Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kupeŵa Matenda a Mtima Wauzimu

Mungathe Kupeŵa Matenda a Mtima Wauzimu

Mungathe Kupeŵa Matenda a Mtima Wauzimu

Katswiri wamaseŵero wotchuka kwambiri padziko lonse, wa luso lake, yemwe anali kuoneka kuti ali ndi thanzi labwino anagwa mwadzidzidzi pokonzekera maseŵero ndipo anamwalira. Katswiri wamaseŵeroyu anali Sergei Grinkov, yemwe anapata mendulo ya golidi kaŵiri konse pa mpikisano wa Olympic m’maseŵero omatsetsereka pa chipale chofeŵa. Motero ntchito yakeyi inaima atangoyamba kumene kutchuka ndipo n’kuti ali ndi zaka 28 zokha basi. Tsoka lalikulutu limeneli! Kodi n’chiyani chinachititsa? Matenda a mtima. Akuti imfa yake inali yosayembekezeka chifukwa panalibe chizindikiro chilichonse chosonyeza kuti anali ndi matenda a mtima. Komabe, atakamupima anapeza kuti mtima unali wotupa ndipo misempha ya mtimawo inatsekeratu.

NGAKHALE zingaoneke kuti matenda a mtima nthaŵi zambiri saonetsa zizindikiro, madokotala amati zimenezi sizichitika kaŵirikaŵiri. Zoona zake n’zakuti anthu nthaŵi zambiri amanyalanyaza zizindikiro ndi zinthu zina zimene zimayambitsa matendaŵa monga phuma, kunenepa kwambiri, ndi kuŵaŵa pachifuwa. Zotsatira zake n’zakuti ngakhale sangamwalire panthaŵi imene akudwalayo, ambiri amakhala opunduka kwa moyo wawo wonse.

Madokotala ambiri masiku ano akuvomereza zoti nthaŵi zonse munthu afunika kusamala zimene amadya ndi mmene akukhalira pamoyo wake wa tsiku ndi tsiku ndiponso kumakapimitsa kuchipatala nthaŵi zonse kuti apeŵe matenda a mtima. * Kutsatira zimenezi, pamodzinso ndi kukhala wokonzeka kusintha ngati n’kofunika, zingathandize munthu kupeŵa matenda a mtima.

Komabe, pali mbali ina ya mtima wathu imene imafunika kuisamalira kwambiri. Baibulo limatichenjeza kuti: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Inde, lembali likunena za mtima wophiphiritsa. N’kofunika kusamala kuti titchinjirize mtima wathu weniweni. Komatu n’kofunika kusamala kwambiri kuposa pamenepa ngati tikufuna kutchinjiriza mtima wathu wophiphiritsa kuti tipeŵe matenda amene angatiphe mwauzimu.

Mmene Matenda a Mtima Wophiphiritsa Alili

Njira yofunika kwambiri yopeŵera matenda a mtima wauzimu ndiyo kudziŵa zimene zimayambitsa matendawo ndi kuchitapo kanthu monga mmene zimakhalira ndi matenda a mtima weniweni. Motero, tiyeni tipende zinthu zina zazikulu zimene zimayambitsa matenda a mtima weniweni ndi wophiphiritsa.

Chakudya. N’zodziŵikiratu kuti chakudya cha mafuta ambiri koma chosamanga thupi sichithandiza kwenikweni kuti tikhale ndi thanzi labwino ngakhale kuti chimakoma kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi chakudya cha maganizo chosamanga thupi chimene chikupezeka paliponse ndipo chimaoneka ngati n’chosangalatsa koma chimawononga thanzi lauzimu. Pali zambiri zimene akugulitsa mochenjera kudzera m’mawailesi a kanema, mafilimu, mabuku ndi magazini zimene zimaonetsa chisembwere ndi mankhwala osokoneza bongo, chiwawa, ndi kukhulupirira mizimu. Kudyetsa maganizo athu chakudya chimenechi kumapha mtima wathu wophiphiritsa. Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”​—1 Yohane 2:16, 17.

Zakudya zopatsa thanzi monga zipatso ndi ndiwo zamasamba sizingakhale zosangalatsa kwa munthu amene amakonda zakudya zamafuta. N’chimodzimodzinso ndi chakudya chopatsa thanzi mwauzimu. Sichingakhale chosangalatsa kwa munthu amene amakonda kudyetsa maganizo ndi mtima wake zinthu zosangalatsa zimene dzikoli limapanga. Munthu wotero atha kumangodalira “mkaka” wa Mawu a Mulungu basi kwa nthaŵi yaitali. (Ahebri 5:13) M’kupita kwa nthaŵi, iye sapita patsogolo kuti akule mwauzimu ndi kutha kulandira maudindo auzimu ofunika kwambiri mumpingo wachikristu ndi mu utumiki. (Mateyu 24:14; 28:19; Ahebri 10:24, 25) Ena amene achita zimenezo alola mphamvu yawo yauzimu kufooka mpaka kukhala Mboni zosakangalika.

Ngozi ina ndiyakuti maonekedwe amapusitsa. Kuchita ntchito zachikristu mwa apo ndi apo kungabise matenda a mtima wophiphiritsa umene ukufooka mwam’seri chifukwa cha maganizo okondetsa zinthu zakuthupi kapena zosangalatsa zimene zimaonetsa chisembwere, chiwawa, ndi kukhulupirira mizimu. Chakudya chauzimu chosakwanira chimenecho chingaoneke ngati sichikuwononga kwenikweni moyo wathu wauzimu. Komatu chingafooketse mtima wophiphiritsa monga mmene chakudya chosamanga thupi chingatsekere mitsempha ndi kuwononga mtima weniweni. Yesu anachenjeza kuipa kolekerera kuti zokhumba zonyansa ziloŵe mumtima mwathu. Anati: “Yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Inde, chakudya chosapatsa thanzi mwauzimu chingayambitse matenda a mtima wauzimu. Komabe, palinso mfundo zina zofunika kuziganizira.

Maseŵero olimbitsa thupi. Pafupifupi aliyense akudziŵa kuti kumangokhala osachita maseŵero olimbitsa thupi kungayambitse matenda a mtima weniweni. N’chimodzimodzinso ndi kumangokhala osachita zinthu zauzimu, kungabweretse mavuto aakulu. Mwachitsanzo, munthu angamapite nawo muutumiki wachikristu koma mwina angachite zimenezo kwa nthaŵi yochepa chifukwa chofuna kukwaniritsa zolinga zake zakuthupi. Mwina angayese pang’ono chabe kapenanso osayesa n’komwe kuti akhale “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Kapenanso munthu angapite ku misonkhano yachikristu koma osakonzekera kwenikweni kuti atenge nawo mbali pa misonkhanoyo. Mwina angakhale wopanda zolinga zilizonse zauzimu kapena osakonda kwambiri zinthu zauzimu. M’kupita kwa nthaŵi, kusachita zinthu zauzimu kumafooketsa ngakhale kuwonongeratu chikhulupiriro chimene munthu anali nacho. (Yakobo 2:26) Mtumwi Paulo anazindikira za ngozi imeneyi polembera Akristu Achihebri, amene ena mwa iwo ayenera kuti ankangokhala osachita zinthu zauzimu. Taonani mmene anawachenjezera kuti zimenezo zikanawononga moyo wawo wauzimu. “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo; komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene pachedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo.”​—Ahebri 3:12, 13.

Nkhaŵa. Vuto lina limene limayambitsa matenda a mtima weniweni ndilo kuda nkhaŵa kwambiri. Mofananamo, nkhaŵa kapena “zosamalira za moyo,” zingawononge mtima wophiphiritsa mosavuta, mwinanso kumuchititsa munthu kusiyiratu kutumikira Mulungu. Chenjezo la Yesu pankhaniyi ndi la panthaŵi yake. Iye anati: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34, 35) Nkhaŵa ingawonongenso mtima wathu wophiphiritsa ngati tikuvutika maganizo kwa nthaŵi yaitali chifukwa cha tchimo limene tinachita mwamseri. Mfumu Davide anaphunzira kupweteka kwa nkhaŵa yowononga imeneyo zitamuchitikira ndipo analemba kuti: “M’mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa. Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga: ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.”​—Salmo 38:3, 4.

Kudzidalira mopambanitsa. Anthu ambiri amene anadwalapo mtima anali kudzidalira kwambiri kuti thanzi lawo linali bwino asanayambe kudwala. Nthaŵi zambiri, ananyalanyaza kukapimitsa ku chipatala ndipo anaona ngati n’kosafunika n’komwe kuti achite zimenezo. N’chimodzimodzinso ndi ena amene amaganiza kuti popeza akhala Mkristu kwa nthaŵi yaitali, palibe chingawachitikire. Mwina anganyalanyaze kuti adzipime mwauzimu mpaka tsoka litawagwera. N’kofunika kwambiri kukumbukira langizo labwino la Paulo lakuti tipeŵe kudzidalira mopambanitsa. Iye anati: “Iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” N’kwanzeru kuzindikira kupanda kwathu ungwiro ndi kudzipima mwauzimu nthaŵi zonse.​—1 Akorinto 10:12; Miyambo 28:14.

Musanyalanyaze Zizindikiro Zochenjeza

Malemba amafuna kuti tisamale kwambiri mmene mtima wathu wophiphiritsa ulili ndipo amatero pachifukwa chabwino. Pa Yeremiya 17:9, 10 timaŵerenga kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa? Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndim’patse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.” Komabe, kuphatikiza pa kuyesa mtima, Yehova amapereka zinthu mwachikondi zotithandiza kuti tithe kudzipenda.

Amatikumbutsa panthaŵi yake kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Mwachitsanzo, njira ina yaikulu imene mtima wathu wophiphiritsa ungatinyengere ndiyo kutichititsa kuyerekezera m’maganizo zinthu za m’dziko lino. Kumeneku ndiko kuganizira zinthu zosatsimikizika, kulota masana. Zimenezi zingativulaze makamaka ngati zikuyambitsa maganizo oipa. Motero tifunika kupeŵa zimenezi kotheratu. Ngati tidana nacho choipa monga mmene Yesu anachitira, tidzateteza mtima wathu kuti usakhale pa zinthu zongoyerekezera za m’dziko lino.​—Ahebri 1:8, 9.

Ndiponso, tili ndi akulu achikondi mumpingo wachikristu amene angatithandize. Komabe, ngakhale kuti thandizo la ena n’lofunika, munthu aliyense payekha ali ndi udindo wosamala mtima wake wophiphiritsa. Ndi udindo wathu aliyense ‘kutsimikizira zinthu zonse’ ndi ‘kudziyesa tokha, ngati tili m’chikhulupiriro.’​—1 Atesalonika 5:21, NW; 2 Akorinto 13:5.

Tetezani Mtima

Mfundo yachikhalidwe ya m’Baibulo yakuti “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta” imagwiranso ntchito pa thanzi la mtima wathu wophiphiritsa. (Agalatiya 6:7) Nthaŵi zambiri, kugwa mwauzimu kumene kungaoneke ngati n’kwadzidzidzi kungapezeke kuti kwachitika chifukwa chakuti munthuyo anayambira kale kuchita mwam’seri zinthu zimene zimawononga mwauzimu. Zimenezi zingakhale zinthu monga kuonera zinthu zolaula, kukhumbira kwambiri kulemera, kapena kufuna kutchuka kapena kulamulira.

Motero, kuti titeteze mtima n’kofunika kwambiri kusamala chakudya chathu chauzimu. Dyetsani mokwanira maganizo ndi mtima chakudya cha Mawu a Mulungu. Peŵani chakudya chowononga maganizo chimene chikupezeka paliponse chomwe n’chosangalatsa thupi koma chimene chingafooketse mtima wophiphiritsa. Wamasalmo anachenjeza mwa kufanizira molondola ndiponso mogwirizana ndi zamankhwala. Anati: “Mtima wawo unona ngati mafuta.”​—Salmo 119:70.

Ngati pali zolakwa zina zomwe mwakhala nazo kwa nthaŵi yaitali, yesetsani kuzichotsa chifukwa ngati simutero, zitseka mitsempha yanu yophiphiritsa. Ngati dziko likukukopani ndipo likuoneka kuti likupereka zosangalatsa zambiri, sinkhasinkhani malangizo a nzeru amene mtumwi Paulo ananena. Iye analemba kuti: “Ichi nditi, abale, yafupika nthaŵi, kuti tsopano iwo . . . akuchita nalo dziko lapansi, [akhale] monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.” (1 Akorinto 7:29-31) Ndipo ngati kufuna kulemera kukukukopani, mverani zimene Yobu ananena kuti: “Ngati ndayesa golidi chiyembekezo changa, ndi kunena ndi golidi woyengetsa, Ndiwe chikhazikitso changa; ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wake; pakuti ndikadakana Mulungu ali m’mwamba.”​—Yobu 31:24, 28; Salmo 62:10; 1 Timoteo 6:9, 10.

Baibulo posonyeza kuopsa kwa chizoloŵezi chonyalanyaza malangizo a m’Baibulo, limachenjeza kuti: “Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chom’chiritsa.” (Miyambo 29:1) Koma ngati tisamala bwino mtima wathu wophiphiritsa, tingasangalale ndi kukhala ndi mtendere wa m’maganizo umene tingapeze ngati tikhala ndi moyo wosafuna zambiri. Kuyambira kale, Akristu oona amafunika kukhala otero. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zopfunda, zimenezi zitikwanire.”​—1 Timoteo 6:6-8.

Inde, kuphunzira ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu kudzatsimikizira kuti tili ndi mtima wophiphiritsa wamphamvu ndiponso wathanzi. Mwa kusamala kwambiri chakudya chathu chauzimu, sitidzapatsa mpata zochitika ndi maganizo owononga a dziko lapansi lino kuti avulaze kapena kuwononga moyo wathu wauzimu. Koposa zonse, tiyeni tizipima mtima wathu wophiphiritsa nthaŵi zonse mwa kulandira zimene Yehova watikonzera kudzera m’gulu lake. Kuchita zimenezo mwakhama kudzatithandiza kwambiri kuti tipeŵe zotsatira zomvetsa chisoni za matenda a mtima wauzimu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kuti mudziŵe zambiri pa nkhani imeneyi, onani nkhani zotsatizana zimene zayamba ndi mutu wakuti: “Nthenda ya Mtima​—Moyo Uli Pangozi” mu Galamukani! ya December 8, 1996 yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

CHAKUDYA CHAUZIMU CHOSAKWANIRA CHINGAFOOKETSE MTIMA WOPHIPHIRITSA MONGA MMENE CHAKUDYA CHOSAMANGA THUPI CHINGATSEKERE MITSEMPHA NDI KUWONONGA MTIMA WENIWENI

[Mawu Otsindika patsamba 10]

KUMANGOKHALA OSACHITA ZINTHU ZAUZIMU KUNGABWERETSE MAVUTO AAKULU

[Mawu Otsindika patsamba 11]

“ZOSAMALIRA ZA MOYO,” ZINGAWONONGE MTIMA WOPHIPHIRITSA MOSAVUTA

[Chithunzi patsamba 11]

Kunyalanyaza thanzi lathu lauzimu kungabweretse mavuto aakulu

[Zithunzi patsamba 13]

Kukulitsa zizoloŵezi zabwino zauzimu kumateteza mtima wophiphiritsa

[Mawu a Chithunzi patsamba 9]

AP Photo/​David Longstreath