Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi “mpumulo” umene akuunena pa Ahebri 4:9-11 n’chiyani, ndipo munthu ‘amaloŵa mpumulowo’ motani?
Mtumwi Paulo anawalembera Akristu achihebri a zaka za zana loyamba kuti: “Utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu. Pakuti iye amene adaloŵa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake ku ntchito zake, monganso Mulungu ku zake za Iye. Chifukwa chake tichite changu cha kuloŵa mpumulowo.”—Ahebri 4:9-11.
Paulo ponena za kupumula kwa Mulungu ku ntchito Zake, mwachionekere anali kufotokoza zimene zili pa Genesis 2:2, pamene timaŵerenga kuti: “Tsiku lachisanu ndi chiŵiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ku ntchito yake yonse.” N’chifukwa chiyani Yehova “anapuma tsiku lachisanu ndi chiŵiri?” Kunena zoona sikuti anapuma chifukwa chakuti anafuna kupezanso mphamvu chifukwa cha “ntchito yake yonse.” Vesi yotsatira ikutithandiza kupeza chifukwa chake. Ikuti: “Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo anapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.”—Genesis 2:3; Yesaya 40:26, 28.
“Tsiku lachisanu ndi chiŵiri” linali losiyana ndi masiku asanu ndi limodzi oyambawo mu lingaliro lakuti linali tsiku limene Mulungu analidalitsa ndi kuliyeretsa, ndiko kuti, analisankha kapena kulipatula ndi cholinga chapadera. Kodi chinali cholinga chanji? Poyambirira, Mulungu anavumbula cholinga chake kwa anthu ndi dziko lapansi. Mulungu anauza mwamuna woyambayo ndi mkazi wake kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.” (Genesis 1:28) Ngakhale kuti Mulungu analenga dziko lapansi ndi munthu wangwiro, pakanapita nthaŵi kuti aligonjetse dziko lapansi ndi kulikonza kuti likhale paradaiso wodzala ndi mabanja a anthu angwiro, malinga ndi mmene Mulungu anafunira. Motero, “tsiku lachisanu ndi chiŵiri,” Mulungu anapuma kapena kusiya kulenga zinthu zina za padziko lapansi kuti apatse mpata zinthu zimene anazilenga kale kuti zichulukane mogwirizana ndi chifuniro chake. Pakutha “tsiku” limenelo, zonse zimene iye anafuna zikanachitikadi. Kodi mpumulowo ndi wanthaŵi yaitali motani?
Tikabwerera ku zimene Paulo anawauza Ahebri, tikuona kuti ananena kuti “utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu,” ndipo analimbikitsa Akristu anzake kuti achite changu “cha kuloŵa mpumulowo.” Zimenezi zikusonyeza kuti nthaŵi imene Paulo analemba mawu ameneŵa, “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” la kupumula kwa Mulungu, limene linayamba zaka pafupifupi 4,000 m’mbuyo mwakemo, linalipobe. Silidzatha mpaka cholinga cha Mulungu kwa anthu ndi dziko lapansi atachikwaniritsa bwinobwino pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Kristu, yemwe ndi “mwini tsiku la Sabata.”—Mateyu 12:8; Chivumbulutso 20:1-6; 21:1-4.
Paulo akuganiza za chiyembekezo chodabwitsa chimenecho, anafotokoza mmene munthu angaloŵere mpumulo wa Mulungu. Analemba kuti: “Iye amene adaloŵa mpumulo [wa Mulungu], adapumulanso mwini wake ku ntchito zake.” Zimenezi zikutiphunzitsa kuti ngakhale chiyambi cha anthu chinali changwiro, iwo sanaloŵe mpumulo wa Mulungu. Zinali choncho chifukwa chakuti Adamu ndi Hava sanasunge mpumulo wa Mulungu kwa nthaŵi yaitali pa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” mwa kuvomereza zimene iye anawakonzera. M’malo mwake, anapanduka ndipo anafuna kuti adziimire paokha, osadalira Mulungu. Ndipotu, anatsatira zolinga za Satana m’malo movomereza malangizo achikondi a Mulungu. (Genesis 2:15-17) Zotsatira zake zinali zakuti anataya mwayi wokhala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Kuyambira pamenepo, anthu onse anakhala akapolo a uchimo ndi imfa.—Aroma 5:12, 14.
Kupanduka kwa anthu sikunalepheretse cholinga cha Mulungu. Tsiku lake lopuma likupitirira. Komabe, Yehova anapanga makonzedwe achikondi a dipo kupyolera mwa Mwana wake Yesu Kristu, kuti onse amene angalivomereze mwa kukhulupirira angayembekeze kuti adzawamasula ku goli la uchimo ndi imfa. (Aroma 6:23) N’chifukwa chake Paulo analimbikitsa Akristu anzake ‘kupumula ku ntchito zawo.’ Anafunika kuvomereza makonzedwe achikondi a Yehova oti apulumuke, osati kuyesa kukonza okha tsogolo lawo, monga mmene anachitira Adamu ndi Hava. Anafunikanso kupeŵa kutsatira zochita zawo zofuna kudzilungamitsa.
Kumakhala kotsitsimula ndiponso kopatsa mpumulo kwambiri ngati munthu asiya zochita zadyera kapena zopanda pake kuti achite zimene Mulungu akufuna. Yesu anaitana motere: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
Kufotokoza kwa Paulo za mpumulo wa Mulungu ndi mmene munthu angauloŵere kunalidi kolimbikitsa kwa Akristu achihebri a ku Yerusalemu, amene anapirira kwambiri pamene anthu anawazunza ndi kuwanyoza chifukwa cha zimene anali kukhulupirira. (Machitidwe 8:1; 12:1-5) Mofananamo, zimene Paulo ananena zingalimbikitse Akristu lerolino. Ifenso, podziŵa kuti zimene Mulungu analonjeza kuti adzabweretsa dziko lapansi la paradaiso mu Ufumu wake wolungama watsala pang’ono kuzikwaniritsa, tiyenera kupumula ku ntchito zathu ndi kuchita changu kuloŵa mpumulowo.—Mateyu 6:10, 33; 2 Petro 3: 13.
[Zithunzi patsamba 31]
Lonjezo la Mulungu la dziko latsopano adzalikwaniritsa pamapeto pa tsiku lake la mpumulo