoni. Motero tiyeni tipende mphatso zina zangwiro za Mulungu.

Mawu a Mulungu Ndi Mphatso Yaulere

4. Kodi anthu a Yehova ali ndi madalitso ndi mphatso yaulere iti m’kati mwa “nthaŵi ya chimaliziro” ino?

4 Ponena za “nthaŵi ya chimaliziro,” ulosi wa Danieli umati: “Chidziŵitso chidzachuluka.” Komabe Danieli anafotokoza kuti: “Palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.” (Danieli 12:4, 10) Tangoganizani! Mawu a Mulungu​—makamaka maulosi​—anawafotokoza ndi nzeru zaumulungu moti anthu oipa sangadziŵe tanthauzo lake ngakhale kuti anthu a Yehova akudziŵa! Mwana wa Mulungu anapemphera kuti: “Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda.” (Luka 10:21) Ndi dalitsotu lalikulu kukhala ndi mphatso yaulere ya Mawu amene Mulungu analemba, Baibulo, ndi kukhala nawo m’gulu la anthu amene Yehova wawazindikiritsa mwauzimu!​—1 Akorinto 1:21, 27, 28; 2:14, 15.

5. Kodi nzeru n’chiyani ndipo tingaipeze motani?

5 Kukanakhala kuti sitinalandire “nzeru yochokera kumwamba,” sitikanazindikira mwauzimu. (Yakobo 3:17) Nzeru ndiyo luso logwiritsa ntchito zomwe munthuwe ukudziŵa ndi kuzindikira pothetsa mavuto, kupeŵa ngozi, kukwaniritsa zolinga, kapena kupereka malangizo oyenera. Kodi timaipeza motani nzeru yaumulungu? Miyambo 2:6 imanena kuti: “Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.” Inde, Yehova adzatipatsa nzeru ngati tipitiriza kuipempherera ndipo atha kutipatsanso “mtima wanzeru ndi wakuzindikira,” monga anam’patsira Mfumu Solomo. (1 Mafumu 3:11, 12; Yakobo 1:5-8) Kuti tipeze nzeru, tiyeneranso kumvera Yehova mwa kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito Mawu ake nthaŵi zonse.

6. N’chifukwa chiyani n’kwanzeru kugwiritsa ntchito malamulo ndi mfundo zachikhalidwe za Mulungu m’moyo wathu?

6 Zitsanzo zazikulu za nzeru yaumulungu timazipeza m’malamulo ndi m’mfundo zachikhalidwe za Baibulo. Zimenezi zimatipindulitsa m’mbali zonse​—mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwauzimu. Wamasalmo moyenerera anaimba kuti: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova ziri zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso. Kuopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthaŵi zonse: Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse. Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa.”​—Salmo 19:7-10; 119:72.

7. Kodi chimachitika n’chiyani ngati munthu satsatira miyezo yolungama ya Mulungu?

7 Koma amene satsatira miyezo yolungama ya Mulungu samapeza chimwemwe ndi ufulu zimene amazifunafuna. Nthaŵi inayake amapeza kuti Mulungu sanyozeka, pakuti munthu amatuta chimene anafesa. (Agalatiya 6:7) Anthu miyandamiyanda amene satsatira mfundo zachikhalidwe za Baibulo akututa zinthu zomvetsa chisoni monga mimba zapathengo, matenda opweteka, kapena kuloŵerera ndi mankhwala osokoneza bongo. M’kupita kwanthaŵi, zimene akuchitazo zidzawaphetsa kapena Mulungu adzawawononga ngati salapa ndi kusintha moyo wawo.​—Mateyu 7:13, 14.

8. N’chifukwa chiyani anthu amene amakonda Mawu a Mulungu ali achimwemwe?

8 Komabe, amene amakonda Mawu a Mulungu ndi kuwagwiritsa ntchito, madalitso ochuluka akuwapeza tsopano lino ndiponso adzawapeza m’tsogolo. Lamulo la Mulungu lawapatsa ufulu, ali ndi chimwemwe chenicheni, ndipo akuyembekeza ndi mtima wonse nthaŵi imene adzamasulidwa ku uchimo ndi zotsatirapo zake zakupha. (Aroma 8:20, 21; Yakobo 1:25) Zimene akuyembekezazi n’zotsimikizika chifukwa zazikidwa pa mphatso yachikondi chachikulu ya Mulungu imene anapatsa anthu​—nsembe ya dipo ya Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; Aroma 6:23) Mphatso yaikulu kwambiri imeneyi ikutsimikizira kuti Mulungu amakonda kwambiri anthu ndiponso kuti amene akumvera Yehova, adzalandira madalitso osatha.​—Aroma 8:32.

Tikuyamikira Mphatso ya Mzimu Woyera

9, 10. Kodi timapindula motani ndi mphatso ya Yehova ya mzimu woyera? Perekani chitsanzo.

9 Mphatso ina yachikondi ya Mulungu imene tiyenera kuyamikira ndiyo mzimu wake woyera. Pa Pentekoste wa 33 C.E., mtumwi Petro anauza khamu la anthu limene linali mu Yerusalemu kuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.” (Machitidwe 2:38) Lerolino, Yehova amapereka mzimu woyera kwa atumiki ake omwe adzipatulira kwa iye komanso amene amapempherera mzimuwo ndi kufuna kuchita chifuniro chake. (Luka 11:9-13) Kale, mphamvu yaikulu kwambiri m’chilengedwe chonse imeneyi​—mzimu woyera wa Mulungu, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito​—inalimbikitsa amuna ndi akazi okhulupirira, kuphatikizapo Akristu oyambirira. (Zekariya 4:6; Machitidwe 4:31) Monga anthu a Yehova, mphamvuyi ingatilimbikitsenso ngakhale titakumana ndi zopinga kapena mavuto aakulu.​—Yoweli 2:28, 29.

10 Taganizirani chitsanzo cha Laurel, amene anadwala poliyo ndipo anakhala m’makina othandiza kupuma kwa zaka 37. * Ngakhale kuti anali pamavuto osaneneka, iye anatumikira Mulungu mwachangu mpaka pamene anamwalira. Kwa zaka zonsezo, madalitso a Yehova ochuluka anamupeza Laurel. Mwachitsanzo, iye anathandiza anthu 17 kudziŵa choonadi cholondola cha Baibulo, ngakhale kuti ankakhala ali pamakina akewo tsiku lonse lathunthu! Zimene zinam’chitikirazi zikutikumbutsa mawu a Paulo akuti: “Pamene ndifoka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:10) Inde, zinthu zimatiyendera bwino polalikira uthenga wabwino osati chifukwa cha mphamvu ndi nzeru zathu, koma chifukwa chakuti Mulungu amatithandiza mwa mzimu woyera, umene amaupereka kwa anthu amene amamvera mawu ake.​—Yesaya 40:29-31.

11. Kodi mzimu wa Mulungu umathandiza amene avala ‘umunthu watsopano’ kukhala ndi mikhalidwe iti?

11 Ngati timvera Mulungu ndi mtima wonse, mzimu wake udzatithandiza kukhala ndi mikhalidwe ya chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso. (Agalatiya 5:22, 23) “Chipatso cha mzimu” chimenechi ndi mbali ya ‘umunthu watsopano’ umene Akristu amavala m’malo mwa mikhalidwe yolusa yonga ya nyama imene mwina anali nayo poyamba. (Aefeso 4:20-24; Yesaya 11:6-9) Chofunika kwambiri pa zipatso za mzimu zimenezi ndicho chikondi, “chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:14.

Chikondi Chachikristu Ndi Mphatso Yofunika Kuinyadira

12. Kodi Tabita ndi Akristu ena a m’zaka za zana loyamba anasonyeza motani chikondi?

12 Chikondi chachikristu ndi mphatso ina yodalitsika ya Yehova imene moyenerera timainyadira. Ngakhale kuti mphatsoyi ili ndi lamulo, ilinso ndi chikondi chachikulu moti imathandiza okhulupirira kukondana kwambiri mwinanso kuposa mmene chibale chingachitire. (Yohane 15:12, 13; 1 Petro 1:22) Mwachitsanzo, taganizirani za Tabita, mkazi wachikristu wabwino kwambiri wa m’zaka za zana loyamba. “Mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo,” zimene anachitira makamaka akazi amasiye mumpingo. (Machitidwe 9:36) Akazi amasiyeŵa mwina anali ndi achibale awo koma Tabita anafuna kuchita zimene akanatha kuti awathandize ndi kuwalimbikitsa. (1 Yohane 3:18) Tabita anaperekatu chitsanzo chabwino zedi! Chikondi chachikristu chinachititsa Priska ndi Akula ‘kupereka makosi awo’ chifukwa cha Paulo. Chikondi chinalimbikitsanso Epafra, Luka, Onesifolo, ndi ena kuthandiza mtumwiyu pamene anali m’ndende ku Roma. (Aroma 16:3, 4; 2 Timoteo 1:16; 4:11; Filemoni 23, 24) Inde, lerolino Akristu ngati amenewo ‘ali nacho chikondano wina ndi mnzake,’ mphatso yodalitsika ya Mulungu imene imawadziŵikitsa monga ophunzira oona a Yesu.​—Yohane 13:34, 35.

13. Kodi tingasonyeze motani kuti timayamikira ndi mtima wonse ubale wathu wachikristu?

13 Kodi mumanyadira chikondi chimene chili mumpingo wachikristu? Kodi mumayamikira ubale wathu wauzimu umene wakuta dziko lonse lapansi? Zimenezinso ndi mphatso ndi madalitso a Yehova amene amatilemeretsa. Kodi tingasonyeze motani kuti timayamikira mphatso zimenezi? Tingatero mwa kuchita utumiki wopatulika kwa Yehova, kutenga nawo mbali m’misonkhano yachikristu, ndiponso mwa kuonetsa chikondi ndi zipatso zina za mzimu wa Mulungu.​—Afilipi 1:9; Ahebri 10:24, 25.

“Mphatso mwa Amuna”

14. Kodi Mbale amafunika kukhala wotani kuti ayenerere kutumikira monga mkulu kapena mtumiki wotumikira?

14 Amuna achikristu amene akukhumba kukhala akulu kapena atumiki otumikira kuti atumikire olambira anzawo ali ndi cholinga chabwino. (1 Timoteo 3:1, 8) Kuti ayenerere maudindo ameneŵa, mbale ayenera kukhala wauzimu, wodziŵa bwino Malemba ndiponso wachangu muutumiki wakumunda. (Machitidwe 18:24; 1 Timoteo 4:15; 2 Timoteo 4:5) Akhale wodzichepetsa, wofatsa, ndiponso woleza mtima, popeza madalitso a Mulungu sapeza anthu odzikuza, onyada, kapena adyera. (Miyambo 11:2; Ahebri 6:15; 3 Yohane 9, 10) Ngati ali wokwatira, adzafunika kukhala mutu wabanja wachikondi, woweruza bwino nyumba yake yonse. (1 Timoteo 3:4, 5, 12) Munthu wotero adzalandira madalitso a Yehova popeza amaika patsogolo zinthu zauzimu.​—Mateyu 6:19-21.

15, 16. Kodi ndani amene ali “mphatso mwa amuna”? Perekani zitsanzo?

15 Pamene akulu mumpingo akudzipereka kulalikira, kuchita ubusa, ndi kuphunzitsa, amatipatsa zifukwa zokwanira zoyamikirira “mphatso mwa amuna” zimenezi. (Aefeso 4:8, 11, NW) Amene akupindula ndi utumiki wawo wachikondi mwina sangayamikire nthaŵi zonse, koma Yehova amaona zonse zimene akulu okhulupirika ameneŵa akuchita. Sadzaiwala chikondi chimene iwo akuonetsera ku dzina lake mwa kutumikira anthu ake.​—1 Timoteo 5:17; Ahebri 6:10.

16 Taganizirani za mkulu wina wolimbikira ntchito amene anachezera mtsikana wachikristu patangotsala nthaŵi yochepa kuti mtsikanayo akam’chite opaleshoni yaubongo. Bwenzi lina la banja la mtsikanayo linalemba kuti: “Anali wachifundo, wolimbikitsa, wosamala ena. Anapempha kuti am’lole kupemphera nafe kwa Yehova. Pamene anali kupemphera, bambo a mtsikanayu [omwe si a Mboni za Yehova] analira, ndipo aliyense amene anali m’chipinda cha chipatalacho anagwetsa misozi. Pemphero la mkuluyo linalitu lachikondi ndipo Yehova anasonyezadi chikondi pom’tumiza iye panthaŵi yeniyeniyo imene chilimbikitso chake chinafunika!” Mboni ina imene inali kudwala inasimba za akulu amene anam’chezera kuchipatala kuti: “Atafika pafupi ndi bedi langa m’chipinda cha anthu odwala mwakayakaya, ndinadziŵa kuti ndipirira chilichonse chimene chingachitike pambuyo pake. Ndinalimba mtima ndiponso ndinakhala wamtendere.” Kodi alipo amene angagule kudera nkhaŵa kwachikondi koteroko? Palibe! Ndi mphatso ya Mulungu imene akupereka kudzera mumpingo wachikristu.​—Yesaya 32:1, 2.

Mphatso ya Utumiki Wakumunda

17, 18. (a) Kodi ndi mphatso yautumiki iti imene Yehova wapereka kwa anthu ake onse? (b) Kodi Mulungu wapereka thandizo lotani kuti tikwanitse utumiki wathu?

17 Ntchito yonyaditsa kwambiri kuposa ina iliyonse imene munthu angapatsidwe ndiyo kutumikira Yehova, Wammwambamwamba. (Yesaya 43:10; 2 Akorinto 4:7; 1 Petro 2:9) Komabe, munthu aliyense wofunitsitsa kutumikira Mulungu ali ndi mwayi wochita nawo utumiki umenewu kaya ndi mwana kapena wachikulire, mwamuna kapena mkazi. Kodi mphatso yamtengo wapatali imeneyi mukuigwiritsa ntchito? Ena angaleke kulalikira chifukwa akuganiza kuti sakukwanira. Koma kumbukirani kuti Yehova amapereka mzimu woyera kwa anthu amene akum’tumikira ndipo umatithandiza m’mbali zimene tikupereŵera.​—Yeremiya 1:6-8; 20:11.

18 Yehova wapereka ntchito yolalikira Ufumu kwa atumiki ake odzichepetsa, osati kwa anthu onyada ndiponso ongodalira nzeru zawo. (1 Akorinto 1:20, 26-29) Anthu ofatsa ndi odzichepetsa amadziŵa kuti ali ndi zofooka ndipo amadalira Mulungu kuti awathandize pochita utumiki wakumunda. Amayamikiranso thandizo lauzimu limene iye amapereka kudzera mwa “mdindo wokhulupirika.”​—Luka 12:42-44; Miyambo 22:4.

Moyo Wabanja Wachimwemwe Ndi Mphatso Yabwino

19. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimathandiza kuti mulere bwino ana?

19 Ukwati ndi moyo wabanja wachimwemwe ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. (Rute 1:9; Aefeso 3:14, 15) Ananso ndi “cholandira cha kwa Yehova” chamtengo wapatali, ndipo amabweretsa chimwemwe kwa makolo amene aphunzitsa bwino anawo kuti akhale ndi makhalidwe amene Mulungu amakondwera nawo. (Salmo 127:3) Ngati ndinu kholo, mverani mawu a Yehova mwa kuphunzitsa ana anu mogwirizana ndi Mawu ake. Makolo amene akuchita zimenezi Yehova adzawathandiza ndi kuwapatsa madalitso ochuluka.​—Miyambo 3:5, 6; 22:6; Aefeso 6:1-4.

20. Kodi n’chiyani chingawathandize makolo amene ana awo asiya kulambira koona?

20 Mwina ana ena angasankhe kusiya kulambira koona pamene akula ngakhale kuti makolo awo oopa Mulungu anayesetsa mwakhama kuwalera bwino. (Genesis 26:34, 35) Zimenezi zingawapweteke mumtima makolowo. (Miyambo 17:21, 25) Komabe, m’malo motaya mtima, kungakhale kothandiza kukumbukira fanizo la Yesu la mwana wosakaza. Ngakhale kuti mwana ameneyo anachoka panyumba n’kumakachita zofuna zake, mkupita kwanthaŵi anabwerera kunyumba kwa bambo ake, amene anamulandira mwachikondi ndiponso mwachimwemwe. (Luka 15:11-32) Mulimonse mmene zingakhalire, makolo achikristu okhulupirika angakhulupirire kuti Yehova akuwamvetsa, akuwadera nkhaŵa mwachikondi, ndiponso sadzalephera kuwathandiza.​—Salmo 145:14.

21. Kodi tiyenera kumvera ndani, ndipo n’chifukwa chiyani?

21 Ndiyetu tiyeni tonsefe tizindikire zimene zili zofunikadi kwambiri pamoyo wathu. Kodi tikutanganidwa ndi kufunafuna chuma chimene chingatibweretsere ife ndi mabanja athu chisoni? Kapena kodi tikufunafuna ‘mphatso zabwino ndi zininkho zangwiro’ zimene zimachokera kwa “Atate wamauniko”? (Yakobo 1:17) Satana, “atate wake wa bodza,” amafuna kuti tikhale akapolo a chuma ndi kulephera kupeza chimwemwe ndi moyo. (Yohane 8:44; Luka 12:15) Koma Yehova amatikondadi ndipo amatifunira zabwino zonse. (Yesaya 48:17, 18) Ndiyetu tiyeni timvere Atate wathu wachikondi wakumwamba ndi ‘kukondwera’ mwa iye nthaŵi zonse. (Salmo 37:4) Tikatero, mphatso zaulere za Yehova ndi madalitso ake ochuluka zidzatilemeretsa ndipo sizidzawonjezapo chisoni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Onani Galamukani! yachingelezi ya January 22, 1993, masamba 18-21.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi chimwemwe chochuluka tingachipeze kuti?

• Kodi zina mwa mphatso zimene Yehova wapatsa anthu ake ndi ziti?

• N’chifukwa chiyani utumiki wakumunda uli mphatso?

• Kodi makolo angachitenji kuti Mulungu awadalitse polera ana awo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi mumayamikira mphatso ya Mulungu ya Mawu amene iye analemba?

[Chithunzi patsamba 17]

Laurel Nisbet anatumikira Mulungu mwachangu ngakhale anali pamavuto osaneneka

[Zithunzi patsamba 18]

Monga Tabita, Akristu amakono akudziŵika ponseponse chifukwa cha ntchito zawo zachikondi

[Chithunzi patsamba 19]

Akulu achikristu amadera nkhaŵa mwachikondi okhulupirira anzawo