Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi langizo la Mulungu limene lili pa Yeremiya 7:16 likutanthauza kuti Akristu sangapempherere munthu amene wachotsedwa mumpingo wachikristu chifukwa cha kuchimwa koma osalapa?

Yehova atalengeza kuti adzalanga Ayuda osakhulupirika, anamuuza Yeremiya kuti: “Iwe usapempherere anthu aŵa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.”​—Yeremiya 7:16.

N’chifukwa chiyani Yehova analetsa Yeremiya kuti asawapempherere Aisrayeli? Mwachionekere, chinali chifukwa chakuti anaswa mwadala Chilamulo chake. Iwo anali ‘kuba, kupha, kuchita chigololo, kulumbira zonama, kupereka nsembe kwa Baala, ndiponso kutsata milungu yina.’ Anali kuchita zimenezi poyera ndiponso mopanda manyazi. N’chifukwa chake Yehova anauza Ayuda osakhulupirikawo kuti: “Ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbewu zonse za Efraimu.” Ndithudi, kunali kosayenera kuti Yeremiya kapena munthu wina aliyense apemphe Yehova kuti asinthe chiweruzo chake.​—Yeremiya 7:9, 15.

Mogwirizana ndi zimenezi, mtumwi Yohane analemba za kupemphera kwa Mulungu moyenera. Choyamba, anawatsimikizira Akristu kuti: “Ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.” (1 Yohane 5:14) Ndiyeno, Yohane pofotokoza za kupempherera ena anapitiriza kuti: “Wina akaona mbale wake ali kuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzam’patsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.” (1 Yohane 5:16) Yesu ananenanso za tchimo limene wochimwayo “sadzakhululukidwa.” Tchimo limeneli ndi lochimwira mzimu woyera.​—Mateyu 12:31, 32.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti onse amene achotsedwa mumpingo wachikristu chifukwa cha kuchimwa koma osalapa achita tchimo “la kuimfa” ndipo motero safunika kuwapempherera? Zimenezi sizingakhale choncho chifukwa nthaŵi zina machimo otero sali a kuimfa. Ndipotu n’kovuta kudziŵa kuti ndi a kuimfa kapena ayi. Chitsanzo chabwino ndi cha Mfumu Manase ya Yuda. Iye anamanga maguwa a nsembe a milungu yonyenga, kupereka ana ake nsembe, kukhulupirira mizimu, ndi kuika fano losema m’kachisi wa Yehova. Ndipo Baibulo limati Manase ndi anthu ‘anachita choipa, kuposa amitundu amene Yehova anawawononga pamaso pa ana a Israyeli.’ Pa zolakwa zonsezi, Yehova analanga Manase mwa kum’pititsa ku ukapolo ku Babulo atam’manga matangadza.​—2 Mafumu 21:1-9; 2 Mbiri 33:1-11.

Kodi machimo a Manase ngakhale kuti anali aakulu kwambiri anali a kuimfa? Ayi, chifukwa nkhaniyo ikupitiriza kuti: “Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. Anam’pempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nam’bwezera ku Yerusalemu m’ufumu wake. Pamenepo anadziŵa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.”​—2 Mbiri 33:12, 13.

Motero, tisafulumire kunena kuti munthu wachita tchimo la kuimfa chabe chifukwa chakuti amuchotsa mu mpingo. Pangatenge nthaŵi kuti munthuyo aonekere bwinobwino mmene alili mumtima mwake. Ndipotu, nthaŵi zambiri cholinga china chom’chotsera munthu mumpingo n’chakuti azindikire kulakwa kwake ndi kuti alape ndi kubwerera.

Popeza munthuyo salinso mu mpingo, anthu oyamba kudziŵa ngati akusintha mtima wake kapena maganizo ake ndi amene amakhala naye pafupi, monga mwamuna kapena mkazi wake kapena a m’banja lake. Amene akuona kusintha kumeneko angadziŵe kuti wolakwayo sanachite tchimo la kuimfa. Mwina angafune kum’pempherera kuti apeze chilimbikitso m’Mawu ouziridwa a Mulungu ndi kuti Yehova amuchitire wochimwayo mogwirizana ndi zimene Iye akufuna.​—Salmo 44:21; Mlaliki 12:14.

Ngakhale kuti ena angaone umboni wokwanira wokhulupirira kuti wochimwayo walapa, si anthu onse mumpingo amene angadziŵe zimenezo. Abale angadabwe, kuima mitu, ngakhalenso kukhumudwa kumene ngati atamva wina akupempherera poyera munthu wochotsedwayo. Chifukwa cha zimenezi, amene akuona kuti afunika kum’pempherera wolakwayo achite zimenezo kwaokha ndi kuisiya nkhaniyo m’manja mwa akulu mumpingo amene ali ndi udindo pankhaniyo.

[Chithunzi patsamba 31]

Yehova anakhululukira machimo aakulu a Manase pamene anadzichepetsa pamaso pake

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Chinthunzichi tachitenga mu Illustrierte Pracht-Bibel/​Heilige Schrift des Alten und Neuen Testaments, nach der deutschen Uebersetzung D. Martin Luther’s