Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndani Adzatisiyanitsa ndi Chikondi cha Mulungu?

Ndani Adzatisiyanitsa ndi Chikondi cha Mulungu?

Ndani Adzatisiyanitsa ndi Chikondi cha Mulungu?

“Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.”​—1 YOHANE 4:19.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani kudziŵa kuti ena amatikonda kuli kofunika kwambiri? (b) Kodi ndani amene ali wofunika kwambiri kuti atikonde?

KODI kudziŵa kuti ena amakukondani n’kofunika motani kwa inu? Anthu kuyambira akali aang’ono mpaka kuuchikulire, amafuna kuti ena aziwakonda. Kodi munaonapo mwana atamuyangata mayi ake mwachikondi? Zilibe kanthu kuti kaya pakuchitika chiyani pafupi naye, akamayang’anitsitsa kumwetulira kwa mayi ake amaona kuti ndi wotetezeka. Amakhala atafatsa m’manja mwa mayi amene akumukonda. Kapena kodi mukukumbukira mmene munalili m’zaka zaubwana wanu pamene nthaŵi zinali zovuta kwambiri? (1 Atesalonika 2:7) Nthaŵi zina mwina simunali kudziŵa zimene munkafuna ndiponso mwina simunkatha kumvetsa mmene munali kuganizira. Komatu, kudziŵa kuti bambo anu ndi mayi anu anali kukukondani kunali kosangalatsa kwambiri. Kodi sikunali kothandiza kudziŵa kuti mutha kuwauza vuto lanu lililonse kapena kuwafunsa mafunso? Inde, pamoyo wathu wonse, chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri ndicho kukondedwa. Kukondedwa kumeneku kumatithandiza kuzindikira kuti ndife ofunika.

2 Chikondi chokhalitsa cha makolo chimathandiza kwambiri kuti munthu akule bwino ndi kukhala wokhazikika. Komabe, kukhulupirira kuti Atate wathu wakumwamba, Yehova, amatikonda n’kofunika kwambiri kuti tilimbe mwauzimu ndi kukhala ndi maganizo abwino. Anthu ena amene amaŵerenga magazini ino mwina analibe makolo amene anali kuwasamala bwino lomwe. Ngati zimenezi n’zomwenso zinakuchitikirani inu, khazikani mtima pansi. Mulungu amakukondani mokhulupirika ngakhale makolo anu sanali kukukondani kapena anali kungokukondani pang’ono chabe.

3. Kodi Yehova watsimikizira motani anthu ake kuti amawakonda?

3 Yehova ananena kudzera mwa mneneri wake Yesaya kuti mayi “angaiŵale” mwana wake wa pabere, koma Iye sangaiŵale anthu ake. (Yesaya 49:15) Mofananamo, Davide ananena motsimikiza kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) N’zolimbikitsatu zimenezo. Kaya chingakuchitikireni n’chiyani, koma ngati muli paubale weniweni ndi Yehova Mulungu, kumbukirani nthaŵi zonse kuti amakukondani kwambiri kuposa mmene munthu angakukondereni.

Dzisungeni M’chikondi cha Mulungu

4. Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anatsimikiza bwanji kuti Mulungu anali kuwakonda?

4 Kodi ndi liti pamene munadziŵa koyamba za chikondi cha Yehova? N’kutheka kuti zimene zinakuchitikirani zinali zofananirako ndi za Akristu a m’zaka za zana loyamba. Chaputala 5 cha kalata ya Paulo kwa Aroma chikufotokoza bwino mmene anthu ochimwa, omwe anapatuka kwa Mulungu, anadziŵira kuti Yehova amawakonda. Mu vesi 5 timaŵerenga kuti: “Chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m’mitima mwathu mwa mzimu woyera, amene wapatsidwa kwa ife.” Mu vesi 8, Paulo akuwonjezera kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.”

5. Kodi n’chiyani chinakuthandizani kuti mumvetse ndi kuyamikira kukula kwa chikondi cha Mulungu?

5 Mofananamo, atakuuzani choonadi cha m’Mawu a Mulungu ndi kuyamba kuchikhulupirira, mzimu woyera wa Yehova unayamba kugwira ntchito mumtima mwanu. Mwa njira imeneyi munayamba kumvetsa ndi kuyamikira kufunika kwa zimene Yehova anachita potumiza Mwana wake wokondedwa kuti akufereni. Motero, Yehova anakuthandizani kudziŵa mmene iye amawakondera kwambiri anthu. Kodi sizinakukhudzeni mtima mutadziŵa kuti ngakhale munabadwa muli wochimwa wotalikirana naye, Yehova watsegula njira kuti anthu awayese olungama ndi kuyembekeza kudzakhala ndi moyo wosatha? Kodi simunaone kuti Yehova amakukondani?​—Aroma 5:10.

6. N’chifukwa chiyani nthaŵi zina tingamve ngati tatalikirana ndi Yehova?

6 Munapatulira moyo wanu kwa Mulungu pamene chikondi cha Atate wanu wakumwamba chinakukhudzani mtima ndi kusintha moyo wanu kuti akulandireni. Tsopano muli pamtendere ndi Mulungu. Komabe, kodi nthaŵi zina mumamva ngati mwatalikirana ndi Yehova? Zimenezo zingatichitikire tonsefe. Koma kumbukirani nthaŵi zonse kuti Mulungu sasinthika. Amakonda nthaŵi zonse ndipo chikondi chake n’chokhazikika monga momwe lilili dzuŵa, limene silileka kuwalira ndi kutenthetsa padziko lapansi. (Malaki 3:6; Yakobo 1:17) Mosiyana, anthufe tingasinthe, ngakhale kusinthako kutakhala kwakanthaŵi chabe. Dziko likamatembenuka, theka la pulanetili limakhala mumdima. N’chimodzimodzinso kuti tikatembenuka n’kusiya Mulungu, ngakhale pang’ono chabe, tingaone kuti ubale wathu ndi iye wazilala. Zikatero, kodi tingatani kuti tibwezeretse ubale wathu wolimba?

7. Kodi kudzipenda kungatithandize motani kuti tidzisunge m’chikondi cha Mulungu?

7 Tikaona kuti tapatuka pa chikondi cha Mulungu, tidzifunse kuti: ‘Kodi ndikupeputsa chikondi cha Mulungu? Kodi ndapatuka kwa Mulungu wamoyo ndi wachikondi ndi kusonyeza kufooka m’chikhulupiriro m’njira zina? Kodi ndikusamalira “zinthu zathupi” m’malo mosamalira “zinthu za mzimu”?’ (Aroma 8:5-8; Ahebri 3:12) Ngati tadzisiyanitsa ndi Yehova, tingachitepo kanthu kuti tikonze vutolo, kuti tibwerere paubale wachikondi ndi wolimba ndi iye. Yakobo akutilimbikitsa kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Mverani mawu a Yuda akuti: “Okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu.”​—Yuda 20, 21.

Kusintha kwa Zinthu Sikumakhudza Chikondi cha Mulungu

8. Kodi pangakhale kusintha kwadzidzidzi kotani m’miyoyo yathu?

8 Moyo wathu m’dziko lino ungasinthe m’njira zambiri. Mfumu Solomo inaona kuti ‘nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimatigwera ife tonse.’ (Mlaliki 9:11, NW) Moyo wathu ungasinthe mwadzidzidzi. Tsiku lina tingakhale bwino koma mwina tsiku lotsatira tingadwale mwakayakaya. Tsiku lina zingaoneke ngati sadzatichotsa ntchito koma tsiku lina tingapezeke tikusoŵa ntchito. Munthu amene tinali kumukonda kwambiri angamwalire mwadzidzidzi. Akristu m’dziko lina angakhale pamtendere kwa nthaŵi yaitali ndithu, ndiyeno mwadzidzidzi pangabuke chizunzo chadzaoneni. Mwina akutiimba mlandu wabodza, ndipo chifukwa cha zimenezi angatiweruze mopanda chilungamo. Inde, moyo si wokhazikika ndiponso si wotetezeka konse.​—Yakobo 4:13-15.

9. N’chifukwa chiyani kuli koyenera kupenda mavesi ena a Aroma chaputala 8?

9 Zikatichitikira zinthu zomvetsa chisoni, mwina tingayambe kuona ngati Mulungu akutinyalanyaza, mwinanso kuganiza kuti wasiya kutikonda. Popeza zimenezi zingatichitikire tonsefe, tingachite bwino kupenda mosamalitsa mawu olimbikitsa a mtumwi Paulo amene ali mu Aroma chaputala 8. Mawuwo anali kuuza Akristu odzozedwa ndi mzimu. Komabe, mfundo zake zingagwirenso ntchito kwa a nkhosa zina, amene Mulungu wawayesa olungama ngati mabwenzi ake, monga analili Abrahamu Chikristu chisanafike.​—Aroma 4:20-22; Yakobo 2:21-23.

10, 11. (a) Kodi adani nthaŵi zina amaimba milandu kapena kuneneza anthu a Mulungu zotani? (b) N’chifukwa chiyani Akristu samadera nkhaŵa ndi milandu kapena kuneneza koteroko?

10 Ŵerengani Aroma 8:31-34. Paulo anafunsa kuti: “Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?” N’zoona kuti Satana ndi dziko lake loipali akulimbana nafe. Adani angatiimbe milandu yabodza, ngakhale m’makhoti a dziko limene tikukhala. Makolo ena awaimba milandu yakuti akudana ndi ana awo chifukwa chakuti sanalole kuti anawo alandire njira zina za mankhwala zimene zimaswa lamulo la Mulungu kapena kuwakaniza kupita kumapwando achikunja. (Machitidwe 15:28, 29; 2 Akorinto 6:14-16) Akristu ena okhulupirika awaimba mlandu wakuti ndi oukira chifukwa chakuti sanalole kupha anthu anzawo mwa kuchita nawo nkhondo kapena kuloŵerera m’nkhani zandale. (Yohane 17:16) Anthu ena otsutsa afalitsa nkhani zabodza m’manyuzipepala, pa wailesi, ndi pa wailesi zakanema. Ndiponso afalitsa mabodza akuti Mboni za Yehova ndi kagulu kachipembedzo koopsa.

11 Koma musaiwale kuti m’nthaŵi za atumwi, anthu ankanena kuti: “Za mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.” (Machitidwe 28:22) Ndiponso kodi kunenezako kuli n’phindu lanji? Alitu Mulungu amene akuwayesa olungama Akristu oona, chifukwa cha kukhulupirira kwawo nsembe ya Kristu. Kodi Yehova angasiyirenji kukonda anthu ake amene amamulambira atawapatsa mphatso yamtengo wapatali kuposa ina iliyonse yomwe ndi Mwana wake wokondedwa? (1 Yohane 4:10) Kristu anauka kwa akufa ndi kukhala kudzanja lamanja la Mulungu ndipo tsopano akuwakhalira kumbuyo Akristu. Ndani angatsutse zoti Kristu akuteteza anthu amene akum’tsatira? Kapena ndani angakwanitse kum’letsa Mulungu kukonda ndi kuona atumiki ake okhulupirika kukhala ofunika? Palibe!​—Yesaya 50:8, 9; Ahebri 4:15, 16.

12, 13. (a) Kodi ndi zochitika ziti zimene sizingatisiyanitse ndi chikondi cha Mulungu? (b) Kodi cholinga cha Mdyerekezi pochititsa mavuto amene tikukumana nawo n’chiyani? (c) N’chifukwa chiyani Akristu amapambana?

12 Ŵerengani Aroma 8:35-37. Kodi alipo kapena chilipo chimene chingatisiyanitse ndi chikondi cha Yehova ndi Mwana wake, Kristu Yesu? Satana angagwiritse ntchito atumiki ake a padziko lapansi kuvutitsa Akristu. M’zaka 100 zapitazi, anthu anazunza mwankhanza abale ndi alongo athu achikristu m’mayiko ambiri. M’madera ena lerolino, abale athu akukumana ndi mavuto a zachuma tsiku ndi tsiku. Ena akuvutika ndi njala kapena kusoŵa zovala zokwanira. Kodi cholinga cha Mdyerekezi pochititsa mavuto ameneŵa n’chiyani? Nthaŵi zambiri, chimodzi mwa zolinga zake ndicho kufooketsa kulambira koona kwa Yehova. Satana akufuna kuti tiziganiza kuti Mulungu wasiya kutikonda. Koma kodi Mulungu wasiyadi kutikonda?

13 Monga Paulo, amene anagwira mawu Salmo 44:22, taphunzira Mawu amene Mulungu analemba. Tikudziŵa kuti zimenezi zikutichitikira ife, “nkhosa” za Mulungu, chifukwa cha dzina lake. Nkhani imeneyi ikukhudza kuyeretsa kwa dzina la Mulungu ndiponso kutsimikizira kuti iye ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Mulungu walola mayesero chifukwa cha nkhani zazikulu ngati zimenezi osati chifukwa chakuti wasiya kutikonda. Mulungu akutitsimikizira kuti sanasiye kukonda anthu ake kuphatikizapo aliyense payekha, ngakhale tingakumane ndi mavuto otani. Vuto lililonse lomwe lingaoneke ngati likutivuta kupirira, tingaligonjetse ngati tipitirizabe kukhala okhulupirika. Kutsimikizika kwa chikondi chosasweka cha Mulungu kumatilimbitsa ndiponso kumatisunga.

14. N’chifukwa chiyani Paulo anatsimikiza kuti Mulungu amakondabe Akristu ngakhale iwo angakumane ndi mavuto?

14 Ŵerengani Aroma 8:38, 39. Kodi n’chiyani chinachititsa Paulo kutsimikiza kuti panalibe chimene chikanasiyanitsa Akristu ndi chikondi cha Mulungu? Mosakayika konse, zimene Paulo anakumana nazo potumikira zinam’chititsa kutsimikiza kuti mavuto sangadodometse chikondi cha Mulungu kwa ife. (2 Akorinto 11:23-27; Afilipi 4:13) Ndiponso, Paulo anali kudziŵa za cholinga chosatha cha Yehova ndiponso zimene Iye anachitira anthu ake mmbuyomo. Kodi imfa ingachititse kuti Mulungu asakonde anthu amene amam’tumikira mokhulupirika? Kutalitali! Mulungu amawakumbukira anthu okhulupirika amenewo akamwalira, ndipo adzawaukitsa panthaŵi yake.​—Luka 20:37, 38; 1 Akorinto 15:22-26.

15, 16. Fotokozani zinthu zina zimene sizingachititse Mulungu kusiya kukonda atumiki ake okhulupirika.

15 Kaya ndi tsoka lanji limene lingatigwere, kaya ndi ngozi yopundula, matenda osatha, kapena mavuto a zachuma, palibe chimene chingalepheretse Mulungu kukonda anthu ake. Angelo amphamvu, monga ngati mngelo wosamvera amene anakhala Satana, sangachititse kuti Yehova asiye kukonda atumiki ake odzipatulira. (Yobu 2:3) Maboma angaletse, kuika m’ndende, ndi kuzunza atumiki a Mulungu ndipo mwina kuwanena kuti ndi “anthu osafunika.” (1 Akorinto 4:13) Kudana nafe kwa mayiko kopanda chifukwa kumeneku kungalimbikitse anthu kutiukira, koma sikungachititse Wolamulira wamkulu wachilengedwe chonse kuti atisiye.

16 Monga Akristu, sitifunika kuopa kuti zinthu zimene Paulo ananena kuti “zilipo,” zochitika zosiyanasiyana m’dziko loipa lino, kapena “zinthu zilinkudza” m’tsogolo, zingachititse kuti Mulungu asiye anthu ake. Ngakhale kuti mphamvu za anthu kapena za mizimu yoipa zikulimbana nafe, chikondi chokhulupirika cha Mulungu chilipo kuti chitilimbitse. Monga mmene Paulo anatsindikira, “ngakhale utali, ngakhale kuya” sizingadodometse chikondi cha Mulungu. Inde, chilichonse chimene chingafune kutifooketsa sichingatisiyanitse ndi chikondi cha Mulungu. Ndiponso, palibe cholengedwa chilichonse chimene chingawononge ubale wa Mlengi ndi atumiki ake okhulupirika. Chikondi cha Mulungu sichitha; chimakhala mpaka muyaya.​—1 Akorinto 13:8.

Nyadirani Kukoma Mtima kwa Mulungu Nthaŵi Zonse

17. (a) N’chifukwa chiyani kukondedwa ndi Mulungu kuli ‘koposa moyo makomedwe ake’? (b) Kodi timasonyeza motani kuti timanyadira kukoma mtima kwa Mulungu?

17 Kodi chikondi cha Mulungu n’chofunika motani kwa inu? Kodi mumaganiza mmene anachitira Davide amene analemba kuti: “Pakuti chifundo [“kukoma mtima,” NW] chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. Potero ndidzakuyamikani m’moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m’dzina lanu.” (Salmo 63:3, 4) Ndithudi, kodi pali china chilichonse chimene moyo m’dziko lapansi lino ungatipatse chomwe n’chabwino kuposa kuti Mulungu atikonde ndi kukhala naye paubale wokhulupirika? Mwachitsanzo, kodi kufunafuna ntchito yapamwamba kuli bwino kusiyana ndi kukhala ndi mtendere wamaganizo ndi chimwemwe zimene zimabwera chifukwa cha kukhala paubale weniweni ndi Mulungu? (Luka 12:15) Akristu ena auzidwa kusankha kusiya kumvera Yehova kapena kuphedwa. Zimenezo zinachitikira Mboni za Yehova zambiri ku misasa ya ukaidi ya Nazi m’nthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Abale athu achikristu ambiri anasankha kukhalabe m’chikondi cha Mulungu ndipo analolera kuphedwa ngati kunafunikira kutero. Amene amakhalabe m’chikondi cha Mulungu mokhulupirika angakhale otsimikiza kuti iye adzawapatsa tsogolo losatha, chinthu chimene dziko lapansi silingapereke. (Marko 8:34-36) Komatu pali zambiri kuposa moyo wosatha wokha.

18. N’chifukwa chiyani moyo wosatha uli wosiririka kwambiri?

18 Ngakhale kuti n’zosatheka kukhala ndi moyo kosatha popanda Yehova, tayesani kuyerekeza mmene moyo wautali kwambiri ungakhalire popanda Mlengi. Ungakhale wosasangalatsa, wopanda cholinga chenicheni. Yehova wapatsa anthu ake ntchito yokhutiritsa yoti aichite m’masiku otsiriza ano. Motero tikukhulupirira kuti Yehova, Wamkulu amene amakwaniritsa zolinga zake, akadzatipatsa moyo wosatha, padzakhala zinthu zambiri zochititsa chidwi zoti tidzaziphunzire ndi kuzichita. (Mlaliki 3:11) Kaya tidzaphunzira zochuluka motani m’zaka zikwizikwi zikubwerazo, sitidzatha kumvetsa zonse za “kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu.”​—Aroma 11:33.

Atate Akonda Inu

19. Kodi Yesu Kristu anawatsimikizira chiyani ophunzira ake pamene anali kusiyana nawo?

19 Pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu pausiku womaliza kukhala ndi ophunzira ake okhulupirika 11, analankhula zambiri kuti awalimbikitse malinga ndi zimene zinali kubwera m’tsogolo. Onsewo anakhalabe ndi Yesu m’mayesero ake ndipo anaona kuti anali kuwakonda kwambiri. (Luka 22:28, 30; Yohane 1:16; 13:1) Ndiyeno Yesu anawatsimikizira kuti: “Atate yekha akonda inu.” (Yohane 16:27) Mawu amenewo anathandizatu ophunzirawo kudziŵa kuti Atate wakumwamba anali kuwakonda kwambiri.

20. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita zotani, ndipo mungakhulupirire zoti chiyani?

20 Ambiri amene ali ndi moyo lerolino, atumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Mosakayikira, tidzakumana ndi mayesero ambiri dongosolo la zinthu loipa lino lisanathe. Musalole mayesero oterowo kapena mavuto kukuchititsani kukayika ngati Mulungu amakukondani mokhulupirika. Mfundo yakuti Yehova amakukondani, ndi yosachita kufunsa. (Yakobo 5:11) Tiyeni tonsefe tipitirize kuchita mbali yathu, kumvera malamulo a Mulungu mokhulupirika. (Yohane 15:8-10) Tigwiritsetu ntchito mpata uliwonse kutamanda dzina lake. Tiyenera kukhala olimba pa zomwe tinasankha zopitiriza kuyandikira kwa Yehova m’pemphero ndi kuphunzira Mawu ake. Kaya m’tsogolo muchitika zotani, ngati tikuchita zonse zimene tingathe kuti tikondweretse Yehova, tidzakhalabe pamtendere ndipo tidzakhala ndi chikhulupiriro chonse kuti iye sangaleke kutikonda.​—2 Petro 3:14.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndani ali wofunika kwambiri kuti atikonde n’cholinga chakuti tikhale olimba mwauzimu ndi kukhala ndi maganizo abwino?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene sizingachititse kuti Yehova aleke kukonda atumiki ake?

• N’chifukwa chiyani kukondedwa ndi Yehova kuli ‘koposa moyo makomedwe ake’?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 13]

Ngati tikuona kuti tasiyana ndi chikondi cha Mulungu, tingachitepo kanthu kuti tikonze vutolo

[Chithunzi patsamba 15]

Paulo anali kudziŵa chifukwa chake anthu anali kumuzunza