Kodi N’zothekadi Kuti Anthu Azikhala Mofanana?
Kodi N’zothekadi Kuti Anthu Azikhala Mofanana?
JOHN ADAMS yemwe anali pulezidenti wachiŵiri wa dziko la United States, anasaina nawo chikalata cha ufulu wodzilamulira cha Declaration of Independence chomwe mwa zina chinali ndi mawu anzeru aŵa: “Tikukhulupirira kuti mfundo zoona zimenezi n’zodziŵika bwino, kuti anthu onse analengedwa ofanana.” Komabe, zikuoneka kuti John Adams ankakayikira zoti anthu onse ndi ofananadi chifukwa iye analemba kuti: “Kusiyana kwa Maganizo ndiponso Thupi anakuika ndi Mulungu Wamphamvuyonse popanga matupi a anthu ndipo palibe njira kapena mfundo zilizonse zomwe zingasinthe zimenezi.” Mosiyana ndi zimenezo, wolemba mbiri wina wa ku Britain, H. G. Wells, ankaganiza kuti n’zotheka kukhala ndi dziko la anthu ofanana mwa kutsatira mfundo zitatu izi: kukhala ndi chipembedzo chosadetsedwa chapadziko lonse, maphunziro ofanana kwa anthu onse, ndiponso kukhala opanda asilikali a nkhondo.
Mpaka lero anthu sanapangebe dziko lokhala ndi anthu ofanana lomwe Wells ankaliganizira.
Anthu ndi osiyanadi kwambiri ndipo kusiyana kwa magulu a anthu n’kwakukulube lerolino. Kodi kusiyana kumeneku kwathandiza magulu onse a anthu? Ayi. Kusiyana kumeneku kumagaŵanitsa anthu ndipo zimenezi zimayambitsa nsanje, chidani, mkwiyo, ndiponso kuphana. Kale ku Africa, Australia, ndiponso North America, anthu akuda anali pa mavuto chifukwa chakuti panthaŵiyo azungu ankaonedwa kukhala apamwamba. Zimenezi zinachititsa kuphedwa kwa mtundu wonse wa Aaborijini a ku Van Diemen’s Land (komwe tsopano amati ku Tasmania). Ku Ulaya, kuona mtundu wa Ayuda kukhala wotsika kunachititsa a Nazi kupululutsa mtunduwo. Chuma chochuluka chomwe anthu apamwamba olamulira anali nacho komanso kusoŵa komwe anthu otsikirapo ndiponso anthu wamba anali nako ndiko kunayambitsa gulu lopanduka la ku France m’ma 1700 ndiponso gulu lopanduka la Bolshevik ku Russia m’ma 1900.Munthu wakale wanzeru analemba kuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Kaya wolamulirayo akhale munthu payekha kapena gulu la anthu, mawu ameneŵa amagwirabe ntchito. Pamene gulu lina la anthu ladzikweza kukhala pamwamba pa gulu lina, zivute zitani, zotsatira zake zimakhala masoka ndiponso mavuto.
Mulungu Amaona Anthu Onse Mofanana
Kodi pali magulu ena a anthu amene ali apamwamba mwachibadwa kuposa ena? Mulungu samaona motero. Baibulo limati: ‘Ndipo ndi munthu mmodzi [Mulungu] analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.’ (Machitidwe 17:26) Komanso, Mlengi ‘sasamalira nkhope za akalonga, sasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka, pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.’ (Yobu 34:19) Anthu onse n’pachibale ndipo Mulungu amawaona kuti anabadwa ofanana.
Kumbukiraninso kuti munthu akamwalira zonse zoti anali wapamwamba zimathera pomwepo. Anthu akale a ku Igupto sankakhulupirira zimenezi. Farao akamwalira ankamuika m’manda pamodzi ndi zinthu za mtengo wapatali n’cholinga choti ati azikasangalala nazo pamene akukapitiriza udindo wake wapamwamba ku moyo wina. Kodi analidi kukasangalala nazo zinthuzo? Ayi. Mapeto ake, mbala ndizo zinkatenga chuma chochuluka chimenecho. Ndipo zinthu zina zambiri zimene zinatsala zomwe mbala sizinabe, mutha kukaziona lerolino ku nyumba zosungirako zinthu zochititsa chidwi.
Popeza kuti anali wakufa, Farao sakanatha m’pang’ono pomwe kugwiritsa ntchito zinthu za mtengo wapamwamba zimenezo. Munthu akafa palibe zoti anali wapamwamba kapena munthu wamba, wolemera kapena wosauka. Baibulo limati: “Anthu anzeru amafa; opusa, opanda nzeru, onsewo amafa. Pakuti anthu ali ngati ng’ombe zomwe moyo wawo sukhalitsa, ali ngati ng’ombe zomwe nthaŵi yawo ndi yaifupi.” (Salmo 49:10, 12, The New English Bible) Kaya ndife mafumu kapena akapolo, mawu ouziridwa otsatiraŵa amagwira ntchito kwa tonsefe: “Akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphoto; pakuti angoiwalika. . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”—Mlaliki 9:5, 10.
Mulungu amaona kuti anthu tonse tinabadwa ofanana ndipo tikamwalira timakhalanso ofanana. Choncho, n’kupusa kwambiri kukweza gulu lina la anthu kwanthaŵi yochepa chabe yomwe tingakhale ndi moyo.
Kodi Zidzathekadi Anthu Kukhala Ofanana?
Komabe, kodi pali chiyembekezo choti tsiku lina anthu adzakhala ofanana moti kusiyana kwa magulu awo sikudzakhalanso kofunika? Inde, chilipo. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo pamene Yesu anali pano padziko lapansi, maziko a chiyembekezo chimenecho anayalidwa. Yesu anapereka moyo wake kuti ukhale nsembe ya dipo yowombolera anthu onse kuti “yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Yesu pofuna kusonyeza kuti pasakhale ophunzira ake ena amene ayenera kudzikweza pamwamba pa okhulupirira anzawo, anati: “Inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. Ndipo musatchedwa Mateyu 23:8-12) Mulungu amaona ophunzira onse oona a Yesu kukhala ofanana m’chipembedzo choona.
atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu. Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa.” (Kodi Akristu oyambirira ameneŵa ankadziona kuti anali ofanana? Amene ankamvetsa zomwe Yesu anali kuphunzitsa anatero. Ankadziŵa kuti onse anali ofanana m’chipembedzo choona ndipo anasonyeza zimenezo mwa kumatchulana kuti “mbale.” (Filemoni 1, 7, 20) Palibe ndi mmodzi yemwe amene analimbikitsidwa kuti azidziona ngati wapamwamba kuposa ena. Mwachitsanzo, talingalirani mmene Petro anadzitchulira modzichepetsa m’kalata yake yachiŵiri. Anati: “Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Kristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife.” (2 Petro 1:1) Petro anali ataphunzitsidwa ndi Yesu, ndipo monga mtumwi, iye anali ndi udindo wofunika kwambiri. Komabe, anasankha kudzitcha kuti kapolo ndiponso ankazindikira kuti Akristu ena nawonso ali ndi mwayi wofanana ndi wake wokhulupirira choonadi.
Ena anganene kuti mfundo yoti anthu azikhala mofanana n’njosemphana ndi mfundo yakuti kale Chikristu chisanayambe Mulungu anasankha Israyeli kukhala mtundu wake wapadera. (Eksodo 19:5, 6) Anthu amaganizo oterowo anganene kuti chimenechi n’chitsanzo chakuti mtundu wina uyenera kukhala wapamwamba kuposa mitundu ina. Koma zimenezo si zoona ayi. N’zoona kuti Aisrayeli, pokhala mbadwa za Abrahamu, analidi paunansi wapadera ndi Mulungu ndipo Iye ankawagwiritsira ntchito monga njira yomwe ankavumbulira zofuna zake. (Aroma 3:1, 2) Koma cholinga cha zimenezi sichinali kuwakweza Aisrayeliwo kukhala apamwamba kuposa mitundu ina ayi. Mmalo mwake, cholinga chinali chakuti ‘mitundu yonse idzadalitsidwe’ kudzera mwa iwo.—Genesis 22:18; Agalatiya 3:8.
Komabe, Aisrayeli ambiri sanatsanzire chikhulupiriro chomwe kholo lawo Abrahamu anali nacho. Iwo anali osakhulupirira ndipo anakana kuti Yesu anali Mesiya. Chifukwa cha zimenezi, Mulungu anawakananso iwo. (Mateyu 21:43) Komabe, anthu ofatsa m’mitundu ya anthu sanataye mwayi wokalandira madalitso omwe Mulungu analonjeza. Pa Pentekoste wa 33 C.E., mpingo wachikristu unabadwa. Gulu la Akristu odzozedwa ndi mzimu woyera limenelo linatchedwa “Israyeli wa Mulungu,” ndipo ndilo linakhala njira yomwe madalitso olonjezedwawo adzadzera.—Agalatiya 6:16.
Ena mwa anthu amene anapanga mpingo umenewo anafunikira kuwaphunzitsa pa nkhani ya kukhala ofanana. Mwachitsanzo, wophunzira Yakobo anapereka uphungu kwa anthu amene ankachitira ulemu kwambiri anthu olemera kuposa anthu osauka. (Yakobo 2:1-4) Kuchita zimenezo kunali kosayenera. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti Akristu omwe sanali Ayuda sikuti anali otsika powayerekeza ndi Akristu omwe anali Ayuda, komanso, Akristu achikazi sanali otsika poyerekeza ndi Akristu achimuna. Iye analemba kuti: “Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Yesu Kristu. Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudavala Kristu. Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.”—Agalatiya 3:26-28.
Anthu Amene Amakhala Mofanana Lerolino
Mboni za Yehova lerolino zimayesetsa kutsatira mfundo za m’Malemba. Izo zimazindikira kuti Mulungu amaona magulu onse a anthu mofanana. N’chifukwa chake sizigaŵa kuti ena ndi atsogoleri 1 Yohane 2:15-17, NW) Mmalo mwake, onse amagwirizana mwa kulambira Wolamulira Wamkulu, Yehova Mulungu.
atchalitchi kapena abusa, ndiponso pochita zinthu sizimaganizira kaonekedwe ka khungu kapena chuma chomwe munthu ali nacho. Ngakhale kuti ena ndi olemera, oterowo saika mtima pa kufuna ‘kuonetsera chuma chawocho mwamatama,’ chifukwa amazindikira kuti chumacho n’chosakhalitsa. (Aliyense amalandira udindo wogwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Monga momwe Yesu anachitira, iwo amalemekeza anthu amene akuponderezedwa ndiponso kunyalanyazidwa mwa kuwachezera m’nyumba zawo, ndi kuwaphunzitsa Mawu a Mulungu. Anthu amene ena angawaone ngati otsika amagwirira ntchito limodzi ndi anthu amene angaoneke ngati apamwamba. Iwo amaona kuti mikhalidwe yauzimu ndiyo yofunika kwambiri osati kukhala apamwamba. Monga momwe zinalili m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, onse ndi abale ndi alongo m’chikhulupiriro.
Anthu Ofanana Amasiyanabe M’zinthu Zina
N’zoona kuti kukhala ofanana sikutanthauza kufanana pa zinthu zonse. M’gulu lachikristu muli anthu a magulu onse, amuna, akazi, okalamba, ndiponso ana. Komanso muli anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana, mitundu yosiyanasiyana, zinenero zosiyanasiyana, ndiponso opeza mosiyanasiyana. Monga munthu payekha, aliyense ali ndi nzeru ndi mphamvu zochitira zinthu mosiyanasiyana. Koma kusiyana kumeneku sikumachititsa ena kukhala apamwamba kuposa anzawo. Mmalo mwake, kusiyana koteroko kumangokhala ngati maluŵa osangalatsa. Akristu ameneŵa amazindikira kuti maluso amene ali nawo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo kuti palibe chifukwa chodzionera kukhala apamwamba kuposa ena.
Kusankhana magulu kukuchitika chifukwa chakuti anthu amafuna kudzilamulira m’malo motsatira chitsogozo cha Mulungu. Posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzatenga ulamuliro wa dziko lapansi ndipo zimenezi zidzachititsa kuti kusankhana magulu komwe anthu anakuyambitsa, pamodzi ndi zinthu zina zonse zomwe zakhala zikusautsa anthu zithe. Kenako “ofatsa adzalandira dziko lapansi” mulingaliro lenileni. (Salmo 37:11) Zonse zomwe anthu amadzitamandira nazo, kumadzitcha kuti ndi apamwamba, zidzakhala zitapita. Kusiyana kwa magulu a anthu sikudzagaŵanitsanso ubale wapadziko lonse wa anthu.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Mlengi ‘sasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka, pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.’—Yobu 34:19.
[Chithunzi patsamba 6]
Mboni za Yehova zimalemekeza anthu omwe zimakhala nawo
[Zithunzi patsamba 7]
Makhalidwe auzimu ndiwo chinthu chofunika kwambiri kwa Akristu oona