Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Wapereka “Mphamvu Yoposa Yachibadwa”

Yehova Wapereka “Mphamvu Yoposa Yachibadwa”

Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Wapereka “Mphamvu Yoposa Yachibadwa”

YOSIMBIDWA NDI HELEN MARKS

Linali tsiku lotentha kwambiri m’chilimwe cha mu 1986. Ndinali ndekhandekha m’chipinda chochitira kasitomu pa bwalo lina la ndege lopanda phokoso ku Ulaya. Kumeneku kunali ku Tiranë mzinda womwe ndi likulu la dziko la Albania lomwe linali litanena kuti ndi “dziko lokana Mulungu loyamba padziko lapansi.”

N’TAGWIDWA njakata ndiponso mantha pa zomwe ndinkayembekezera kuti zindichitikira, ofisala yemwe anali ndi mfuti anayamba kusecha chikwama changa. Ndikanachita kapena kunena chinachake chomwe chikanam’pangitsa ofisalayo kundikayikira, ndiye kuti akadandigwira n’kundithamangitsa m’dzikolo ndipo amene anabwera kudzandichingamira akanaikidwa m’ndende kapena mumsasa wachibalo. Mwamwayi, ndinamuchititsa ofisalayo kukhala wokoma mtima kwambiri mwa kum’patsa chingamu ndiponso mandasi. Koma kodi zinatheka bwanji kuti zinthu ngati zimenezi zichitikire mkazi ngati ine wa zaka za m’ma 60 panthaŵiyo? N’chifukwa chiyani ndinalolera kusiya moyo wosangalatsa ndiponso kuika moyo wanga pachiswe pofuna kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu m’dziko lomwe munali anthu ambiri otsatira ziphunzitso za chikomyunizimu za Marx ndi Lenin?

Mtsikana Wodwaladwala Yemwe Anali ndi Mafunso Ambiri

N’tabadwa mu 1920 ku Ierápetra, Crete, bambo anga anamwalira ndi chibayo patangotha zaka ziŵiri. Mayi anali osauka ndiponso osadziŵa kulemba ndi kuŵerenga. Mwa ana awo anayi, wam’ng’ono kwambiri ndinali ine. Popeza ndinadwala matenda a chikasu, ndinali wonyentchera, ndipo ndinkadwaladwala. Anthu omwe tinkakhala moyandikana nawo ankauza mayi kuti azigwiritsa ntchito zochepa zomwe amapeza kusamalira kwambiri ana athanzi enawo ndipo ine andisiye kuti ndimwalire. Ndimathokoza kwambiri kuti sanatsatire malangizo amenewo.

Pofuna kuonetsetsa kuti mzimu wa bambo ukuusa mumtendere kumwamba, Mayi ankapita kumanda kaŵirikaŵiri kukapemphera. Nthaŵi zambiri ankauza wansembe watchalitchi cha Orthodox kuti awapempherere. Komabe, mapempherowo sanali aulere. Ndimakumbukirabe zomwe zinachitika tsiku lina la Khirisimasi lomwe kunazizira kwambiri. Mayi anali kundikhwekhwereza pochokera kumanda komwe anali atapereka kwa wansembe ndalama zonse zomwe tinali nazo. Titafika kunyumba, Mayi anaphika ndiwo zamasamba kuti anafe tidye, ndipo iwo anapita kuchipinda kukagona osadya chilichonse. Anali otaya mtima kwambiri ndipo misozi inali itayenderera masaya awo onse. Patapita nthaŵi, ndinalimba mtima kupita kwa wansembe kukam’funsa chifukwa chomwe bambo anafera ndiponso chifukwa chomwe mayi osaukawo amalipira wansembeyo. Anachita manyazi kwambiri ndipo anayankha mondinong’oneza, amvekere: “Mulungu anawatenga. Ndizo zimachitika m’moyo. Usadandaule chisoni chako chidzatha.”

Zinali zovuta kwambiri kugwirizanitsa zomwe wansembeyo ananena ndi Pemphero la Ambuye lomwe ndinaphunzira kusukulu. Ndikukumbukirabe mawu oyambirira a m’pemphero limeneli akuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:​9, 10) Ngati Mulungu amafunadi kuti chifuno chake chichitike padziko lapansi, n’chifukwa chiyani timavutika kwambiri chonchi?

Ndinatsala pang’ono kupeza yankho la funso limeneli mu 1929, pamene Emmanuel Lionoudakis, yemwe anali mlaliki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, anabwera kunyumba kwathu. * Mayi atam’funsa Emmanuel chomwe wabwerera, iye sanalankhule kanthu koma anawapatsa mayiwo khadi laumboni. Mayi anandipatsa kuti ndiŵerenge. Popeza ndinali ndi zaka zisanu ndi zinayi zokha, ndinamvamo zochepa chabe m’khadilo. Mayi poganizira kuti mwina wolalikirayo anali wosalankhula, anamuuza kuti: “Pepani kwambiri bambo! Inu simutha kulankhula ndipo inenso sinditha kuŵerenga.” Kenako, anam’lozera khomo mwaulemu kuti atuluke azipita.

Patapita zaka zingapo, ndinapeza mayankho a mafunso anga. Mlongo wanga wamkulu Emmanuel Paterakis analandira kabuku kwa mlaliki wanthaŵi zonse yemweyo kamutu wakuti, Akufa Alikuti?, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. * N’taŵerenga kabukuka, ndinali womasuka maganizo chifukwa ndinazindikira kuti Mulungu sanatenge bambo anga. Ndinazindikiranso kuti anthu amafa chifukwa cha kupanda ungwiro ndipo kuti bambo anga akuyembekeza kudzauka ndi kudzakhala ndi moyo m’dziko lapansi la paradaiso.

“Buku Ili Lakuwononga!”

Choonadi cha m’Baibulo chinatitsegula maso. Tinapeza Baibulo lakale lomwe linali la bambo athu ndipo tinayamba kuliŵerenga. Nthaŵi zambiri tinali kuliŵerenga usiku pogwiritsa ntchito makandulo kwinaku tikuwotha moto. Popeza kuti mkazi ndinalipo ndekha amene ndinali ndi chidwi chophunzira Baibulo, sindinali kuchita nawo zomwe kagulu kakang’ono ka Mboni zachimuna m’deralo kankachita. Nthaŵi zina chifukwa cha zimenezi ndinkaganiza molakwa kuti chipembedzo chimenechi n’cha amuna okhaokha.

Changu cha mlongo wanga pantchito yolalikira chinkandilimbikitsa kwambiri. Pasanapite nthaŵi yaitali, apolisi anayamba kukayikira banja lathu, ndipo anayamba kubwera kunyumba kwathu nthaŵi iliyonse masana ndi usiku womwe kudzafuna Emmanuel ndiponso kudzafufuza mabuku. Ndikukumbukira bwino kwambiri pamene wansembe anabwera kudzatinyengerera kuti tiyambenso kupita ku tchalitchi. Emmanuel atam’sonyeza wansembeyo kuchokera m’Baibulo kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova, iye analanda Baibulolo ndikuligwedeza moopseza pafupi ndi nkhope ya mlongo wangayo, amvekere: “Buku ili lakuwononga!”

Emmanuel atakana kukaloŵa usilikali mu 1940 anamumanga ndipo anamutumiza ku nkhondo m’gulu lakutsogolo la asilikali a ku Albania. Sitinathe kulemberana naye makalata moti tinaganiza kuti anafa. Komabe mosayembekezeka patapita zaka ziŵiri, tinalandira kalata yomwe analemba kuchokera kundende komwe anali. Anali wamoyo ndipo anali bwinobwino. Mwa malemba amene anawatchula m’kalatayo, lemba limodzi silichoka m’maganizo mwanga. Lembali limati: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Tinafunikiradi kwambiri chilimbikitso choterocho!

Emmanuel ali kundende komweko, anapempha abale ena kuti adzacheze nane. Nthaŵi yomweyo tinakonza zoti tizikhala ndi misonkhano yachikristu mobisa m’nyumba yomwe inali pa famu ina kunja kwa tauniyo. Sitinkadziŵa n’komwe kuti anthu ena anali kutiona. Lamlungu lina apolisi okhala ndi mfuti anatizinga. Anatikweza m’galimoto ina yaikulu yachingolongolo ndipo anatigubitsa m’tauni yonseyo. Ndikukumbukirabe phokoso la anthu omwe ankatiseka ndiponso kutinyoza, koma Yehova anatilimbitsa mitima pogwiritsa ntchito mzimu wake.

Kenako, anatisamutsira m’tauni ina komwe anatiika m’ndende. Selo zomwe anatiika zinali zamdima ndiponso zauve kwambiri. Chimbudzi cha m’selo yomwe ndinali ine chinali kachitini ndipo zonyansazo anali kuzitaya kamodzi pa tsiku. Anandilamula kuti ndikhale m’ndendemo kwa miyezi isanu ndi itatu chifukwa ankaganiza kuti ndinali “mphunzitsi” wa gululo. Komabe, mbale wina amene anali m’ndende yomweyo anakonza zoti loya wake akatiimire pa mlandu wathuwo ndipo zinachitikadi moti anatithandiza kutulutsidwa m’ndendemo.

Moyo Watsopano

Emmanuel atatuluka kundende anayamba kuyendera mipingo ya mumzinda wa Athens monga woyang’anira woyendayenda. Ndinasamukira ku Athens komweko mu 1947. Kumeneko, ndinakumana ndi Mboni zambiri, zachimuna ndiponso zachikazi ndi ana omwe. Kenako mu July 1947 ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa kubatizidwa m’madzi. Nthaŵi zambiri ndinkaganizira zodzakhala mmishonale. Choncho, ndinayamba kupita ku sukulu ya Chingelezi imene ankaphunzira madzulo kuti ndizitha kuchilankhula bwino. Mu 1950, ndinayamba upainiya. Mayi anga anabwera kudzakhala nane ndipo nawonso anaphunzira choonadi cha m’Baibulo. Anakhalabe a Mboni za Yehova mpaka pamene anamwalira patatha zaka 34.

M’chaka chomwecho ndinakumana ndi John Marks (Markopoulos) wa ku United States. Iye anali munthu waulemu wake ndiponso wokhwima mwauzimu. John anabadwira kumwera kwa Albania ndipo anakhala wa Mboni za Yehova atasamukira ku United States. Mu 1950 iye anapita ku Girisi kuti akatenge chikalata choyendera cha visa kuti apite ku Albania. Panthaŵiyo anthu a m’mayiko ena sanali kuwalola kuloŵa m’dzikolo chifukwa cha ulamuliro wankhanza wa Chikomyunizimu. Ngakhale kuti John anali asanaone abale ake kuchokera mu 1936, iye sanamulole kuloŵa m’dziko la Albania. Ndinakopeka kwambiri ndi changu chake potumikira Yehova ndiponso kukonda kwake abale kwambiri. Choncho, tinakwatirana pa April 3, 1953. Kenako, ndinanyamuka naye kupita kunyumba yathu yatsopano ku New Jersey, U.S.A.

Pofuna kupeza zofunika pa moyo wathu kwinaku tikulalikira nthaŵi zonse, John ndi ine tinali kuchita kabizinesi kophikira mfisulo asodzi a nsomba m’mphepete mwa nyanja ya ku New Jersey. Tinkachita zimenezi m’nyengo yachilimwe yokha. Tinkayamba ntchitoyo mbandakucha mpaka m’ma 9 koloko m’mawa. Tinkathera nthaŵi yathu yochuluka pa ntchito yolalikira chifukwa tinali kukhala moyo wosalira zambiri ndiponso tinkaika zinthu zauzimu patsogolo. Kwa zaka zambiri, anali kutipempha kusamukira ku matauni osiyanasiyana komwe kunkafunika olalikira ambiri. Kumeneko mothandizidwa ndi Yehova, tinathandiza anthu achidwi, kukhazikitsa mipingo, ndiponso kuthandiza kumanga Nyumba za Ufumu.

Kuthandiza Abale Athu Osoŵa

Komabe, pasanapite nthaŵi yaitali, mwayi wosangalatsa kwambiri unatitsegukira. Abale amaudindo anaganiza zokhazikitsa njira yolankhulirana ndi abale a m’mayiko a m’chigawo cha Balkan komwe ntchito yathu inali yoletsedwa. Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova m’mayiko ameneŵa sanali kuzilola kuonana kapena kulankhulana ndi Mboni za m’mayiko ena. Zinali kulandira chakudya chauzimu chochepa kwambiri mwinanso osalandira n’komwe ndiponso zinali kutsutsidwa kwadzaoneni. Mboni zambiri ankazilondalonda nthaŵi zonse ndipo zina anaziika m’ndende kapena m’misasa yachibalo. Zinkafunikiradi mabuku ofotokoza Baibulo, malangizo, ndiponso chilimbikitso chamwamsanga. Mwachitsanzo, uthenga wolembedwa mobisa womwe unachokera ku Albania unanena kuti: “Tipempherereni kwa Ambuye. M’nyumba zonse atilanda mabuku. Sakutilola kuŵerenga. Amuna atatu awamanga.”

Choncho, mu November 1960, tinayamba ulendo wamiyezi isanu ndi umodzi woyendera ena mwa mayiko ameneŵa. Zinali zodziŵikiratu kuti tinafunikira “mphamvu zoposa za chibadwa,” kulimba mtima komwe Mulungu amapereka, ndiponso luntha, kuti tikakwaniritse ntchito yomwe tinapitira. (2 Akorinto 4:​7, NW) Dziko lathu loyamba kuyendera linali Albania. Tinagula galimoto ku Paris ndikuyamba ulendo wathu. Titafika ku Rome, John yekha ndiye anamulola kutenga chikalata cha visa choloŵera m’dziko la Albania. Zitatero, ine ndinapita mumzinda wa Athens, ku Girisi, kukayembekeza mwamuna wanga.

John analoŵa m’dziko la Albania kumapeto kwa mwezi wa February, 1961 ndipo anakhala m’dzikolo mpaka kumapeto kwa March. Ali mumzinda wa Tiranë, John anakumana ndi abale okwana 30. Analitu okondwa kwambiri kulandira mabuku ndiponso chilimbikitso zomwe ankazifuna kwambiri. Anali asanalandirepo mbale wodzawachezera wochokera kunja kwa dzikolo kwa zaka 24.

John analimbikitsidwa kwambiri ndi kukhulupirika ndiponso kupirira kwa abalewo. Anamuuza kuti ambiri mwa abalewo anawachotsa ntchito ndiponso kuwamanga chifukwa chokana kutenga nawo mbali m’zochitika za dziko la Chikomyunizimulo. Anachita chidwi kwambiri makamaka pamene abale aŵiri a zaka za m’ma 80 anapereka chopereka cha ndalama pafupifupi madola 100 (U.S) zothandizira ntchito yolalikira. Ndalamazi zinali za penshoni yawo yochepa yomwe boma linawapatsa ndipo ankazisunga ku banki.

Tsiku lomwe John anamaliza kucheza ku Albania linali March 30, 1961. Tsikuli linali la Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Pamwambowo panafika anthu 37 ndipo John ndiye anakamba nkhani ya Chikumbutsocho. Nkhaniyo itatha, abale mwamsanga anauza John kuti atulukire khomo lakuseri ndipo anamuthaŵitsa pagalimoto kupita ku doko la Durrës. Kumeneko, anakwera sitima yapamadzi ya wamalonda wina wa ku Turkey kupita ku Piraiévs (Piraeus), m’dziko la Girisi.

Ndinali wosangalala kwambiri kumuona atabwerako bwinobwino. Kenako tinapitiriza ulendo wathu woopsawo kupita m’mayiko ena otsala. Tinapita m’mayiko ena atatu a m’chigawo cha Balkan komwe ntchito yathu inali yoletsedwa. Popeza tinanyamula mabuku ofotokoza Baibulo, tayipi, ndiponso katundu wina, kupita m’mayiko ameneŵa kunali kuika moyo pachiswe. Tinali ndi mwayi wapadera chifukwa tinkakumana ndi abale ndi alongo ena okhulupirika kwambiri amene anali okonzeka kuchotsedwa ntchito, kutaya ufulu wawo, ngakhale kulolera kufa kumene chifukwa cha Yehova. Changu chawo ndiponso chikondi chawo chenicheni chinkatilimbikitsa kwambiri. Yehova anatipatsanso “mphamvu yoposa yachibadwa” ndipo zimenezi zinatilimbikitsanso kwambiri.

Titamaliza bwinobwino ulendo wathu, tinabwerera ku United States. Zaka zotsatira, tinapitirizabe kutumizira abale athu a ku Albania mabuku ndiponso kulandira malipoti a ntchito yawo, pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana.

Kuyenda Maulendo Kaŵirikaŵiri, Ndiponso Kukumana ndi Zoopsa

Patapita zaka, John anamwalira mu 1981 ali ndi zaka 76, ndipo ndinatsala ndekha. Mwana wa mkulu wanga dzina lake Evangelia pamodzi ndi mwamuna wake George Orphanides mokoma mtima ananditenga ndipo akhala akundilimbikitsa ndiponso kundithandiza mpaka lero. Iwonso aona Yehova akuwathandiza pamene anali kutumikira ku Sudan panthaŵi yomwe ntchito yathu inali yoletsedwa m’dzikolo. *

M’kupita kwanthaŵi, njira yatsopano yolankhulirana ndi abale a ku Albania inakonzedwa. Popeza kuti abale a mwamuna wanga anali ku Albania, anandipempha ngati ndingakonde kupita m’dzikolo. Ndinavomera ndi mtima wonse.

M’May 1986, chifukwa cha khama, ndinatenga chikalata choyendera cha visa kuchokera ku ofesi ya kazembe wa dziko la Albania yomwe inali ku Athens. Ogwira ntchito muofesi ya kazembeyo anandichenjeza mosapita m’mbali kuti, ngati nditakakumana ndi mavuto ku Albania ndisakayembekeze kuti maofesi a akazembe a mayiko ena akandithandiza ayi. Anthu anadabwa kwambiri nditapita ku kampani ina ya zaulendo kukagula tikiti ya ndege yopita ku Albania. Sindinalole mantha kulepheretsa ulendo wanga moti ndinakwera ndege yomwe imachoka mumzinda wa Athens kupita mumzinda wa Tiranë kamodzi pa mlungu. M’ndegeyo munali anthu a ku Albania atatu okha omwe anali okalamba kwambiri. Iwo anapita ku Girisi kukalandira chithandizo chamankhwala.

Ndegeyo itangotera ku Albania, anandiloŵetsa m’chipinda chomwe ankachitiramo kasitomu. Mlamu wanga wamwamuna ndiponso wamkazi, ngakhale kuti si Mboni, anandithandiza kukumana ndi abale a m’deralo. Malinga ndi lamulo lakumeneko, abale angawo anayenera kudziŵitsa mfumu ya m’deralo kuti ndabwera. Chifukwa cha zimenezo, apolisi anali kuonetsetsa kwambiri zomwe ndinkachita. Choncho, abale angawo anaganiza kuti ineyo ndizingokhala panyumba ndipo iwowo ndiwo azikafunafuna abale aŵiri omwe ankakhala m’tauni ya Tiranë ndi kubwera nawo.

Panthaŵiyo n’kuti m’dziko la Albania muli Mboni zodzipatulira zodziŵika zisanu ndi zinayi zokha basi. Mavuto monga, kuletsedwa kwa ntchito yathu kwanthaŵi yaitali, chizunzo, ndiponso kulondedwa nthaŵi zonse, kunachititsa Mbonizo kukhala zosamala kwambiri pochita zinthu. Nkhope zawo zinali ndi masinya akuluakulu. Nditawatsimikizira abalewo kuti ndine Mboni, funso loyamba lomwe anandifunsa linali lakuti: “Magazini a Nsanja ya Olonda ali kuti?” Kwa zaka zambiri Mboni za ku Albania zinali ndi mabuku akale aŵiri okha basi ndipo zinalibe ngakhale ndi Baibulo lomwe.

Abalewo anasimba kwambiri nkhani zokhudza nkhanza zomwe boma linkawachitira. Anatchula zomwe zinachitikira mbale wina yemwe anakana kwamtuwagalu kuloŵerera m’nkhani za ndale panthaŵi ya chisankho chomwe chinali kuyandikira. Popeza kuti boma ndilo linkalamulira chilichonse, kukana kwakeko kukanachititsa kuti banja lake lisalandire chakudya. Ana ake okwatira ndiponso okwatiwa pamodzi ndi mabanja awo akanamangidwa ngakhale kuti sanali a Mboni. Chifukwa cha mantha, akuti banja la mbaleyu linamupha n’kuponya mtembo wake m’chitsime, ndipo kenako n’kumanena kuti anadzipha yekha chifukwa cha mantha.

Umphaŵi wa Akristu anzathu amenewo unali womvetsa chisoni kwambiri. Komabe, n’tawapatsa aliyense ndalama zokwana madola 20, iwo anakana amvekere: “Tikufuna chakudya chauzimu chokha basi.” Abale athu apamtima ameneŵa anakhala zaka zambiri mu ulamuliro wankhanza umene unakwanitsa kuphunzitsa anthu ambiri kukhala okana Mulungu. Komabe chikhulupiriro chawo chinali cholimba kwambiri ndiponso anatsimikiza mtima monga momwe Mboni zachitira m’mayiko ena. Yehova amapereka “mphamvu yoposa yachibadwa” ngakhale panthaŵi yovuta kwambiri ndipo zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri panthaŵi yomwe ndinali ku Albania ndisanachoke pambuyo pa milungu iŵiri.

Ndinalinso ndi mwayi wopita ku Albania mu 1989 ndiponso mu 1991. Olambira Yehova anawonjezeka mofulumira kwambiri pamene ufulu wa kulankhula ndiponso wachipembedzo zinafika m’dzikolo. Kuchokera pa Akristu odzipatulira oŵerengeka omwe analipo mu 1986 tsopano ofalitsa achangu achuluka kupitirira pa 2, 200. Mwa ofalitsa oyambirirawo panali Melpo yemwe ndi mlamu wanga wamkazi. Kodi tingakayikire kuti Yehova anali kudalitsa gulu lokhulupirika limenelo?

Kukhala ndi Moyo Wokhutiritsa Chifukwa cha Mphamvu ya Yehova

Ndikamaganiza za mmbuyo, ndimatsimikiza kuti ntchito ya John ndiponso yanga sinapite pachabe. Tinagwiritsa ntchito mphamvu za unyamata wathu m’njira yopindulitsa kwambiri. Ntchito yathu ya utumiki wanthaŵi zonse yakhala yopindulitsa kwambiri kuposa ntchito ina iliyonse yomwe tikanagwira. Ndimasangalala kwambiri ndi anzanga apamtima ambiri amene tinawathandiza kuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Popeza tsopano ndakalamba, nditha kulimbikitsa achinyamata ndi mtima wonse kuti ‘akumbukirenso Mlengi wawo masiku a unyamata wawo.”​—Mlaliki 12:1.

Ngakhale kuti tsopano ndili ndi zaka 81, ndikutumikirabe monga wofalitsa wanthaŵi zonse wa uthenga wabwino. Ndimadzuka m’mamaŵa kukalalikira mmalo okwerera mabasi, m’malo oimika magalimoto, m’misewu, m’masitolo, kapena m’mapaki. Ndikuvutika kwambiri tsopano chifukwa cha ukalamba. Komabe, abale ndi alongo anga okondedwa auzimu ndiponso banja la mwana wa mkulu wanga andithandiza kwambiri. Koposa zonse ndazindikira kuti, “mphamvu yoposa yachibadwa [ndi] ya Mulungu ndipo osati yochokera mwa ife eni.”​—2 Akorinto 4:7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Kuti mumve nkhani yosimba za moyo wa Emmanuel Lionoudakis, onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1999, masamba 25-9.

^ ndime 11 Kuti mumve nkhani yosimba za Moyo wa Emmanuel Paterakis, onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1996, masamba 22-7.

^ ndime 31 Onani Yearbook ya Mboni za Yehova ya 1992 masamba 91-2, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 25]

Pamwambapa: John (kumanzere), ine (pakati), mlongo wanga Emmanuel kumanzere kwanga, mayi athu kumanzere kwa John, ndipo enawo ndi a pa Beteli ku Athens, mu 1950

[Chithunzi patsamba 25]

Kumanzere: Ndili ndi John pa malo athu a bizinesi m’mphepete mwa nyanja ya ku New Jersey, mu 1956

[Chithunzi patsamba 26]

Msonkhano wachigawo ku Tiranë, Albania, mu 1995

[Chithunzi patsamba 26]

Beteli ya ku Tiranë, Albania, yomwe inatha kumangidwa mu 1996

[Chithunzi patsamba 26]

Pamwamba: Nkhani ya mu “Nsanja ya Olonda” ya 1940 imene inatembenuzidwa mwachinsinsi kupita m’chinenero cha chi Alubaniya

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili ndi mwana wa mkulu wanga Evangelia Orphanides (kumanja) ndi mwamuna wake, George