Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Timachita Zonse Zomwe Tingathe!

Timachita Zonse Zomwe Tingathe!

Timachita Zonse Zomwe Tingathe!

“KACHITENI zonse zomwe mungathe.” Limeneli linali langizo lomwe wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova wina anauza mmishonale. Koma kodi anaperekeranji langizo lotereli kwa mtumiki yemwe wagwira ntchito kwa nthaŵi yaitali? Amishonale nawonso ndi anthu amene tsiku ndi tsiku amalimbana ndi mphemvu, njoka, kutentha, matenda, ndi mavuto ena osiyanasiyana.

Ndiponsotu amishonale a Mboni za Yehova ndi amuna ndi akazi wamba, Akristu omwe kukonda kwawo Yehova ndi anthu anzawo kumawalimbikitsa kukatumikira m’mayiko ena. Akuyesetsa kugwiritsa ntchito mphamvu zawo momwe angathere kutumikira Yehova, n’kumayembekezera iye kuti awapatse mphamvu zina.​—Aefeso 6:10.

Kuti tidziŵe zambiri zokhudza ntchito ya umishonale, tiyeni tiyerekeze kuti tsiku lina tapita kukacheza ku nyumba ya amishonale m’dziko la kumadzulo kwa Africa.

Zomwe Amishonale Amachita pa Tsiku

Nthaŵi yangotsala pang’ono kukwana 7 koloko yam’maŵa. Tafika ku nyumba ya amishonale pa nthaŵi yake kuti tichite nawo lemba la tsiku. Amishonale khumi atilandira ndi manja aŵiri ndipo atipatsa malo pa tebulo kuti tidye chakudya cha mmaŵa. Titakhazikika, m’mishonale wina wamkazi amene wagwira ntchito yake kwa zaka zambiri akuyamba kutisimbira nkhani zoseketsa zomwe anakumana nazo mu utumiki. Tili m’kati mokambirana, tcheyamani akutiuza kuti nthaŵi yakwana yoyamba lemba la tsiku. Lembalo akuti likhala m’chifalansa. Ngakhale kuti sitidziŵa kulankhula chinenerocho, kungoona mmene amishonale omwe anabadwira m’mayiko ena akulankhulira, zikuonekeratu kuti ali ndi khama lophunzira chinenerocho.

Litatha lemba la tsiku, akupemphera mochokera pansi pa mtima, ndipo kenako tikuyamba kudya chakudya cha mmaŵa. Titaika phala m’mbale yathu, mmishonale yemwe wakhala moyandikana nafe akutiuza kuti tiikemonso nthochi zoduladula. Tikumuuza kuti sitikonda nthochi, koma iye akuti tikangolawa nthochi zimenezo zomwe amalima m’deralo, tizikonda. Choncho, tikuika nthochizo pang’ono m’mbale yathu ya phala ija. Ee! Wanenadi zoona. Nthochizi zikukomadi kwambiri! N’zozuna ngati kirimu! Ndipo akutinso buledi wophikidwa mwa chifalansa yemwe ali pa tebuloyo am’phika mmamaŵa pa kasitolo kena koyandikana ndi nyumba ya amishonaleyo.

Tikadya chakudyachi, tiyenda ndi amishonale aŵiri okwatirana, Ben ndi Karen. Tamva kuti anthu amalabadira kwambiri uthenga wabwino m’dziko la kumadzulo kwa Africa limeneli, ndipo tikufuna titsimikize zimenezi.

Titafika pokwerera basi, tikupeza anthu ambiri akudikira basi. Pasanapite nthaŵi, amishonale amene tatsagana nawoŵa akuyamba kukambirana nkhani ya m’Baibulo ndi mayi wina pamodzi ndi mwana wake wamwamuna. Ife tangoima kumangomwetulira popeza sitidziŵa kulankhula Chifalansa! Pamene mayiyo akulandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, basi ikufika ndipo aliyense akufuna kukwera nthaŵi yomweyo. Pamene tikulimbana kuti tikwere, anthu akutikankha kumbuyo. N’zovuta kwambiri kuti ulimbe mpaka kukafika kumbuyo kwenikweni. Dalaivala atayamba kuyendetsa, tikugwirana mwamphamvu kwambiri. Nthaŵi iliyonse basiyo ikaima, anthu ena akukwerabe. Tikumwetulira anthu m’basiyo ndipo nawonso akutimwetulira. Tikufunitsitsa titalankhula nawo.

Pamene basiyo ikuyenda, tikumva phokoso ndipo tikusuzumira m’mawindo kuti tione zomwe zikuchitika kunja. Amayi aŵiri akuyenda m’mphepete mwa msewuwo atasenza katundu wolemera. Mayi winayo wadendekera mtsuko waukulu wa madzi. Ndipo munthu wina wogulitsa zinthu, wayala bulangete m’mphepete mwa msewu ndipo waikapo tinthu tosiyanasiyana kuti agulitse. Anthu ali piringupiringu kugula ndi kugulitsa zinthu zosiyanasiyana.

Mwadzidzidzi, Ben yemwe waimirira pafupi ndi ine akumva kuti chinachake chikumujompha mwendo. Kodi chingakhale chiyani? M’povuta kudziŵa chifukwa basi yadzaza kwambiri. Koma kenako akumvanso kujompha. Akuyang’ana pansi, ndipo akuona kuti m’thumba lomwe lili pansi muli bakha wamoyo yemwe wakhala akutulutsa mutu wake n’kumamujompha mwendo. Ben akufotokoza kuti n’kutheka kuti mwini bakhayo akupita naye ku msika kuti akam’gulitse.

Tafika ku gawo lathu ndipo tikusangalala kuti ticheza m’mudzi weniweni wa ku Africa. Pofika pa nyumba yoyamba, Ben akuwomba m’manja mwamphamvu kudziŵitsa mwininyumba. Ndi mmene anthu kuno “amagogodera pa khomo.” Mwamuna wachinyamata akutuluka ndipo akunena kuti watanganidwa koma akuti tibwerenso masana.

Pa nyumba yotsatira tikupeza mayi amene akulankhula chinenero china moti Ben sakutha kumva. Mayiyo akuitana mwana wake wamwamuna kuti azimasulira zomwe Ben akunena. Pamene Ben akumaliza, mayiyo akulandira kabuku kofotokoza nkhani za m’Baibulo ndipo mwanayo akulonjeza kuti aziwafotokozera mayi akewo. Pa nyumba yachitatu tikupeza achinyamata ambiri atakhala panja. Aŵiri akuchoka mwamsanga pa mipando yawo kuti alendo akhalepo. Kenako tikuyamba kukambirana nkhani ya kugwiritsa ntchito mtanda polambira. Pomaliza tikugwirizana kuti mlungu wotsatira tidzapitiriza kukambiranako. Nthaŵi yakwana tsopano yoti tikaonane ndi munthu wotanganidwa uja. Ndipotu iye wamva kale zina zomwe tinali kukambirana ndi achinyamata aja. Ali ndi mafunso ambiri okhudza Baibulo ndipo akupempha kuti tiziphunzira naye Baibulo. Ataona ndandanda ya zochita zake, Ben akuvomera kudzabweranso nthaŵi ngati yomweyo mlungu wamaŵa. Pobwerera ku nyumba ya amishonale kuti tikadye nkhomaliro, Ben ndi Karen akunena kuti ayenera kukonzanso bwino ndondomeko yawo yochititsa maphunziro a Baibulo kuopera kuti atha kuyambitsa maphunziro ambiri koma n’kumalephera kuwachititsa.

Tikuwathokoza chifukwa cholankhula bwino Chifalansa. Ben akufotokoza kuti iye ndi Karen akhala amishonale kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndipo tsopano azoloŵera kulankhula Chifalansa. Kuphunzira chinenero china si kophweka, koma khama ndilo lawathandiza, iwo akutero.

Nthaŵi yakwana 12:30  masana ndipo amishonale onse ali pa tebulo kuti adye nkhomaliro. Wina akutiuza kuti tsiku lililonse pamakhala mmishonale mmodzi yemwe amakonza chakudya cha mmawa, cha masana, ndiponso kutsuka mbale. Lero, mmodzi wa amishonalewo waphika chakudya chomwe amachidziŵa bwino kwambiri maphikidwe ake ndipo n’chokhetsa dovu. Wakazinga nkhuku ndiponso wawotcha mbatata mwa chifalansa ndi kukonza saladi.

Kodi Ben ndi Karen achita chiyani masana ano? Iwo akufotokoza kuti munthu aliyense masana amabisala kutentha kwa dzuŵa la m’ma 1 koloko mpaka 3 koloko. Choncho, imeneyi ndiyo nthaŵi imene amishonale amaŵerenga kapena kupuma. Sitikudadwa pamene Karen akutiuza kuti sizimatenga nthaŵi kuti amishonale atsopano azoloŵere zimenezi.

Tikapuma, tipitanso kukalalikira. Munthu wina wachidwi yemwe Ben wakhala akufika ku nyumba kwake maulendo angapo sitikumupezabe pa nyumba, koma pamene Ben akuwomba m’manja amuna aŵiri achinyamata akutuluka m’nyumbamo. Iwo akunena kuti mwininyumbayo anatchulapo za kubwera kwa Ben ndipo wawauza kuti alandire buku lophunzirira Baibulo la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tikuwasiyira bukulo. Kenako, tikunyamuka kukakwera basi kupita komwe Karen akachititse phunziro la Baibulo ndi mayi wina wachidwi.

Pamene tikuyenda mumsewu umene anthu ali piringupiringu, Karen akutiuza kuti tsiku lina anakumana ndi mayi ameneyu pamene iwo pamodzi ndi anthu ena anali m’galimoto. Karen anam’patsa mayiyo thirakiti kuti aŵerenge pa ulendowo. Ataŵerenga, mayiyo anapempha thirakiti lina. Anaŵerenga thirakiti lachiŵirilo ndi chidwi kwambiri. Potsika, iwo anapangana kuti Karen azipita ku nyumba ya mayiyo kuti azikaphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Ndipo lero, Karen akaphunzira ndi mayiyo mutu wachisanu m’bulosha limeneli.

Lero tasangalala kwambiri kulalikira, komabe pali mbali zinanso zomwe tikufuna kudziŵa zokhudza ntchito ya umishonale. Amishonale omwe atilandira akutiuza kuti tikabwerera ku nyumba akatikonzera zakudya zongokhwasula ndipo akayankha mafunso athu.

Mmene Amakhalira

Pamene tikudya mazira okazinga, buledi wophikidwa mwa chifalansa, komanso tchizi, iwo akutiuza zambiri zokhudza moyo wa umishonale. Lolemba ndilo tsiku lomwe amishonale amapuma kapena kuchita zomwe akufuna. Pa tsikuli, amishonale ambiri amalembera makalata mabanja awo ndiponso anzawo. Kumva zomwe zikuchitika kumudzi ndi chinthu chofunika kwambiri kwa iwo, ndipo amishonale amakonda kutumiza ndi kulandira makalata.

Kulankhulana kwabwino nthaŵi zonse pocheza ndi amishonale anzawo ndiponso kukambirana nkhani zauzimu n’kofunika kwambiri chifukwa amishonale amagwira ntchito ndiponso kukhala m’nyumba imodzi. Kuwonjezera pa kuchita phunziro la umwini nthaŵi zonse, Lolemba lililonse madzulo, amishonale amaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito magazini a Nsanja ya Olonda. Ben akufotokoza kuti pamene amishonale ochokera m’mayiko osiyanasiyana akukhalira limodzi n’kosatheka kupeŵa kusiyana maganizo pa nkhani zina zazing’ono. Komabe, zochita zauzimu monga phunziro la banja zimawathandiza kukhalabe amtendere ndi ogwirizana. Iye akunena motsindika kuti kusadziona ngati wofunika kuposa ena kumathandiza kwambiri.

Kudzichepetsa n’kofunika kwambiri. Amishonale amawatumiza osati kuti anthu akawatumikire koma kuti akatumikire anthu. Amishonale anzathu aona kuti mawu ovuta kwambiri kunena m’chinenero chilichonse ndi akuti “pepani,” makamaka pamene munthu akupepesa pa zomwe wanena kapena kuchita mosakonzekera. Ben akutikumbutsa chitsanzo cha m’Baibulo cha Abigayeli yemwe anapepesa chifukwa cha nkhanza za mwamuna wake ndipo zimenezo zinathetsa vuto lomwe likanakhala ngozi yaikulu. (1 Samueli 25:23-28) ‘Kukhala mwamtendere’ n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale mmishonale wabwino.​—2 Akorinto 13:11.

Amishonale amachita msonkhano kamodzi pa mwezi kuti akambirane nkhani zokhudza banja lawo komanso kusintha ndandanda ya kusamalira nyumba yawo. Akatero, onse amadya zokhwasulakhwasula. Zimenezi n’zothandiza kwambiri ndipo n’zosangalatsa.

Tikatha kudya chakudya chamadzulo tiyendera nyumba ya amishonaleyi. Tikuona kuti ngakhale nyumbayi ndi yaikulu bwino amishonale amagwirizana kuisamalira kuti ikhale yaukhondo. M’nyumbayi muli firiji, makina ochapira, ndiponso chitofu. Karen akutiuza kuti m’nyumba za m’mayiko otentha ngati kuno kumadzulo kwa Africa mumakhalanso zipangizo zobweretsa mphweya wozizira. Nyumba zoyenera, zakudya zabwino, ndiponso kusamala pa nkhani zaumoyo zimathandiza amishonale kukhalabe athanzi ndi kupindula pa ntchito yawo.

Kuika Mtima pa Zinthu Zolimbikitsa

Tachita chidwi kwambiri ndi zonse zomwe taona. Kodi ifenso tingachite nawo umishonale? Kodi tingadziŵe bwanji zimenezi? Amishonale omwe atilandiraŵa akutiuza zinthu zingapo zoti tiziganizire.

Choyamba akutiuza kuti amishonale achikristu sapita kukafunafuna chuma. Amafunafuna anthu oona mtima amene akufuna kuphunzira malonjezo osangalatsa a Mulungu. Amalalikira kwa maola 140 pa mwezi. Choncho, kukonda kulalikira ndi chinthu chofunika kwambiri.

Ndiyeno tikudzifunsa kuti, ‘bwanji nanga za njoka, abuluzi, ndiponso mphemvu’? Ben akutiuza kuti ngakhale amishonale ambiri amakumana ndi zimenezi, iwo amazizoloŵera. Iye akuwonjezera kuti kulikonse kumene munthu angapite kukachita umishonale kumakhala ndi zovuta zake zapadera. Ndipo m’kupita kwa nthaŵi amishonale amaika mtima pa zinthu zolimbikitsa ntchito yawo. Zinthu zomwe poyamba ungazione ngati “zovuta,” zimadzakhala zosadetsa nkhaŵa ndipo mwinanso zosangalatsa. Mmishonale wina yemwe anatumikira m’mayiko a kumadzulo kwa Africa kwa zaka zambiri asanabwerere kwawo chifukwa cha maudindo ake, ananena kuti kunali kovuta kwambiri kusiya utumiki wake kuposa mmene zinalili pochoka m’dziko la kwawo zaka zambiri mmbuyomo. Ntchito yake ya umishonale ndiyo inali kumudzi kwawo.

Kodi Mwakonzeka?

Ben ndi Karen atiuza zambiri zoti tiziganizire. Nanga bwanji inuyo? Kodi munayamba mwaganizapo zokatumikira monga mmishonale ku dziko lina? Ngati ndi choncho, mwina mwatsala pang’ono kukwaniritsa cholinga chimenechi koposa mmene mumaganizira. Kukonda utumiki wa nthaŵi zonse ndiponso kukonda kuthandiza anthu ndizo zinthu zofunika kwambiri. Kumbukirani kuti amishonale ndi amuna ndi akazi ngati inu nomwe osati zimphona zauzimu ayi. Amachita zonse zomwe angathe kuti akwaniritse ntchito yofunika kwambiri imeneyi.

[Zithunzi patsamba 27]

Tsiku lililonse amaliyamba ndi kukambirana lemba la m’Baibulo

[Zithunzi pamasamba 28, 29]

Zochitika ku Africa

[Chithunzi patsamba 29]

Moyo wa umishonale umakhala wosangalatsa kwambiri