Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“M’kuunika Kwanu Tidzaona Kuunika”

“M’kuunika Kwanu Tidzaona Kuunika”

“M’kuunika Kwanu Tidzaona Kuunika”

NTHAŴI zambiri kuunika timakuona mopepuka ndipo timazindikira kufunika kwake nyali kapena magetsi akazima. N’zosangalatsa kuti “malo opangira magetsi” a kuthambo, omwe ndi dzuŵa, ndi odalirika kwambiri. Timatha kuona, kudya, kupuma, ndi kukhala ndi moyo chifukwa cha kuunika kwa dzuŵa.

Popeza kuunika n’kofunika kwambiri kuti tikhale ndi moyo, tisadabwe kuti pamene tiŵerenga buku la Genesis timapeza kuti Mulungu analenga kuunika pa tsiku loyamba. “Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.” (Genesis 1:3) Amuna oopa Mulungu monga Mfumu Davide anazindikira nthaŵi zonse kuti Yehova ndiye gwero la moyo ndi kuunika. Iye analemba kuti: “Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu: m’kuunika kwanu tidzaona kuunika.”​—Salmo 36:9.

Mawu a Davide akugwira ntchito m’ganizo lenileni ndiponso mophiphiritsa. Buku la Encyclopædia Britannica linati: “Timatha kuona chifukwa cha kuunika.” Ndiyeno linapitiriza kuti: “Ubongo umalandira mauthenga ambiri kudzera m’maso kuposa ziwalo zina zonse zimene zimatumiza mauthenga ku ubongo.” Popeza timatha kuphunzira zambiri chifukwa cha mphatso ya maso​—imene imadalira kuunika kuti munthu athe kuona bwino​—kuunika amakugwiritsanso ntchito m’Malemba mophiphiritsa.

N’chifukwa chake Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Kuunika kophiphiritsa kumene Yesu ananena unali uthenga wa choonadi umene analalikira, umene ukanaunikira maganizo ndi mitima ya omvera ake. Ophunzira a Yesu tsopano akanamvetsetsa cholinga cha Mulungu kwa anthu ndi chiyembekezo cha Ufumu pambuyo poti akhala zaka zambiri mumdima. Kumeneku kunalidi “kuunika kwa moyo,” popeza kudziŵa zimenezo kukanawathandiza kudzakhala ndi moyo wosatha. Yesu ananena m’pemphero kwa Atate ake akumwamba kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Tiyenitu tisakuone mopepuka kuunika kwauzimu kumeneku.