Akristu Onse Oona Amalalikira
Akristu Onse Oona Amalalikira
“M’yimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.”—SALMO 96:2.
1. Kodi anthu afunika kumva uthenga wabwino wotani, ndipo Mboni za Yehova zakhala bwanji chitsanzo chabwino pofalitsa uthenga umenewu?
M’DZIKO lino m’mene masoka amachitika tsiku ndi tsiku, n’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti nkhondo, umbanda, njala ndi kuponderezana zitha posachedwapa malinga ndi mmene Baibulo limafotokozera. (Salmo 46:9; 72:3, 7, 8, 12, 16) Kodi umenewu si uthenga wabwino umene aliyense afunikadi kuumva? Mboni za Yehova zimaganiza choncho. Izo zimadziŵika kulikonse monga anthu amene amalalikira “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yesaya 52:7) N’zoona kuti Mboni zambiri zazunzidwa chifukwa chotsimikiza mtima kulengeza uthenga wabwino. Koma iwo amafunira zabwino anthu. Ndipotu, Mboni zili ndi mbiri ya changu ndi khama pa ntchito yawoyi.
2. Kodi chifukwa choyamba chimene Mboni za Yehova zimachitira khama kulalikira n’chiti?
2 Khama la Mboni za Yehova lerolino likugwirizana ndi la Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Nyuzipepala ya Aroma Katolika yakuti L’Osservatore Romano inanena molondola za Akristu amenewo kuti: “Akristu oyambirira akangobatizidwa ankaona kuti ndi ntchito yawo kulalikira Uthenga Wabwino. Akapolo anafalitsa Uthenga Wabwinowu mwa kulankhula ndi anthu.” N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova n’zakhama monga Akristu akalewo? Chifukwa choyamba n’chakuti uthenga wabwino umene akufalitsa ndi wochokera kwa mwini wake Yehova Mulungu. Kodi pangakhale chifukwa china chochitira khama kuposa chimenechi? Kulalikira kwawoku akutsatira zimene wamasalmo ananena kuti: “M’yimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.”—Salmo 96:2.
3. (a) Kodi chifukwa chachiŵiri chimene Mboni za Yehova zimachitira khama n’chiti? (b) Kodi “chipulumutso cha [Mulungu]” chimafuna chiyani?
3 Zimene wamasalmoyo ananena zikutikumbutsa chifukwa chachiŵiri chimene Mboni za Yehova zimachitira khama. Uthenga wawo ndi uthenga wa chipulumutso. Anthu ena amagwira ntchito ya zaumoyo, ya zachikhalidwe, ya zachuma ndi ntchito zina n’cholinga choti athandize anthu anzawo, ndipo amachitadi bwino kugwira ntchito zimenezi. Koma zimene munthu angam’chitire munthu mnzake n’zochepa poyerekezera ndi “chipulumutso [cha Mulungu].” Yehova kudzera mwa Yesu Kristu adzapulumutsa ofatsa ku uchimo, matenda ndi imfa. Amene adzalandira madalitso ameneŵa, adzakhala ndi moyo wosatha. (Yohane 3:16, 36; Chivumbulutso 21:3, 4) Lerolino, chipulumutso ndi chimodzi mwa ntchito “zodabwiza” zimene Akristu amazitchula potsatira mawu akuti: “Fotokozerani ulemerero wa [Mulungu] mwa amitundu; zodabwiza zake mwa mitundu yonse ya anthu. Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.”—Salmo 96:3, 4.
Chitsanzo cha Mbuye Wawo
4-6. (a) Kodi chifukwa chachitatu chimene Mboni za Yehova zimachitira khama n’chiti? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani khama pa ntchito yolalikira uthenga wabwino?
4 Chifukwa chachitatu chimene Mboni za Yehova zimachitira khama n’chakuti zimatsatira chitsanzo cha Yesu Kristu. (1 Petro 2:21) Munthu wangwiro ameneyo analandira ndi mtima wonse ntchito ‘yolalikira mawu abwino kwa ofatsa.’ (Yesaya 61:1; Luka 4:17-21) Motero, iye anali mlaliki. Ankalengeza uthenga wabwino. Anayenda mu Galileya ndi mu Yudeya monse, ‘kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mateyu 4:23) Ndipo popeza ankadziŵa kuti ambiri adzachitapo kanthu akamva uthenga wabwinowo, anauza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.”—Mateyu 9:37, 38.
5 Yesu mogwirizana ndi pemphero lake anaphunzitsa ena kuti akhale alaliki. M’kupita kwa nthaŵi, anatumiza atumwi ake paokha ndi kuwauza kuti: “Pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” Kodi zikanawathandiza kwambiri ngati akanakonza njira zochepetsera mavuto amene anthu anali kukumana nawo nthaŵi imeneyo? Kapena kodi akanayenera kuloŵa ndale kuti alimbane ndi chinyengo chimene chinali ponseponse panthaŵiyo? Ayi. M’malo mwake, Yesu anaika miyezo kwa alaliki achikristu onse pamene anawauza kuti: “Pamene mulikupita lalikani.”—Mateyu 10:5-7.
6 Yesu kenako anatumiza gulu lina la ophunzira kuti akalengeze kuti: “Ufumu wa Mulungu wayandikira.” Atabwerako ndi kukapereka lipoti lakuti zinawayendera bwino pa ulendo wawo wokalalikira, Yesu anakondwera. Ndiyeno anapemphera kuti: “Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda.” (Luka 10:1, 8, 9, 21) Ophunzira a Yesu, omwe kale ankagwira ntchito ya usodzi, ulimi, ndi ntchito zina, anali ngati ana powayerekezera ndi atsogoleri achipembedzo ophunzira kwambiri a m’dzikolo. Koma ophunzirawo anawaphunzitsa kulengeza uthenga wabwino woposa wina uliwonse.
7. Kodi otsatira a Yesu anayamba kulalikira kwa ndani iye atapita kumwamba?
7 Yesu atapita kumwamba, otsatira ake anapitiriza kufalitsa uthenga wabwino wa chipulumutso. (Machitidwe 2:21, 38-40) Kodi anayamba kulalikira kwa ndani? Kodi anapita kwa anthu amene sanali kudziŵa Mulungu? Ayi. Munda wawo woyamba unali Israyeli, anthu amene anali akudziŵa za Yehova kwa zaka zoposa 1,500. Kodi kunali koyenera kulalikira m’dziko limene anthu anali akulambira kale Yehova? Inde. Yesu anali atawauza kuti: “Mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Aisrayeli anafunika kumva uthenga wabwino monga mmene anafunikira anthu a mitundu ina.
8. Kodi Mboni za Yehova masiku ano zikutsanzira bwanji otsatira a Yesu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino?
8 N’chimodzimodzinso kuti lerolino Mboni za Yehova zikulalikira padziko lonse lapansi. Akugwirizana ndi mngelo amene Yohane anamuona amene anali ndi “Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) M’chaka cha 2001, Mboni za Yehova zinali kulalikira m’mayiko ndi m’madera okwana 235 kuphatikizapo mayiko amene anthu ambiri a kumeneko amati ndi Akristu. Kodi n’zolakwika kuti Mboni za Yehova zizilalikira ku madera kumene Matchalitchi Achikristu aliko kale? Anthu ena amanena kuti n’zolakwika ndipo mwina angafike poganiza kuti kulalikira koteroko ndiko “kuba nkhosa.” Komabe, Mboni za Yehova zimakumbukira mmene Yesu ankawaganizira Ayuda odzichepetsa amene analipo m’nthaŵi yake. Ngakhale kuti anthuwo anali ndi ansembe, Yesu sanazengereze kuwauza uthenga wabwino. Iye “anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Kodi Mboni za Yehova zizibisa uthenga wabwino zikapeza anthu odzichepetsa amene sakudziŵa za Yehova ndi Ufumu wake chabe chifukwa chakuti chipembedzo china chikunena kuti ndi anthu ake? Potsatira chitsanzo cha ophunzira a Yesu, tikuyankha kuti ayi. Uthenga wabwino uyenera kulalikidwa kwa “anthu a mitundu yonse,” popanda kupatula aliyense.—Marko 13:10.
Akristu Oyambirira Onse Ankalalikira
9. Kodi ndani amene anali kulalikira nawo mumpingo wachikristu wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino?
9 Kodi ndani amene ankalalikira nawo m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino? Maumboni akusonyeza kuti Akristu onse anali kulalikira. Wolemba mabuku wina, W. S. Williams, anati: “Umboni ndi wakuti Akristu onse m’Tchalitchi choyambirira . . . anali kulalikira uthenga wabwino.” Baibulo posimba zimene zinachitika pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E., limati: “Anadzazidwa onse [amuna ndi akazi] ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga mzimu anawalankhulitsa.” Amene anali kulalikira anali amuna ndi akazi, ana ndi achikulire, akapolo ndi mfulu. (Machitidwe 1:14; 2:1, 4, 17, 18; Yoweli 2:28, 29; Agalatiya 3:28) Akristu atathaŵa mu Yerusalemu chifukwa cha chizunzo, “iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mawuwo.” (Machitidwe 8:4) Onse “akubalalitsidwa” ankalalikira osati anasankha anthu ochepa chabe kuti ndiwo azichita zimenezo.
10. Kodi ndi ntchito ya mbali ziŵiri iti imene inakwaniritsidwa dongosolo la Chiyuda lisanawonongedwe?
10 M’zaka zonse zoyambirira anali kuchita zimenezi. Yesu analosera kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Pokwaniritsa mawu ameneŵa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, uthenga wabwino unalalikidwa ponseponse Aroma asanawononge dongosolo la chipembedzo ndi la ndale la Chiyuda. (Akolose 1:23) Ndiponso, otsatira a Yesu onse anamvera lamulo lake lakuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Akristu oyambirirawo sanangothandiza anthu ofatsa kukhulupirira Yesu n’kuwasiya kuti atumikire Mulungu mmene angafunire popanda kuwatsogolera, monga mmene alaliki ena a masiku ano amachitira. M’malo mwake, anawaphunzitsa kukhala ophunzira a Yesu, anawalinganiza kukhala m’mipingo, ndipo anawaphunzitsa kuti nawonso alalikire uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. (Machitidwe 14:21-23) Mboni za Yehova masiku ano zimachitanso chimodzimodzi.
11. Kodi ndani lerolino amene akulalikira nawo uthenga wabwino woposa wina uliwonse?
11 Mboni za Yehova zina, potsatira zitsanzo za Paulo, Barnaba, ndi anthu ena a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, zapita kukatumikira ku mayiko ena monga amishonale. Ntchito yawo yapindula zedi, chifukwa sanaloŵerere nawo ndale kapena kuloŵerera m’zinthu zina n’kusiya ntchito yawo yolalikira uthenga wabwino. Iwo angomvera lamulo la Yesu lakuti: “Pamene muli kupita lalikani.” Komabe, Mboni za Yehova zambiri sizikuchita umishonale ku mayiko ena. Ambiri amagwira ntchito kuti apeze zofunika pa moyo wawo, ndipo ena adakali pasukulu. Ena akulera ana. Koma Mboni zonse zimauza anthu ena uthenga wabwino umene izo zaphunzira. Ana ndi achikulire, amuna ndi akazi, amatsatira mwachimwemwe lamulo la Baibulo lakuti: “Lalikira mawu; chita nawo pa nthaŵi yake, popanda nthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Akupitiriza “kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu” monga m’mene ankachitira Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. (Machitidwe 5:42) Akulengeza kwa anthu uthenga wabwino woposa wina uliwonse.
Kodi N’kutembenuza Anthu Kapena Kulalikira?
12. Kodi anthu masiku ano amakuona motani kutembenuza anthu?
12 Masiku ano, anthu ena amanena kuti kutembenuza anthu n’kovulaza. Chikalata chimene anafalitsa a bungwe la World Council of Churches chimanena za “uchimo wotembenuza anthu.” Chifukwa chiyani? Lipoti la Catholic World Report limati: “Chifukwa cha kudandaula kwambiri kwa tchalitchi cha Orthodox, ‘kutembenuza anthu’ tsopano kukuonedwa ngati n’kuumiriza.”
13. Kodi zitsanzo zina za kutembenuza anthu kovulaza n’ziti?
13 Kodi kutembenuza anthu n’kovulaza? Ee, kungatero. Yesu ananena kuti kutembenuza anthu kumene alembi ndi Afalitsi ankachita kunali kovulaza kwa anthu amene anawatembenuzawo. (Mateyu 23:15) Inde, “kutembenuza anthu moumiriza” n’kolakwika. Mwachitsanzo, wolemba mbiri wina, Josephus, anati pamene Mmakabeyo wina dzina lake John Hyrcanus anagonjetsa anthu a ku Idumeya, iye “anawalola kukhalabe m’dzikolo kokha ngati analola kudulidwa ndi kutsatira malamulo a Ayuda.” Ngati anthu a ku Idumeya anafuna kukhala ndi moyo molamulidwa ndi Ayuda, anafunika kutsatira chipembedzo chachiyuda. Olemba mbiri amatiuza kuti m’zaka za m’ma 700 C.E., Charlemagne anagonjetsa anthu achikunja a ku Saxon, kumpoto kwa Ulaya ndipo anawaumiriza mwankhanza kuti atembenuke. * Komabe, kodi kutembenuka kwa a anthu a ku Saxon kapena a ku Idumeya kunalidi kwenikweni? Mwachitsanzo, kodi kutsatira Chilamulo cha Mose chouziridwa ndi Mulungu komwe Mfumu ya ku Idumeya, Herode, ankachita kunalidi kwenikweni poganizira kuti ndi yemwenso anafuna kupha Yesu ali mwana?
14. Kodi amishonale ena a Matchalitchi Achikristu amaumiriza motani anthu kuti atembenuke?
14 Kodi kutembenuza anthu koumiriza kukuchitikanso masiku ano? Inde, alipo ena amene akuchita zimenezo. Akuti amishonale ena a Matchalitchi Achikristu amauza anthu amene angatembenuke kuti awalipirira maphunziro kunja kwa dziko lawo. Kapenanso amauza anthu othaŵa kwawo omwe ali ndi njala kuti amvetsere ulaliki wawo kuti alandire chakudya. Malinga ndi lipoti limene linatuluka pa msonkhano wa Mabishopu a Orthodox mu 1992, “nthaŵi zina kutembenuza anthu kumachitika mwa kuwakopa ndi zinthu zakuthupi ndiponso nthaŵi zina mwa kuchita ziwawa za mitundu ina.”
15. Kodi Mboni za Yehova zimatembenuza anthu malinga ndi mmene tanthauzo la liwuli lilili masiku ano? Fotokozani.
15 Kuumiriza anthu kuti asinthe chipembedzo chawo n’kulakwa. N’chifukwa chake Mboni za Yehova sizichita zimenezo. * Motero, izo sizitembenuza anthu malinga ndi mmene tanthauzo la liwuli lilili masiku ano. M’malo mwake, amalalikira uthenga wabwino kwa aliyense monga mmene ankachitira Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Aliyense amene angamvetsere mwa kufuna kwake amamupempha kuti adziŵe zambiri mwa kuphunzira Baibulo. Anthu achidwi amenewo amaphunzira kukhala ndi chikhulupiriro chimene amachizika zolimba pa kudziŵa zoona zake za Baibulo, Mulungu, ndiponso zolinga zake. Zotsatira zake n’zakuti amaitanira pa dzina la Mulungu, Yehova, kuti apulumuke. (Aroma 10:13, 14, 17) Munthu amasankha yekha kuvomera kapena kukana uthenga wabwino. Mboni sizikakamiza. Akanati azikakamiza, ndiye kuti kutembenuza anthuko kukanakhala kopanda phindu. Kuti Mulungu avomereze kulambira kumene munthu akuchita, kuyenera kuchokera mumtima.—Deuteronomo 6:4, 5; 10:12.
Kulalikira Masiku Ano
16. Kodi ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova yawonjezereka motani masiku ano?
16 Nthaŵi zamakono zino, Mboni za Yehova zalalikira kwambiri uthenga wabwino wa Ufumu kuposa kale lonse pokwaniritsa Mateyu 24:14. Chida chachikulu chimene amagwiritsa ntchito polalikira ndicho magazini ya Nsanja ya Olonda. * Pamene anafalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda yoyamba mu 1879, anatulutsa magazini okwana pafupifupi 6,000 m’chinenero chimodzi. M’chaka cha 2001, patapita zaka 122 kuyambira nthaŵi imeneyo, magazini amene anafalitsa anakwana 23,042,000 m’zinenero 141. Kuwonjezereka kumeneku kwatsatananso ndi kukula kwa ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova. Tayerekezerani maola zikwi zochepa amene Mboni zinathera m’ntchito yolalikira m’zaka za m’ma 1800 ndi maola 1,169,082,225 amene zinathera m’ntchito yolalikira m’chaka cha 2001. Zinkachititsa maphunziro a Baibulo aulere okwana 4,921,702 pa avareji mwezi uliwonse. Zinachita ntchito yabwino ndiponso yaikulutu zedi! Ndipo alaliki a Ufumu a changu okwana 6,117,666 ndi amene anachita ntchitoyi.
17. (a) Kodi ndi milungu yonyenga iti imene anthu akuilambira masiku ano? (b) Kodi munthu aliyense afunika kudziŵa chiyani mosaganizira kuti ndi wa chinenero chanji, kaya mtundu wake, kapena udindo wake?
17 Wamasalmo ananena kuti: “Milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano: koma Yehova analenga zakumwamba.” (Salmo 96:5) Masiku ano, anthu m’dzikoli akulambira utundu, zizindikiro zautundu, anthu otchuka, zinthu zakuthupi, ngakhalenso chuma chimene. (Mateyu 6:24; Aefeso 5:5; Akolose 3:5) Mohandas K. Gandhi nthaŵi ina anati: “Ndikutsimikiza kuti . . . anthu ku Ulaya masiku ano ndi Akristu mwa dzina lokha. Kunena zoona, akulambiradi chuma.” Mfundo ndi yakuti, anthu kulikonse afunika kumva uthenga wabwino. Aliyense kaya ndi wa chinenero chanji, wa dziko liti, kapena kaya ali ndi udindo wotani, afunika kudziŵa za Yehova ndi zolinga zake. Tikanakonda anthu onse akanatsatira zimene wamasalmo ananena kuti: “Mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu. Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake.” (Salmo 96:7, 8) Mboni za Yehova zimathandiza ena kuphunzira za Yehova kuti athe kum’patsa ulemerero moyenera. Ndipo anthu amene akumvera amapindula kwambiri. Kodi amapindula chiyani? Tikambirana zimenezi m’nkhani yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Malinga ndi buku lakuti The Catholic Encyclopedia, m’nyengo ya kukonzanso zinthu ya Reformation, kuumiriza anthu kutsatira chipembedzo chinachake ankakufotoza m’mawu a Chilatini amene kwenikweni amatanthauza kuti: “Amene akulamulira dziko ndi amenenso amasankha chipembedzo cha dzikolo.”
^ ndime 15 Pamsonkhano wa bungwe la zipembedzo lakuti United States International Religious Freedom Commission pa November 16, 2000, mmodzi mwa anthu amene analipo anasiyanitsa anthu amene amatembenuza anthu moumiriza ndi ntchito ya Mboni za Yehova. Ananena kuti, Mboni za Yehova zikamalalikira kwa ena, zimatero mwa njira yakuti munthu atha kungoyankha kuti “sindifuna kumva uthenga wanu” n’kutseka chitseko.
^ ndime 16 Mutu wonse wa magaziniyi ndi Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova.
Kodi Mungafotokoze?
• N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimalalikira mwakhama?
• N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimalalikira ngakhale kumene kuli Matchalitchi Achikristu?
• N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova sizitembenuza anthu malinga ndi mmene tanthauzo la liwuli lilili masiku ano?
• Kodi ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova yawonjezereka motani masiku ano?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 9]
Yesu anali mlaliki wakhama ndipo anaphunzitsa anthu ena kuti achite ntchito yomweyo
[Chithunzi patsamba 10]
Anthu onse mu mpingo wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anali kulalikira
[Chithunzi patsamba 11]
Kuumiriza anthu kusintha chipembedzo chawo n’kulakwa