Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Madzi Opatsa Moyo Akuyenda ku Andes

Madzi Opatsa Moyo Akuyenda ku Andes

Madzi Opatsa Moyo Akuyenda ku Andes

Mapiri a Andes anadutsa pakati pa dziko la Peru ndipo anagaŵa dzikoli m’zigawo ziŵiri. Chigawo china ndi cha m’mphepete mwa nyanja chomwe chili kumadzulo ndipo n’chouma pamene chinacho chomwe chili kum’maŵa n’chanthaka ndipo chili ndi nkhalango yaikulu yomwe imatuŵa ndi nkhungu nthaŵi zonse. M’dziko la Peru muli anthu 27,000,000 ndipo opitirira 9,000,000 mwa anthu ameneŵa amakhala pamwamba pa mapiriwo. Anthuŵa amakhala pamwamba pathyathyathya ndi m’mphepete motsetsereka mwa mapiri a Andes ameneŵa, kapena m’zigwembe ndi m’zigwa za chonde.

ZIGWEMBE za mapiri a Andes zimalepheretsa anthu kuyenda kuchoka m’madera ena kukafika pamwamba pake. Pa chifukwa chimenechi, anthu miyandamiyanda a kumeneko zimawavuta kuonana ndi anthu a m’madera ena. Ndipo zomwe zikuchitika m’madera ena sazidziŵa.

Anthu kumeneko anamanga midzi ing’onoing’ono m’mphepete mwa mitsinje kuti asamavutike kutunga madzi othirira mbewu zawo komanso kumwetsa zoŵeta zawo. Amaŵeta nyama monga llamas, alpacas, vicuñas, ndi nkhosa. Komabe, kulinso madzi a mtundu wina amene akuyenda ku mapiri a Andes​—madzi otsitsimula auzimu ochokera kwa Yehova, “kasupe wa madzi a moyo.” (Yeremiya 2:13) Mulungu akugwiritsa ntchito Mboni zake kuthandiza anthu okhala pamwamba pa mapiri a Andes kuti adziŵe zolondola zokhudza Iye ndi zolinga zake.​—Yesaya 12:3; Yohane 17:3.

Popeza kuti Mulungu akufuna kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi,” atumiki ameneŵa akuyesetsa kulalikira uthenga wopulumutsa moyo wa m’Baibulo kwa anthu omwe amakhala m’madera ovuta kufikamo. (1 Timoteo 2:4) Uthenga wa m’Baibulo umenewu ndi wopatsa nzeru ndiponso wapamwamba kwambiri. Uthengawu wamasula anthu oona mtima a kumapiri a Andes ku zikhulupiriro za mizimu, miyambo, ndiponso ziphunzitso zomwe zimawachititsa kuopa akufa, mizimu yoipa, ndi mphamvu za chilengedwe. Koposa zonse, uthenga umenewu umawapatsa chiyembekezo cha ulemerero chodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi.

Kuyesetsa Kwambiri

Olalikira Ufumu amene amapita ku madera a kumidzi ameneŵa amasintha zinthu zambiri pa moyo wawo. Kuti akaphunzitse uthenga wa m’Baibulo kwa anthu mogwira mtima, aphunzitsi a Baibulo ameneŵa ayenera kudziŵa zinenero ziŵiri za m’deralo za Quechua kapena Aymara.

Kukafika ku midzi ya kumapiri a Andes si chinthu chapafupi ayi. Kulibe njanji zambiri zopita kumeneko. Mayendedwe ndi ovuta kwambiri ndipo misewu n’njowonongeka chifukwa cha nyengo yoipa ndiponso mapiri. Kodi nanga Mboni zimakafika bwanji kumeneko kukalalikira uthenga wa Ufumu?

Olalikira uthenga wabwino olimba mtima, adzipereka kukumana ndi mavutowo ndipo ayankha monga mneneri Yesaya kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Iwo agwiritsa ntchito galimoto zokhala ndi nyumba kupita ku madera a kumpoto, pakati, ndi kum’mwera. Atumiki a khama a nthaŵi zonse ameneŵa amanyamula makatoni ambiri a mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo ndipo afesa mbewu za choonadi cha m’Baibulo kwa anthu a ubwenzi, ochereza alendo, ndiponso oona mtima omwe amakhala m’derali.

Makona a misewu ya m’mapiri ndi oopsa kwambiri. Kuti adutse bwinobwino m’makona ena otereŵa, magalimoto amayenda m’misewu yokhotakhota. Paulendo wina, mmishonale yemwe anakhala kumbuyo kwa basi anayang’ana pawindo ndi kuona wilo limodzi la kumbuyo litaponda m’mphepete mwenimweni mwa chiphompho chakuya mamita oposa 190. Anatsinzina mpaka basiyo itachoka pamalopo.

Misewu ina n’njoipa ndiponso yaing’ono kwambiri. Galimoto ina yokhala ndi nyumba yomwe inkayenda mumsewu waung’ono woterewu inakumana ndi galimoto ina yaikulu. Galimoto yokhala ndi nyumbayo inayenda chambuyo mpaka pamwamba pa phiri pomwe panali kampata koti galimoto ziŵirizo zitha kudutsana.

Komabe, zotsatira za khama lotereri n’zochititsa chidwi kwambiri. Kodi mungakonde kumva zambiri zokhudza khama limeneli?

“Kuthirira” Nyanja ya Titicaca

Pamwamba pa mapiri a Andes pa mtundu wa mamita 3,800 pali Nyanja ya Titicaca. Nyanja imeneyi ili pamwamba kwambiri kuposa nyanja zonse za padziko lapansi zozunguliridwa ndi nthaka. Yambiri mwa mitsinje 25 yomwe imathira m’nyanja ya Titicaca imachokera m’mapiri ataliatali okutidwa ndi chipale chofeŵa. Ena mwa mapiri ameneŵa ndi aatali mamita 6,400. Chifukwa choti n’kokwera kwambiri, nyengo ya kumeneko n’njozizira ndipo alendo amalimbana ndi matenda odza chifukwa chopita ku dera lokwera kwambiri.

Zaka zingapo zapitazi, gulu la apainiya amene amalankhula chinenero cha Quechua ndi Aymara anapita ku zilumba za Amantani ndi Taquile pa Nyanja ya Titicaca. Popita anatenga nkhani ya pa filimu ya mutu wakuti “Kupenda Matchalitchi Mosamalitsa.” Nkhaniyo inasonyeza mosapita m’mbali chinyengo cha Matchalitchi Achikristu. Anthu anakondwera nayo kwambiri nkhaniyo. Munthu wina analandira abalewo mpaka anawapatsa chipinda m’nyumba yake kuti azikhalamo ndi kuphunzitsiramo Baibulo.

Pa msonkhano woyamba pachilumba cha Amantani panafika anthu 100 ndipo pa msonkhano wa pachilumba cha Taquile panafika anthu 140. Nkhani anaikamba m’chinenero cha chi Quechua. Munthu wina ndi mkazi wake omwe ankakhala kumtunda anati: “Nthaŵi yakwana yoti inu Mboni za Yehova mutikumbukire. Takhala tikupempherera kuti mubwere kuno.”

Kuwonjezera pa zilumba zikuluzikulu ziŵirizi, uthenga wabwino unafikanso pa zilumba zina “zoyandama” zokwana pafupifupi 40 za pa Nyanja ya Titicaca. Zilumba zoyandama? Inde, zilumbazi zinapangidwa ndi udzu wolimba womwe umamera m’malo osazama kwambiri a nyanja. Udzuwo umatumphuka ndi kuyanga pamwamba pa madzi. Kuti apange chilumba, anthuwo amawanda udzuwo n’kuulukaluka kupanga poti amangepo nyumba. Kenako amazirapo ndi matope n’kumanga kanyumba ka bango komwe amakhalamo.

Mboni za Yehova zinapeza boti kuti zikalalikire anthu a pa zilumba za pa Nyanja ya Titicaca. Botilo limatha kunyamula anthu 16. Zikafika pa zilumbazo, Mbonizo zimayenda pamwamba pa maudzu olukanawo kupita nyumba ndi nyumba. Mbonizo zinanena kuti nthaŵi zambiri zikamayenda zimamva kunjenjemera kwa chilumba cha maudzucho. Anthu a chizungulire safunika kuyenda pa malo ngati ameneŵa.

Koma midzi yambiri ya anthu olankhula chinenero cha chi Aymara ili m’mphepete mwa nyanja. Madera ameneŵa kumapitika mosavuta pa boti kusiyana ndi kuyenda pamtunda. Maboti athandiza kwambiri kuti anthu pafupifupi 400,000 amene amakhala m’chigawo chimenechi alandire uthenga wa Ufumu. Maboti adzagwirabe ntchito mpaka m’tsogolomu.

Kuthetsa Ludzu Lauzimu

Flavio ankakhala kumapiri a Andes m’mudzi wa Santa Lucía pafupi ndi Juliaca. Ku Tchalitchi chake cha Evangelical, akhala akum’phunzitsa za moto wa helo. Kwa zaka zambiri wakhala akuopa chilango cha moto wosatha chimenechi. Nthaŵi zambiri ankadzifunsa kuti zingatheke bwanji Mulungu wachikondi kulanga anthu kwamuyaya pa moto. Tito yemwe ndi mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova atafika m’mudziwo, anacheza ndi Flavio.

Funso loyamba lomwe Flavio anafunsa linali lakuti: “Kodi chipembedzo chanu chimaphunzitsa kuti anthu akalangika ku moto wa helo?” Tito anayankha kuti maganizo ameneŵa ndi osemphana kwambiri ndi maganizo a Mlengi ndiponso amanyozetsa dzina la Mulungu wachikondi, Yehova. Tito anagwiritsa ntchito Baibulo lomwe Flavio anali nalo kumuuza kuti anthu akufa sadziŵa kanthu koma kuti akuyembekezera kudzauka mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. (Mlaliki 9:5; Yohane 5:28, 29) Zimenezo zinam’tsegula maso Flavio. Nthaŵi yomweyo anavomera kumaphunzira Baibulo ndipo pasanapite nthaŵi yaitali anakhala Mkristu wobatizidwa.

Mudzi Womwe Umayamikira

Tangoganizani kusangalatsa kwake kubweretsa Malemba m’midzi yomwe anthu ake sanaonepo Baibulo kapena kulalikira kwa anthu omwe sanamvepo za Mboni za Yehova ndi uthenga wabwino umene zimalalikira! Zimenezo n’zimene zinachitikira apainiya atatu achikazi, Rosa, Alicia, ndi Cecilia, omwe analalikira m’midzi ya Izcuchaca ndi Conayca yomwe ili pamtunda wa mamita 3,600 m’dera lapakati pa dziko la Peru.

Atafika pamudzi woyamba, iwo sanapeze malo ogona. Analankhula ndi mkulu wa apolisi wa m’deralo kumuuza zomwe abwerera. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mkulu wa apolisiyo anawalola kugona kupolisi komweko. Mmaŵa kutacha, apainiyawo anapeza kanyumba komwe ankakhalamo pogwira ntchito yawo.

Posakhalitsa, inafika nthaŵi ya Chikumbutso cha pachaka cha Imfa ya Ambuye. Apainiyawo anali atalalikira m’nyumba zonse za m’mudzi wa Izcuchaca, kugaŵira mabaibulo ambiri, ndiponso kuyambitsa maphunziro a Baibulo ambiri. Chikumbutso chisanachitike, apainiyawo anapita kukawaitanira anthu ku mwambo umenewu. Ankawauza cholinga cha mwambowo ndiponso tanthauzo la zizindikiro zomwe amagwiritsa ntchito pamwambowo. Abale angapo anapemphedwa kuti adzathandize pamwambowo ndipo mbale wina anakamba nkhani. Zinalitu zosangalatsa kwambiri kuona kuti anthu 50 ochokera m’mudzi waung’onowo anafika pa mwambo wapadera umenewu. Kwa nthaŵi yawo yoyamba anazindikira zomwe Chakudya Chamadzulo cha Ambuye chimatanthauza. Komanso, chinali chamtengo wapatali kwa iwo kukhala ndi Mawu a Mulungu, Baibulo, m’manja mwawo.

Kutula Mitolo Yolemera

Kupereka madzi otsitsimula a choonadi cha m’Baibulo kwa anthu omwe ali akapolo a chipembedzo chonyenga kumasangalatsa nthaŵi zonse. Pisac anali munthu wolimbikira kwambiri za Ufumu wakale wa Inca. Anthu ambiri omwe tsopano akukhala m’dera limeneli akhala akuphunzitsidwa ziphunzitso zosemphana ndi malemba za moto wa helo. Ansembe amawauza kuti munthu atha kukaloŵa kumwamba pokhapokha iwo atam’pempherera.

Mpake kuti anthu ameneŵa ali ndi ludzu la madzi otsitsimula a choonadi cha m’Baibulo. Pamene Santiago yemwe ndi mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, ankalalikira khomo ndi khomo, anali ndi mwayi wouza munthu wina kuti anthu olungama adzakhala padziko lapansi la paradaiso. (Salmo 37:11) Santiago anamusonyeza munthuyo kuchokera m’Baibulo kuti akufa adzaukitsidwa ndipo kuti anthu adzaphunzira njira zangwiro za Yehova akumadziŵa kuti apeza moyo wosatha. (Yesaya 11:9) Nthaŵi yonse ya m’mbuyo yomwe munthuyo anali Mkatolika wodzipereka anakhala akukhulupirira mizimu ndiponso kumwa moŵa mwauchidakwa. Koma tsopano ali ndi chiyembekezo cha m’Baibulo ndiponso cholinga chodzakhala ndi moyo m’Paradaiso. Iye anatentha zinthu zonse zamizimu ndiponso anasiya kumwa mwauchidakwa. Anasonkhanitsa banja lake lonse n’kuyamba kuphunzira Baibulo. Kenako onse a m’banja lake anadzipatulira kwa Yehova Mulungu ndipo anabatizidwa.

Kuyamikira Kuchereza Alendo

Anthu okhala m’mapiri ameneŵa amalandira bwino alendo. Ngakhale kuti nyumba zawo si zazikulu kwambiri ndiponso kuti ndi anthu osauka, amagaŵirabe alendo zomwe ali nazo. Munthu wa m’deralo amene sanaphunzire miyezo yapamwamba ya m’Baibulo, angapatse alendo masamba a coca kuti azitafuna kwinaku akucheza. Koma akakhala Mboni, iye angapatse alendo shuga wodzaza sipuni yemwe mtengo wake n’ngofanana ndi masamba a coca kumeneko.

Mbale wina anapempha mmishonale wina kuti apite naye kuulendo wobwereza. Atakwera phiri lalitali movutika anafika ndipo anawomba m’manja kudziŵitsa mwininyumba. Iye anawauza kuti aloŵe m’nyumba ya udzuyo. Kuti aloŵe m’nyumbamo anachita kuŵerama chifukwa khomo lake linali lalifupi kwambiri. Ataloŵa m’nyumba yosasamalidwayo anayenda mosamala kudutsa pakatikati pomwe mayi anakumba dzenje n’kuikapo bulangete, n’kugonekapo mwana wake. Chifukwa chakuti anali kulephera kutuluka, mwanayo ankangodziimbira mosangalala, kwinaku makolo ake akucheza. Atakambirana kwambiri za madalitso a Ufumu, mayiyo anatulutsa chipanda chachitali cha thobwa. Kenako abalewo anachoka kupita kumunsi kwa phirilo kukacheza ndi anthu ena.

Zotuta Zochuluka

Tsopano m’chigawo chimenechi muli anthu opitirira 1,000 omwe akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Anthuŵa ali m’magulu pafupifupi 100. Abale amene anamaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki mumzinda wa Lima akuwatumiza kuti akakulitse magulu ameneŵa kukhala mipingo. Anthu oona mtima amene akhala mu ukapolo wa chipembedzo chonyenga ndi wa zamizimu kwa nthaŵi yaitali apeza ufulu chifukwa cha uthenga wabwino wa Ufumu. (Yohane 8:32) Ludzu lawo la madzi a choonadi likuthetsedwa.

[Chithunzi patsamba 10]

Kulalikira pazilumba “zoyandama” pa Nyanja ya Titicaca