Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi mkazi wachikristu angakhulupirike bwanji kwa Mulungu komanso kugonjera mwamuna wake wosakhulupirira ngati mwamunayo amatenga nawo mbali m’zochitika za maholide a chipembedzo?

Pakufunika nzeru ndi luso kuti achite zimenezi. Koma akuchita bwino kuyesetsa kusamala maudindo aŵiriwo. Yesu anapereka malangizo pa nkhani yofanana ndi imeneyi. Anati: “Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) N’zoona kuti ankafotokoza zoyenera kuchitira maboma, amene kenako Akristu anauzidwa kuti afunika kuwagonjera. (Aroma 13:1) Komabe, malangizo ake angagwirenso ntchito kwa mkazi pamene akusamala udindo wake kwa Mulungu ndi udindo wake wa m’Malemba wogonjera mwamuna wake, ngakhale mwamunayo ndi wosakhulupirira.

Aliyense amene amadziŵa Baibulo angavomereze kuti limatsindika zoti Mkristu afunika kumvera choyamba Mulungu Wamphamvuyonse, kukhulupirika kwa iye nthaŵi zonse. (Machitidwe 5:29) Komabe, nthaŵi zambiri wolambira woona angalolere zimene munthu yemwe ali ndi udindo pa iye wamupempha kapena kumulamula kuchita koma osaswa malamulo apamwamba a Mulungu.

Ahebri atatu amene nkhani yawo ili pa Danieli chaputala 3 ndi chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Wolamulira wawo wa boma, Nebukadinezara, analamula kuti iwo pamodzi ndi anthu ena akapezeke ku chigwa cha Dura. Mwachionekere, Ahebri atatuŵa akanakonda kungokhala osapitako pozindikira kuti kukakhala kulambira konyenga. Danieli mwinamwake anatha kupereka zifukwa zomveka zoti sakapezekako, koma atatuwo sakanatha kutero. * Motero anamvera mpaka anakapezekako. Koma sakanachita nawo cholakwika chilichonse ndipo sanachitedi.​—Danieli 3:1-18.

N’chimodzimodzinso pa nthaŵi ya holide, mwamuna wosakhulupirira angapemphe kapena kulamula mkazi wake kuti achite chinachake chimene mkaziyo sangafune kuchita. Mwachitsanzo, angamuuze mkazi wakeyo kuti am’phikire chakudya chinachake patsiku limene iye ndi ena adzakondwerera holideyo. Kapena angalamule kuti banja lonse (kuphatikizapo mkazi wake) apite kwa abale ake kukadya chakudya kapena kukangocheza chabe. Kapenanso tsiku la holide litayandikira, angauze mkazi wake kuti pokagula zinthu, akamugulire zinthu zina monga zakudya za pa holideyo, zinthu zoti adzapereke mphatso, kapena mapepala okutira mphatsozo pamodzi ndi makadi a mafuno abwino oti adzaperekere limodzi ndi mphatso zakezo.

Apanso, mkazi wachikristu afunika kutsimikiza mtima kusachita nawo zinthu za chipembedzo chonyenga. Koma bwanji ngati wamupempha kuti achite zimenezo? Mwamunayo ndiye mutu wa banja, ndipo Mawu a Mulungu amati: “Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.” (Akolose 3:18) Kodi mkazi angasonyeze kugonjera kwa mwamuna wake komabe akukhulupirika kwa Mulungu pankhani ngati zimenezi? Afunika kuona mmene angachitire kuti amvere mwamuna wake kwinaku akumvera Yehova yemwe ayenera kukhala patsogolo.

Nthaŵi zina osati za holide, mwamuna wake angamuuze kuti aphike chakudya chinachake, mwina chifukwa chakuti amachikonda kwambiri kapena amakonda kudya chakudya chimenecho pa nyengo inayake. Mkaziyo angafune kusonyeza chikondi ndi kuzindikira kuti mwamunayo ndi mutu wa banja. Kodi angachitenso zimenezo ngati mwamunayo wamuuza kuchita zimenezo pa nthaŵi ya holide? Akazi ena achikristu angachite zimenezo ndi chikumbumtima chabwino, akumaona monga ntchito ya nthaŵi zonse yokonza chakudya cha tsiku ndi tsiku. Inde, palibe Mkristu wokhulupirika amene angagwirizanitse zimenezo ndi holideyo, ngakhale mwamuna wakeyo akutero. N’chimodzimodzinso ngati mwamunayo angafune kuti azipita ndi mkazi wakeyo kwa abale a mwamunayo nthaŵi zosiyanasiyana mwezi uliwonse kapena chaka chilichonse. Kodi angachitenso zimenezo ngati lili tsiku la holide? Kapena kodi mkaziyo pokagula zinthu, angakamugulire mwamunayo zinthu zimene wam’tuma mosaganizira zimene mwamunayo akufuna kuchita nazo zinthuzo?

Ndithudi, mkazi wachikristu ayenera kuganizira anthu ena ndi mmene zochita zake zingawakhudzire. (Afilipi 2:4) Afunika kupeŵa kuchititsa ena kuganiza kuti akugwirizana ndi holideyo, monga mmene Ahebri atatu aja ayenera kuti sanafune kuti anthu ena awaone popita ku chigwa cha Dura. Motero angayese kukambirana mwaluso ndi mwamuna wakeyo kuti aone ngati mwamunayo pofuna kulemekeza malingaliro a mkaziyo, angamachite yekha zinthu zina zokhudzana ndi holide kuti akomere mtima mkazi amene amam’konda ndi kumulemekeza. Mwina mwamunayo angaone kuti n’kwanzeru kupeŵa kuti onse asakhumudwe ngati mkaziyo akanakana kuchita nawo zinthu zokhudza chipembedzo chonyenga. Inde, kukambirana mofatsa vuto lisanabuke kungathandize kupeza njira yothetsera nkhaniyo mwamtendere.​—Miyambo 22:3.

Pomaliza, Mkristu wokhulupirika afunika kupenda mfundo zonse kenako n’kusankha zoti achite. Kumvera Mulungu kufunika kukhala patsogolo monga mmene anachitira Ahebri atatu aja. (1 Akorinto 10:31) Komabe akuganiza zimenezo, Mkristu aliyense payekha afunika kuona zinthu zimene sangalolere kuzichita ngati yemwe ali ndi ulamuliro m’banja kapena kulikonse kumene ali, amuuza kuti achite.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2001.