Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimene Chidzabweretse Dziko Lachimwemwe

Chimene Chidzabweretse Dziko Lachimwemwe

Chimene Chidzabweretse Dziko Lachimwemwe

“YESU wa ku Nazarete ndiye munthu yekhayo wamkulu koposa onse, osati m’zaka masauzande aŵiri okha, koma m’mbiri yonse ya anthu, “inatero magazini ya Time. Pamene Yesu anali pano pa dziko lapansi, anthu oona mtima ambiri anazindikira osati ukulu wake wokha komanso kuganizira kwake anthu ena. Choncho, si zodabwitsa kuti anthuwo anafuna kum’longa ufumu. (Yohane 6:10, 14, 15) Koma monga momwe nkhani yangothayi yanenera, Yesu anakana kuloŵerera m’nkhani zandale.

YESU anachita zimenezo pazifukwa zitatu izi: choyamba chinali maganizo a Atate wake pa zimene anthu anachita zosonyeza kufuna kudziimira komanso kudzilamulira. Chachiŵiri, Yesu ankadziŵa kuti pali magulu osaoneka amphamvu kwambiri omwe amalepheretsa anthu ngakhale atayesetsa motani kuti achite zabwino polamulira. Ndipo chachitatu chinali chokhudza cholinga cha Mulungu chokhazikitsa boma lakumwamba kuti lidzalamulire dziko lonse lapansi. Pamene tikupenda mosamalitsa mfundo zitatu zimenezi, tiona chifukwa chake anthu alephera kupanga dziko kukhala labwino. Tionanso mmene zimenezi zidzathekere.

Kodi Anthu Angadzilamulire?

Mulungu atalenga anthu, anawauza kuti alamulire nyama. (Genesis 1:26) Ndipo Mulungu ndiye anali kulamulira anthu. Mwamuna ndi mkazi oyambawo anayenera kugonjera Mulungu mwa kupeŵa kudya chipatso cha mtengo umodzi wokha, “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 2:17) N’zachisoni kuti Adamu ndi Hava anagwiritsa ntchito molakwa ufulu wawo wakudzisankhira mwa kusankha kusamvera Mulungu. Kudya chipatso choletsedwacho sikunali kuba kokha. Kunali kupandukira ulamuliro wa Mulungu. Mawu am’munsi pa Genesis 2:17 m’Baibulo la The New Jerusalem Bible amanena kuti Adamu ndi Hava anasonyeza “kufuna kudziimira kotheratu pankhani yosankha chabwino ndi choipa ndipo mwakutero anthu anakana kuvomereza kuti anachita kulengedwa . . . Tchimo loyambali linasonyeza kuukira ulamuliro wa Mulungu.”

Chifukwa cha kukula kwa nkhani zomwe zinakhudzidwa, Mulungu analola kuti Adamu ndi Hava ndi mbadwa zawo azidzisankhira zochita pa moyo wawo, ndipo anadzikhazikitsira okha miyezo ya chabwino ndi choipa. (Salmo 147:19, 20; Aroma 2:14) Kuyambira pamenepo anthu anayamba kuyesa kukhala moyo wodziimira. Kodi zawayendera bwino? Kungoona zomwe zachitika zaka masauzande ambiri zapitazi, tingayankhe kuti sizinayende bwino m’pang’ono pomwe! Mlaliki 8:9 amanena kuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” Mbiri yomvetsa chisoni imeneyi ya kudzilamulira kwa anthu ikutsimikiza kuti mawu a pa Yeremiya 10:23 ndi oona. Lembali limati: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Zomwe zachitika mmbuyomu zatsimikiza kuti anthu alibe mphamvu zolamulira bwinobwino pawokha popanda Mlengi wawo.

Yesu anavomereza mfundo imeneyi. Kukhala wodziimira popanda Mulungu chinali chinthu chonyansa kwa iye. Yesu anati: “Sindichita kanthu kwa Ine ndekha, . . . Ndichita Ine zimene zim’kondweretsa [Mulungu] nthaŵi zonse.” (Yohane 4:34; 8:28, 29) N’chifukwa chake Yesu sanafune n’komwe kulandira ufumu kuchokera kwa anthu popanda chilolezo cha Mulungu. Komabe zimenezi sizikutanthauza anali sankafuna kuthandiza anthu anzake. M’malo mwake, anachita zonse ndi mphamvu zake kuthandiza anthu kuti apeze chimwemwe chochuluka panthaŵiyo ndiponso m’tsogolo. Ndipo mpaka anapereka moyo wake chifukwa cha anthu. (Mateyu 5:3-11; 7:24-27; Yohane 3:16) Komabe Yesu ankadziŵa kuti “kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake,” kuphatikizapo nthaŵi yoti Mulungu akhazikitse ulamuliro wake kwa anthu. (Mlaliki 3:1; Mateyu 24:14, 21, 22, 36-39) Komabe kumbukirani kuti mu Edene makolo athu oyambawo anagonjera zofuna za mngelo woipa yemwe analankhula pogwiritsa ntchito njoka. Zimenezi zikutiuza chifukwa chachiŵiri chomwe Yesu anakanira kuloŵerera m’nkhani zandale.

Wolamulira wa Dziko Wosaoneka

Baibulo limatiuza kuti Satana anauza Yesu kuti am’patsa “mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo” ngati atam’lambira. (Mateyu 4:8-10) Pamenepa Mdyerekezi kwenikweni ankafuna kupatsa Yesu ulamuliro wa dziko lapansi. Yesu sanagonje pa chiyeso chimenechi. Koma kodi chinalidi chiyeso? Kodi Satana akanaperekadi ulamulirowo? Inde akanatero, chifukwa Yesu weniweniyo anatcha Mdyerekezi kuti, “mkulu wa dziko lapansi,” ndipo mtumwi Paulo nayenso anatchula Mdyerekezi kuti, “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.”​—Yohane 14:30; 2 Akorinto 4:4; Aefeso 6:12.

Yesu ankadziŵanso kuti Mdyerekezi alibe chidwi chothandiza anthu. Iye anatchula Satana kuti “wambanda” ndiponso “atate wake wa bodza ndi zonse zomwe zili zabodza.” (Yohane 8:44, The Amplified Bible) N’zodziŵikiratu kuti dziko lomwe “ligona” mwa mngelo woipa ngati ameneyu silingakhale ndi chimwemwe chenicheni. (1 Yohane 5:19) Komabe, Mdyerekezi sadzalamulira mpaka kalekale. Yesu, yemwe tsopano ali munthu wamphamvu wauzimu, posachedwapa adzachotseratu Satana ndi ntchito zake zonse.​—Ahebri 2:14; Chivumbulutso 20:1-3.

Satanayo akudziŵa kuti nthaŵi yake yolamulira dziko lapansi yatsala pang’ono kum’thera. N’chifukwa chake akuyesetsa mwachangu kugwiritsa ntchito chilichonse chomwe angathe kusokoneza anthu kotheratu, monga anachitira chisanafike Chigumula cha m’nthaŵi ya Nowa. (Genesis 6:1-5; Yuda 6) Lemba la Chivumbulutso 12:12 limati: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.” Ulosi wa m’Baibulo komanso zomwe zikuchitika padziko lapansi zikusonyeza kuti tatsala pang’ono kufika kumapeto kwa “kanthaŵi” kameneka. (2 Timoteo 3:1-5) Ndithudi, mpumulo tsopano uli pafupi.

Boma Lomwe Lidzabweretse Chimwemwe

Chifukwa chachitatu chomwe Yesu anakanira kuloŵerera m’nkhani zandale chinali chakuti iye ankadziŵa kuti nthaŵi ina yake m’tsogolo, Mulungu adzakhazikitsa boma lakumwamba kuti lilamulire pa dziko lapansi. Baibulo limatchula boma limenelo kuti Ufumu wa Mulungu, ndipo ndiwo unali mfundo yaikulu ya zomwe Yesu anaphunzitsa. (Luka 4:43; Chivumbulutso 11:15) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera Ufumuwo kuti udze, chifukwa chakuti ndi mu ulamuliro umenewu wokha pamene ‘chifuno cha Mulungu chidzachitike padziko lapansi monga kumwamba.’ (Mateyu 6:9, 10) Mwina mungafunse kuti, ‘Ngati Ufumu umenewu ndiwo udzalamulire dziko lonse lapansi, kodi maboma aanthu alipoŵa chidzaŵachitikire n’chiyani?’

Yankho la funso limeneli lili pa Danieli 2:44. Lembali limati: ‘Masiku a mafumu aja [omwe akulamulira m’nthaŵi ya mapeto ino] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [aanthu], nudzakhala chikhalire.’ N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya” maboma a dziko lapansi? Chifukwa chakuti maboma ameneŵa amalimbikitsa mzimu wolimbana ndi Mulungu wofuna kudziimira womwe Satana anayambitsa m’munda wa Edene. Kuwonjezera pa kuchita zinthu zosonyeza kupanda chidwi chothandiza ena, anthu amene amalimbikitsa mzimu umenewu amadziika m’gulu la anthu omwe Mlengi adzawawononge. (Salmo 2:6-12; Chivumbulutso 16:14, 16) Choncho, tidzifunse kuti, ‘Kodi ndikuvomereza kapena kutsutsa ulamuliro wa Mulungu?’

Kodi Musankha Ulamuliro wa Ndani?

Pofuna kuthandiza anthu kusankha atadziŵa zolondola zokhudza ulamuliro, Yesu analamula ophunzira ake kulalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi, kuti ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse’ chimaliziro chisanafike. (Mateyu 24:14) Kodi ndani lerolino akudziŵika padziko lonse chifukwa cha kulalikira Ufumu wa Mulungu? Ndi Mboni za Yehova basi. Ndipotu, kwanthaŵi yaitali pa chikuto cha magazini ino pakhala mawu akuti, “Yolengeza Ufumu wa Yehova.” Lerolino, Mboni pafupifupi mamiliyoni asanu ndi limodzi m’mayiko oposa 230 zikuthandiza anthu kuti adziŵe zolondola zokhudza Ufumu. *

Madalitso kwa Nzika za Ufumu

Yesu nthaŵi zonse anachita zinthu monga momwe Mulungu anafunira. N’chifukwa chake m’malo mosankha kukhala wodziimira ndi kuyesa kuthandiza kapena kuwongolera zinthu pogwiritsa ntchito ndale, iye anagwira ntchito mwakhama kulimbikitsa zinthu za Ufumu wa Mulungu womwe ndiwo njira yokhayo yothetsera mavuto a dziko lapansi. Chifukwa cha kukhulupirika kwake, Yesu analandira mpando waulemerero kumwamba monga Mfumu ya Ufumuwo. Imeneyi ndi mphoto yosangalatsatu kwambiri imene wapatsidwa chifukwa cha kumvera Mulungu!​—Danieli 7:13, 14.

Anthu miyandamiyanda lerolino amene amatsanzira Yesu mwa kuika zinthu za Ufumu wa Mulungu patsogolo ndiponso kugonjera zofuna za Mulungu nawonso amasangalala ndi mphatso yabwino kwambiri, mwayi wamtengo wapatali wodzakhala nzika za pa dziko lapansi za Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 6:33) Mu ulamuliro wachikondi umenewo, iwo adzakhala anthu angwiro, n’kumayembekezera kukhala ndi moyo wosatha. (Chivumbulutso 21:3, 4) Lemba la 1 Yohane 2:17 limanena kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” Satana ndi om’tsatira ake akadzachotsedwa, dziko adzalisandutsa paradaiso wa pa dziko lonse, wopanda kusankhana mitundu, ziphuphu, ndiponso chipembedzo chonyenga. Ha! Dziko lidzakhaladi malo osangalatsa kwambiri kukhalamo kosatha.​—Salmo 37:29; 72:16.

Inde, Ufumu wa Mulungu ndiwo chinsinsi choloŵera m’dziko lachimwemwe ndipo moyenerera uthenga wolengeza za Ufumuwo umatchedwa uthenga wabwino. Ngati uthengawu simunaulandire, bwanji mudzamvetsere Mboni za Yehova zikadzafika pakhomo panu?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Polalikira Ufumu wa Mulungu, Mboni za Yehova siziloŵerera m’nkhani zandale kapena kupanga magulu oukira boma ngakhale m’mayiko omwe amaziletsa kapena kuzizunza. (Tito 3:1) M’malo mwake, zimayesetsa mosaloŵetsapo ndale kuthandiza mwauzimu monga momwe Yesu ndi ophunzira ake anachitira. Mboni zimayesetsa kuthandiza anthu oona mtima m’madera osiyanasiyana omwe zimakhala kuti aphunzire makhalidwe abwino a m’Baibulo monga chikondi cha pa banja, kuona mtima, kudzisunga, ndiponso makhalidwe abwino a ku ntchito. Kwenikweni, Mboni zimayesetsa kuphunzitsa anthu mmene angatsatirire mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo ndiponso kuti aziyembekezera Ufumu wa Mulungu wokha kuti ndiwo udzathetse mavuto a anthu.

[Zithunzi patsamba 5]

Zomwe zachitika mmbuyomu zikutsimikizira kuti anthu sangalamulire bwinobwino popanda Mulungu

[Chithunzi patsamba 5]

Popeza kuti Satana amalamulira “pansi pano” iye akanapereka kwa Yesu “mayiko onse a dziko lapansi”

[Zithunzi patsamba 7]

Yesu anaphunzitsa kuti m’nthaŵi ya ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, dziko lapansi lidzakhala malo abwino kwambiri