Zinthu Zowononga Mitengo
Zinthu Zowononga Mitengo
M’NTHAŴI za m’Baibulo mitengo inali yamtengo wapatali. Mwachitsanzo, Abrahamu atagula malo oti aikepo maliro a mkazi wake wokondedwa Sara, mitengo anaiŵerengera m’pangano logulitsa malowo.—Genesis 23:15-18.
Lerolinonso, mitengo n’njamtengo wapatali zedi ndipo mayiko ambiri amaikirapo mtima kwambiri kuiteteza. Buku lakuti State of the World 1998, limanena kuti: “Ngakhale kuti anthu ambiri m’mayiko ozizira amadera nkhaŵa kwambiri mitengo ya m’mayiko otentha, mwina sakudziŵa kuti mitengo yomwe ili m’mayiko awo ndiyo ili patalipatali ndiponso pangozi yowonongedwa ndi zinthu zowononga mitengo kuposa ina yonse.” Kodi n’chiyani chikuopseza mitengo ya m’mayiko a kumpoto kwa Ulaya ndi ku North America? Anthu ambiri amati kudula mitengo, koma pali zinthu zina zomwe zikuwononga mitengo mobisa. Kodi zinthu zimenezi n’chiyani? Kuipitsa mphweya ndiponso mvula ya asidi. Zinthu zimenezi zimafooketsa mitengo pang’onopang’ono ndipo zimaichititsa kukhala yosavuta kugwidwa ndi tizilombo kapena matenda.
Kwa zaka makumi ambiri, akatswiri a zachilengedwe ndiponso anthu ena, akhala akuchenjeza za kufunika kosamala zinthu za moyo ndi chikhalidwe chawo. Cha m’ma 1980, asayansi a ku Germany atafufuza zomwe kuipitsa mphweya ndi mvula ya asidi zimachita pa zinthu zamoyo ndi chikhalidwe chawo, anaona kuti: ‘Ngati sitichitapo kanthu, ndiye kuti pofika m’chaka cha 2000, anthu azidzangoona mitengo pa zithunzi ndi m’mafilimu basi. Mwayi kuti dziko lili ndi mphamvu yodzikonzanso yomwe mpaka pano yathandiza mitengo kuti ithe kulimbana ndi zinthu zowononga zimenezi.
Komabe, pomaliza pake Mulungu ndiye adzachite zonse kuteteza zamoyo ndi chikhalidwe chawo. “Iye amwetsa mapiri mochokera m’zipinda zake” ndipo “ameretsa msipu ziudye ng’ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu.” Ndipo Iye walonjeza “kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Salmo 104:13, 14; Chivumbulutso 11:18) Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri pamene kuipitsa mpweya kudzakhala kulibe m’dziko lapansi lomwe anthu adzakhalemo kwamuyaya!—Salmo 37:9-11.