Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Lamulo la Chikhalidwe Likugwirabe Ntchito

Lamulo la Chikhalidwe Likugwirabe Ntchito

Lamulo la Chikhalidwe Likugwirabe Ntchito

Ngakhale anthu ambiri amaona kuti Yesu ndi amene analankhula za Lamulo la Chikhalidwe lophunzitsa anthu khalidwe labwino, iyeyo anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.”​—Yohane 7:16

INDE, Gwero la chiphunzitso cha Yesu, kuphatikizapo chomwe anthu amati Lamulo la Chikhalidwe, ndiye Mlengi wathu, dzina lake Yehova Mulungu, amene anatuma Yesu.

Pachiyambi Mulungu anafuna kuti anthu onse azichitira anzawo zimene akufuna kuti anzawowo aziwachitira. Mwa njira imene analengera anthu, anaika chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene anthuwo angachitire anthu ena zabwino. “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Genesis 1:27) Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu mwachikondi anapatsa anthu makhalidwe ake apadera pamlingo winawake kuti iwo azikhala ndi mtendere, chimwemwe ndi umodzi​—ngakhale kosatha. Chikumbumtima chawo chimene Mulungu anawapatsa atachiphunzitsa bwino, chikanawathandiza kuchitira anzawo zimene akufuna anzawowo aziwachitira.

Dyera Linakula

Popeza chiyambi cha munthu chinali chabwino chotere, chinalakwika n’chiyani? Yankho losavuta ndi lakuti anthu analola makhalidwe oipa monga dyera ndi kudzikonda kukula. Anthu ambiri amaidziŵa bwino nkhani ya m’Baibulo yopezeka mu Genesis chaputala 3 imene imasimba za banja la anthu oyamba. Satana mdani wa Mulungu atalimbikitsa Adamu ndi Hava, iwo chifukwa cha dyera anakana ulamuliro wa Mulungu pofuna ufulu wodzilamulira ndi wodzisankhira okha zochita. Dyera lawo ndi kupanduka kwawo kunawatayitsa zambiri, komanso zimenezi zinaloŵetsa ana awo oti adzabadwe kutsogolo m’mavuto aakulu. Zimenezo zinasonyeza bwino lomwe mapeto ake omvetsa chisoni onyalanyaza chiphunzitso chomwe chinadzadziŵika monga Lamulo la Chikhalidwe. Choncho “uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”​—Aroma 5:12.

Ngakhale kuti mtundu wa anthu unakana njira za Yehova Mulungu zachikondi, iye sanautaye. Chitsanzo chake n’chakuti Yehova anapatsa mtundu wa Israyeli Chilamulo kuti chiwatsogolere. Chinawaphunzitsa kuchitira anzawo zimene akanafuna anzawowo kuwachitira. Chilamulocho chinawapatsa malangizo a mmene akanasamalira akapolo, ana a masiye, ndi akazi a masiye. Chinafotokoza mmene akanasamalira milandu ngati yopwetekana, kuba munthu ngakhalenso katundu. Malamulo a ukhondo anasonyeza kusamala za thanzi la ena. Analiponso malamulo ena okhudza za kugonana. Pofotokoza chidule chake cha Chilamulo chonsecho, Yehova anati kwa anthuwo: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha,” ndipo Yesu analankhulanso mawu ameneŵa. (Levitiko 19:18; Mateyu 22:39, 40) Chilamulo chinafotokozanso mmene Aisrayeli akanachitira ndi alendo okhala pakati pawo. Chinati: “Usam’psinja mlendo; pakuti mudziŵa mtima wa mlendo popeza munali alendo m’dziko la Aigupto.” Kunena kwina, Aisrayeli anafunika kuwachitira chifundo osoŵa ndi kuwakomera mtima.​—Eksodo 23:9; Levitiko 19:34; Deuteronomo 10:19.

Yehova anadalitsa mtunduwo pamene iwo anatsata Chilamulocho mokhulupirika. Nthaŵi imene Davide ndi Solomo amalamulira, mtunduwo unatukuka ndipo anthu anali kusangalala. Mbiri yakale imatiuza kuti: “Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera. Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake.”​—1 Mafumu 4:20, 25.

Nkhani yomvetsa chisoni ndi yakuti mtendere wa mtunduwo ndi chitetezo chawo sizinakhalitse. Ngakhale kuti Aisrayeli anali ndi Chilamulo cha Mulungu, iwo sanachisunge koma analola dyera kuwalanda mtima wosamala ena. Mapeto ake a zonsezi komanso mpatuko wawowo anali akuti munthu aliyense anali ndi mavuto kudzanso mtundu wonsewo. Pomaliza pake, Yehova analola Ababulo kuwononga ufumu wa Yuda, mzinda wa Yerusalemu ndi kachisi wake wokongola mu 607 B.C.E. Chifukwa chiyani? “Popeza simunamvera mawu anga, taonani, Ine ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.” (Yeremiya 25:8, 9) Kalanga ine, tsoka lake kukula chifukwa chosiya kulambira Yehova koyera!

Chitsanzo Chofunika Kutengera

Yesu Kristu sanaphunzitse chabe Lamulo la Chikhalidwe. Anatiikiranso chitsanzo chabwino politsata. Anali kuchitira anthu ena zabwino kuchokera pansi pa mtima. (Mateyu 9:36; 14:14; Luka 5:12, 13) Tsiku lina Yesu ali pafupi ndi mudzi wa Nayini, anaona mkazi wa masiye ali wachisoni pamwambo wokaika maliro a mwana wake mmodzi yekhayo. Nkhaniyo m’Baibulo imati: “Pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye.” (Luka 7:11-15) Malinga ndi mtanthauzira mawu wa Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, mawuwo akuti “anagwidwa ndi chifundo” amatanthauza “kukhudzika mtima kwambiri.” Anamva mtima wake ukupweteka ngati wa mkaziyo, ndipo zinam’limbikitsa kuchita zotheka kuti athetse chisonicho. Yesu ataukitsa mnyamatayo ndi ‘kum’pereka kwa amake, ‘ mkazi wa masiyeyo anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya!

Ndiponso, Yesu analolera kuvutika ndi kupereka moyo wake dipo kuti anthu akamasuke ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Anachita zimenezi mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. Ngati pali chitsanzo chopambana chotsata Lamulo la Chikhalidwe, ndi chimenechi.​—Mateyu 20:28; Yohane 15:13; Ahebri 4:15.

Anthu Amene Amatsata Lamulo la Chikhalidwe

Kodi alipo anthu masiku athu ano amene amatsata Lamulo la Chikhalidwe? Inde alipo, ndipo amatero osati chabe pamene zikuwakomera kutero. Mwachitsanzo, pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse imachitika, Mboni za Yehova ku Germany, dziko limene chipani cha Nazi chimalamulira, zinakhalabe zokhulupirika kwa Mulungu ndipo chikondi chawo pa mnansi sichinathe. Izo zinakana kuswa Lamulo la Chikhalidwe. Pamene boma linalimbikitsa anthu kudana ndi Ayuda onse ndi kuwachitira tsankho, Mboni zinapitiriza kutsata Lamulo la Chikhalidwe. Ngakhale kumisasa ya chibalo, zinasamalabe anthu anzawo, ndipo zinali kupatsako anzawo chakudya, Ayuda ndi omwe sanali Ayuda omwe anali kusoŵa chakudyacho. Ndiponso, ngakhale kuti boma linazilamula kupita ku nkhondo kukapha anzawo, Mbonizo zinakana monganso mmene sizinafunire anzawowo kuzipha. Zikanatheka bwanji kupha anthu amene izo zinafunikira kuwakonda ngati mmene zimadzikondera? Chifukwa chokana zimenezo, ambiri anawatumiza ku misasa ya chibalo, koma si zokhazo ayi. Ambiri anaphedwanso.​—Mateyu 5:43-48.

Pamene mukuŵerenga nkhani ino, mukupindula ndi chitsanzo china chotsatira Lamulo la Chikhalidwe. Mboni za Yehova zikudziŵa kuti masiku ano anthu ambiri akuvutika kwadzaoneni opanda owathandiza. N’chifukwa chake Mbonizo mwaufulu zikuchita zonse zotheka kuthandiza anzawo kuphunzira zinthu zopatsa chiyembekezo cha m’tsogolo ndi malangizo aphindu opezeka m’Baibulo. Imeneyi ndi ntchito yophunzitsa imene ikuchitika padziko lonse lapansi kuposa kale. Ndiye chachitika n’chiyani? Malinga ndi ulosi wa Yesaya 2:2-4, “anthu ambiri,” inde, oposa mamiliyoni asanu ndi imodzi padziko lonse lapansi ‘aphunzitsidwa njira za Yehova, ndipo akuyenda m’mayendedwe ake.’ Mophiphiritsa aphunzira ‘kusula malupanga awo kukhala zolimira, ndi nthungo zawo kukhala anangwape.’ Apeza mtendere ndi chitetezo masiku ano ovuta.

Nanga Bwanji Inuyo?

Taganizani kaye za chisoni ndi mavuto amene akhalapo pa mtundu wa anthu chifukwa cha kuswa Lamulo la Chikhalidwe kuyambira pa kupanduka kwa mu Edene kumene Satana Mdyerekezi anayambitsa. Cholinga cha Yehova n’chakuti asinthe zinthu posachedwa pomwepa. Motani? “Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akawononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yohane 3:8) Zimenezi zidzachitika mu Ufumu wa Mulungu umene uli m’manja mwa Yesu Kristu, wanzeru ndiponso wamphamvu, amene anaphunzitsa Lamulo la Chikhalidwe ndi kulitsata.​—Salmo 37:9-11; Danieli 2:44.

Mfumu Davide ya Israyeli wakale inati: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya. Tsiku lonse achitira chifundo, nakongoletsa; ndipo mbumba zake zidalitsidwa.” (Salmo 37:25, 26) Kodi simukuvomereza kuti anthu ambiri masiku ano amangolanda ndi kufunkha m’malo ‘mochitira chifundo ndi kukongoza’? Zoona, kutsata Lamulo la Chikhalidwe kungadzetse mtendere weniweni ndi chitetezo chifukwa kumapatsa munthu mpata wolandira madalitso tsopano ndi m’tsogolo mu Ufumu wa Mulungu. Ufumu wa Mulungu udzathetseratu mbali iliyonse yotsala ya dyera ndi kuipa padziko lapansi, kuchotsa dziko lilipoli ndi olamulira ake oipa ndi kubweretsa dziko latsopano limene Mulungu apange. Zikadzatero, anthu onse adzasangalala kutsata Lamulo la Chikhalidwe.​—Salmo 29:11; 2 Petro 3:13.

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Yesu sanaphunzitse chabe Lamulo la Chikhalidwe. Anatiikiranso chitsanzo chabwino politsata

[Zithunzi patsamba 7]

Kutsata Lamulo la Chikhalidwe kungadzetse mtendere weniweni ndi chitetezo