Anthu Miyandamiyanda Padziko Lonse Akuyamikira Baibulo la New World Translation
Imani Amphumphu Ndi Otsimikiza Kotheratu
Anthu Miyandamiyanda Padziko Lonse Akuyamikira Baibulo la New World Translation
NTCHITO yofuna kusamala kwambiri imeneyi yomasulira Baibulo inatenga zaka 12, miyezi itatu, ndi masiku 11. Komabe, mbali yomaliza ya Baibulo latsopanoli inatha pa March 13, 1960. Baibuloli linatchedwa New World Translation of the Holy Scriptures.
Patangopita chaka chimodzi Mboni za Yehova zinasindikiza mbali za Baibuloli kukhala Baibulo limodzi. Panthaŵiyo, mu 1961 anafalitsa mabaibulo okwana 1,000,000. Koma panopa mabaibulo amene afalitsidwa aposa pa 100,000,000. Zimenezi zachititsa Baibulo la New World Translation kukhala limodzi mwa mabaibulo ofalitsidwa kwambiri kuposa ena onse. Koma kodi n’chiyani chinachititsa Mboni kumasulira Baibulo limeneli?
N’chifukwa Chiyani Anamasulira Baibulo Latsopano?
Mboni za Yehova zakhala zikugwiritsa ntchito mabaibulo a Chingelezi osiyanasiyana kwa zaka zambiri kuti zimvetse ndiponso kulalikira uthenga wa m’Malemba Opatulika. Ngakhale kuti mabaibulo ameneŵa ali ndi ubwino wake, nthaŵi zambiri mawu ake amakhala osakanikirana ndi miyambo yachipembedzo ndiponso ziphunzitso za Matchalitchi Achikristu. (Mateyu 15:6) Choncho Mboni za Yehova zinazindikira kuti n’kofunika kukhala ndi Baibulo lomwe limanena ndendende zomwe zinalembedwa poyambirira ndiponso mouziridwa.
Ntchito yokonzekera kumasulira Baibulo latsopanoli inayambika mu October 1946 pamene Nathan H. Knorr yemwe anali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ananena kuti Baibulo latsopano likufunika. Pa December 2, 1947, komiti yotchedwa New World Bible Translation Committee inayamba kumasulira Baibulo lomwe linali lofanana ndendende ndi zomwe zinalembedwa poyambirira. Baibuloli linaphatikizapo mfundo zochokera m’mipukutu ya Baibulo yolembedwa pamanja yomwe akatswiri apeza posachedwapa ndipo komitiyi inagwiritsa ntchito mawu omwe oŵerenga a masiku ano amamva mosavutikira.
Mbali yoyamba ya Baibulo limeneli yotchedwa New World Translation of the Christian Greek Scriptures itatulutsidwa mu 1950, zinali zoonekeratu kuti omasulirawo anakwaniritsa zolinga zawo. Nkhani za m’Baibulo zomwe kale zinali zovuta kumva, tsopano zinali kumveka bwino kwambiri. Mwachitsanzo, talingalirani za mawu ovuta kuwamvetsa aŵa opezeka pa Mateyu 5:3: “Odala ali osauka mumzimu.” M’Baibulo la New World Translation, vesili analimasulira kuti: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” Funso lomwe ophunzira ake anafunsa Yesu lakuti: “Chizindikiro cha kufika kwanu n’chiyani?” analimasulira kuti, “chizindikiro cha kukhalapo kwanu n’chiyani?” (Mateyu 24:3) Mwachionekere, Baibulo la New World Translation limamveka mwatsopano.
Akatswiri ambiri amaphunziro anagoma nalo Baibulo limeneli. Mwachitsanzo, katswiri wina wachinenero cha Chihebri ndi Chigiriki wa ku Britain, Alexander Thomson, ananena kuti Baibulo la New World Translation n’lolondola mochititsa chidwi pa nkhani ya mmene analembera mawu a Chigiriki osonyeza kuti zinthu zikuchitikabe. Mwachitsanzo, lemba la Aefeso 5:25 analimasulira kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu” m’malo mongonena kuti, “Amuna inu kondani akazi anu.” Thomson pofotokoza za Baibulo la New World Translation anawonjezera kuti: “Palibe Baibulo lina lililonse lomwe limagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki mokwanira ndi mochititsa chidwi chonchi komanso mosasinthasintha.”
Mbali yomwe Baibulo la New World Translation limachititsanso chidwi kwambiri ndi mmene limagwiritsira ntchito dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova m’Malemba Achihebri ndiponso Achigiriki. Popeza kuti dzina la Mulungu m’Chihebri linkapezeka nthaŵi pafupifupi 7,000 m’mbali ya Baibulo imene amati Chipangano Chakale, n’zodziŵikiratu kuti Mlengi wathu amafuna kuti olambira ake azigwiritsa ntchito dzina lakelo. Amafunanso kuti olambira ake azimudziŵa monga munthu. (Eksodo 34:6, 7) Choncho, Baibulo la New World Translation lathandiza anthu miyandamiyanda kuchita zimenezo.
Baibulo la New World Translation Alisindikiza M’zinenero Zambiri
Kungoyambira pomwe Baibulo la New World Translation linatulutsidwa m’Chingelezi, Mboni za Yehova padziko lonse zikulakalaka zitakhala nalo m’chinenero chakwawo. Ndipotu mpake kulakalaka zimenezo. M’mayiko ena kupeza Baibulo m’chinenero chakumeneko kunali kovuta kwambiri chifukwa chakuti akuluakulu a mabungwe ogulitsa mabaibulo sanali kusangalala kuona mabaibulo awo ali ndi Mboni za Yehova. Ngakhale zinali choncho, nthaŵi zambiri mabaibulo otereŵa anali kubisa ziphunzitso zofunika kwambiri. Chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi ndi Baibulo lina la m’chinenero chakum’mwera kwa Ulaya lomwe limabisa mawu ofunika kwambiri omwe Yesu ananena okhudza dzina la Mulungu akuti “Dzina lanu liyeretsedwe.” Baibulo limenelo limati “Anthu akulemekezeni.”—Mateyu 6:9.
Pomwe chimafika chaka cha 1961 n’kuti omasulira atayamba kale kumasulira Baibulo la Chingelezi la New World Translation m’zinenero zina. Patangopita zaka ziwiri zokha Baibulo la New World Translation of the Christian Greek Scriptures anali atalimasulira m’zinenero zina zisanu ndi chimodzi. Panthaŵiyo n’kuti Mboni zitatu mwa Mboni zinayi zilizonse padziko lonse zikuŵerenga Baibuloli m’chinenero chakwawo. Komabe kuti Mboni za Yehova zikwanitse kugaŵira Baibulo limeneli kwa anthu miyandamiyanda panafunika kugwira ntchito mwachamuna.
Mu 1989 kukwaniritsa cholinga chimenechi kunayamba kuoneka kuti n’kotheka pamene anakhazikitsa dipatimenti yothandiza pa nkhani yomasulira mabuku yotchedwa Translation Services ku likulu la Mboni za Yehova. Dipatimenti imeneyi inakonza njira yomasulira yomwe imagwiritsa ntchito kompyuta pofufuza mawu a m’Baibulo. Kugwiritsa ntchito njira imeneyi kwachititsa kuti Malemba Achigiriki Achikristu aziwamasulira m’zinenero zina kwa chaka chimodzi ndipo Malemba Achihebri aziwamasulira m’zaka ziŵiri zokha. Nthaŵi imeneyi n’njochepa kwambiri poyerekezera ndi nthaŵi yomwe imafunika pantchito yomasulira Baibulo. Chiyambireni kugwiritsa ntchito njirayi, mabaibulo a New World Translation a m’zinenero zina 29 zomwe anthu oposa mabiliyoni aŵiri amalankhula, amasuliridwa kuchokera m’Chingelezi ndi kutulutsidwa. Panopa ntchito ili m’kati kumasulira Baibuloli m’zinenero zina 12. Pakadali pano Baibulo la Chingelezi la New World Translation, lathunthu kapena mbali yake chabe, alimasulira kale m’zinenero 41.
Zaka 50 zadutsa tsopano kuchokera pamene mbali yoyamba ya Baibulo la New World Translation inatulutsidwa pa August 3, 1950 pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti Kuwonjezeka kwa Teokalase womwe unachitikira ku New York City. Pa msonkhanowo, Nathan H. Knorr analimbikitsa osonkhanawo kuti: “Landirani Baibulo limeneli. Liŵerengeni lonse. Mudzasangalala kwambiri poliŵerenga. Liphunzireni, chifukwa lidzakuthandizani kumvetsa bwino Mawu a Mulungu. Ligaŵireni Akolose 4:12, NW.
kwa anthu ena.” Tikukulimbikitsani kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, chifukwa chakuti uthenga wake utha kukuthandizani ‘kuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.’—[Chithunzi pamasamba 8, 9]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
“Kutulutsa Baibulo la New World Translation”
Baibulo la New World Translation lomwe koyamba linatuluka m’Chingelezi, tsopano likupezeka lonse lathunthu, kapena mbali yake ina, m’zinenero zina 41.
Malemba Achigiriki Achikristu Baibulo lathunthu
1950 1
1960-69 6 5
1970-79 4 2
1980-89 2 2
1990-Panopa 29 19