Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Yehova Pophunzitsa Ana Anu

Tsanzirani Yehova Pophunzitsa Ana Anu

Tsanzirani Yehova Pophunzitsa Ana Anu

“Kodi makolo onse salangiza ana awo?”​—AHEBRI 12:7, Contemporary English Version.

1, 2. N’chifukwa chiyani makolo amavutika polera ana awo masiku ano?

KUFUFUZA kumene anachita ku Japan zaka zingapo zapitazo kunavumbula kuti pafupifupi theka la achikulire amene anawafunsa anaona kuti nthaŵi zambiri makolo salankhulana ndi ana awo ndi kuti akuwalekerera anawo mopitirira muyeso. Pakufufuza kwinanso kumene anachita m’dziko lomwelo, pafupifupi munthu mmodzi mwa anayi alionse amene anayankha anavomereza kuti sanali kudziŵa mmene angalankhulire ndi ana awo. Vuto limeneli silili kumayiko a Kum’maŵa okha. Nyuzipepala ya The Toronto Star inati: “Makolo ambiri a ku Canada anavomereza kuti sadziŵa mmene angakhalire makolo abwino.” Makolo kulikonse akuvutika kuti alere ana awo.

2 Kodi n’chifukwa chiyani makolo akuvutika kuti alere ana awo? Chifukwa chachikulu n’chakuti tikukhala mu “masiku otsiriza” ndipo “nthaŵi zoŵaŵitsa” zafikadi. (2 Timoteo 3:1) Ndiponso, “ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake,” Baibulo likutero. (Genesis 8:21) Achinyamata alinso pangozi yaikulu youkiridwa mosavuta ndi Satana amene, monga “mkango wobuma,” amagwira anthu amene sadziŵa zambiri. (1 Petro 5:8) Makolo achikristu amavutikadi kwambiri pofuna kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Kodi makolo angathandize motani ana awo kuti akule ndi kukhala olambira Yehova okhwima maganizo omwe angathe kusiyanitsa “chabwino ndi choipa”?​—Ahebri 5:14.

3. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuti makolo aziphunzitsa ndi kutsogolera ana awo kuti akule bwinobwino?

3 Mfumu yanzeru Solomo inati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” (Miyambo 13:1; 22:15) Makolo afunika kulangiza ana awo mwachikondi kuti utsiru umenewo uchoke m’mitima yawo. Komabe, achinyamata nthaŵi zina amakana malangizo oterowo. Nthaŵi zina amaipidwa kwambiri ndi malangizo mosaganizira kuti akuwalangizayo ndani. Motero, makolo aphunzire ‘kuphunzitsa mwana poyamba njira yake.’ (Miyambo 22:6) Ana akatsatira malangizo amenewo angathe kudzakhala ndi moyo. (Miyambo 4:13) Ndiyetu n’kofunika kuti makolo adziŵe zimene zimafunika pophunzitsa ana awo.

Tanthauzo la Kulanga

4. Kodi tanthauzo lalikulu la “kulanga” monga momwe analigwiritsira ntchito m’Baibulo n’chiyani?

4 Makolo ena salanga ana awo poopa kuti anthu ena aziwanena kuti akuzunza ana awowo kuthupi, mwa mawu, kapena m’maganizo. Tisakhale ndi mantha amenewo. Liwu lakuti “kulanga” monga mmene aligwiritsira ntchito m’Baibulo silitanthauza kuzunza kapena kuchita nkhanza. Tanthauzo lalikulu la liwu la Chigiriki limene analimasulira kuti “kulanga” ndilo kulangiza, kuphunzitsa, kuwongolera, ndipo nthaŵi zina kukwapula ndithu koma mwachikondi.

5. N’chifukwa chiyani n’kopindulitsa kupenda mmene Yehova amachitira ndi anthu ake?

5 Yehova Mulungu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pakulanga koteroko. Mtumwi Paulo anayerekeza Yehova ndi tate waumunthu. Anati: “Kodi makolo onse salangiza ana awo? . . . Atate athu aumunthu amatilangiza kwa nthaŵi yochepa, ndipo amachita zimenezo akaona kuti n’koyenera kutero. Koma Mulungu amatilangiza kuti tipindule, chifukwa akufuna kuti tikhale oyera.” (Ahebri 12:7-10, Contemporary English Version) Inde, Yehova amalanga anthu ake n’cholinga choti akhale oyera kapena opanda banga. Tingaphunziredi zambiri pankhani ya kulanga ana mwa kupenda mmene Yehova waphunzitsira anthu ake.​—Deuteronomo 32:4; Mateyu 7:11; Aefeso 5:1.

Chikondi​—Mphamvu Yolimbikitsa

6. Kodi n’chifukwa chiyani kungakhale kovuta kuti makolo atsanzire chikondi cha Yehova?

6 Mtumwi Yohane ananena kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” Ndiyetu, Yehova amatiphunzitsa chifukwa chotikonda. (1 Yohane 4:8; Miyambo 3:11, 12) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti makolo amene akuwakonda ana awo mwachibadwa sikungawavute kutsanzira Yehova pankhani imeneyi? Ayi. Chikondi cha Mulungu n’chozikidwa pa mfundo zachikhalidwe. Katswiri wina wa Chigiriki ananena kuti chikondi chimenecho “nthaŵi zina n’chosiyana ndi chikondi chachibadwa.” Mulungu sachita zinthu chifukwa chongotengeka maganizo. Nthaŵi zonse amaganizira zimene zithandize kwambiri anthu ake.​—Yesaya 30:20; 48:17.

7, 8. (a) Kodi Yehova anapereka chitsanzo chotani cha chikondi chozikidwa pa mfundo zachikhalidwe posamala anthu ake? (b) Kodi makolo angatsanzire motani Yehova pothandiza ana awo kuti akulitse luso lotsatira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo?

7 Taganizani mmene Yehova anaonetsera chikondi kwa Aisrayeli. Mose anagwiritsa ntchito fanizo lokhudza mtima pofotokoza mmene Yehova anaukondera mtundu waung’ono wa Israyeli. Timaŵerenga kuti: “Monga mphungu ikasula chisa chake, nikapakapa pa ana ake, Iye anayala mapiko ake, nawalandira, nawanyamula pamapiko ake; Yehova yekha anam’tsogolera [Yakobo].” (Deuteronomo 32:9, 11, 12) Mphungu yaikazi pofuna kuphunzitsa ana ake kuuluka, ‘imakasula chisa chake,’ ndipo imagwedeza ndi kukupiza mapiko ake n’cholinga chowalimbikitsa anawo kuti ayambe kuuluka. Mwana wakeyo akadumpha kuchoka m’chisamo, chimene nthaŵi zambiri chimakhala pathanthwe lotsetsereka, mayiyo ‘amakapakapa’ pa mwana wakeyo. Akaona kuti mwana wakeyo agwa, mayiyo amaulukira pansi pa mwanayo, ndi kum’nyamula ‘pamapiko ake.’ Yehova mwachikondi anasamaliranso chimodzimodzi mtundu wa Israyeli umene unali utangobadwa kumene. Anawapatsa anthuwo Chilamulo cha Mose. (Salmo 78:5-7) Ndiyeno Mulungu anateteza mtundu wakewo mosamala ndipo anali wokonzeka kuwapulumutsa akagwa m’mavuto.

8 Kodi makolo achikristu angatsanzire motani chikondi cha Yehova? Choyamba, ayenera kuphunzitsa ana awo mfundo zachikhalidwe ndi miyezo imene ili m’Mawu a Mulungu. (Deuteronomo 6:4-9) Cholinga n’chakuti amuthandize mwanayo kuphunzira kusankha zochita motsatira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo. Pochita zimenezi, makolo achikondi amaona mmene anawo akugwiritsira ntchito mfundo zachikhalidwe zimene aphunzirazo, motero tinganene kuti amakapakapa pa ana awowo. Anawo akamakula ndi kuwapatsa pang’onopang’ono ufulu wokulirapo, makolo achikondi amakhala okonzeka ‘kuulukira pansi’ ndi ‘kuwanyamula ana awo pa mapiko awo’ ngati iwo ali pangozi. Ngozi yotani?

9. Kodi ndi ngozi iti makamaka imene makolo ayenera kukhala nayo tcheru? Perekani chitsanzo.

9 Yehova Mulungu anawachenjeza Aisrayeli za kuopsa koyanjana ndi anthu oipa. (Numeri 25:1-18; Ezara 10:10-14) Kuyanjana ndi anthu osayenera ndi ngozi yaikulunso lerolino. (1 Akorinto 15:33) Makolo achikristu ayenera kutsanzira Yehova pankhani imeneyi. Mtsikana wina wazaka 15 dzina lake Lisa, anafuna kuti akhale pachibwenzi ndi mnyamata wina yemwe makhalidwe ake ndi maganizo ake pa zauzimu anali osiyana ndi a m’banja la Lisa. Lisa akuti: “Makolo anga anaona mwamsanga kuti ndasintha ndipo anada nkhaŵa. Nthaŵi zina anali kundilangiza ndipo nthaŵi zina anali kundilimbikitsa mokoma mtima.” Anakhala pansi ndi Lisa ndi kumvetsera maganizo ake moleza mtima. Mwa kuchita zimenezo, anamuthandiza kuti athane ndi vuto lomwe iwo anaona kuti n’limene linayambitsa zonsezi​—kufuna kuti anzake amuyanje. *

Pitirizani Kulankhulana Kwabwino

10. Kodi Yehova anapereka motani chitsanzo chabwino polankhula ndi Aisrayeli?

10 Makolo ayesetse kupitiriza kulankhulana kwabwino ndi ana awo kuti apambane pakuwaphunzitsa. Yehova amatilimbikitsa kuti tizilankhula naye ngakhale kuti amadziŵa zimene zili m’mitima yathu. (1 Mbiri 28:9) Yehova atawapatsa Chilamulo Aisrayeli, anasankha Alevi kuti aziwaphunzitsa ndipo anatumiza aneneri kuti azikalankhula nawo ndi kuwalangiza. Ndiponso anafunitsitsa kumva mapemphero awo.​—2 Mbiri 17:7-9; Salmo 65:2; Yesaya 1:1-3, 18-20; Yeremiya 25:4; Agalatiya 3:22-24.

11. (a) Kodi makolo angalimbikitse motani kulankhulana kwabwino ndi ana awo? (b) Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kuti makolo azimvetsera bwino polankhulana ndi ana awo?

11 Kodi makolo angatsanzire motani Yehova polankhulana ndi ana awo? Choyamba ndiponso chofunika kwambiri ndicho kupatula nthaŵi yolankhula nawo. Ayeneranso kupeŵa kulankhula kopanda nzeru, konyoza, monga kuti, “Kankhani kake kameneka basi? Ndimayesatu ndi nkhani yofunika”; “Zopanda pake zimenezo”; “Tsono iwe umaganiza kuti zikhala bwanji? Iwe ndiwe mwana basi.” (Miyambo 12:18) Makolo anzeru amayesetsa kuwamvetsera bwino ana awo kuti awalimbikitse kukhala omasuka kulankhula nawo. Makolo amene amanyalanyaza ana awo akali aang’ono angapeze kuti nawonso anawo akakula akunyalanyaza makolowo. Yehova nthaŵi zonse amafunitsitsa kumvetsera anthu ake. Amawamvera anthu amene amalankhula naye modzichepetsa kudzera m’pemphero.​—Salmo 91:15; Yeremiya 29:12; Luka 11:9-13.

12. Kodi makolo angaonetse makhalidwe otani amene angachititse kuti ana awo alankhule nawo mosavuta?

12 Taganizaninso mmene makhalidwe ena a Mulungu achititsira kuti anthu ake azilankhula naye momasuka. Mwachitsanzo, Mfumu Davide ya Israyeli wakale inachimwa kwambiri mwa kuchita chigololo ndi Bateseba. Davide, monga munthu wopanda ungwiro, anachita machimo ena aakulu pamoyo wake. Komabe, sanaleke kulankhula ndi Yehova ndi kum’pempha kuti amukhululukire ndi kum’dzudzula. Mosakayika, kukoma mtima kwa Mulungu ndi chifundo chake zinam’chititsa Davide kubwerera kwa Yehova mosavuta. (Salmo 103:8) Mwa kuonetsa makhalidwe aumulungu monga chifundo ndi kukoma mtima, makolo angathandize kuti kulankhulana kwabwino kupitirire ngakhale anawo alakwa.​—Salmo 103:13; Malaki 3:17.

Khalani Wololera

13. Kodi kukhala wololera kumaphatikizapo chiyani?

13 Makolo akhale ololera ndi kusonyeza “nzeru yochokera kumwamba” pomvetsera ana awo. (Yakobo 3:17) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kufatsa [“Kulolera,” NW] kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.” (Afilipi 4:5) Kodi kukhala wololera kumatanthauzanji? Tanthauzo lina la liwu la Chigiriki limene anatembenuza kuti “kulolera” ndilo “kusaumirira malamulo monkitsa.” Kodi makolo angakhale bwanji ololera pamene akulimbikitsa makhalidwe ndi miyezo yosasinthika yauzimu?

14. Kodi Yehova anasonyeza motani kulolera pochita ndi Loti?

14 Yehova ndi chitsanzo chabwino pankhani ya kulolera. (Salmo 10:17) Loti “anachedwa” Yehova atamuuza kuti iye ndi banja lake atuluke mu mzinda wa Sodomu umene anafuna kuuwononga. Kenaka, mngelo wa Yehova atamuuza kuti athaŵire ku phiri, Loti anati: “Ine sindikhoza kuthaŵira ku phiri . . . taonanitu, mudzi uwu [Zoari] uli pafupi pothaŵirapo, ndipo uli waung’ono; ndithaŵiretu kumeneko, suli waung’ono nanga?” Kodi Yehova anamuyankha bwanji? Anati: “Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzawononga mudzi uwu umene wandiuza.” (Genesis 19:16-21, 30) Yehova anavomereza zimene Loti anapempha. Inde, makolo afunika kutsatira miyezo ya Yehova Mulungu imene ili m’Mawu ake, Baibulo. Komabe mungavomereze zofuna za anawo ngati sizikuphwanya mfundo zachikhalidwe za Baibulo.

15, 16. Kodi makolo angaphunzire chiyani ndi fanizo limene lili pa Yesaya 28:24, 25?

15 Kukhala wololera kumaphatikizapo kukonzekeretsa mitima ya ana kuti athe kulandira uphungu. Yesaya anafotokoza fanizo limene anayerekeza Yehova ndi mlimi. Anati: “Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? Kodi amachocholabe, ndi kuswa zibuma za nthaka? Atakonza tyatyatya pamwamba pake, kodi safesa ponse maŵere, ndi kumwazamwaza chitowe, nafetsa tirigu m’mizere ndi barele m’malo ake osankhika, ndi mcheŵere m’maliremo?”​—Yesaya 28:24, 25.

16 Yehova ‘amalima kuti abzale’ ndipo ‘amachochola, ndi kuswa zibuma za nthaka.’ Motero amakonzekeretsa mitima ya anthu ake asanawalange. Kodi makolo ‘angalime’ motani mtima wa mwana wawo pomulangiza? Tate wina anatsanzira Yehova polangiza mwana wake wa zaka zinayi. Mwana wake atamenya mnzake, tateyo choyamba anamvetsera moleza mtima pamene mwanayo anali kufotokoza chifukwa chake anachita zimenezo. Ndiyeno, pochita ngati ‘akulima’ mtima wa mwanayo, tateyo anasimba nkhani ya mwana wina amene munthu wina wankhanza anam’zunza. Mwana wakeyo atamvetsera nkhaniyo, zinam’khudza mtima ndipo ananena kuti munthu wankhanzayo afunika kulandira chilango. ‘Kulima’ kumeneko kunakonzekeretsa mtima wa mwanayo ndipo sizinam’vute kuzindikira kuti pomenya mnzakeyo iye anafanana ndi munthu wankhanzayo ndipo analakwa.​—2 Samueli 12:1-14

17. Kodi pa Yesaya 28:26-29 pali phunziro lotani la mmene makolo angalangizire ana awo?

17 Yesaya anayerekezanso kulangiza kwa Yehova ndi ntchito ina yaulimi​—kupuntha. Mlimi amagwiritsa ntchito zipangizo zopunthira zosiyanasiyana malinga ndi kulimba kwa mankhusu a mbewuzo. Amagwiritsa ntchito munsi popuntha maŵere ndipo chibonga amachigwiritsa ntchito popuntha chitowe. Koma chopunthira chachitsulo kapena njinga ya galeta amazigwiritsa ntchito popuntha mbewu zimene zili ndi mankhusu olimba kwambiri. Komabe, mlimiyo sapuntha mbewu zolimbazo mpaka kuziphwanya. N’chimodzimodzinso ndi Yehova akafuna kuchotsa choipa mwa anthu ake, amachita zimenezo m’njira zosiyanasiyana malinga ndi zimene zikufunika panthaŵiyo ndi mmene zinthu zilili. Sapondereza kapena kuchita mwankhanza. (Yesaya 28:26-29) Ana ena amamva makolo awo akangowayang’ana chabe. Ana ena amafunika kuwakumbutsa nthaŵi ndi nthaŵi pamene ena angafunike kuwalangiza mwamphamvu. Makolo ololera amalangiza mwana aliyense mogwirizana ndi zosoŵa zake.

Makambirano Anu a Banja Akhale Osangalatsa

18. Kodi makolo angapeze bwanji nthaŵi yoti azichita phunziro la Baibulo la banja nthaŵi zonse?

18 Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zolangizira ana anu ndiyo kuphunzira Baibulo monga banja nthaŵi zonse ndi kukambirana Malemba tsiku lililonse. Phunziro la banja limapindulitsa kwambiri ngati limachitika nthaŵi zonse. Koma ngati limangochitika mwamwayi kapena modzidzimutsira, silingakhale lopindulitsa. Motero, makolo ayenera ‘kuombola nthaŵi’ kuti achite phunziroli. (Aefeso 5:15-17, NW) Kusankha nthaŵi yabwino imene aliyense m’banjamo angagwirizane nayo kungakhale kovuta. Tate wina anapeza kuti pamene ana anali kukula, aliyense anali ndi zochita zake ndipo kunali kovuta kuti banja lonse likumane pamodzi. Komabe, anthu onse m’banjamo anali kukhalira limodzi nthaŵi zonse pamisonkhano ya mpingo imene inali kuchitika usiku. Motero tateyo anakonza kuti azichita phunziro la banja tsiku lina usiku mwa masiku a msonkhano aja. Zimenezi zinathandiza kwambiri. Panopa ana onse atatu anabatizidwa ndipo akutumikira Yehova.

19. Kodi makolo angatsanzire motani Yehova pochititsa phunziro la banja?

19 Komabe, kungophunzira nkhani ya m’Malemba n’kosakwanira. Yehova anawaphunzitsa Aisrayeli amene anabwerako ku ukapolo pogwiritsa ntchito ansembe amene ‘anatanthauzira’ Chilamulo, “nawazindikiritsa choŵerengedwacho.” (Nehemiya 8:8) Tate wina amene anakwanitsa kuthandiza ana ake onse asanu ndi aŵiri kukonda Yehova, anali kuloŵa m’chipinda chake nthaŵi zonse asanachite phunziro la banja kuti akonzekere ndi kufufuza mmene nkhaniyo angaigwirizanitsire ndi zosoŵa za mwana aliyense. Anali kuchititsa phunzirolo kukhala losangalatsa kwa anawo. Mwana wake wina yemwe panopa ndi wamkulu akukumbukira kuti: “Phunzirolo linali losangalatsa nthaŵi zonse. Ngati tinali kuseŵera mpira panja ndiyeno n’kutiitana kuti tikaphunzire, tinali kusiya mpira nthaŵi yomweyo ndi kuthamangira ku phunzirolo. Nthaŵi ya madzulo imene tinkachita phunziro ndiyo inali yosangalatsa kwambiri mlungu wonsewo.”

20. Kodi tiyenera kupenda za vuto liti limene titha kukumana nalo polera ana athu?

20 Wamasalmo ananena kuti: “Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.” (Salmo 127:3) Pamatenga nthaŵi yaitali ndiponso pamafunika kudzipereka kuti tiphunzitse ana athu, koma kuchita zimenezo moyenera kudzathandiza kuti anawo adzakhale ndi moyo wosatha. Idzakhala mphoto yaikulutu imeneyo! Ndiyetu tiyeni titsanzire Yehova ndi mtima wonse pophunzitsa ana athu. Komabe, ngakhale kuti makolo awapatsa udindo ‘wolera ana m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye,’ sikuti nthaŵi zonse adzapambana. (Aefeso 6:4) Mwana angapanduke ndi kusiya kutumikira Yehova ngakhale atamuphunzitsa bwino zedi. Zikatere kodi n’kuchitanji? Umenewu ukhala mutu wa nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Nkhani zosimba zimene ena anakumana nazo zimene zili m’nkhani ino ndi nkhani yotsatira zingakhale za kumayiko amene chikhalidwe chawo n’chosiyana ndi chanu. Yesani kupeza mfundo zake za nkhanizo ndi kuzigwiritsa ntchito pa chikhalidwe chanu.

Kodi Muyankhe Kuti Chiyani?

• Kodi makolo angatsanzire motani chikondi cha Yehova chofotokozedwa pa Deuteronomo 32:11, 12?

• Kodi mwaphunzirapo chiyani ndi mmene Yehova analankhulira ndi Aisrayeli?

• Kodi kumvetsera kwa Yehova pempho la Loti kukutiphunzitsa chiyani?

• Kodi mwaphunzira chiyani pa Yesaya 28:24-29 pankhani ya kulangiza ana?

[Mafunso]

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mose anayerekeza mmene Yehova amaphunzitsira anthu ake ndi mmene mphungu imachitira ndi ana ake

[Zithunzi patsamba 10]

Makolo afunika kupeza nthaŵi yocheza ndi ana awo

[Chithunzi patsamba 12]

“Nthaŵi ya madzulo imene tinkachita phunziro ndiyo inali yosangalatsa kwambiri mlungu wonsewo”