Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Popeza kuti 1 Mafumu 8:8 amasonyeza kuti mitengo yonyamulira likasa la chipangano inali kuonekera m’Malo Opatulika, kodi mitengoyo anaiika bwanji?

Yehova, atam’patsa Mose pulani ya chihema m’chipululu, chinthu chachikulu m’pulaniyo chinali likasa la chipangano. M’kati mwa bokosi lokutidwa ndi golidi limeneli munali miyala ya Chilamulo ndi zinthu zina. Likasalo anali kulisunga m’chipinda cham’kati mwenimweni chotchedwa Malo Opatulikitsa. Pamwamba pa Likasalo panali akerubi aŵiri a golidi atatambasula mapiko awo. Mbali zonse ziŵiri za Likasa kunali mphete zomwe ankaloŵetsamo mitengo iŵiri ya sitimu yokutidwa ndi golidi kuti athe kunyamula Likasalo. Mwachionekere mitengoyo inali kudutsa kunsi kwa Likasalo mpaka kuseri. Choncho, Likasa likakhala m’Malo Opatulikitsa a chihema chomwe chinkayang’ana kummaŵa, mitengoyo inali kupingasa kuloza kum’mwera ndi kumpoto. Zimenezi sizinasinthe ngakhale pamene Likasalo linali m’kachisi yemwe Solomo anamanga.​—Eksodo 25:10-22; 37:4-9; 40:17-21. *

Chinsalu ndicho chinali kulekanitsa Malo Opatulikitsa ndi Malo Opatulika (chipinda cha kunja). Ansembe akakhala m’Malo Opatulika sanali kuyang’ana m’Malo Opatulikitsa ndi kuona Likasalo lomwe Mulungu anali kudzionetserapo. (Ahebri 9:1-7) N’chifukwa chake zomwe 1 Mafumu 8:8 amanena zingaoneke zovuta kumvetsa. Lembali limati: “Mitengoyo inali yaitali moti nsonga zake zinkaonekera ku Malo Opatulika, kumaso kwa chipinda cham’kati, koma siinali kuonekera kubwalo,” NW. Mfundo yomweyi ilinso pa 2 Mbiri 5:9. Kodi aliyense m’Malo Opatulika a kachisi ankaiona bwanji mitengoyo?

Anthu ena anena kuti mwina mitengoyo inkagunda chinsalu chotchinga kotero kuti inkaoneka chifukwa chinsalucho chinkatukumuka. Koma zimenezo sizingakhale zoona ngati mitengoyo inali kuloza kumpoto ndi kum’mwera popeza kuti chinsalucho chinkatchinga kummaŵa. (Numeri 3:38) Koma mwina zoona zingakhale zakuti mitengoyo inkaonekera ngati panali kam’mpata kakang’ono pakati pa chinsalu chotchingacho ndi khoma la kachisi kapena pamene mkulu wa ansembe akufuna kuloŵa m’Malo Opatulikitsa. N’kutheka kuti mitengo yaitaliyo inali kuonekera pa kam’mpata chifukwa chinsalucho chinali kutchinga Likasa lenilenilo kuti lisaoneke. Ngakhale kuti zimenezi zikuoneka kuti n’zoona, sitingatsimikize kotheratu kuti ndi mmene zinaliri.

Mwachionekere, pali zinthu zambiri zomwe tidzazidziŵabe m’tsogolo. Mtumwi Paulo anatchula mbali zina zoŵerengeka m’kalata yake yomwe analembera Ahebri. Kenako anati: “Ino si nthaŵi yoti tingafotokoze mwatsatanetsatane za zinthu zimenezi.” (Ahebri 9:5, NW) Kuuka kwa anthu okhulupirika kudzatsegula mwayi wophunzira kuchokera kwa anthu monga Mose, Aroni, Bezaleli ndi ena amene ankadziŵa bwino za kapangidwe ndi ntchito ya chihema.​—Eksodo 36:1.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mitengoyo sanali kuisolola m’mphete zija ngakhale pamene Likasalo linali pa malo ake m’chihema. Pachifukwa chimenechi, mitengoyo sanali kuigwiritsa ntchito ina. Komanso Likasalo sanayenera kuligwira. Akanakhala kuti mitengoyo anali kuisolola bwenzi pa ulendo uliwonse akuligwira poloŵetsa mitengoyo m’mphete za likasalo. Zomwe Numeri 4:6 amanena zokhudza “kupisako mphiko zake,” [“kuloŵetsanso mitengo,” NW] kungatanthauze kusendeza mitengoyo pokonzekera kunyamula likasa lolemeralo kupita nalo ku malo atsopano.