Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsopano Ndadziŵa Vuto Langa!”

“Tsopano Ndadziŵa Vuto Langa!”

“Tsopano Ndadziŵa Vuto Langa!”

ZIMENEZI n’zimene mwamuna wina ku Tokyo ananena ataŵerenga mbiri ya moyo wa munthu winawake mu Nsanja ya Olanda ya December 1, 2000. Nkhaniyo inali ndi mutu wakuti “Simudziŵa Chimene Chidzagwa Maŵa,” ndipo inasimba zomwe zinachitikira yemwe kale anali m’mishonale amene ankadwala matenda a kuvutika maganizo.

M’kalata yake yomwe analembera ofalitsa magazini ino, munthu wa ku Tokyoyo ananena kuti: “Zizindikiro zomwe zinali m’nkhaniyo zinali ndendende ndi momwe ndinali kumvera m’thupi mwanga. Choncho ndinapita ku chipatala komwe anakandiuza kuti ndili ndi matenda a kuvutika maganizo. Dokotala yemwe anandiyeza anadabwa kwambiri. Iye anati, ‘Nthaŵi zambiri anthu amene ali ndi matendaŵa sadziŵa kuti akudwala.’ Munandithandiza kudziŵa vuto langa, matendaŵa asanafike poipa.”

Anthu miyandamiyanda pa dziko lonse lapansi amapindula m’njira zosiyanasiyana akaŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Nkhani zake zimakhala zowaphunzitsa ndiponso zogwira mtima. Magazini a Nsanja ya Olonda tsopano amasindikizidwa m’zinenero 141, ndipo magazini a Galamukani! amasindikizidwa m’zinenero 83. Inunso mudzasangalala kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthaŵi zonse.