Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akulu—Phunzitsani Ena Kusenza Maudindo

Akulu—Phunzitsani Ena Kusenza Maudindo

Akulu​—Phunzitsani Ena Kusenza Maudindo

M’MIPINGO ya Mboni za Yehova pa dziko lonse, mukufunika mwamsanga amuna amene angamayang’anire mipingoyo. Pali zifukwa zazikulu zitatu zimene zikuchititsa kuti amunaŵa afunike.

Chifukwa choyamba n’chakuti Yehova akukwaniritsa lonjezo lake lochititsa ‘wochepa kusanduka mtundu wamphamvu.’ (Yesaya 60:22) Kukoma mtima kwake kwachititsa kuti m’zaka zitatu zapitazi, ophunzira atsopano pafupifupi 1,000,000 abatizidwe kukhala Mboni za Yehova. Amuna amene angathe kusenza maudindo akufunika kuti athandize anthu amene abatizidwa kumeneŵa, kuti afike pokhwima mwauzimu.​—Ahebri 6:1.

Chifukwa chachiŵiri n’chakuti ukalamba ndi matenda zachititsa kuti ena amene atumikira monga akulu kwa zaka zambiri achepetse ntchito zina zimene ankachita mu mpingo.

Chifukwa chachitatu n’chakuti akulu achikristu achangu ambiri akutumikiranso m’Makomiti Olankhulana ndi Chipatala, m’Makomiti Omanga a Chigawo kapena m’Makomiti Omanga Nyumba za Msonkhano. Nthaŵi zina abale ameneŵa akakamizika kusiya maudindo ena a kumpingo kwawo kuti athe kusamalira mbali zonse.

Kodi amuna ena oyeneretsedwa amene akufunikaŵa angapezeke bwanji? Angapezeke mwa kuphunzitsa amuna ena. Baibulo limalimbikitsa oyang’anira achikristu kuphunzitsa “anthu okhulupirika, amene adzadziŵa kuphunzitsa enanso.” (2 Timoteo 2:2) Mawu oti “phunzitsa” amatanthauza kuphunzitsa munthu kuti akhale woyenerera, wokhoza, kapena waluso. Tiyeni tione mmene akulu angaphunzitsire amuna ena oyenerera.

Tsanzirani Chitsanzo cha Yehova

Yesu Kristu mosakayikira anali ‘woyenerera, wokhoza ndiponso waluso’ pa ntchito yake ndipo zimenezi n’zosadabwitsa. Yehova Mulungu mwiniyo ndi amene anam’phunzitsa. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti kuphunzitsa kumeneku kukhale kogwira mtima? Yesu anatchula zinthu zitatu zimene zinachititsa zimenezi malinga ndi mmene timaŵerengera pa Yohane 5:20. Pamenepo amati: ‘Pakuti Atate [1] akonda Mwana, [2] namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa [3] ntchito zoposa izi.’ Kupenda zinthu zitatu zimenezi kutithandiza kuona mmene akulu angaphunzitsire ena.

Onani kuti Yesu anayamba ndi kuti: ‘Atate akonda mwana.’ Panali ubale weniweni pakati pa Yehova ndi Mwana wake kuyambira pamene anayamba kulenga zinthu. Pa Miyambo 8:30 pamatithandiza kuona mmene ubale umenewo unalili. Pamenepo timaŵerenga kuti: ‘[Ine, Yesu] ndinali pambali pake [pa Yehova Mulungu] ngati mmisiri; ndinam’sekeretsa [“anandikonda kwambiri,” NW] tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse.’ Yesu sanakayike kuti Yehova anali ‘kum’konda kwambiri.’ Ndipo Yesu sanabise chimwemwe chimene anali nacho pamene anali kugwira ntchito pambali pa Atate wake. Zimakhalatu bwino kwambiri pakakhala ubale weniweni, womverana pakati pa akulu achikristu ndi anthu amene akuwaphunzitsa!

Chinthu chachiŵiri chimene Yesu anatchula n’chakuti Atate ‘anamuonetsa zonse azichita yekha.’ Mawu ameneŵa akutsimikizira zimene zili pa Miyambo 8:30 zoti Yesu ‘anali pambali’ pa Yehova pamene ankalenga zinthu zonse. (Genesis 1:26) Akulu angatsanzire chitsanzo chabwino kwambiri chimenechi mwa kugwira ntchito limodzi ndi atumiki otumikira, kuwaonetsa mmene angagwirire bwino ntchito yawo. Komabe, amene akufunika kuwaphunzitsa si atumiki otumikira amene angoikidwa kumene okha ayi. Bwanji za abale okhulupirika amene akhala akuyesetsa kwa zaka zambiri kuti akhale paudindo woyang’anira koma omwe mpaka lero sanaikidwe? (1 Timoteo 3:1) Akulu afunika kulangiza abale oterowo mosapita m’mbali kuti adziŵe mbali zimene afunika kuwongolera.

Mwachitsanzo, mtumiki wotumikira angakhale wodalirika, wosunga nthaŵi, ndiponso wogwira ntchito zake mosamala zedi. Mwina angakhalenso wophunzitsa bwino. Angamachite ntchito zabwino zambiri mumpingo. Komabe, mwina sangazindikire kuti nthaŵi zambiri amachitira zinthu Akristu anzake mwaukali. Akulu afunika kusonyeza “nzeru yofatsa.” (Yakobo 3:13) Kodi mkulu sangasonyeze chifundo mwa kulankhula ndi mtumiki wotumikirayo, kumufotokozera momveka bwino vutolo, kum’patsa zitsanzo zenizeni, ndi kumuuza mfundo zothandiza za mmene angawongolerere? Ngati mkuluyo ‘akoleretsa uphungu wakewo’ mosamala, mtumiki wotumikirayo adzamvera ndi kutsatira zimene walangizidwazo. (Akolose 4:6) Komanso naye mtumiki wotumikira angachititse ntchito ya mkuluyo kukhala yosangalatsa ngati amvetsera ndi kulandira malangizo amene wapatsidwawo.​—Salmo 141:5.

M’mipingo ina, akulu akuphunzitsa atumiki otumikira nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, amatenga atumiki otumikira oyenerera kuti atsagane nawo popita kokaona odwala kapena okalamba. Mwakuchita zimenezi, atumiki otumikira amapeza luso la ntchito ya ubusa. Komabe, pali zambiri zimene mtumiki wotumikira angachite kuti awonjezere kupita kwake patsogolo mwauzimu.​—Onani bokosi limene lili pansipa lakuti “Zimene Atumiki Otumikira Angachite.”

Chinthu chachitatu chimene chinachititsa kuti kuphunzira kwa Yesu kukhale kogwira mtima n’chakuti Yehova anamuphunzitsa akudziŵa kuti Yesuyo adzachita zambiri m’tsogolo. Yesu ananena kuti Atate adzamuonetsa Mwana ‘ntchito zoposa izi.’ Zimene Yesu anaphunzira pamene anali padziko lapansi zinamuthandiza kukhala ndi makhalidwe amene anafunikira kuti adzathe kuchita ntchito za m’tsogolo. (Ahebri 4:15; 5:8, 9) Mwachitsanzo, Yesu adzalandira ntchito yaikulu kwambiri posachedwapa​—ntchito youkitsa akufa ndi kuweruza anthu miyandamiyanda amene pakalipano ali m’manda.​—Yohane 5:21, 22.

Akulu lerolino afunika kumaganizira za m’tsogolo pophunzitsa atumiki otumikira. Ngakhale kuti zingaoneke ngati pakalipano atumiki otumikira ndi akulu alipo okwanira kusamalira ntchito zimene zilipo, kodi padzakhalanso akulu ndi atumiki otumikira okwanira ngati mpingo watsopano wapangika? Kodi adzakhalapo okwanirabe ngati mipingo ingapo itapangika? M’zaka zitatu zapitazi, panali mipingo yatsopano yoposa 6,000 pa dziko lonse. Pakufunikatu akulu ndi atumiki otumikira ambiri kuti asamalire mipingo yatsopano imeneyi.

Akulu, kodi mukutsanzira Yehova mwa kukulitsa ubale weniweni ndi amuna amene mukuwaphunzitsa? Kodi mukuwaonetsa mmene angagwirire ntchito yawo? Kodi mukuganizira za m’tsogolo? Kutsanzira chitsanzo cha Yehova pamene ankaphunzitsa Yesu kudzathandiza kuti anthu ambiri apeze madalitso aakulu.

Musaumire Kugaŵa Maudindo

Akulu aluso amene azoloŵera kusamalira okha maudindo akuluakulu ambiri panthaŵi imodzi angaumire kugaŵira ena maudindo. Mwina angakhale atayesapo kuchita zimenezo mmbuyomu koma sizinathandize. Motero, angakhale ndi maganizo akuti, ‘Ngati munthu ukufuna kuti ntchito igwirike bwino, uigwire wekha.’ Koma kodi maganizo ameneŵa akugwirizana ndi zimene Yehova amafuna, monga mmene Malemba amafotokozera kuti amuna amene akudziŵa zambiri aphunzitse omwe sakudziŵa?​—2 Timoteo 2:2.

Mtumwi Paulo anakhumudwa pamene mnzake wina woyenda naye, Yohane Marko, anasiya ntchito yake ku Pamfuliya ndi kubwerera kumudzi kwawo. (Machitidwe 15:38, 39) Komabe, Paulo sanalole kuti chokhumudwitsa chimenechi chimulepheretse kuphunzitsanso ena. Anasankha mbale wina wachinyamata, Timoteo, ndipo anam’phunzitsa kuchita umishonale. * (Machitidwe 16:1-3) Ali ku Bereya, amishonalewo anatsutsidwa modetsa nkhaŵa moti sizikanathekanso kuti Paulo akhalebe kumeneko. Motero, iye anasiya mpingo watsopanowo m’manja mwa mbale wachikulire wokhwima mwauzimu Sila, ndi Timoteo kuti aziusamalira. (Machitidwe 17:13-15) Mosakayika, Timoteo anaphunzira zambiri kwa Sila. Kenako, Timoteo atakonzeka kulandira maudindo ena, Paulo anam’tumiza iye ku Tesalonika kuti akalimbikitse mpingo wa kumeneko.​—1 Atesalonika 3:1-3.

Ubale wa Paulo ndi Timoteo sunali wozilala. Unali ubale weniweni, wolimba. Paulo polembera mpingo wa ku Korinto ananena za Timoteo, amene ankafuna kum’tumiza kumeneko, kuti anali ‘mwana wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye.’ Anapitiriza kuti: ‘Timoteo adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Kristu.’ (1 Akorinto 4:17) Timoteo anamvera ndi kugwiritsa ntchito zimene Paulo anam’phunzitsa n’kukhala woyenerera kugwira ntchito yake. Abale achinyamata ambiri akhala atumiki otumikira, akulu, ngakhalenso oyang’anira oyendayenda chifukwa chopindula ndi zimene anaphunzira kwa abale achikulire ofuna kuthandiza amene anali ndi chidwi mwa achinyamatawo, monga mmene anachitira Paulo pophunzitsa Timoteo.

Akulu, Phunzitsani Ena!

Ulosi womwe uli pa Yesaya 60:22 ukukwaniritsidwa ndendende lerolino. Yehova akuchititsa ‘wochepa kusanduka mtundu wamphamvu.’ Kuti mtundu umenewu ukhalebe “wamphamvu,” ufunika kuulinganiza bwino. Akulu, bwanji osaganizira njira zoperekera maphunziro ena kwa amuna odzipatulira amene akuyenerera maphunzirowo? Onetsetsani kuti mtumiki wotumikira aliyense akudziŵa bwinobwino mbali zimene afunika kuwongolera kuti apite patsogolo. Ndipo inu abale obatizidwa, pindulani ndi malangizo alionse amene angakupatseni. Pindulani ndi mipata yokulitsira nzeru zanu, chidziŵitso chanu ndi luso lanu. Mosakayika, Yehova adzadalitsa pulogalamu imeneyi yothandiza ena mwachikondi.​—Yesaya 61:5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Patapita nthaŵi, Paulo anagwiranso ntchito pamodzi ndi Yohane Marko.​—Akolose 4:10.

[Bokosi patsamba 30]

Zimene Atumiki Otumikira Angachite

Ngakhale kuti akulu afunika kuphunzitsa atumiki otumikira, pali zambiri zimene atumiki otumikirawo angachite kuti awonjezere kupita kwawo patsogolo mwauzimu.

​—Atumiki otumikira akhale akhama ndiponso odalirika pogwira ntchito zawo. Afunikanso kukhala ndi chizoloŵezi chabwino chophunzira. Nthaŵi zambiri, kupita patsogolo kumadalira kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito zimene munthu waphunzirazo.

​—Mtumiki wotumikira akamakonzekera kukakamba nkhani pamsonkhano wachikristu, asakayike kufunsa mkulu waluso kuti amufotokozere mmene angakambire nkhaniyo.

​—Mtumiki wotumikira angapemphenso mkulu kuti azimuyang’anira mwatcheru mmene akukambira nkhani ya Baibulo ndi kumulangiza mmene angawongolere.

Atumiki otumikira azipempha, kulandira, ndi kugwiritsa ntchito malangizo ochokera kwa akulu. Mwakuchita zimenezi, kupita kwawo patsogolo ‘kudzaonekera kwa anthu onse.’​—1 Timoteo 4:15.