Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi

Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi

Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi

SUKULU ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo anaikhazikitsa kuti iziphunzitsa amuna ndi akazi odzipatulira kuti akachite umishonale ku mayiko ena. Kodi ndani amayenerera kupita ku Sukulu ya Gileadi? Anthu ofunitsitsa ndi mtima wonse ndiwo oyenerera kupita kumeneko. (Salmo 110:3) Kufunitsitsa kumeneku kunaonekadi pa September 8, 2001, pamene ophunzira a m’kalasi la 111 anali kumaliza maphunziro awo.

Ophunzira ena a m’kalasilo anali atadzipereka kale kusiya mabanja awo, mabwenzi awo ndi dziko lawo kukatumikira kumadera kumene kukufunika atumiki ambiri. Mwakuchita zimenezo, anadziyesa n’kuona ngati angathe kusintha kuti athe kukhala kumalo achilendo. Mwachitsanzo, Richer ndi Nathalie anakonza zoti asamuke kupita ku Bolivia, Todd ndi Michelle anakonza zopita ku Dominican Republic, ndipo David ndi Monique anafuna kupita ku dziko lina la ku Asia kuti akafalitse uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ophunzira ena anali atatumikira kale ku Nicaragua, Ecuador ndi Albania.

Christy analimbikitsidwa kuphunzira chinenero cha Chispanya pamene anali ku sekondale ndipo zimenezi zinamuthandiza kukonzekera kukatumikira ku Ecuador kwa zaka ziŵiri asanakwatiwe. Ophunzira ena anali kusonkhana m’mipingo imene ankalankhula chinenero chomwe si chawo m’dziko lawo. Saul ndi Priscilla omwe sanali kudziŵa bwino Chingelezi, anasonyeza kufunitsitsa ndi mtima wonse mwa kuyesetsa zolimba kuti azitha kuchilankhula bwino asanapite ku sukuluyo.

Milungu 20 imene anakhala akuphunzira za umishonale, siinachedwe kutha. Tsiku lomaliza maphunziro linakwana ndipo ophunzira anali pamodzi ndi mabwenzi ndi mabanja awo pamene anali kumvetsera malangizo a nzeru ndi mawu otsanzikana olimbikitsa.

Tcheyamani wa pulogalamuyo anali Theodore Jaracz amene anamaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi m’kalasi yachisanu ndi chiŵiri ndipo pakalipano ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Mawu ake oyamba anatsindika mfundo yakuti monga gulu, sitinasiye cholinga chophunzitsa ophunzira ku Gileadi chomwe ndicho kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse. (Marko 13:10) Sukulu ya Gileadi imakonzekeretsa ophunzira oyenerera kuti akagwire ntchito yolalikira imeneyi pamlingo wokulirapo kusiyana ndi mmene ankachitira asanachite maphunziroŵa ndiponso kumayiko kumene amishonale ophunzitsidwa akufunika kwambiri. Mbale Jaracz analangiza ophunzirawo kuti agwiritse bwino ntchito zimene aphunzira m’Sukulu ya Gileadi pamene akukagwira ntchito pamodzi ndi amishonale amene panopa akutumikira m’mayiko 19 kumene amishonaleŵa akupita.

Malangizo a Panthaŵi Yake kwa Omaliza Maphunziro

Atatero, nkhani zotsatizana zinayamba. William Van De Wall, yemwe ali m’ Komiti ya Nthambi ya United States anakamba nkhani yakuti “Changu cha Umishonale Ndicho Chizindikiro cha Akristu Oona.” Anatsindika kwambiri pa ntchito ‘yophunzitsa anthu,’ imene ili pa Mateyu 28:19, 20, ndipo anawauza ophunzirawo kuti: “Tsanzirani Yesu amene anachita ntchito yake ya umishonale mwachangu ndiponso mokhudzidwa mtima.” Mbale Van De Wall powathandiza amishonale a m’tsogolowo kuti akhalebe ndi changu pa ntchito yawo, anawalimbikitsa kuti: “Tsatirani ndandanda yabwino; khalani ndi chizoloŵezi chabwino cha phunziro laumwini, mukumatsatira mfundo zaumulungu zatsopano; ndiponso nthaŵi zonse kumbukirani chifukwa chomwe mukukagwirira ntchito imeneyi.”

Kenako, Guy Pierce, wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yake ya mutu wakuti, “Pitirizani Kukulitsa ‘Mphamvu Yanu ya Kulingalira.’” (Aroma 12:1, NW) Anapereka malangizo othandiza kwa omaliza maphunzirowo, kuwalimbikitsa kugwiritsa ntchito luso la kulingalira limene Mulungu anawapatsa. Anati: “Pitirizani kusinkhasinkha zimene Yehova akukuuzani kudzera m’Mawu ake. Zimenezi zidzakutetezani.” (Miyambo 2:11) Mbale Pierce analangizanso omaliza maphunzirowo kuti asamangoumirira mtunda wopanda madzi kuti asabwezere m’mbuyo ‘mphamvu yawo ya kulingalira.’ Mosakayika, mfundo zowakumbutsa za panthaŵi yake zimenezi zidzawathandiza amene anamaliza maphunzirowo pamene akukachita umishonale.

Kenako tcheyamani anaitana mmodzi mwa alangizi a Sukulu ya Gileadi, Lawrence Bowen amene anakamba nkhani yakuti “Tsimikizani Mtima Kuti Musadziŵe Kanthu.” Iye ananena kuti mtumwi Paulo pogwira ntchito yake ya umishonale ku Korinto, ‘anatsimikiza mtima kuti asadziŵe kanthu koma Yesu Kristu, ndi iye wopachikidwa.’ (1 Akorinto 2:2) Paulo ankadziŵa kuti mphamvu yoposa ina iliyonse m’chilengedwe chonse, yomwe ndi mzimu woyera, imalimbikitsa uthenga umene uli m’Baibulo lonse womwe ndiwo: kutsimikiza kudzera m’Mbewu yolonjezedwa kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. (Genesis 3:15) Anthu okwana 48 amene anamaliza maphunzirowo anawalimbikitsa kuti akhale ngati Paulo ndi Timoteo kuti ziwayendere bwino pa ntchito yawo ya umishonale, kugwiritsitsa “chitsanzo cha mawu a moyo.”​—2 Timoteo 1:13.

Nkhani yomaliza pa nkhani zotsatizana zotsegulira pulogalamuyi inali yakuti “Yamikirani Mwayi Wanu Wapaderawu Womwe Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu.” Wallace Liverance, wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi, ndi amene anakamba nkhaniyi ndipo anathandiza omaliza maphunzirowo kuzindikira kuti kulandira mwayi wa utumiki wapadera umenewo kukusonyeza kukoma mtima kwa Mulungu, osati chifukwa chakuti iwo anali oyenerera kuulandira kapena kuti aulandira chifukwa chakuti anagwira ntchito yoyenera kulandira utumikiwu. Mbale Liverance, pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mtumwi Paulo, anati: “Yehova sanasankhe Paulo kukhala mtumwi wa amitundu chifukwa cha ntchito zake, kuti zioneke ngati kuti Paulo anali woyenerera kulandira ntchito imeneyo. Sanamusankhe chifukwa chakuti anali atatumikira kwa nthaŵi yaitali kapena chifukwa chakuti anali kudziŵa zambiri. N’kutheka kuti mwina anthu ankaona kuti Barnaba ndiye anali woyenerera kum’patsa ntchito imeneyo. Kapena akanakhala kuti anapereka ntchitoyo malinga ndi luso la munthu, ndiye kuti akanam’patsa Apolo chifukwa iye ankadziŵa kulankhula bwino kuposa Paulo. Kum’patsa ntchitoyo kunasonyeza kukoma mtima kwa Mulungu.” (Aefeso 3:7, 8) Mbale Liverance analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti agwiritse ntchito mphatso yawo, kapena mwayi wawo wautumiki, kuthandiza anthu ena kuti akhale mabwenzi a Mulungu ndi kuti adzalandire ‘mphatso ya Mulungu yomwe ndi moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.’​—Aroma 6:23.

Itatha nkhani imeneyi, Mark Noumair, mlangizi wina wa Sukulu ya Gileadi, anakambirana mosangalatsa ndi ophunzira nkhani yakuti “Kukonzekera Kumabweretsa Zabwino.” (Miyambo 21:5) Zimene ophunzirawo anakumana nazo zinasonyeza kuti mtumiki akakonzekera bwino ntchito yake, makamaka mwa kukonzekeretsa mtima wake, adzakhaladi ndi chidwi chenicheni mwa anthu. Sadzasoŵa chonena. M’malo mwake, adzalankhula ndi kuchita zinthu zoti ziwathandize anthuwo mwauzimu. “Chimenechi ndi chinsinsi chakuti mmishonale zimuyendere bwino,” anatero Mbale Noumair, akumatsimikizira zimenezi poona zimene iye anakumana nazo akuchita umishonale ku Africa.

Utumiki wa Umishonale Ndi Ntchito Yokhutiritsa

Ralph Walls ndi Charles Woody anafunsa amishonale ena amene anali atagwira ntchitoyi kwa nthaŵi yaitali omwe analinso ku Patterson kukachita maphunziro apadera a mamembala a Komiti za Nthambi. Atawafunsa, mayankho awo anatsindika kuti kukonda anthu n’kumene kumabweretsa chimwemwe mu utumiki wa umishonale. Zinali zolimbikitsa kwa ophunzirawo pamodzi ndi mabanja ndi mabwenzi awo kumvetsera amishonale amene anagwira kale ntchitoyi, akufotokoza chifukwa chimene utumiki waumishonale ulili wokhutiritsa.

John E. Barr, yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yaikulu ya tsikuli. Nkhaniyi inali ndi mutu wakuti “Imbirani Yehova Nyimbo Yatsopano.” (Yesaya 42:10) Mbale Barr ananena kuti mawu akuti “nyimbo yatsopano” amapezeka kasanu ndi kanayi m’Baibulo. Anafunsa kuti, “Kodi nyimbo imeneyi n’chiyani?” Ndiyeno anayankha kuti: “Nkhani yonse ikuvumbula kuti nyimbo yatsopano ikuimbidwa chifukwa cha zinthu zatsopano zimene zikuchitika posonyeza ulamuliro wa Yehova.” Iye analimbikitsa ophunzirawo kuti apitirize kuimba nawo nyimbo yotamanda Ufumu wopambana wa Mulungu womwe uli m’manja mwa Mfumu Yaumesiya, Kristu Yesu. Mbale Barr ananena kuti zimene aphunzira ku Sukulu ya Gileadi zawathandiza kudziŵa mozama mbali zosiyanasiyana za “nyimbo yatsopano” imeneyi kuposa ndi mmene ankadziŵira kale. “Sukuluyi yatsindika kufunika koti ‘muziyimba’ zitamando za Yehova mogwirizana ndi abale ndi alongo anu a kumene mukupita. Nthaŵi zonse gwirizanani ndi anthu ena pamene mukugwira ntchito yanu.”

Ophunzirawo atalandira madipuloma awo, woimira ophunzirawo anaŵerenga kalata yoyamikira ndi mtima wonse chifukwa cha zimene anaphunzira ku Sukulu ya Gileadi.

Kodi mungafutukule utumiki wanu kwa Mulungu ndi kuuchititsa kukhala wopindulitsa kwambiri? Ngati ndi choncho, dziperekeni monga mmene omaliza maphunziroŵa achitira. Zimenezi n’zimene zawathandiza kuyenerera kukachita umishonale. Munthu angapeze chimwemwe chochuluka ngati akufunitsitsa kudzipereka mosangalala ndi mtima wonse kuti atumikire Mulungu.​—Yesaya 6:8.

[Bokosi patsamba 25]

ZIWERENGERO ZA KALASI

Chiŵerengero cha mayiko kumene achokera: 10

Chiŵerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 19

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Avareji ya zaka zakubadwa: 33.2

Avareji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 16:8

Avareji ya zaka zimene akhala akuchita utumiki wa nthaŵi zonse: 12.6

[Chithunzi patsamba 26]

Kalasi la 111 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

M’ndandanda umene uli pansipa, mizera taiiŵerenga kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kumka kumanja mumzera uliwonse.

(1) Yeomans, C.; Toukkari, A.; Nuñez, S.; Phillips, J.; Dawkin, M.; Silvestri, P. (2) Morin, N.; Biney, J.; López, M.; Van Hout, M.; Cantú, A.; Szilvassy, F. (3) Williams, M.; Itoh, M.; Van Coillie, S.; Levering, D.; Fuzel,  F.; Geissler, S. (4) Yeomans, J.; Moss, M.; Hodgins, M.; Dudding, S.; Briseño, J.; Phillips, M. (5) López, J.; Itoh, T.; Sommerud, S.; Kozza, C.; Fuzel, G.; Moss, D. (6) Williams, D.; Dudding, R.; Geissler, M.; Morin, R.; Biney, S.; Cantú, L. (7) Dawkin, M.; Hodgins, T.; Levering, M.; Silvestri, S.; Van Hout, D.; Briseño, A. (8) Van Coillie, M.; Nuñez, A.; Kozza, B.; Sommerud, J.; Toukkari, S.; Szilvassy, P.