Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni—Kodi N’kothekanso Lerolino?
Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni—Kodi N’kothekanso Lerolino?
“Chikhulupiriro ndicho kudalira chisomo cha Mulungu molimba mtima ndipo wokhulupirirayo amakhala wotsimikiza ndiponso wosakayikira moti atha kulolera kuika moyo wake pachiswe kambirimbiri,” anatero MARTIN LUTHER MU 1522.
“Anthu ambiri lerolino sititsatira n’komwe chikhulupiriro ndi zochita zachikristu,” anatero LUDOVIC KENNEDY MU 1999.
MAGANIZO okhudza chikhulupiriro amasiyanasiyana kwambiri. Kukhulupirira Mulungu kunali kofala kwambiri mmbuyomu. Masiku ano, m’dziko la anthu okayikira ndiponso lamavutoli, kukhulupirira Mulungu ndi Baibulo kukuzilala mofulumira kwambiri.
Chikhulupiriro Chenicheni
Kwa anthu ambiri, “chikhulupiriro” chimangotanthauza kukhulupirira zomwe chipembedzo chinachake chimaphunzitsa kapena kutsatira kulambira kwinakwake. Koma m’Baibulo mawu akuti “chikhulupiriro” kwenikweni amatanthauza kutsimikiza ndi mtima wonse kudalira Mulungu ndi malonjezo ake. Chikhulupiriro choterocho ndi chizindikiro cha ophunzira a Yesu Kristu.
Nthaŵi ina, Yesu Kristu anatchulapo za kufunika kopemphera nthaŵi zonse, “osafooka mtima.” Potchula mfundo imeneyi, anafunsa ngati chikhulupiriro chenicheni chidzakhalapo n’komwe m’masiku athu ano. Iye anafunsa kuti: “Mwana wamunthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro [ichi] padziko lapansi kodi?” N’chifukwa chiyani anafunsa funso limeneli?—Luka 18:1, 8.
Kutaya Chikhulupiriro
Anthu angataye chikhulupiriro chomwe angakhale nacho pazifukwa zambiri. Zina zomwe zimachititsa zimenezi ndi masoka komanso mayesero a tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, Pulofesa Michael Goulder anali wansembe paparishi ya ku Manchester m’dziko la England panthaŵi yomwe anthu ambiri a m’timu yampira wamiyendo ya Manchester United anafa pangozi ya ndege ku Munich m’dziko la Germany mu 1958. Papulogalamu yapawailesi yakanema ya BBC, woulutsa nkhani Joan Bakewell anafotokoza kuti Goulder “anataya mtima kwambiri ataona kukula kwa chisoni chomwe anthu anali nacho.” Zotsatira zake zinali zakuti
“anasiya kukhulupirira Mulungu amene amapulumutsa anthu panthaŵi yatsoka.” Goulder ananena kuti anali kukhulupirira kuti “Baibulo si . . . mawu osalephera a Mulungu” koma kuti ndi “mawu olephera aanthu mwina osakanikirana mwa apo ndi apo ndi mawu ouziridwa a Mulungu.”Nthaŵi zina chikhulupiriro chimangozilala. Zimenezo ndizo zinam’chitikira Ludovic Kennedy yemwe amalemba mabuku ndi kuulutsa nkhani pawailesi. Iye ananena kuti, kuyambira ali mwana “maganizo okayikira [Mulungu] anali ku[mu]bwerera nthaŵi ndi nthaŵi ndipo kusakhulupirira [kwake] [Mulungu] kunakula.” Zikuoneka kuti panalibe amene anamuyankha mafunso ake mogwira mtima. Imfa yadzidzidzi ya abambo ake panyanja inafooketsa kwambiri chikhulupiriro chake chomwe chinali chofooka n’kale. Mapemphero opita kwa Mulungu kuti “atipulumutse ku ngozi zapanyanja ndiponso kwa adani” sanayankhidwe chifukwa sitima yapamadzi yomwe munakwera abambo a Kennedy inaphwasulidwa ndi sitima zankhondo zapamadzi za ku Germany pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse.—Linatero buku lakuti All in the Mind—A Farewell to God.
Zochitika ngati zimenezi sizachilendo. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi kukhulupirira Mulungu ndi Mawu ake n’kothekanso lerolino m’dziko lomwe kukayikira kukukulirakulira? Tamvani zomwe nkhani yotsatirayi ikunena pankhani imeneyi.