Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Zosayembekezeka Potumikira Yehova

Zochitika Zosayembekezeka Potumikira Yehova

Mbiri ya Moyo Wanga

Zochitika Zosayembekezeka Potumikira Yehova

YOSIMBIDWA NDI ERIC NDI HAZEL BEVERIDGE

“Ndikukulamula kuti ukakhale m’ndende miyezi isanu ndi umodzi.” Ndikuganizira mawu ameneŵa, ananditengera ku ndende ya Strangeways mumzinda wa Manchester, ku England. Zimenezi zinachitika mu December 1950, ndili ndi zaka 19. Ndinali nditangokumana kumene ndi chimodzi mwa ziyeso zovuta kwambiri za paubwana wanga​—kukana kuloŵa usilikali.​—2 Akorinto 10:3-5.

NDINALI mpainiya wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Ntchitoyi ikanachititsa kuti asandilembe usilikali koma malamulo a boma la Britain sankalola zimenezo. Choncho, anandiika m’ndende. Ndinayamba kuganiza za bambo anga popeza ndinali m’ndende chifukwa cha iwo.

Lekani ndikuuzeni. Bambo anga anali ofesala woyang’anira ndende. Kwawo kunali ku Yorkshire ndipo ankakhulupirira zinthu kwambiri komanso anali ndi mfundo zachikhalidwe zokhwima. Iwo ankadana kwambiri ndi Chikatolika chifukwa chokhalitsa pantchito ya usilikali ndiponso chifukwa choti anali ofesala wandende. Anakumanapo ndi Mboni cha m’ma 1930. Panthaŵiyo anatuluka m’nyumba kuti akazithamangitse zitafika pakhomo. Komabe, anabwera atatenga mabuku a Mbonizo. Kenako analembetsa kuti azilandira nthaŵi ndi nthaŵi magazini a Consolation (omwe tsopano ndi Galamukani!). Mbonizo zinali kubwera chaka chilichonse kudzawalimbikitsa kuti alembetsenso magaziniwo. Ndili ndi zaka 15, Mboni zinabwera kudzakambirana nkhani inayake ndi bambo ndipo ine ndinaloŵerera kugwirizana ndi Mbonizo. Kuyamba kuphunzira Baibulo kunali komweko.

M’March 1949, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa kubatizidwa ndili ndi zaka 17. Chaka chomwecho ndinakumana ndi John ndi Michael Charuk omwe anali kupita ku Nigeria atamaliza maphunziro kusukulu yophunzitsa amishonale ya Gileadi. Ndinachita chidwi kwambiri ndi mzimu wawo wa umishonale. Iwo anadzala mzimu umenewu mumtima mwanga kaya ankadziŵa zimenezi kapena ayi.

Pamene ndinali kuphunzira Baibulo chidwi chofuna kupita ku yunivesite chinatha. Chaka chisanathe, nditangochoka panyumba kukayamba ntchito ku ofesi yoona za katundu woloŵa ndi wotuluka yomwe inali mumzinda wa London, ndinaganiza kuti sindingatumikire Mulungu mokwanira ngati nditapitiriza kugwira ntchito ya boma. Nditasiya ntchitoyo, munthu wina yemwe anali atagwira ntchito pa ofesiyo kwanthaŵi yaitali anandiyamikira chifukwa chosiya “ntchito yowononga maganizoyo.”

Ndisanasiye ntchitoyo, chiyeso china chinali chakuti ndiwauza bwanji bambo anga kuti ndikufuna kusiya ntchito kuti ndikhale mtumiki wanthaŵi zonse. Tsiku lina usiku nditapita kunyumba panthaŵi ya tchuti, ndinalimba mtima n’kuwauza nkhaniyi. Ndinali kuyembekeza kuti andikalipira kwambiri. Koma ndinadabwa kuti anangoti: “Izo ndi zako; wakula watha. Koma zikakukanika osathamangira kwa ine.” Posimba zochitika za pa January 1, 1950, kabuku kanga kolembamo zochitika za tsiku ndi tsiku kamati: “Ndinauza bambo kuti ndikufuna kuchita upainiya. Ndinadabwa kwambiri ndi mtima wawo wabwino ndi wothandiza. Sindikanachitira mwina koma kulira chifukwa cha kukoma mtima kwawo.” Ndinasiya ntchito ya boma ndikuyamba upainiya wa nthaŵi zonse.

Upainiya Ndiponso Kukhala “M’kanyumba Kakang’ono”

Kenako ndinakumana ndi chiyeso china cha kudzipereka kwanga kwa Mulungu. Atandipatsa gawo langa la upainiya, anandiuza kuti ndizikakhala ndi Mkristu mnzanga wa ku Wales, Lloyd Griffiths, “m’kanyumba kakang’ono” ku Lancashire. Nditanyamuka ndinali kulingalira za kanyumbako ndipo mosakhalitsa ndinafika m’tauni yamatope ndiponso yosasangalatsayo ya Bacup. Nditangoloŵa m’kanyumbako ndinatsimikiza zomwe ndinkaganiza chifukwa kanalidi kang’ono kwambiri. Munali mphemvu ndi makoswe adzaoneni. Ndinatsala pang’ono kusintha maganizo kuti ndibwerere kunyumba. Komabe m’pemphero langa la mumtima ndinapempha nyonga kuti ndithe kupirira chiyeso chimenechi. Nthaŵi yomweyo ndinayamba kuona zochitikazo moyenera. Ndinazindikira kuti imeneyo inali ntchito yomwe gulu la Yehova linandipatsa. Ndinadalira kwambiri Yehova kuti andithandiza. Ndikuyamikira kwambiri kuti ndinapirira chifukwa ndikanapanda kutero moyo wanga ukanasintha mpaka kalekale.​—Yesaya 26:3, 4.

Asanandiike m’ndende chifukwa chokana kuloŵa usilikali, ndinalalikira kwa miyezi isanu ndi inayi m’chigwa cha Rossendale, dera lomwe panthaŵiyo linali pamavuto aakulu a zachuma. Nditakhala milungu iŵiri kundende ya ku Strangeways, anandisamutsira kundende ya ku Lewes, kugombe la kum’mwera kwa dziko la England. M’kupita kwa nthaŵi, tinakwana Mboni zisanu ndipo tinali kuchita chikumbutso cha imfa ya Kristu m’ndende momwemo.

Bambo anga anabwera kudzandiona kamodzi. Zimenezo ziyenera kuti zinali chiyeso chachikulu kwa iwo chifukwa monga ofesala wandende wotchuka, zinali zochotsa ulemu kuti adzaone mwana wawo kundende. Ndidzayamikirabe zomwe anachitazo mpaka kalekale. Kenako mu April 1951, anandimasula.

Atandimasula kundende ya ku Lewes, ndinakwera sitima yapamtunda kupita ku Cardiff, ku Wales, komwe bambo anga ankagwira ntchito monga ofesala wamkulu wa pandende. Ine ndinali wamkulu mwa ana awo aamuna atatu ndi mtsikana mmodzi. Ndinafunikira kupeza kaganyu kuti ndizidzithandiza kwinaku ndikuchita upainiya. Ndinali kugwira ntchito m’sitolo yazovala koma cholinga changa chachikulu m’moyo chinali utumiki wachikristu. Zisanachitike zimenezi, mayi athu anatichokera. Zinalitu zopweteka kwambiri kwa bambo komanso kwa ife ana a zaka zoyambira 8 mpaka 19. Zinali zomvetsa chisoni kuti makolowo anasudzulana.

Iye Amene Apeza Mkazi Wabwino . . .

Mumpingo wathu munali apainiya angapo. Mwa apainiya ameneŵa panali mlongo amene ankabwera tsiku lililonse kudzagwira ntchito yolembedwa komanso kudzalalikira kuchokera m’chigwa cha Rhondda komwe kunali mgodi wa malasha. Dzina lake linali Hazel Green​—mpainiya wakhama kwambiri. Hazel anali atadziŵa choonadi kwa zaka zambiri kuposa ine. Makolo ake anali atayamba kupita kumisonkhano ya Ophunzira Baibulo (omwe tsopano ndi Mboni za Yehova) kale kwambiri m’ma 1920. Lekani akuuzeni yekha mbiri ya moyo wake.

“Baibulo sindinkaliona ngati lofunika kwenikweni mpaka mu 1944 pamene ndinaŵerenga kabuku kakuti Religion Reaps the Whirlwind. Amayi anga anandilimbikitsa kupita kumsonkhano wadera ku Cardiff. Ngakhale kuti Baibulo sindinali kulidziŵa, ndinapita nawo m’tauni ina yaikulu nditavala chikwangwani cholengeza nkhani ya onse. Ngakhale kuti atsogoleri a matchalitchi ndi anthu ena anandizunza, ndinapirira. Mu 1946 ndinabatizidwa ndipo ndinayamba upainiya mu December chaka chomwecho. Kenako mu 1951, Eric, mpainiya wachinyamata, anabwera ku Cardiff atangom’tulutsa m’ndende.

“Tinkapitira limodzi kokalalikira ndipo tinali kugwirizana kwambiri. Tinali ndi zolinga zofanana zofuna kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu wa Mulungu. Choncho mu December 1952 tinakwatirana. Ngakhale kuti tonse tinali kuchita utumiki wa upainiya wanthaŵi zonse ndipo kuti tinali ndi ndalama zochepa, sitinasoŵepo zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu. Nthaŵi zina tinali kulandira mphatso kuchokera kwa Mboni ina yomwe inali kugula jamu kapena sopo wochuluka. Ndipo zinthu zimenezi zinkabwera panthaŵi yake. Tinali kuyamikira kwambiri zinthu ngati zimenezi. Komabe zochitika zazikulu zosayembekezeka zinali m’tsogolo.”

Chochitika Chosayembekezeka Chomwe Chinasintha Miyoyo Yathu

Mu November 1954, Hazel ndi ine tinalandira chinthu chomwe sitinali kuchiyembekezera, chikalata chochokera ku ofesi ya Mboni za Yehova ku London chondipempha kuti ndikakhale woyang’anira woyendayenda, kumachezera mipingo yosiyanasiyana mlungu uliwonse. Tinkaganiza kuti alakwitsa moti sitinauze aliyense mumpingo. Komabe, ndinalemba zofunika pa chikalatacho ndi kuchitumiza. Tinali kuyembekeza yankho mitima ili m’mwamba. Patangopita masiku oŵerengeka anatiyankha amvekere: “Bwerani ku London kuti mudzaphunzire ntchitoyi”!

Titafika ku ofesi ya ku London, sindinakhulupirire kuti ineyo wa zaka 23 ndingakhale pagulu la abale omwe anali ngati zimphona zauzimu. Abaleŵa anali Pryce Hughes, Emlyn Wynes, Ernie Beavor, Ernie Guiver, Bob Gough, Glynn Parr, Stan ndi Martin Woodburn, ndi ena ambiri amene ena mwa iwo tsopano anamwalira. Abale ameneŵa ndiwo anayala maziko olimba a changu ndi chikhulupiriro m’dziko la Britain m’ma 1940 ndi m’ma 1950.

Ntchito Yoyang’anira Dera ku England Inkandisangalatsa

Tinayamba ntchito yoyendayenda m’nyengo yachisanu m’chaka cha 1954/55. Anatitumiza ku East Anglia, dera lathyathyathya ku England lomwe kumawomba mphepo yozizira yochokera ku Nyanja ya Kumpoto. Panthaŵiyo n’kuti ku Britain kuli Mboni zokwana 31,000 zokha basi. M’dera loyambali zinthu zinali kutivuta kwambiri ndipo ngakhale abale amene tinali kuwayendera nawonso zinali kuwavuta kwambiri. Chifukwa chosazoloŵera ndiponso chifukwa cha kulankhula kosapita m’mbali kwa anthu a ku Yorkshire, nthaŵi zina ndinali kuwakhumudwitsa abale. M’kupita kwa nthaŵi, ndinaphunzira kuti kukoma mtima n’kofunika kwambiri kuposa kulongosola ntchito. Ndinaphunziranso kuti anthu ndiwo ofunika kwambiri kuposa njira zogwirira ntchito. Mpaka lero ndikuyesetsabe kutsanzira chitsanzo cha Yesu chotsitsimula ena koma si nthaŵi zonse pamene zimatheka.​—Mateyu 11:28-30.

Titakhala ku East Anglia kwa miyezi 18, anatitumiza kuti tikatumikire ku Newcastle kenako ku Tyne ndi ku Northumberland, dera lomwe lili kumpoto chakum’maŵa kwa dziko la England. Anthu a m’dera limeneli ndinkawakonda kwambiri chifukwa cha kukoma mtima kwawo. Atabwera woyang’anira chigawo, Don Ward, kuchokera ku Seattle, Washington, U.S.A. anandithandiza kwambiri. Iye anali atamaliza maphunziro a sukulu ya Gileadi m’kalasi ya 20. Ndinkakonda kulankhula mofulumira kwambiri pokamba nkhani. Koma anandiphunzitsa kulankhula modekha, kuima polankhula, ndi kuphunzitsa.

Chochitika China Chosayembekezeka Chomwe Chinasintha Miyoyo Yathu

Mu 1958, tinalandira kalata yomwe inasintha miyoyo yathu. Kalatayo inali yotipempha kuti tipite ku Sukulu ya Gileadi ku South Lansing, New York, U.S.A. Tinagulitsa galimoto yathu ya mtundu wa 1935 Austin Seven n’kugula matikiti a sitima yapamadzi kupita ku New York. Titafika, tinachita kaye msonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova ku New York City. Kenako tisanapite ku Sukulu ya Gileadi tinapita ku Peterborough, Ontario, kukachita upainiya kwa miyezi isanu ndi umodzi.

Ena mwa alangizi ku Sukulu ya Gileadi anali Albert Schroeder, yemwe tsopano ali m’Bungwe Lolamulira komanso Maxwell Friend ndi Jack Redford, omwe tsopano anamwalira. Kucheza pakati pa ophunzira 82 ochokera m’mayiko 14 kunali kolimbikitsa kwambiri. Pang’ono ndi pang’ono tinayamba kudziŵana chikhalidwe. Ophunzira omwe ankavutika kulankhula Chingelezi anatipatsa chitsanzo cha mavuto omwe tikakumane nawo pophunzira chinenero china. Tinamaliza maphunziro athu m’miyezi isanu ndipo anatiuza kuti tipita ku mayiko 27 osiyanasiyana. Ndiyeno tinachita mwambo wokondwerera kuti tamaliza maphunziro athu. Kenako tinanyamuka kupita ku New York City kukadikira sitima yathu yotchedwa Queen Elizabeth, kubwerera ku Ulaya.

Dziko Lachilendo Loyamba Kukatumikirako

Kodi anatitumiza kuti? Ku Portugal! Tinafika mumzinda wa Lisbon mu November 1959. Ndiyeno tinayamba kuvutika kuphunzira chinenero komanso kuzoloŵera chikhalidwe chatsopano. Mu 1959, ku Portugal kunali Mboni zachangu zokwana 643 pakati pa anthu pafupifupi 9 miliyoni a m’dzikolo. Koma ntchito yathu yolalikira inali yoletsedwa. Tinali ndi Nyumba za Ufumu koma zinalibe zikwangwani zoonekera panja.

Mmishonale Elsa Piccone atatiphunzitsa chipwitikizi, Hazel ndi ine tinayamba kuyendera mipingo ndi magulu a m’dera lozungulira mizinda ya Lisbon, Faro, Evora, ndi Beja. Kenako mu 1961 zinthu zinayamba kusintha. Ndinali kuphunzira Baibulo ndi munthu wina wachinyamata dzina lake João Gonçalves Mateus. Iye monga Mkristu anaganiza zokana kuloŵa usilikali. Atangochita zimenezi, apolisi anandiitanira kulikulu lawo kuti akandifunse. Chinalitu chochitika china chomwe sindinali kuchiyembekezera! Patangopita masiku oŵerengeka, anatiuza kuti tichoke m’dzikolo asanathe masiku 30. Nawonso amishonale anzathu, Eric ndi Christina Britten komanso Domenick ndi Elsa Piccone anawauza zomwezo.

Ndinachita apilo nkhaniyo ndipo anatilola kuti tikaonane ndi mkulu wa apolisi. Iye anatiuza mosapita m’mbali chifukwa chomwe atithamangitsira m’dzikolo ndipo anatchula dzina la wophunzira Baibulo wanga, Gonçalves Mateus. Ananena kuti mosiyana ndi dziko la Britain, boma la Portugal silingalolere kuti anthu azikana kuloŵa usilikali chifukwa cha chipembedzo. Choncho tinachoka ku Portugal ndipo kusiyana ndi João kunali komweko. Kenako patapita zaka 26, zinalitu zosangalatsa kwambiri kuonananso ndi João pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aakazi atatu pamwambo wopatulira nyumba yatsopano ya Beteli ya ku Portugal. Ndithudi, ntchito yathu ku Portugal sinapite pachabe.​—1 Akorinto 3:6-9.

Kodi dziko lathu lachiŵiri kukatumikira linali liti? Mosayembekezeka, anatitumiza ku Spain, dziko lomwe layandikana ndi Portugal. Mu February 1962, misozi ili m’maso, tinakwera sitima yapamtunda kuchokera mumzinda wa Lisbon kupita mumzinda wa Madrid.

Kuzoloŵera Chikhalidwe China

Ku Spain tinazoloŵera kulalikira ndiponso kuchita misonkhano mobisa. Nthaŵi zambiri tikamalalikira sitinali kulalikira nyumba zoyandikana. Timati tikalalikira nyumba ina timadumpha kukalalikira nyumba ina. Zimenezi zinkachititsa kuti apolisi kapena atsogoleri amatchalitchi asatigwire. Kumbukirani kuti panthaŵiyo n’kuti tili mu ulamuliro wankhanza wa Akatolika, a Fascist, ndipo ntchito yathu yolalikira inali yoletsedwa. Kuti asatidziŵe monga anthu ochokera ku mayiko ena, tinasintha mayina athu ndi kutenga mayina achisipanya. Ine ndinali Pablo ndipo Hazel anali Juana.

Titakhala miyezi yoŵerengeka ku Madrid, anatitumiza ku Barcelona monga woyang’anira dera. Tinayendera mipingo yosiyanasiyana mumzindawo ndipo nthaŵi zambiri tinkakhala milungu iŵiri kapena itatu pampingo uliwonse. Izi zinali choncho chifukwa chakuti tinalinso kuyendera gulu la phunziro la buku lililonse ngati kuti tikuyendera mpingo ndipo chifukwa cha zimenezo tinali kuyendera magulu aŵiri mlungu uliwonse.

Ntchito Yovuta Yomwe Sitinali Kuiyembekezera

Mu 1963 anatipempha kuti tiyambe ntchito yoyang’anira chigawo ku Spain. Kuti titumikire Mboni pafupifupi 3,000, tinali kuzungulira dziko lonselo, kuyendera zigawo zisanu ndi zinayi zomwe zinalipo panthaŵiyo. Misonkhano yathu ina yobisa ya dera tinkachitira kutchire lina kufupi ndi Seville, pa famu ina pafupi ndi Gijon, ndi m’mphepete mwa mitsinje yomwe inali kufupi ndi mizinda ya Madrid, Barcelona, ndi Logroño.

Ndikamalalikira ku nyumba ndi nyumba ndimakhala nditapezeratu njira zothaŵira ngati zinthu zitathina. Nthaŵi ina tikulalikira mumzinda wa Madrid, Mboni ina pamodzi ndi ine tinali panyumba ina yapamwamba ndipo tinamva phokoso pa nyumba yapansi. Titatsika tinapeza kuti panali atsikana achikatolika a m’gulu la Hijas de María (Ana Aakazi a Mariya). Phokosolo linali lochenjeza anthu a nyumba zoyandikana nawo za ife. Sitikanatha kulankhula nawo ndipo tinadziŵa kuti m’pofunika kuchoka mwamsanga, apo ayi, apolisi akanatigwira. Chotero tinachoka chothaŵa!

Nthaŵi imeneyo inali yosangalatsa kwambiri ku Spain. Tinali kuyesetsa kulimbikitsa abale ndi alongo ndiponso apainiya apadera. Sanali kuopa kupita kundende ndipo nthaŵi zambiri anali kupirira umphaŵi n’cholinga chofuna kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiponso kukhazikitsa ndi kulimbikitsa mipingo.

Mkati mwa nyengo imeneyi tinalandira uthenga wachisoni. Hazel akufotokoza kuti: “Mu 1964 mayi anga omwe anali Mboni yokhulupirika anamwalira. Zinali zopweteka kwambiri kumva kuti mayi anga amwalira osatsanzikana nawo. Zimenezo ndi zina mwa zomwe zachitikira amishonale ambiri.”

Ufulu Wolambira ku Spain

Mu July 1970 zaka za chizunzo zitatha, boma la Franco linatilola kulembetsa ntchito yathu ku boma. Hazel ndi ine tinali okondwa kwambiri pamwambo wotsegulira Nyumba ya Ufumu yoyamba mumzinda wa Madrid ndiponso yachiŵiri ku Lesseps mumzinda wa Barcelona. Nyumba zimenezi zinali ndi zikwangwani zazikulu zowala ndi magetsi. Tinkafuna kuti anthu adziŵe kuti tsopano Mboni za Yehova ndi zodziŵika ku boma ndipo kuti zidzakhazikika ku Spain. Panthaŵiyo, mu 1972, n’kuti ku Spain kuli Mboni zokwana 17,000.

Zimenezi zisanachitike, ndinalandira uthenga wolimbikitsa kwambiri kuchokera ku England. Bambo anga atabwera kudzationa ku Spain mu 1969, anachita chidwi kwambiri ndi mmene Mboni za ku Spain zinawalandirira moti atabwerera ku England anakayamba kuphunzira Baibulo. Kenako mu 1971, ndinamva kuti bambo anga anabatizidwa. Zinalitu zosangalatsa kwambiri titapita kwathu, kuona bambo anga monga mbale wanga wachikristu akupempherera chakudya. Ndinali n’tayembekezera tsiku limeneli kwa zaka zopitirira 20. Mng’ono wanga Bob ndi mkazi wake Iris, anali atakhala Mboni mu 1958. Mwana wawo wamwamuna Phillip tsopano akutumikira monga woyang’anira dera ku Spain pamodzi ndi mkazi wake Jean. Zimatisangalatsa kwambiri kuti iwo akutumikira m’dziko labwino limenelo.

Zomwe Zatichitikira Mosayembekezeka Posachedwapa

Mu February 1980, wa m’Bungwe Lolamulira anabwera ku Spain monga woyang’anira woyendera nthambi. Ndinadabwa kuti ananena kuti akufuna kupita nane kukalalikira. Sindinkadziŵa n’komwe kuti ankafuna kundiona mmene ndimachitira. Kenako mu September anatipempha kuti tisamukire ku likulu la dziko lonse ku Brooklyn, New York. Tinadabwa nazo kwambiri. Tinavomereza pempholo ngakhale kuti kusiyana ndi abale a ku Spain kunali kopweteka kwambiri. Panthaŵiyo n’kuti ku Spain Mboni zitakwana 48,000!

Ponyamuka, mbale wina anandipatsa mphatso ya wotchi yam’thumba. Pa wotchiyo analembapo malemba aŵiri​—“Luka 16:10; Luka 17:10.” Iye ananena kuti malemba ameneŵa ndiwo ndinkawakonda kwambiri. Luka 16:10 amanena motsindika za kufunika kokhala wokhulupirika pa zinthu zazing’ono. Ndipo Luka 17:10 amanena kuti ndife “akapolo opanda pake” moti palibe chifukwa chodzikwezera. Nthaŵi zonse ndakhala ndikukumbukira kuti chilichonse chomwe tingachite potumikira Yehova changokhala udindo wathu monga Akristu odzipatulira.

Mavuto Osayembekezeka a Zaumoyo

Mu 1990, ndinayamba kudwala matenda a mtima. M’kupita kwa nthaŵi anandiika kachitsulo kokhala ndi boo kotchedwa stent n’cholinga choti mitsempha isatsekeke. Nthaŵi ya mavuto a zaumoyo yonseyi, Hazel wakhala akundithandiza m’njira zambiri. Nthaŵi zambiri anali kundinyamulira zikwama zomwe sindikanatha kunyamula. Kenako mu May 2000 anandiika kanthu kothandiza kuti mtima uzigunda bwino. Tsopano ndikupezako bwino.

Kwa zaka 50 zapitazi, Hazel ndi ine taona kuti dzanja la Yehova sililephera ndipo amakwaniritsa zolinga zake panthaŵi yake yoikika osati yomwe anthufe tikufuna. (Yesaya 59:1; Habakuku 2:3) Takumana ndi zinthu zambiri zosangalatsa komanso zina zingapo zomvetsa chisoni zomwe sitinali kuziyembekezera koma Yehova watithandiza kudutsa monsemo. Kuno ku likulu la dziko lonse la anthu a Yehova tili ndi mwayi wolankhula ndi a m’Bungwe Lolamulira tsiku ndi tsiku. Nthaŵi zina ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi tilidi kuno ife?’ Ha! Ndimwayi wapadera kwambiri. (2 Akorinto 12:9) Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kutisunga ndi kutiteteza ku misampha ya Satana kuti tidzasangalale ndi ulamuliro wake wolungama pa dziko lapansi.​—Aefeso 6:11-18; Chivumbulutso 21:1-4.

[Chithunzi patsamba 26]

Ndende ya ku Strangeways ku Manchester, komwe ndinayambira ukaidi wanga

[Chithunzi patsamba 27]

Tili ndi galimoto yathu yamtundu wa Austin Seven mu ntchito yoyang’anira dera ku England

[Chithunzi patsamba 28]

Msonkhano wochita mobisa ku Cercedilla, Madrid, ku Spain, mu 1962

[Chithunzi patsamba 29]

Tili patebulo la mabuku ofotokoza Baibulo ku Brooklyn