Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mwaimba Nambala Yolakwika”

“Mwaimba Nambala Yolakwika”

Olengeza Ufumu Akusimba

“Mwaimba Nambala Yolakwika”

LESLIE ndi Caroline anali kusinthana kulalikira pa telefoni ku mudzi wa anthu opuma pa ntchito ku Johannesburg, South Africa. Mudziwu unali ndi zinthu zotetezera pakhomo loloŵera. Caroline ndi mnzakeyo anali kupeza anthu ochepa okha m’nyumba zawo ndipo anthuwo analibe chidwi kwenikweni ndi uthenga wawo wachikristu. Motero Caroline analimbikitsidwa pamene mayi wina anayankha.

“Kodi ndikulankhula ndi Mayi B​—?” anafunsa motero Caroline.

“Ayi,” anamveka motero mawu a nsangala, “ndine Mayi G​—. Mwaimba nambala yolakwika.”

Caroline atamva mawu a nsangalawo anati: “Chabwino, komabe ndifotokoze zimene ndimafuna kuwauza Mayi B​—.” Ndiyeno anafotokoza madalitso a Ufumu wa Mulungu umene ukubwera. Atagwirizana zoti akam’patse mayiyo bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, Mayi G​— anafunsa kuti: “Kodi ndinu a chipembedzo chiti?”

“Ndife Mboni za Yehova,” anayankha motero Caroline.

“Mmm, ayi, sindifuna chipembedzo chimenecho! Musabwere.”

Ndiyeno Caroline anati: “Koma Mayi G​—, ndakufotokozerani kwa mphindi 20 zapitazi chiyembekezo chabwino kwambiri, ndipo taona kuchokera m’Baibulo zimene Ufumu wa Mulungu udzachitira anthu posachedwapa. Mwasangalala kumva zimenezi ngakhalenso kuchita chidwi ndiponso kufuna kuti mudziŵe zambiri. Kodi mukudziŵa zotani za Mboni za Yehova? Kodi mutadwala mungapite kwa makaniko? Bwanji ndikuuzeni zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira?”

Anakhala duu ndiyeno anati: “Mukunenadi zoona. Bwerani. Koma mudziŵiretu kuti sizitheka kuti mundikope kupita ku chipembedzo chanu!”

Caroline anati: “Mayi G​—, sindingathe kukukopani ngakhale ndikanafuna kutero. Yehova yekha ndi amene angathe kutero.”

Zonse zinayenda bwino pa ulendo wokam’patsa bulosha lija ndipo Mayi G​— (Betty) anavomera kuti Caroline adzabwerenso. Iye atabweranso, Betty ananena kuti anauza azimayi amene ankadya nawo limodzi kuti adzakambirana ndi Mboni za Yehova. Azimayiwo atamva izi anaipidwa nati: “N’chifukwa chiyani ukufuna kukambirana ndi Mboni za Yehova? Anthu amene aja sakhulupirira Yesu!”

Nthaŵi yomweyo Caroline anakumbutsa Betty mfundo zazikulu za Ufumu wa Mulungu zimene anakambirana poyamba paja.

Caroline anafunsa kuti: “Ndani amene adzakhala Mfumu?”

“Si winanso, koma Yesu,” anayankha motero Betty.

“Inde,” anatero Caroline. Ndiyeno anapitiriza kufotokoza kuti Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Yesu ndi mwana wa Mulungu, koma sakufanana ndi Mulungu monga mbali ya Utatu.​—Marko 13:32; Luka 22:42; Yohane 14:28.

Atamuchezera maulendo angapo, anapeza kuti ngakhale Betty anali ndi maganizo abwino a m’tsogolo ndiponso wansangala, anali kudwala. Anali ndi matenda a kansa ndipo ankaopa kufa. Iye anaulula kuti: “Ndikanakonda ndikanadziŵa zimenezi zaka za m’mbuyomo ndi kukhala ndi chikhulupiriro ngati chanu.” Caroline anam’limbikitsa mwa kumusonyeza malemba amene amafotokoza kuti imfa ndiyo tulo tatikulu ndipo anthu adzauka. (Yohane 11:11, 25) Zimenezi zinamulimbikitsa kwambiri Betty amene pakalipano akuphunzira Baibulo mokhazikika. Bwenzi pano akupezeka pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu akanakhala kuti sakudwala.

Caroline akuti: “Ndaona kuti angelo akutsogolera ntchito imeneyi. Betty anali ‘nambala yolakwika,’ ndiponso ali ndi zaka 89!”​—Chivumbulutso 14:6.