Zomwe Tingaphunzire ku Mtengo wa Kanjedza
Zomwe Tingaphunzire ku Mtengo wa Kanjedza
INSAIKULOPEDIYA ina ya Baibulo imanena kuti kanjedza kapena kuti mgwalangwa “ndi mtengo wokongola mochititsa kaso.” M’nthaŵi za m’Baibulo ndiponso masiku ano, mitengo ya kanjedza imakongoletsa chigwa cha m’tsinje wa Nile ku Egypt ndiponso imapereka mthunzi wabwino m’malo a chinyontho a m’chipululu cha Negeb.
Mofanana ndi mitundu yake ina yambiri, mtengo wa kanjedza ndi wowongoka mochititsa chidwi. Mitengo ina imatalika mpaka mamita 30 ndipo imapitirizabe kubala zipatso kwa zaka 150. Inde, mtengo wa kanjedza ndi wokongola kwambiri ndiponso umabalanso zipatso modabwitsa. Chaka chilichonse mtengowu umatulutsa mikoko yambiri ya zipatso. Mkoko umodzi wokha umakhala ndi zipatso zopitirira 1,000. Ponena za zipatso za kanjedza, wolemba mabuku wina anati: “Anthu amene . . . anangodya zipatso zouma zokha za kanjedza za m’sitolo sangadziŵe mmene zaziŵisi zimakomera.”
Baibulo moyenerera limayerekezera anthu ena ndi mitengo ya kanjedza. Kuti munthu akhale wokongola kwa Mulungu monga mtengo wa kanjedza wobala zipatso, ayenera kukhala wowongoka mwamakhalidwe ndiponso ayenera kupitiriza kuchita ntchito zabwino. (Mateyu 7:17-20) Pachifukwa chimenechi, zithunzi za mitengo ya kanjedza zinali kukongoletsa m’kachisi wa Solomo ndiponso m’kachisi yemwe Ezekieli anaona m’masomphenya. (1 Mafumu 6:29, 32, 35; Ezekieli 40:14-16, 20, 22) Choncho, kuti kulambira kukhale kovomerezeka kwa Mulungu, wolambirayo ayenera kukhala ndi mikhalidwe yabwino monga ya mtengo wa kanjedza. Mawu a Mulungu amati: “Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa.”—Salmo 92:12.