Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Valani Kuleza Mtima’

‘Valani Kuleza Mtima’

‘Valani Kuleza Mtima’

‘Valani mtima wachifundo ndi kuleza mtima.’​—AKOLOSE 3:12.

1. Fotokozani chitsanzo chabwino cha kuleza mtima.

RÉGIS yemwe akukhala kumwera chakumadzulo kwa France, anabatizidwa n’kukhala Mboni ya Yehova mu 1952. Kwa zaka zambiri, mkazi wake anachita chilichonse chimene anatha kuti amulepheretse kutumikira Yehova. Ankabaya matayala a galimoto yake kuti amulepheretse kupita ku misonkhano. Ndipo tsiku lina anam’tsatira pamene anali kulalikira uthenga wa Baibulo ku nyumba ndi nyumba n’kumamuseka pamene anali kulankhula ndi eninyumbawo za uthenga wabwino wa Ufumu. Komabe, Régis anapitiriza kuleza mtima ngakhale kuti mkazi wakeyo sanaleke kutsutsa. Motero, Régis ndi chitsanzo chabwino kwa Akristu, popeza Yehova amafuna kuti anthu onse amene amamulambira akhale oleza mtima kwa ena.

2. Kodi tanthauzo lenileni la liwu la Chigiriki limene analitembenuza kuti “kuleza mtima” ndi liti, ndipo liwulo limasonyeza chiyani?

2 Tanthauzo lenileni la liwu la Chigiriki limene analitembenuza kuti “kuleza mtima” ndilo “mzimu wautali.” Baibulo la Chicheŵa la Revised Nyanja (Union) Version linamasulira liwu limeneli kuti “kuleza mtima” maulendo asanu ndi anayi, ndipo maulendo anayi analimasulira kuti “chilekerero” kapena “kulekerera,” ndipo kamodzi analimasulira kuti “kuonetsera chipiriro.” Mawu onse a Chihebri ndi Chigiriki amene anawamasulira kuti “kuleza mtima” amaphatikizapo kulolera ndiponso kusakwiya msanga.

3. Kodi maganizo a Akristu ndi osiyana motani ndi a Agiriki a m’zaka za zana loyamba pa nkhani ya kuleza mtima?

3 Agiriki a m’zaka za zana loyamba ankati kuleza mtima si khalidwe labwino. Afilosofi a Chistoiki sanali kuligwiritsa ntchito n’komwe liwuli. William Barclay amene anachita maphunziro apamwamba a Baibulo, ananena kuti kuleza mtima “n’kotsutsana ndi khalidwe la Agiriki” amene mwa zina ankanena kuti “osalolera ngati wina wakunyoza kapena kukuvulaza.” Iye akuti: “Kwa Agiriki, mwamuna weniweni anali munthu amene anali kuyesetsa kubwezera. Koma kwa Akristu, mwamuna weniweni ndi munthu amene safuna kubwezera ngakhale kuti angathe kutero.” Agiriki mwina ankaganiza kuti kuleza mtima kumasonyeza kupanda mphamvu, koma pano, monganso zilili ndi nkhani zina, “chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zawo; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yawo.”​—1 Akorinto 1:25.

Chitsanzo cha Kristu cha Kuleza Mtima

4, 5. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chabwino chotani cha kuleza mtima?

4 Kristu Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha kuleza mtima ndipo chitsanzo chake n’chotsatira kwa Yehova yekha basi. Iye anasonyeza kuleza mtima kodabwitsa nthaŵi imene anavutika maganizo kwambiri. Ulosi unanena za iye kuti: “Anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa om’senga, motero sanatsegula pakamwa pake.”​—Yesaya 53:7.

5 Yesu anasonyezatu kuleza mtima kwakukulu nthaŵi yonse imene anatumikira padziko lapansi. Anapirira mafunso onyenga a adani ake ndi chipongwe chimene om’tsutsa anali kumunenera. (Mateyu 22:15-46; 1 Petro 2:23) Analeza mtima kwa ophunzira ake, ngakhale pamene ankapitiriza kukangana kuti wamkulu ndani pakati pawo. (Marko 9:33-37; 10:35-45; Luka 22:24-27) Ndipotu Yesu analeza mtima kwambiri pa usiku woti aperekedwa maŵa pamene Petro ndi Yohane anagona atawauza kuti ‘akhale maso.’​—Mateyu 26:36-41, NW.

6. Kodi Paulo anapindula motani ndi kuleza mtima kwa Yesu, ndipo tikuphunzirapo chiyani pamenepa?

6 Yesu anapitiriza kuleza mtima atamwalira ndi kuukitsidwa. Mtumwi Paulo anadziŵa bwino kwambiri zimenezi, chifukwa poyamba iye anali kuzunza Akristu. Paulo analemba kuti: “Mawuŵa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwoŵa ine ndine woposa; komatu mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m’tsogolo kufikira moyo wosatha.” (1 Timoteo 1:15, 16) Kaya moyo wathu unali wotani m’mbuyomo, ngati tikhulupirira Yesu, adzaleza nafe mtima ngakhale kuti adzafuna kuti tichite “ntchito zoyenera kutembenuka mtima.” (Machitidwe 26:20; Aroma 2:4) Mauthenga amene Kristu anatumiza ku mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asia Minor amasonyeza kuti ngakhale amaleza mtima, amayembekezera kuti munthu awongolere makhalidwe ake.​—Chivumbulutso, chaputala 2 ndi 3.

Chipatso cha Mzimu

7. Kodi kuleza mtima ndi mzimu woyera n’zogwirizana motani?

7 Paulo m’chaputala 5 cha kalata yake kwa Agalatiya anafotokoza kusiyana kwa ntchito za thupi ndi chipatso cha mzimu. (Agalatiya 5:19-23) Popeza kuleza mtima ndi khalidwe lina la Yehova, ndiye kuti khalidweli limachokera kwa iye ndipo ndi chipatso cha mzimu wake. (Eksodo 34:6, 7) Ndipotu, kuleza mtima n’kwachinayi pa m’ndandanda wa chipatso cha mzimu chimene Paulo anafotokoza pamodzi ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, . . . chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Choncho, mzimu woyera ndi umene umalimbikitsa atumiki a Mulungu pamene akuonetsa kuleza mtima kumene Iye amasonyeza.

8. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikulitse chipatso cha mzimu, kuphatikizapo kuleza mtima?

8 Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amaumiriza munthu kuti alandire mzimu wake. Tiyenera kuulola kuti ugwire ntchito mwa ife. (2 Akorinto 3:17; Aefeso 4:30) Timalola kuti mzimuwo ugwire ntchito m’moyo mwathu mwa kukulitsa zipatso zake m’zochita zathu zonse. Paulo atafotokoza ntchito za thupi ndi chipatso cha mzimu, anawonjezera kuti: “Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.” (Agalatiya 5:25; 6:7, 8) Kuti tikwanitse kukhala oleza mtima, tiyeneranso kukulitsa zipatso zina zonse zimene mzimu woyera umabala mwa Mkristu.

“Chikondi Chikhala Chilezere”

9. Kodi Paulo ayenera kuti anauza Akorinto kuti “chikondi chikhala chilezere” pa chifukwa chiti?

9 Paulo anasonyeza kuti pali kugwirizana kwapadera pakati pa chikondi ndi kuleza mtima pamene ananena kuti: “Chikondi chikhala chilezere.” (1 Akorinto 13:4) Albert Barnes, wa maphunziro apamwamba a Baibulo, anapereka ganizo lakuti Paulo anatsindika zimenezi chifukwa cha kulimbana ndi mikangano imene inali mumpingo wachikristu wa ku Korinto. (1 Akorinto 1:11, 12) Barnes anati: “Liwu limene analigwiritsa ntchito pano [lotanthauza kuleza mtima] limatsutsana ndi kuchita zinthu mopupuluma. Limatsutsananso ndi kulankhula kapena kulingalira moipidwa ndiponso kupsa mtima msanga. Limasonyeza KULOLERA KWA NTHAŴI YAITALI munthu akavutitsidwa kapena kuputidwa.” Lerolinonso, chikondi ndi kuleza mtima zimathandiza kwambiri kuti mumpingo wachikristu mukhale mtendere.

10. (a) Kodi chikondi chimatithandiza motani kuti tikhale oleza mtima, ndipo mtumwi Paulo analangiza motani pankhani imeneyi? (b) Kodi munthu wina wa maphunziro apamwamba a Baibulo anapereka ndemanga yotani pa kuleza mtima ndi chifundo cha Mulungu? (Onani mawu a m’munsi.)

10 “Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima. Chikondi . . . sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima.” Motero, chikondi chimatithandiza m’njira zambiri kuti tikhale oleza mtima. * (1 Akorinto 13:4, 5) Chikondi chimatithandiza kuti tilolerane wina ndi mnzake moleza mtima ndi kukumbukira kuti tonse ndife opanda ungwiro ndipo timalakwa. Chimatithandiza kuti tikhale oganizira ena ndi okhululuka. Mtumwi Paulo akutilimbikitsa kuti tiyende koyenera “ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.”​—Aefeso 4:1-3.

11. N’chifukwa chiyani kuleza mtima kuli kofunika kwambiri pamene Akristu akugwirira ntchito pamodzi, kuphunzira pamodzi, kapena kukhalira limodzi?

11 Kuleza mtima kwa Akristu kumathandiza kuti pakhale mtendere pamene akugwirira ntchito pamodzi, kuphunzira pamodzi, kapena kukhalira limodzi, kaya ndi m’mipingo, panyumba za Beteli, m’nyumba za amishonale, magulu antchito yomanga, kapena m’sukulu zachikristu. Popeza kuti ndi anthu osiyana, amakonda zosiyana, analeredwa mosiyana, ali ndi miyezo ya ulemu yosiyana, mwinanso angasiyane pankhani za ukhondo, pangakhale kukhumudwitsana nthaŵi zina. Kukhumudwitsana kungakhaleponso m’mabanja. Kusakwiya msanga n’kofunika kwambiri. (Miyambo 14:29; 15:18; 19:11) Inde, tonsefe tifunika kuleza mtima, kupirira moleza poyembekezera kuti zinthu zikhala bwino.​—Aroma 15:1-6.

Kuleza Mtima Kumatithandiza Kuti Tipirire

12. N’chifukwa chiyani kuleza mtima kuli kofunika kwambiri pamene tikuyesedwa?

12 Kuleza mtima kumatithandiza kupirira ziyeso zooneka ngati zamuyaya kapena zosatha msanga. Ndizo zinachitikira Régis amene tam’tchula m’ndime yoyamba ija. Mkazi wake anam’tsutsa kwa zaka zambiri kuti asatumikire Yehova. Koma tsiku lina anauza mwamuna wakeyu misozi ikutuluka kuti: “Ndadziŵa, ichi n’choonadi. Ndithandizeni. Ndikufuna kuphunzira Baibulo.” M’kupita kwa nthaŵi mkaziyu anabatizidwa n’kukhala Mboni. Régis anati: “Zimenezi zinasonyeza kuti Yehova anadalitsa zaka zimene ndakhala ndikuvutika, kuleza mtima, ndi kupirira.” Kuleza mtima kwake kunapindula.

13. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti apirire, ndipo chitsanzo chake chingatithandize motani kupirira?

13 Kale m’zaka za zana loyamba C.E., mtumwi Paulo anali chitsanzo chabwino cha kuleza mtima. (2 Akorinto 6:3-10; 1 Timoteo 1:16) Atatsala pang’ono kumwalira, anamulangiza mnzake wachinyamata Timoteo, ndi kum’chenjeza kuti Akristu onse adzayesedwa. Paulo ananena kuti iye anali chitsanzo ndipo anafotokoza makhalidwe achikristu omwe ndi ofunika kuti munthu apirire. Analemba kuti: “Iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro, mazunzo, kumva zoŵaŵa; zotere zonga anandichitira m’Antiokeya, m’Ikoniyo, m’Lustra, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m’zonsezi Ambuye anandilanditsa. Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:10-12; Machitidwe 13:49-51; 14:19-22) Tonsefe tifunika chikhulupiriro, chikondi, ndi kuleza mtima kuti tipirire.

Kuvala Kuleza Mtima

14. Kodi Paulo anayerekezera makhalidwe a Mulungu monga kuleza mtima ndi chiyani, ndipo analangiza chiyani Akristu a ku Kolose?

14 Mtumwi Paulo anayerekezera kuleza mtima komanso makhalidwe ena a Mulungu ndi zovala zimene Akristu ayenera kuvala atachotsa zochita za ‘umunthu wakale.’ (Akolose 3:5-10) Analemba kuti: “Valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:12-14.

15. Kodi n’chiyani chimachitika Akristu ‘akavala’ kuleza mtima ndi makhalidwe ena a Mulungu?

15 Anthu mumpingo ‘akavala’ mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima, ndi chikondi, amatha kuthetsa mavuto ndi kupitirizabe kutumikira Yehova mogwirizana. Makamaka oyang’anira achikristu afunika kukhala oleza mtima. Pangakhale nthaŵi zambiri pamene afunika kudzudzula Mkristu wina, koma angadzudzule m’njira zosiyanasiyana. Paulo anafotokoza maganizo abwino pamene analembera Timoteo kuti: “Tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.” (2 Timoteo 4:2) Inde, nkhosa za Yehova zimafunika kuzisamala nthaŵi zonse moleza mtima, mwaulemu, ndiponso mwachifundo.​—Mateyu 7:12; 11:28; Machitidwe 20:28, 29; Aroma 12:10.

“Oleza Mtima pa Onse”

16. Kodi tikakhala “oleza mtima pa onse” zotsatira zake zingakhale zotani?

16 Kuleza mtima kwa Yehova kwa anthu kumafuna kuti ifenso tikhale “oleza mtima pa onse.” (1 Atesalonika 5:14) Zimenezi zikutanthauza kuti tifunika kuleza mtima kwa achibale athu omwe si Mboni, anansi athu, anthu amene timagwira nawo ntchito, ndi anzathu a kusukulu. Mboni zathetsa malingaliro olakwika ambiri amene anthu anali nawo pa iwo mwa kupirira chipongwe ndi kutsutsa kwa anthu amene ankagwira nawo ntchito kapena kuphunzira limodzi kusukulu. Nthaŵi zina achita zimenezi kwa zaka zambiri. (Akolose 4:5, 6) Mtumwi Petro analemba kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.”​—1 Petro 2:12.

17. Kodi tingatsanzire motani chikondi ndi kuleza mtima kwa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezo?

17 Kuleza mtima kwa Yehova kudzachititsa kuti anthu miyandamiyanda apulumuke. (2 Petro 3:9, 15) Ngati titsanzira chikondi ndi kuleza mtima kwa Yehova, tidzapitiriza moleza mtima kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa ena kuti agonjere ku ulamuliro wa Ufumu wa Kristu. (Mateyu 28:18-20; Marko 13:10) Ngati titati tisiye kulalikira, kudzakhala ngati tikufuna kuletsa kuleza mtima kwa Yehova ndi kusazindikira cholinga chake chothandiza anthu kuti alape.​—Aroma 2:4.

18. Kodi Paulo anawapempherera chiyani Akolose?

18 Paulo analembera Akristu a ku Kolose, ku Asia Minor kuti: “Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tinamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti mukayende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu; olimbikitsidwa m’chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe.”​—Akolose 1:9-11.

19, 20. (a) Kodi tingapeŵe bwanji kuona kuleza mtima kwa Yehova komwe kukupitirira kukhala chiyeso? (b) Kodi tingapindule chiyani ngati tikhala oleza mtima?

19 Kuleza mtima kwa Yehova komwe kukupitirira sikungakhale chiyeso kwa ife ngati ‘tadzazidwa ndi chizindikiritso cha chifuniro chake,’ chomwe n’chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Tidzapitiriza “kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino,” makamaka yolalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) Ngati tipitiriza kuchita zimenezi mokhulupirika, Yehova ‘adzatilimbitsa m’chilimbiko chonse,’ kuti tithe “kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe.” Tikachita zimenezo, ‘tidzayenda koyenera Ambuye,’ ndipo tidzakhala ndi mtendere umene umabwera ngati ‘tikum’kondweretsa monsemo.’

20 Tiyenitu titsimikize kotheratu kuti kuleza mtima kwa Yehova n’kwanzeru. Kumatithandiza kuti tipulumuke ndiponso kupulumutsa anthu amene amamvetsera pamene tiwalalikira ndi kuwaphunzitsa. (1 Timoteo 4:16) Kukulitsa chipatso cha mzimu monga chikondi, chifundo, ubwino, chifatso, ndi kudziletsa kudzatithandiza kuleza mtima mokondwera. Tidzatha kukhala mwamtendere ndi anthu a m’banja lathu ndiponso abale ndi alongo athu mumpingo. Kuleza mtima kudzatithandizanso kukhala bwino ndi anzathu a kuntchito kapena kusukulu. Ndiponso kuleza mtima kwathu kudzakhala ndi cholinga chopulumutsa olakwa ndi kulemekeza Mulungu woleza mtima, Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Pothirira ndemanga zimene Paulo ananena kuti “chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima,” Gordon D. Fee yemwe ndi wa maphunziro apamwamba a Baibulo analemba kuti: “Malinga ndi zimene Paulo anaphunzitsa, mawu ameneŵa [kuleza mtima ndi kukoma mtima] akuimira mbali ziŵiri za maganizo a Mulungu kwa anthu (yerekezerani ndi Aroma 2:4). Kulolera kwachikondi kwa Mulungu kukuonekera m’kuletsa kwake ukali pa kupanduka kwa anthu ndiponso kukoma mtima kwake kumene kumaonekera m’nthaŵi zambirimbiri zimene wasonyeza chifundo. Motero Paulo analongosola za chikondi mwa kuyamba kufotokoza mbali ziŵiri zimenezi za Mulungu amene kudzera mwa Kristu analolera ndi kuwachitira chifundo anthu amene anayenera kuwalanga.”

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Kristu ali chitsanzo chabwino cha kuleza mtima m’njira ziti?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale oleza mtima?

• Kodi kuleza mtima kumathandiza motani mabanja, Akristu amene akuchitira zinthu pamodzi kapena kukhalira pamodzi, ndiponso akulu?

• Kodi tingapindule ndiponso kupindulitsa ena motani ngati tikhala oleza mtima?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Yesu analeza nawo mtima ophunzira ake ngakhale pamene anavutika maganizo kwambiri

[Chithunzi patsamba 16]

Oyang’anira achikristu akulimbikitsidwa kusonyeza chitsanzo chabwino cha kuleza mtima pochitira zinthu abale awo

[Chithunzi patsamba 17]

Ngati titsanzira chikondi ndi kuleza mtima kwa Yehova, tidzapitiriza kulalikira uthenga wabwino

[Chithunzi patsamba 18]

Paulo anapemphera kuti Akristu ‘akhale oleza mtima pamodzi ndi chimwemwe’