Makolo Kwaniritsani Zomwe Ana Anu Amafunikira!
Makolo Kwaniritsani Zomwe Ana Anu Amafunikira!
ANA amafunika kuwatsogolera ndiponso kuwalanga mwachikondi. Makolo ndiwo kwenikweni ali ndi udindo umenewu. Pankhani imeneyi, mphunzitsi wina wa ku Brazil, Tania Zagury, ananena kuti: “Mwana aliyense ali ndi chizoloŵezi chofuna zosangalatsa. Kuwaikira malire n’kofunika kwambiri. Makolo ndiwo ayenera kuchita zimenezi. Ngati sangachite zimenezi ndiye kuti ana adzakhala opulupudza.”
Komabe, m’mayiko ambiri malangizo ameneŵa ndi ovuta kuwatsatira chifukwa chakuti anthu kumeneko amaona kuti ufulu wa aliyense ndi wofunika kwambiri. Ndiyeno, kodi makolo angapeze kuti thandizo? Makolo oopa Mulungu amazindikira kuti ana ndi “cholandira cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Chotero, amagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, Baibulo, kuti liwatsogolere polera ana. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 13:24 limati: “Wolekerera mwana wake osam’menya amuda; koma wom’konda am’yambize kum’langa.”
Baibulo limagwiritsa ntchito liwu lakuti ‘kumenya’ koma zimenezi sizikutanthauza kumenya kwenikweni kokha. Liwu limeneli limatanthauza kuwongolera pogwiritsa ntchito njira ina iliyonse. Inde, nthaŵi zambiri mawu okha amakhala okwanira kuwongolera mwana wopulupudza. Lemba la Miyambo 29:17 limati: “Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako.”
Ana amafunikira kuwalanga mwachikondi kuti asiye makhalidwe osakondweretsa. Makolo amasonyeza kuti amasamalira ana awo ngati akuwawongolera mokoma mtima. (Miyambo 22:6) Choncho makolonu, musagwe mphwayi! Mukatsatira uphungu wabwino ndi wothandizadi wa m’Baibulo, mudzasangalatsa Yehova Mulungu ndipo ana anu adzakulemekezani.