Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwana “Wosakaza” Mungamuthandize Bwanji?

Kodi Mwana “Wosakaza” Mungamuthandize Bwanji?

Kodi Mwana “Wosakaza” Mungamuthandize Bwanji?

‘Tikondwere chifukwa anatayika, ndipo wapezeka.’​—LUKA 15:32.

1, 2. (a) Kodi ana ena achita motani ndi choonadi chachikristu? (b) Kodi makolo ndi ana amene zimenezo zawachitikira angamve bwanji?

“NDIKUSIYA choonadi!” N’zopwetekatu kwambiri kwa makolo oopa Mulungu amene ayesetsa mwakhama kulera ana awo m’njira yachikristu kumva mwana wawo akulankhula zimenezi! Ana ena ‘amangosiya’ osanena n’komwe kuti aganiza zimenezo. (Ahebri 2:1) Ambiri mwa ana ameneŵa amafanana ndi mwana wosakaza wa m’fanizo la Yesu amene anachoka kunyumba kwa atate ake ndi kukawononga choloŵa chake kudziko lakutali.​—Luka 15:11-16.

2 Inde, Mboni za Yehova zambiri sizikumana ndi vuto limeneli. Komabe, kwa amene akumana nalo, palibe mawu otonthoza amene angachotseretu chisoni chawo. Ndiponso taganizani kusoŵa chimwemwe kumene mwana wopulupudzayo angakhale nako. Pansi pa mtima, chikumbumtima chingamuvutitse. M’fanizo la Yesu, mwana wosakazayo m’kupita kwa nthaŵi “anakumbukira mumtima,” ndipo zimenezo zinasangalatsa kwambiri atate ake. Kodi makolo ndi anthu ena mumpingo angathandize bwanji ana osakaza kuti ‘akumbukire mumtima mwawo’?​—Luka 15:17.

Zimene Ana Ena Amasiyira Choonadi

3. Kodi zina mwa zifukwa zimene ana amasankhira kuchoka mumpingo wachikristu n’zotani?

3 Pali ana zikwizikwi amene amatumikira Yehova mosangalala mumpingo wachikristu. Nangano, n’chifukwa chiyani ana ena amasiya choonadi? Mwina amaganiza kuti akuphonya zinthu zabwino zimene dziko likupereka. (2 Timoteo 4:10) Kapena angaganize kuti khola la chitetezo la Yehova ndi lokhwimitsa zinthu. Angasiyenso gulu la Yehova chifukwa chakuti chikumbumtima chikumudzudzula kuti ndi wolakwa, chifukwa chakuti akulakalaka kuti akhale ndi chibwenzi, kapena akufuna kuti anzake azimukonda. Wachinyamata angasiyenso kutumikira Mulungu chifukwa choganiza kuti makolo ake kapena Akristu ena achita chinyengo.

4. Kodi chifukwa chachikulu chimene ana amatayikira n’chiti?

4 Nthaŵi zambiri, maganizo ndi makhalidwe opanduka a mwana amakhala chizindikiro cha kufooka kwauzimu, kusonyeza zimene zili mumtima mwake. (Miyambo 15:13; Mateyu 12:34) Zilibe kanthu kuti mwana watayika pazifukwa ziti, nthaŵi zambiri chifukwa chachikulu chimakhala chakuti alibe “chizindikiritso [“chidziŵitso cholondola,” NW] cha choonadi.” (2 Timoteo 3:7) Ana afunika kukulitsa ubale weniweni ndi Yehova m’malo mongomulambira mwamwambo chabe. Kodi n’chiyani chingawathandize kuti achite zimenezo?

Yandikirani kwa Mulungu

5. Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti wachinyamata akulitse ubale wake ndi Mulungu?

5 “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” analemba motero mtumwi Yakobo. (Yakobo 4:8) Kuti achite zimenezo, wachinyamata afunika kum’thandiza kuti azikonda kwambiri Mawu a Mulungu. (Salmo 34:8) Poyamba adzafuna “mkaka,” zomwe ndi ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Koma akayamba kukonda kwambiri Mawu a Mulungu ndi “chakudya chotafuna”​—mfundo zakuya zauzimu​—sachedwa kukula mwauzimu. (Ahebri 5:11-14; Salmo 1:2) Wachinyamata wina amene anavomera kuti analoŵerera moyo wa dziko, anayamba kukonda zinthu zauzimu. Kodi n’chiyani chinam’thandiza kuti asinthe? Pomvera zimene ena anamuuza zoti aŵerenge Baibulo lonse, anatsatira ndandanda yoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. Inde, kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse n’kofunika kwambiri kuti munthu akulitse ubale wake ndi Yehova.

6, 7. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azikonda kwambiri Mawu a Mulungu?

6 Ndiyetu makolo afunikadi athandize ana awo kuti azikonda kwambiri Mawu a Mulungu. Mtsikana wina anali kugwirizana ndi anzake opulupudza ngakhale anali kupezeka pa phunziro la banja nthaŵi zonse. Posimba za phunziro la banja, iye akukumbukira kuti: “Atate akafunsa mafunso, ndinali kungoŵerenga mayankho ake m’bukumo, osawayang’ana n’komwe atatewo.” Paphunziro la banja, makolo anzeru amagwiritsa ntchito luso lophunzitsa m’malo mongochita phunzirolo mwapatalipatali. (2 Timoteo 4:2) Kuti wachinyamata alikonde phunzirolo, ayenera kuona kuti likumukhudza kwambiri. Bwanji osafunsa mafunso oti afotokoze maganizo ake n’kumva mmene akuyankhira? Mulimbikitseni kuti agwiritse ntchito zimene mukuphunzirazo. *

7 Ndiponso, chititsani kuti kukambirana Malembako kukhale kosangalatsa. Ngati n’koyenera, auzeni anawo kuchita maseŵero a nkhani za m’Baibulo. Athandizeni kuyerekeza m’maganizo mwawo malo ndi zinthu zimene zinali kumalo kumene kunachita nkhani imene mukukambiranayo. Kugwiritsa ntchito mapu ndi matchati kungathandize. Inde, mwa kungoganiza mofatsa kaye, mungachititse phunziro la banja kukhala losangalatsa komanso kukhala ndi mbali zosiyanasiyana. Makolo ayeneranso kupenda ubale wawo ndi Yehova. Akamayandikira kwambiri kwa Yehova, angathandize ana awo kuchitanso chimodzimodzi.​—Deuteronomo 6:5-7.

8. Kodi pemphero limathandiza bwanji kuti munthu ayandikire kwa Mulungu?

8 Pemphero limathandizanso kwambiri kuti munthu ayandikire kwa Mulungu. Mtsikana wina wa zaka zapakati pa 13 ndi 15 zinamuvuta kuti asankhepo chinthu chimodzi. Anafunika kusankha moyo wachikristu kapena kuyanjana ndi anzake omwe anali akunja. (Yakobo 4:4) Nanga anachitanji? Anati: “Koyamba, ndinapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse, kum’fotokozera mmene ndinali kumvera.” Anati pemphero lake linayankhidwa pamene anapeza mnzake mumpingo wachikristu amene akanatha kum’fotokozera zakukhosi. Ataona kuti Yehova anali kum’tsogolera, anayamba kulimbitsa ubale wake ndi Mulungu. Makolo angathandize ana awo mwa kuwongolera mapemphero awo makolowo. Popemphera monga banja, makolo angafotokoze maganizo awo ndi mavuto awo kuchokera pansi pa mtima kuti anawo azimva kuti pali ubale weniweni pakati pa makolowo ndi Yehova.

Muzileza Mtima Komanso Muzilimba

9, 10. Kodi Yehova anapereka chitsanzo chotani pamene analeza mtima kwa Aisrayeli opulupudza?

9 Wachinyamata akayamba kusiya choonadi, angayese kudzipatula ndipo makolo ake akafuna kukambirana naye zinthu zauzimu, angakane. Kodi makolo angatani panthaŵi yovuta ngati imeneyo? Taganizani mmene Yehova anachitira ndi Aisrayeli akale. Analeza mtima kwa Aisrayeli “opulupudza” kwa zaka zoposa 900 asanawasiye kuti atsatire njira zawo zopulupudzazo. (Eksodo 34:9; 2 Mbiri 36:17-21; Aroma 10:21) Yehova ‘anali wachifundo’ ngakhale kuti iwo ‘anamuyesa’ mobwerezabwereza. “Nabweza mkwiyo wake kaŵirikaŵiri, sanautsa ukali wake wonse.” (Salmo 78:38-42) Mulungu sanalakwe pa zonse zimene anawachitira. Makolo achikondi amatsanzira Yehova ndipo amaleza mtima ngati mwanayo sakulabadira mwamsanga pamene iwo akuyesayesa kuti amuthandize.

10 Ndiponso, munthu safunika kutaya mtima poganiza kuti sizitheka kubwezeretsa ubale umene wawonongeka. Yehova anapereka chitsanzo cha mmene tingakhalire oleza mtima. Ndi iye amene anayamba kuchitapo kanthu mwa kutumiza amithenga ake kwa Aisrayeli “mobwerezabwereza.” (NW) Yehova “anamvera chifundo anthu ake” ngakhale kuti anthuwo “ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake.” (2 Mbiri 36:15, 16) Iye anadandaulira Aisrayeli kuti: “Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa.” (Yeremiya 25:4, 5) Komabe, Yehova sanasinthe miyezo yake yolungama. Anawalangiza Aisrayeli kuti ‘abwerere’ kwa iye ndi kutsata njira zake.

11. Kodi makolo angatani kuti akhale oleza mtima komabe olimba pothandiza mwana amene wapanduka?

11 Makolo angatsanzire kuleza mtima kwa Yehova mwa kusatayiratu mtima mofulumira pamene mwana wapanduka. Popanda kutaya mtima, angachitepo kanthu kuti apitirize kukambirana kapena kuti ayambenso kukambirana ndi mwanayo. Angamuthandize “mobwerezabwereza” kuti abwerere m’njira ya choonadi komabe iwo osasiya kutsata mfundo zolungama zachikhalidwe.

Mwana Wamng’ono Akamuchotsa mu Mpingo

12. Kodi makolo amene akukhala ndi mwana wamng’ono yemwe amuchotsa mu mpingo ali ndi udindo wotani kwa mwanayo?

12 Bwanji ngati mwana wamng’ono amene akukhala ndi makolo ake wachita tchimo lalikulu ndipo amuchotsa mu mpingo chifukwa cha kusalapa kwake? Popeza mwanayo akukhala ndi makolo ake, iwo akali ndi udindo wom’phunzitsa ndi kumulangiza mogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Kodi angachite bwanji zimenezi?​—Miyambo 6:20-22; 29:17.

13. Kodi makolo angayese motani kum’fika pamtima mwana wolakwa?

13 Zingatheke​—ndipo zingakhale bwino kwambiri​—kum’phunzitsa ndi kumulangiza mwa njira imeneyo pophunzira naye Baibulo payekha. Makolo asangoganiza za kukanika kwa mwanayo koma ayese kuona zimene zili mumtima mwake. Kodi makamaka matenda ake auzimuwo ndi aakulu bwanji? (Miyambo 20:5) Kodi mungathe kum’fika pamtima m’mbali zina? Kodi ndi malemba ati amene mungawagwiritse ntchito kuti amugwire mtima? Mtumwi Paulo akutitsimikizira kuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Inde, makolo angachite zambiri osati kungomuuza chabe mwana wawoyo kuti asadzalakwenso. Angayambe ndi kupitiriza kumuthandiza kuti achire.

14. Kodi njira yoyamba imene mwana amene walakwa angatsatire kuti abwezeretse ubale wake ndi Yehova ndi iti, ndipo kodi makolo angamuthandize bwanji mwanayo kuti atsate njira imeneyo?

14 Mwana amene walakwa afunika kubwezeretsa ubale wake ndi Yehova. Chinthu choyamba chimene afunika kuchita ndicho ‘kulapa ndi kubwerera.’ (Machitidwe 3:19; Yesaya 55:6, 7) Pothandiza mwana wawo panyumba pawo kuti alape, makolo afunika ‘kuleza ndi kulangiza mofatsa’ mwana amene alibe chidwi. (2 Timoteo 2:24-26) Afunika ‘kum’dzudzula’ m’lingaliro la Baibulo. Liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti ‘kudzudzula’ lingamasuliridwenso kuti “kupereka umboni wokhutiritsa.” (Chivumbulutso 3:19; Yohane 16:8) Choncho, kudzudzula kumaphatikizaponso kusonyeza umboni wokwanira kuti mwanayo akhutire kuti zimene anachitazo n’zolakwikadi. N’zoona kuti kuchita zimenezo n’kovuta. Kukakhala kotheka, makolo angam’fike pamtima mwa kugwiritsa ntchito njira zonse zoyenera za m’Malemba kuti amukhutiritse. Ayesetse kum’thandiza kuti amvetse kufunika kwa ‘kudana nacho choipa ndi kukonda chokoma.’ (Amosi 5:15) Mwina angabwerere ndi ‘kudzipulumutsa ku msampha wa Mdyerekezi.’

15. Kodi pemphero limathandiza motani pobwezeretsa ubale wa munthu amene walakwa ndi Yehova?

15 Pemphero ndi lofunika kwambiri munthu akamafuna kubwezeretsa ubale wake ndi Yehova. Inde, palibe amene ayenera ‘kupempherera’ tchimo loonekeratu limene munthu amene anali kusonkhana ndi mpingo wachikristu akulichita mosalapa. (1 Yohane 5:16, 17; Yeremiya 7:16-20; Ahebri 10:26, 27) Komabe, makolo angapemphe Yehova kuti awapatse nzeru za mmene angachitire ndi nkhaniyo. (Yakobo 1:5) Ngati mwana wochotsedwayo akusonyeza umboni wa kulapa koma alibe “ufulu wa kulankhula ndi Mulungu,” makolo angapemphere kuti ngati Mulungu wapeza maziko okhululukira mphulupulu ya mwanayo, chifuniro Chake chichitike. (1 Yohane 3:21, NW) Kumva mapemphero ameneŵa kungamuthandize mwanayo kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo. *​—Eksodo 34:6, 7; Yakobo 5:16.

16. Kodi tingawathandize bwanji a m’mabanja amene ana awo aang’ono anachotsedwa?

16 Ngati mwana amene anabatizidwa wachotsedwa, anthu a mumpingo sayenera ‘kuyanjana naye.’ (1 Akorinto 5:11; 2 Yohane 10, 11) M’kupita kwa nthaŵi, zimenezi zingamuthandize ‘kukumbukira mumtima’ mwake ndi kubwerera kugulu lotetezeka la Mulungu. (Luka 15:17) Komabe, kaya abwerera kapena ayi, abale ndi alongo mumpingo angalimbikitse banja limene lili ndi mwana wochotsedwayo. Tonsefe tingafufuze mipata yosonyezera “chifundo” ndi kulimvera ‘chisoni’ banjalo.​—1 Petro 3:8, 9.

Mmene Ena Angathandizire

17. Kodi anthu mumpingo ayenera kukumbukira chiyani poyesa kuthandiza mwana wotayika?

17 Nanga bwanji za mwana amene sanam’chotse mumpingo wachikristu koma wafooka m’chikhulupiriro? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chingakhale chiwalo chimodzi chimva choŵaŵa, ziwalo zonse zimva pamodzi [naye].” (1 Akorinto 12:26) Ena angafune kumuthandiza mwana woteroyo. Komabe, m’pofunika kusamala kwambiri chifukwa mwana wodwala mwauzimu angasocheretse ana ena. (Agalatiya 5:7-9) Mumpingo wina, achikulire omwe anali ndi zolinga zabwino anafuna kuthandiza ana ena amene anafooka mwauzimu. Anawaitana kuti akacheze ndi kumvera limodzi nyimbo zotchuka. Ngakhale kuti achinyamatawo anagwirizana nazo ndipo anasangalala ndi machezawo, m’kupita kwa nthaŵi anasiya kusonkhana ndi mpingo chifukwa cha kusonkhezerana kwawo wina ndi mnzake. (1 Akorinto 15:33; Yuda 22, 23) Macheza amene angathandize kukonda kwambiri zinthu zauzimu ndi amene angachiritse mwana wodwala mwauzimu osati macheza opanda malangizo auzimu. *

18. Kodi tingatsanzire motani mzimu wa atate a mwana wosakaza wa m’fanizo la Yesu?

18 Taganizani mmene Mwana amene anasiya mpingo amamvera mumtima mwake akabweranso ku Nyumba ya Ufumu kapena kupezeka pa msonkhano waukulu. Kodi sitiyenera kum’landira ndi manja aŵiri monga mmene anachitira atate a mwana wosakaza wa m’fanizo la Yesu? (Luka 15:18-20, 25-32) Mnyamata wina amene anasiya mpingo wachikristu ndiyeno n’kudzapezeka pamsonkhano wachigawo anati: “Ndinaganiza kuti aliyense andinyalanyaza, koma abale ndi alongo anabwera kudzandilandira. Zinandikhudza mtima kwambiri.” Anayamba kuphunziranso Baibulo ndipo anabatizidwa.

Musataye Mtima

19, 20. N’chifukwa chiyani tingayembekezebe kuti mwana wosakaza atha kudzasintha?

19 Kuthandiza mwana “wosakaza” kuti ‘akumbukire mumtima’ mwake kumafuna kuleza mtima ndipo kungawavute makolowo ndi anthu ena. Koma musataye mtima. “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Malemba akutitsimikizira kuti Yehova akufuna kuti anthu alape ndi kukhala ndi moyo. Ndipotu ndi iye amene anayamba kuchitapo kanthu mwa kukonza zowayanjanitsa anthu kwa iye mwini. (2 Akorinto 5:18, 19) Kuleza mtima kwake kwatheketsa anthu miyandamiyanda kutembenukira kwa iye.​—Yesaya 2:2, 3.

20 Motero, kodi makolo safunika kugwiritsa ntchito njira iliyonse ya Malemba kuthandiza mwana wawo wamng’ono wosakaza kuti akumbukire mumtima mwake? Tsanzirani Yehova, lezani mtima pamene mukutsatira njira zoyenera kuti muthandize mwana wanu kubwerera kwa Yehova. Tsatirani zolimba mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo, ndipo yesani kusonyeza makhalidwe a Yehova monga chikondi, chilungamo, ndi nzeru ndiponso kum’pempha kuti akuthandizeni. Mwana wanu wosakaza kaya wamwamuna kapena wamkazi angabwerere m’gulu lotetezeka la Yehova monga mmene achitira anthu ambiri opanduka polabadira kuitana kwachikondi kwa Yehova kuti abwerere.​—Luka 15:6, 7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani mfundo zina za mmene mungaphunzitsire ana mogwira mtima mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999, masamba 13-17.

^ ndime 15 Mapemphero ngati ameneŵa m’malo mwa mwana wamng’ono wochotsedwayo sayenera kuperekedwa poyera pamisonkhano ya mpingo, chifukwa ena mwina sakudziŵa mmene munthuyo akuchitira.​—Onani Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya October 15, 1979, tsamba 31.

^ ndime 17 Onani mfundo zapadera mu Galamukani! ya Chingelezi ya June 22, 1972 masamba 13-16 ndi ya Chicheŵa ya October 8, 1996, masamba 28-30.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi chifukwa chachikulu chimene chimachititsa ana kusiya mpingo n’chiyani?

• Kodi mungathandize bwanji ana kuti akulitse ubale weniweni ndi Yehova?

• N’chifukwa chiyani makolo afunika kuleza mtima komanso kulimba pothandiza mwana wosakaza?

• Kodi anthu mumpingo angamuthandize bwanji mwana wosakaza kuti abwerere?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Kuŵerenga Mawu a Mulungu n’kofunika kwambiri pokulitsa ubale weniweni ndi Yehova

[Chithunzi patsamba 15]

Pemphero la makolo lochokera pansi pa mtima lingathandize ana awo kuona kuti pali ubale weniweni pakati pa iwo ndi Yehova

[Chithunzi patsamba 17]

Mulandireni mwana wosakaza ‘akakumbukira mumtima’ mwake

[Chithunzi patsamba 18]

Tsatirani njira zoyenera kuti muthandize mwana wanu kubwerera kwa Yehova