Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mankhwala Omwe Angathandize Kuthetsa Nkhaŵa

Mankhwala Omwe Angathandize Kuthetsa Nkhaŵa

Mankhwala Omwe Angathandize Kuthetsa Nkhaŵa

“Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.”​—MATEYU 11:28.

1, 2. (a) Kodi Baibulo lili ndi chiyani chimene chimathandiza kuchepetsa nkhaŵa zopitirira muyeso? (b) Kodi zimene Yesu anaphunzitsa zinali zogwira mtima motani?

MWINA mungavomereze kuti kuda nkhaŵa kwambiri kumavulaza ndipo kumayambitsa kuvutika maganizo. Baibulo linanena kuti anthu onse ndi othodwa ndi mavuto motero kuti ambiri akufunitsitsa atamasuka ku nkhaŵa za moyo wa masiku ano. (Aroma 8:20-22) Koma Malemba ananenanso mmene tingapezere mpumulo wa nkhaŵa zina pakalipano. Mpumulo umenewo tingaupeze potsatira malangizo ndi chitsanzo cha munthu amene anakhala ndi moyo zaka zikwi ziŵiri zapitazo. Iye anali kalipentala, komabe ankakonda kwambiri anthu kuposa ntchito yakeyo. Anakhudza kwambiri mitima ya anthu, anawathandiza mavuto awo, anathandiza ofooka ndiponso anasangalatsa ovutika maganizo. Ndipo kuposa zonsezi, iye anathandiza anthu ambiri kuzindikira zinthu zauzimu. Motero, anthu anapezadi mpumulo wa nkhaŵa zawo zopitirira muyeso, monga mmenenso inu mungapezere.​—Luka 4:16-21; 19:47, 48; Yohane 7:46.

2 Munthu ameneyu, yemwe ndi Yesu wa ku Nazarete, sanachite zimenezi chifukwa cha maphunziro apamwamba amene ena anali kuphunzira ku mizinda yakale ya Roma, Atene ndi Alesandriya. Komabe, zimene anaphunzitsa n’zotchuka kwambiri. Zinali ndi mfundo yaikulu imodzi: boma limene Mulungu adzagwiritsa ntchito kulamulira bwinobwino dziko lathu lapansili. Yesu anafotokozanso mfundo zachikhalidwe zofunika kwambiri pamoyo wathu zomwe n’zothandiza kwambiri lerolino. Amene amaphunzira ndi kugwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa amapindula kwambiri kuphatikizapo kupumula ku nkhaŵa zawo zopitirira muyeso. Kodi simungakonde zimenezo?

3. Kodi ndi pempho lalikulu liti limene Yesu anapereka?

3 Mwina mungakayike kuti ‘kodi munthu amene anakhala ndi moyo kalekale angakhudze moyo wanga lerolino?’ Tamvani mawu a Yesu okhudza mtima akuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Kodi anali kutanthauza chiyani? Tiyeni tipende mawu ameneŵa mwatsatanetsatane ndi kuona mmene angakuthandizireni kuti mupeze mpumulo wa nkhaŵa zanu.

4. Kodi Yesu analankhula kwa ndani, ndipo n’chifukwa chiyani omvera akewo mwina anaona kuti n’kovuta kuchita zimene anawapempha?

4 Yesu analankhula ndi anthu ambiri amene ankayesetsa ndi mtima wonse kuchita zimene malamulo ankafuna koma omwe ‘anathodwa’ chifukwa atsogoleri a Chiyuda anachititsa chipembedzo kukhala chinthu cholemetsa. (Mateyu 23:4) Anaika malamulo ankhaninkhani pafupifupi pa mbali iliyonse ya moyo. Kodi simukanatha kuona kuti n’zolemetsa kumamva nthaŵi zonse akuti “musachite” izi kapena izo? Mosiyana ndi atsogoleri a chipembedzoŵo, pempho la Yesu linali lothandiza anthu kuti apeze choonadi, chilungamo ndi moyo wabwinopo mwa kumumvetsera. Inde, njira yodziŵira Mulungu woona inaphatikizapo kumvera Yesu Kristu chifukwa anthu akanatha ndipo ngakhale lerolino angathe kudziŵa mmene Yehova alili kudzera mwa Yesu. Iye anati: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.”​—Yohane 14:9.

Kodi Muli ndi Nkhaŵa Yomkitsa?

5, 6. Kodi kagwiridwe kantchito ndi malipiro a m’nthaŵi ya Yesu zikufanana bwanji ndi zathu masiku ano?

5 Nkhani imeneyi ingakukhudzeni kwambiri chifukwa mwina mmene ntchito yanu kapena banja lanu lilili zingakudetseni nkhaŵa kwabasi. Kapenanso mwina maudindo ena angaoneke kukhala olemetsa kwambiri. Ngati ndi choncho, ndiye kuti mukufanana ndi anthu oona mtima amene Yesu ankakumana nawo ndi kuwathandiza. Mwachitsanzo, taganizani vuto lopeza zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Anthu ambiri masiku ano ali ndi vuto limeneli ndipo ndi mmenenso zinalili ndi anthu ambiri amene analipo m’nthaŵi ya Yesu.

6 Nthaŵi imeneyo, munthu ankagwira ntchito zolimba kwa maola 12 tsiku lililonse ndipo amatero masiku 6 pa mlungu. Nthaŵi zambiri, akagwira ntchito tsiku lonse lathunthu, ankangolandira lupiya la theka basi. (Mateyu 20:2-10) Kodi zimenezi zikufanana bwanji ndi malipiro anu kapena a anzanu? N’kovuta kuyerekezera malipiro akale ndi a masiku ano. Njira imodzi yoyerekezera ndiyo kuona mitengo ya zinthu. Katswiri wina anati m’nthaŵi ya Yesu mtengo wa buledi mmodzi yemwe anali kum’panga pogwiritsa ntchito makapu anayi a ufa watirigu unali kufanana ndi malipiro a ola limodzi. Katswiri winanso anati mtengo wa vinyo wabwino wodzala kapu imodzi unali kufanana ndi malipiro a maola aŵiri. Mutha kuona pa mfundo zimenezi kuti anthu m’nthaŵi imeneyo ankagwira ntchito zolimba kwa nthaŵi yaitali kuti apeze zofunika pa moyo. Ankafunadi kumasuka ku mavuto ameneŵa ndi kupeza mpumulo monganso mmene ife timafunira. Ngati muli pa ntchito, mungaone kuti mukukakamizika kuti mukhale wantchito wopindulitsa kwambiri. Kaŵirikaŵiri sitipeza nthaŵi yokwanira kuti tisankhe kuchita chinthu titaganiza mozama. Mungavomereze kuti mumalakalaka mpumulo.

7. Kodi anthu anachita chiyani atamva uthenga wa Yesu?

7 Inde, zimene Yesu anapempha kwa onse “akulema ndi akuthodwa” ziyenera kuti zinakhudza mtima anthu ambiri amene anali kumumvetsera kalelo. (Mateyu 4:25; Marko 3:7, 8) Ndiponso kumbukirani kuti Yesu anaphatikizapo lonjezo lakuti, “ndidzakupumulitsani inu.” Lonjezo limeneli likugwiranso ntchito lerolino. Lingatithandizenso ife ngati tili “akulema ndi akuthodwa.” Ndipo lingagwirenso ntchito kwa anthu amene timawakonda amene alinso ndi mavuto ngati omweŵa.

8. Kodi kulera ana, ndi ukalamba zimawonjezera bwanji nkhaŵa?

8 Pali zinthu zinanso zimene zikulemetsa anthu. Kulera ana ndi vuto lalikulu. Ngakhalenso anawo ali ndi mavuto awo. Anthu owonjezerekawonjezereka, kaya ana kapena akulu, akuvutika ndi matenda a maganizo ndi akuthupi. Ndipo ngakhale kuti anthu angakhale ndi moyo kwa nthaŵi yaitali, anthu okalamba ali ndi mavuto apadera amene amalimbana nawo ngakhale kuti sayansi ya zamankhwala yapita patsogolo kwambiri.​—Mlaliki 12:1.

Kugwira Ntchito Mutasenza Goli

9, 10. Kodi kale goli linali chizindikiro cha chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani Yesu anapempha anthu kuti asenze goli lake?

9 Kodi munaona kuti pa Mateyu 11:28, 29 paja Yesu anati: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine”? Kalelo, munthu wamba mwina amamva ngati ankagwira ntchito atasenza goli. Kuyambira kale, goli linali chizindikiro cha ukapolo. (Genesis 27:40; Levitiko 26:13; Deuteronomo 28:48) Anthu ambiri amene anali kugwira ntchito masana amene Yesu ankakumana nawo, anali kugwira ntchito atasenzadi goli pamapeŵa awo, kunyamula katundu wolemera. Goli linkakhala labwino losavulaza pakhosi ndi paphewa kapena linkasupula malinga ndi mmene analikonzera. Popeza Yesu anali kalipentala, ayenera kuti ankapanga magoli, ndipo ankadziŵa mmene angapangire goli “lofewa.” Mwina anali kulikuta ndi chikopa kapena nsalu pamalo amene linkakhudza khosi ndi phewa kuti likhale lofeŵa.

10 Pamene Yesu ananena kuti, “Senzani goli langa,” ayenera kuti anali kudzifanizira ndi munthu amene ankapanga magoli abwino amene anali ‘ofeŵa’ pakhosi ndi pamapewa a munthu wogwira ntchito. Motero, Yesu anawonjezera kuti: “Katundu wanga ali wopepuka.” Zimenezi zikusonyeza kuti golilo linali labwino kuligwiritsa ntchito ndipo ntchito yake sinali ya ukapolo. N’zoona kuti Yesu popempha anthu amene anali kumumvera kuti asenze goli lake sanali kupereka mpumulo wa msangamsanga wa mavuto onse amene analipo nthaŵi imeneyo. Komabe, mfundo zatsopano zimene iye anawauza zikanawapumulitsa ku mavuto ena. Kusintha mmene anali kukhalira pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndi mmene anali kuchitira zinthu zikanawapumulitsanso. Chofunika kwambiri chinali chakuti chiyembekezo choŵala ndi cholimba chikanawathandiza kusakhala ndi nkhaŵa zambiri pamoyo wawo.

Inunso Mutha Kupeza Mpumulo

11. N’chifukwa chiyani Yesu sanali kutanthauza kungosinthanitsa magoli chabe?

11 Onani kuti Yesu sanali kunena kuti anthu asinthanitse magoli. Ufumu wa Roma ukanapitirizabe kulamulira m’dzikolo monga mmene maboma lerolino akulamulirabe m’mayiko mmene Akristu amakhala. Anthu akanapitirizabe kukhoma msonkho wachiroma wa m’zaka za zana loyamba. Matenda ndi mavuto a zachuma akanakhalapobe. Anthu akanavutikabe ndi kupanda ungwiro ndi uchimo. Komabe, akanapeza mpumulo ngati akanatsatira zimene Yesu anali kuphunzitsa monga mmenenso ifeyo tingaupezere lerolino.

12, 13. Kodi Yesu anatsindika kuti n’chiyani chimene chingabweretse mpumulo, ndipo ena anachita motani atamva zimenezo?

12 Tanthauzo lalikulu la fanizo la Yesu la goli linaonekera bwino pa nkhani yopanga ophunzira. Mosakayika, ntchito yaikulu ya Yesu inali yophunzitsa anthu ndipo anatsindika kwambiri pa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:23) Motero, pamene ananena kuti, “ Senzani goli langa,” zimenezo mosakayika zikanaphatikizapo kumutsanzira kuchita ntchito yomweyo. Nkhani ya m’Mauthenga Abwino imasonyeza kuti Yesu analimbikitsa anthu oona mtima kusiya ntchito yawo, yomwe ndi nkhani yaikulu m’miyoyo ya anthu ambiri. Kumbukirani mmene anaitanira Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane. Iye anati: “Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.” (Marko 1:16-20) Yesu anawasonyeza asodzi amenewo mmene akanakhalira okhutira ngati akanachita ntchito imene iye anali kuiika patsogolo m’moyo wake, kwinaku akuwatsogolera ndi kuwathandiza pochita zimenezo.

13 Ena mwa Ayuda amene anali kumva, anamvetsa zimene anali kuphunzitsa ndipo anazigwiritsa ntchito. Tayesani kuona m’maganizo mwanu zimene zinachitika m’mphepete mwa nyanja pamene tikuŵerenga pa Luka 5:1-11. Asodzi anayi anali atagwira ntchito zolimba usiku wonse koma osapeza kanthu. Ndiyeno mwadzidzidzi makoka awo anadzaza nsomba. Zimenezi sizinangochitika mwamwayi. Yesu ndi amene anachititsa. Pamene anayang’ana ku gombe, anaona khwimbi la anthu amene anachita chidwi kwambiri ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa. Zimenezi zinathandiza kuona chifukwa chake Yesu anawauza asodzi anayiwo kuti: ‘Kuyambira tsopano mudzakhala asodzi a anthu.’ Kodi asodziwo anachita chiyani atamva zimenezi? “Mmene iwo anakocheza ngalaŵa zawo pamtunda, anasiya zonse, nam’tsata Iye.”

14. (a) Kodi tingapeze bwanji mpumulo lerolino? (b) Kodi ndi uthenga wabwino wotsitsimula uti umene Yesu analengeza?

14 Inunso mungachite chimodzimodzi. Ntchito yophunzitsa anthu choonadi cha Baibulo ikupitirizabe. Mboni za Yehova pafupifupi mamiliyoni asanu ndi limodzi zavomera pempho la Yesu lakuti ‘asenze goli lake.’ Iwo ndi “asodzi a anthu.” (Mateyu 4:19) Ena amagwira ntchitoyi nthaŵi zonse ndipo ena amaigwira mmene angathere pa nthaŵi zosiyanasiyana. Onse amapeza kuti ndi ntchito yotsitsimula, ndipo motero sakhala ndi nkhaŵa zambiri pa moyo wawo. Imaphatikizapo kuchita zimene iwo amakonda, kuuza ena uthenga wabwino​—“uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 4:23) Nthaŵi zonse zimasangalatsa kulankhula za uthenga wabwino koma makamaka uthenga wabwino wa Ufumuwu. Baibulo lili ndi nkhani zofunika kwambiri zimene tingakhutiritse nazo anthu kuti atha kuchepetsa nkhaŵa pa moyo wawo.​—2 Timoteo 3:16, 17.

15. Kodi mungapindule motani ndi zimene Yesu anaphunzitsa za mmene tingakhalire?

15 Ngakhale anthu amene angoyamba kumene kuphunzira za Ufumu wa Mulungu apindula ku mlingo wina wake ndi zimene Yesu anaphunzitsa za mmene angakhalire. Ambiri anganene moona mtima kuti zimene Yesu anaphunzitsa zawatsitsimula ndipo zawathandiza kusinthiratu moyo wawo. Mutha kutsimikiza nokha zimenezi mwa kupenda mfundo zina za mmene mungakhalire zimene zili m’nkhani zosimba moyo wa Yesu ndi utumiki wake, makamaka Mauthenga Abwino amene analemba Mateyu, Marko, ndi Luka.

Mmene Tingapezere Mpumulo

16, 17. (a) Kodi ziphunzitso zazikulu za Yesu mungazipeze kuti? (b) Kodi n’chiyani chimafunika kuti tipeze mpumulo pogwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa?

16 Yesu m’ngululu ya 31 C.E., anaphunzitsa chiphunzitso chomwe mpaka lero n’chodziŵika kwambiri padziko lonse. Nthaŵi zambiri chimatchedwa Ulaliki wa pa Phiri. Chiphunzitsochi chili pa Mateyu machaputala 5 mpaka 7 ndi Luka chaputala 6, ndipo chikufotokoza mwachidule ziphunzitso zake zambiri. Mungapeze zina zimene Yesu anaphunzitsa m’mbali zina za Mauthenga Abwino. Mfundo zambiri zimene ananena n’zosavuta kuzimvetsa, ngakhale kuti mwina kungakhale kovuta kuzigwiritsa ntchito munthu payekha. Bwanji osaŵerenga machaputala amenewo mosamalitsa ndiponso mukumasinkhasinkha? Mphamvu ya mfundo zake ilimbikitsetu maganizo ndi mtima wanu.

17 N’zachidziŵikire kuti zimene Yesu anaphunzitsa tingaziike m’magulu osiyanasiyana. Tiyeni tiike m’gulu limodzi ziphunzitso zake zazikulu kuti tikhale ndi chiphunzitso chimodzi tsiku lililonse la mwezi, tili n’cholinga chozigwiritsa ntchito pa moyo wathu. Motani? Eya, musangoziyang’ana mfundozo mwa patalipatali. Kumbukirani wolamulira wolemera amene anafunsa Yesu Kristu kuti: “Ndizichita chiyani, kuti ndiloŵe moyo wosatha?” Yesu atabwereza zofunika zazikulu za Chilamulo cha Mulungu, munthuyo anati anali kuzisunga zonsezi. Komabe, anazindikira kuti anafunika kuchita zambiri. Yesu anam’pempha kuchita zowonjezereka kuti agwiritse ntchito mfundo zachikhalidwe za Mulungu m’njira zothandiza kuti akhale wophunzira wachangu. Mwachionekere, munthuyu sanali wokonzeka kuchita zambiri. (Luka 18:18-23) Choncho, munthu amene lerolino akufuna kuphunzira zimene Yesu anaphunzitsa, afunika kukumbukira kuti pali kusiyana pakati pa kuvomereza zimene Yesu anaphunzitsa ndi kuzitsatira kuti zichepetse nkhaŵa.

18. Perekani chitsanzo cha mmene mungagwiritsire ntchito mopindulitsa bokosi limene lili m’nkhani ino.

18 Poyamba kupenda ndi kugwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa, taonani mfundo yoyamba m’bokosi limene lili m’nkhani ino. Mfundo yoyambayi yachokera pa Mateyu 5:3-9. Inde, tonsefe tingatenge nthaŵi ndithu kusinkhasinkha malangizo abwino amene ali m’mavesi ameneŵa. Komabe, kuwatenga mavesi onsewo pamodzi, kodi munganene kuti akufotokoza chiyani za mtima wa munthu? Ngati mukufunadi kugonjetsa nkhaŵa zopitirira muyeso m’moyo wanu, kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Kodi moyo wanu ungasinthe motani ngati muika mtima kwambiri pa zinthu zauzimu ndi kumaganiza zimenezo nthaŵi zonse? Kodi pali zinthu zina m’moyo wanu zimene mufunika kuchepetsa kuti muike mtima kwambiri pa zinthu zauzimu? Ngati mungatero, zidzawonjezera chimwemwe chanu pakalipano.

19. Kodi mungatani kuti mupeze nzeru ndi kumvetsa kowonjezereka?

19 Pali zinanso zimene mungachite. Bwanji osakambirana mavesi amenewo ndi mtumiki wina wa Mulungu, mwina mwamuna kapena mkazi wanu, wachibale, kapena mnzanu? (Miyambo 18:24; 20:5) Kumbukirani kuti wolamulira wolemera uja anafunsa munthu wina​—Yesu​—za nkhani ngati imeneyi. Zimene anamuyankha zikanakulitsa chiyembekezo chake chokhudza chimwemwe ndi moyo wautali. Wolambira mnzanu amene mungakambirane naye mavesiŵa safanana ndi Yesu. Komabe, kukambirana zimene Yesu anaphunzitsa kukupindulitsani nonsenu. Tayesani kuchita zimenezo mwamsanga.

20, 21. Kodi mungatsatire ndondomeko yotani kuti muphunzire zimene Yesu anaphunzitsa, ndipo mungaone bwanji kuti mukupita patsogolo?

20 Tayang’ananinso m’bokosilo lakuti “Ziphunzitso Zokuthandizani.” Ziphunzitsozi aziika m’magulu motero kuti tsiku lililonse pali chiphunzitso chimodzi choti mupende. Choyamba mungaŵerenge zimene Yesu ananena m’mavesi amene tasonyeza. Ndiyeno ganizirani mawu akewo. Sinkhasinkhani mmene mungawagwiritsire ntchito pa moyo wanu. Ngati mukuona kuti mukuchita kale zimenezo, sinkhasinkhani kuti muone zina zimene mungachite kuti muzitsatira chiphunzitso cha Mulungu chimenecho nthaŵi zonse. Yesani kugwiritsa ntchito chiphunzitso chimenecho patsikulo. Ngati simunamvetse chiphunzitsocho kapena mmene mungachigwiritsire ntchito, chibwerezeni tsiku lotsatira. Komabe, kumbukirani kuti simufunika kuchita kukwanitsa bwinobwino chiphunzitso chilichonse musanayambe kupenda chiphunzitso china. Tsiku lotsatira, mungapende chiphunzitso china. Pakutha pa mlungu, mungabwereremo ndi kuona ngati mwakwanitsa kutsatira ziphunzitso za Yesu zinayi kapena zisanu. Mlungu wotsatira wonjezerani, tsiku ndi tsiku. Ngati muona kuti penapake mwalephera kugwiritsa ntchito chiphunzitso china, musagwe mphwayi. Zimenezo zingachitikire Mkristu aliyense. (2 Mbiri 6:36; Salmo 130:3; Mlaliki 7:20; Yakobo 3:8) Pitirizani kugwiritsa ntchito ziphunzitsozo mlungu wachitatu ndi wachinayi.

21 Pakutha pa mwezi kapena kuposerapo, mungakhale mutapenda mfundo zonse 31. Kaya mudzakhala mutapenda zonse kapena ayi, kodi zotsatira zake zidzakhala zotani? Kodi simudzakhala wachimwemweko, mwinanso kuchepetsa nkhaŵa? Ngakhale mutasintha pang’ono chabe, mosakayika mudzaona kuti mwachepetsako nkhaŵa, kapena muzitha kuthana nazo bwinoko, ndipo mudzakhala ndi njira yopitirizira. Musaiŵale kuti pali mfundo zina zabwino kwambiri zimene Yesu anaphunzitsa zimene sizili mu mndandandawo. Bwanji osafufuza zina mwa mfundo zimenezi ndi kuyesa kuzigwiritsa ntchito?​—Afilipi 3:16.

22. Kodi n’chiyani chingachitike ngati titatsatira zimene Yesu anaphunzitsa, koma ndi mbali inanso iti imene tifunika kuiphunzira?

22 Mutha kuona kuti goli la Yesu n’lofeŵadi ngakhale kuti lili ndi kulemera kwake. Katundu wa zimene anaphunzitsa ndi kukhala wophunzira ali wopepuka. Mtumwi Yohane, mnzake wapamtima wa Yesu, atadzionera yekha kwa zaka zoposa 60, anavomereza kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Inunso mungakhale ndi chidaliro ngati chimenechi. Mukagwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa mudzapeza kuti zinthu zimene zikudetsa nkhaŵa anthu ambiri lerolino sizidzakudetsani nkhaŵa kwambiri monga mmene ena akuchitira. Mudzaona kuti mwapeza mpumulo waukulu ndithu. (Salmo 34:8) Komabe, pali mbali ina ya goli lofeŵa la Yesu imene mufunika kuiphunzira. Yesu ananenanso kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” Kodi zimenezo zikugwirizana motani ndi kuphunzira kwathu kwa Yesu ndi kumutsanzira? M’nkhani yotsatirayi, tipenda zimenezi.​—Mateyu 11:29.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyang’ana kwa Yesu pofunafuna mpumulo wa nkhaŵa zathu zopitirira muyeso?

• Kodi goli linali chizindikiro cha chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?

• N’chifukwa chiyani Yesu anapempha anthu kuti asenze goli lake?

• Kodi mungapeze bwanji mpumulo wauzimu?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Lemba la chaka cha 2002 la Mboni za Yehova likhala lakuti: “Idzani kuno kwa Ine . . . ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.”​—Mateyu 11:28.

[Bokosi/​Chithunzi pamasamba 12, 13]

Ziphunzitso Zokuthandizani

Kodi ndi zinthu zabwino zotani zimene mungapeze m’buku la Mateyu machaputala 5 mpaka 7? M’machaputala ameneŵa muli ziphunzitso zimene Mphunzitsi Wamkulu, Yesu, anaphunzitsa ali m’mphepete mwa phiri la Galileya. Ŵerengani mavesi amene tasonyeza m’munsiŵa pogwiritsa ntchito Baibulo lanu ndipo dzifunseni mafunso amene akutsatira mavesiwo.

1. 5:3-9 Kodi zimenezi zikundiphunzitsa chiyani za mtima wanga? Kodi ndingatani kuti ndipeze chimwemwe chachikulu? Kodi nditani kuti ndiike mtima kwambiri pa zinthu zauzimu?

2. 5:25, 26 Kodi chofunika n’chiyani kuposa kutengera khalidwe lokonda kukangana limene anthu ambiri ali nalo?​—Luka 12:58, 59.

3. 5:27-30 Kodi mawu a Yesu akutsindika chiyani pankhani ya kuyerekezera m’maganizo za kugonana? Kodi kupeŵa kuchita zimenezi kungawonjezere bwanji chimwemwe changa ndi mtendere wanga wa maganizo?

4. 5:38-42 N’chifukwa chiyani ndiyenera kuyesetsa kupeŵa chiwawa chimene anthu masiku ano akulimbikitsa?

5. 5:43-48 Kodi ndingapindule motani ngati ndiyanjana ndi anthu amene ndinkawaona ngati adani anga? Kodi zimenezi zidzathandiza bwanji kuchepetsa kapena kuthetsa udani?

6. 6:14, 15 Ngati nthaŵi zina sindikhululukira ena, kodi ingakhale nsanje kapena mkwiyo umene umachititsa zimenezi? Ndingatani kuti ndisinthe zimenezi?

7. 6:16-18 Kodi ndimasamala kwambiri za maonekedwe anga kuposa mmene ndilili mumtima mwanga? Kodi ndizisamala kwambiri za chiyani?

8. 6:19-32 Kodi chingachitike n’chiyani ngati ndimadera nkhaŵa mopitirira muyeso nkhani za ndalama ndi chuma? Kodi n’kuganizira chiyani kumene kungandithandize kukhala wosamala pa nkhani imeneyi?

9. 7:1-5 Kodi ndimamva bwanji ndikakhala ndi anthu okonda kuweruza ndi kunena za anthu ena ndiponso kupezera zifukwa anzawo nthaŵi zonse? N’chifukwa chiyani n’kofunika kuti ndipeŵe kukhala ngati anthu otero?

10. 7:7-11 Ngati khama n’lofunika ndikamam’pempha Mulungu, bwanji nanga m’mbali zina za moyo?​—Luka 11:5-13.

11. 7:12 Ngakhale kuti Lamulo la Chikhalidwe ndikulidziŵa, kodi ndimaligwiritsa ntchito nthaŵi zochuluka motani pamene ndichitira zinthu anthu ena?

12. 7:24-27 Popeza ndili ndi udindo wolamulira moyo wanga, kodi ndingatani kuti ndikhale wokonzeka kulimbana ndi mavuto ndiponso masautso ambiri amene ndingakumane nawo? N’chifukwa chiyani ndiyenera kuganizira zimenezi pakalipano?​—Luka 6:46-49.

Ziphunzitso zina zimene ndingapende:

13. 8:2, 3 Kodi ndingachitire chifundo motani anthu ovutika monga mmene Yesu anachitira nthaŵi zambiri?

14. 9:9-38 Kodi kuchita chifundo n’kofunika motani pa moyo wanga, ndipo nditani kuti ndisonyeze kwambiri khalidweli?

15. 12:19 Potengapo phunziro pa ulosi wonena za Yesu, kodi ndimayesetsa kupeŵa kukangana?

16. 12:20, 21 Kodi pangakhale phindu lotani ngati ndipeŵa kukhumudwitsa anthu ena mwa zimene ndingalankhule kapena kuchita?

17. 12:34-37 Kodi nthaŵi zambiri ndimakonda kulankhula nkhani zotani? Ndimadziŵa kuti ndikafinya lalanje, madzi ake amatuluka. Motero, n’chifukwa chiyani ndiyenera kuganizira kwambiri zimene zili mumtima mwanga?​—Marko 7:20-23.

18. 15:4-6 Kodi ndikuphunzira chiyani pa zimene Yesu ananena za kusamala mwachikondi anthu achikulire?

19. 19:13-15 Kodi ndiyenera kupatula nthaŵi kuchita chiyani?

20. 20:25-28 N’chifukwa chiyani si bwino kugwiritsa ntchito udindo mosayenera? Kodi ndingatsanzire bwanji Yesu pankhani imeneyi?

Mfundo zina zimene Marko analemba:

21. 4:24, 25 Kodi kachitidwe kanga ka zinthu ndi anthu ena n’kofunika motani?

22. 9:50 Ngati zimene ndimalankhula ndi kuchita n’zoyenera, kodi pangakhale zotsatira zabwino zotani?

Malizani ndiziphunzitso zochepa zimene Luka analemba:

23. 8:11, 14 Ngati ndilekerera nkhaŵa, chuma ndi zosangalatsa kulamulira moyo wanga, kodi zotsatira zake zikhala zotani?

24. 9:1-6 Ngakhale Yesu anali ndi mphamvu zochiritsa odwala, kodi n’chiyani chimene anachiika patsogolo kwambiri?

25. 9:52-56 Kodi ndimafulumira kupsa mtima munthu akandilakwira? Kodi ndimapeŵa kubwezera?

26. 9:62 Kodi udindo wanga wolankhula za Ufumu wa Mulungu ndiyenera kuuona motani?

27. 10:29-37 Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndine mnansi osati ngati munthu woti sizikumukhudza?

28. 11:33-36 Kodi ndingasinthe zinthu ziti kuti moyo wanga ukhale wosalira zambiri?

29. 12:15 Kodi moyo ndi chuma n’zogwirizana motani?

30. 14:28-30 Ngati ndipatula nthaŵi kupenda mosamalitsa zoti ndisankhe kuchita, kodi ndingapeŵe chiyani ndipo pangakhale phindu lotani?

31. 16:10-12 Kodi ndingapindule chiyani ngati ndipitirizabe kukhulupirika?

[Zithunzi patsamba 10]

Ntchito yopulumutsa moyo titasenza goli la Yesu ndi yotsitsimula