Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomwe Mfumu Henry VIII Inachita Zokhudza Baibulo

Zomwe Mfumu Henry VIII Inachita Zokhudza Baibulo

Zomwe Mfumu Henry VIII Inachita Zokhudza Baibulo

WINSTON CHURCHILL m’buku lake lakuti History of the English-Speaking Peoples (Voliyumu 2), analemba kuti: “Gulu lachipembedzo lomwe linayambitsa matchalitchi achipulotesitanti linasintha zinthu kwambiri pankhani za chipembedzo. Baibulo linayamba kukhala ndi mphamvu kwambiri kwa anthu m’madera ambiri. Anthu a kalewo ankaganiza kuti n’zoopsa kuti anthu osaphunzira azikhala ndi Baibulo ndipo ankati ansembe okha ndiwo ayenera kuŵerenga Malemba Opatulikaŵa.”

Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Mabaibulo athunthu a Chingelezi omwe Tyndale ndi Coverdale anamasulira anayamba kutuluka kwa nthaŵi yoyamba kumapeto kwa m’ma 1535. Ndipo kuchokera panthaŵiyo, mabaibulo ena ambiri anayamba kupangidwa. Boma linalangiza atsogoleri amatchalitchi kuti azilimbikitsa anthu awo kuŵerenga Baibulo.” Choncho, anthu a ku England anayamba kudziŵa Baibulo patatha zaka mazana ambiri ali mu umbuli wosadziŵa Baibulo. Komabe, zimenezi zinachitika chifukwa cha boma la mfumu Henry VIII osati matchalitchi ayi. *

“Chochititsa manyazi chinanso kwa anthu akalewo omwe ankatsatira zochita ndi maganizo oletsa kuŵerenga Baibulo n’chakuti, Boma linalamula ku Paris kuti mabaibulo ambiri a Chingelezi awasindikize ndipo kuti mabaibulowo akhale apamwamba kwambiri kuposa omwe anawasindikiza kale. Ndipo mu September 1538, Bomalo linalamula kuti tchalitchi chilichonse chachikulu chigule Baibulo lalikulu la Chingelezi lomwe lizikhala m’tchalitchimo kuti anthu onse pa tchalitchilo azitha kuligwiritsa ntchito ndiponso kuliŵerenga. Mabaibulo okwana asanu ndi limodzi anawaika m’tchalitchi chachikulu cha St Paul, mumzinda wa London. Anthu ambirimbiri anali kusonkhana ku tchalitchilo tsiku lonse kuti aŵerenge ma Baibulowo. Ndipo akuti anthuwo ankati akapeza munthu wina wa mawu amphamvu anali kumuuza kuti aziŵerenga mokweza.”

N’zachisoni kuti anthu ambiri m’mayiko ochuluka sagwiritsa ntchito mwayi womwe ali nawo kuti aziŵerenga Baibulo nthaŵi ndi nthaŵi. Zimenezi n’zodandaulitsa kwambiri chifukwa chakuti Baibulo ndilo buku lokha lomwe ‘adaliuzira Mulungu, ndipo limapindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’​—2 Timoteo 3:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mfumu Henry VIII inalamulira dziko la England kuchokera mu 1509 mpaka mu 1547.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Henry VIII: Chithunzi chomwe chili mu Royal Gallery ku Kensington, kuchokera m’buku lakuti The History of Protestantism (Vol. I)