Aphunzitsi a Mawu a Mulungu Analimbikitsidwa Kukwaniritsa Ntchito Yawo
Aphunzitsi a Mawu a Mulungu Analimbikitsidwa Kukwaniritsa Ntchito Yawo
APHUNZITSI miyandamiyanda anasonkhana kuti alandire malangizo m’miyezi yapitayi. Kuyambira m’mwezi wa May chaka chathachi, iwo anasonkhana pa Misonkhano ya Chigawo mazanamazana ya Mboni za Yehova pa dziko lonse. Mutu wa misonkhanoyi unali wakuti, “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.” Nthumwi zinalimbikitsidwa kudziphunzitsa kaye zokha, kuti zikhale zoyenerera kukwaniritsa ntchito yawo yophunzitsa.
Kodi inuyo munalipo pa umodzi mwa misonkhanoyi? Ngati munalipo, ndiye kuti mosakayika munayamikira kwambiri chakudya chabwino chauzimu chomwe chinaperekedwa pa misonkhanoyi yomwe cholinga chake ndicho kulambira Mulungu woona, Yehova. Tiyeni tsopano tionenso pulogalamu yophunzitsa ya msonkhanowo.
Tsiku Loyamba—Malemba Ouziridwa Apindulitsa Pophunzitsa
Tcheyamani wa msonkhano analandira nthumwi zonse ndi manja aŵiri ndi nkhani yakuti, “Landirani Malangizo, Inu Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.” Yesu anakhala Mphunzitsi Wamkulu chifukwa anaphunzira kwa “Mlangizi Wamkulu”, Yehova. (Yesaya 30:20; Mateyu 19:16) Ngati ifenso tikufuna kupita patsogolo monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu, tiyenera kuphunzitsidwa ndi Yehova.
Nkhani yotsatira inali yakuti, “Kuphunzitsa za Ufumu Kumabala Zipatso Zabwino.” Phindu ndiponso chimwemwe zomwe zimapezeka pa ntchito yopanga ophunzira zinagogomezedwa mwa kufunsa aphunzitsi a Mawu a Mulungu omwe akhala nthaŵi yaitali akugwira ntchitoyi.
Nkhani yotsatira ya mutu wakuti “Talimbikitsidwa Machitidwe 2:11, NW) Ifenso tingasonkhezere anthu kuchitapo kanthu mwa kulalikira “zinthu zazikulu” zoterozo monga ziphunzitso za m’Malemba zokhudza dipo, chiukiriro, ndiponso pangano latsopano.
ndi Zinthu ‘Zazikulu za Mulungu’” inali yolimbikitsa kwambiri. M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino “zinthu zazikulu” zokhudza Ufumu wa Mulungu zinasonkhezera anthu kuchitapo kanthu. (Nkhani yotsatira yakuti “Sangalalani ndi Chilungamo cha Yehova,” inalimbikitsa onse kusangalala ndi chilungamo cha Yehova. (Salmo 35:27) Timalimbikitsidwa kulondola chilungamo mwa kuphunzira kukonda chimene chili cholungama ndi kudana ndi choipa, kuphunzira Baibulo, kukana kwamtuwagalu zinthu zowononga mwauzimu, ndiponso kukhala odzichepetsa. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kupeŵa mayanjano oipa, mzimu wadziko wokondetsa zinthu zakuthupi, komanso zosangalatsa zosayenera ndiponso zachiwawa.
Nkhani yaikulu yamutu wakuti “Okonzeka Mokwanira Kukhala Aphunzitsi a Mawu a Mulungu,” inatikumbutsa kuti Yehova amatipanga kukhala atumiki oyenerera pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake woyera, ndiponso gulu lake la padziko lapansi. Pa mfundo yogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, wokamba nkhaniyi anatilangiza kuti: “Cholinga chathu ndicho kutenga uthenga wa m’Baibulo kuchokera m’masamba a Baibulo n’kuukhomereza m’mitima ya omvetsera athu.”
Nkhani yoyamba yosiyirana ya msonkhanowu inali ndi mutu wakuti, “Kudziphunzitsa Tokha Pamene Tikuphunzitsa Ena.” Mbali yoyamba inagogomeza kuti tizitsatira miyezo yapamwamba yamakhalidwe achikristu yomwe timaphunzitsa anthu ena. Mbali yotsatira, inatilangiza ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:15) Kaya tatumikira Mulungu kwa nthaŵi yaitali bwanji kuchita phunziro la Baibulo laumwini nthaŵi zonse n’kofunika kwambiri kuti tidziphunzitse. Mbali yomaliza ya nkhani yosiyiranayi, inasonyeza kuti Mdyerekezi akutiona, ndipo akufunafuna amene ali ndi mtima wonyada, mzimu wofuna kudziimira, kudziona ngati wofunika, nsanje, njiru, mkwiyo, chidani, ndiponso kupeza ena zifukwa. Komabe, ngati titamukaniza mwamphamvu Mdyerekezi, adzatithaŵa. Koma kuti timukanize, tifunika kuyandikira kwa Mulungu.—Yakobo 4:7, 8.
Nkhani yapanthaŵi yake yakuti “Danani ndi Habakuku 1:13) Tiyenera ‘kudana nacho choipa.’ (Aroma 12:9) Makolo analangizidwa kuyang’anira zomwe ana awo akuonera pa Intaneti ndiponso pa wailesi yakanema. Wokamba nkhaniyi ananena kuti amene akopeka kuonerera zolaula ayenera kupeza thandizo kwa anzawo okhwima mwauzimu. Zidzakhalanso zothandiza kwambiri kuloweza pamtima ndiponso kusinkhasinkha malemba monga awa, Salmo 97:10; Mateyu 5:28; 1 Akorinto 9:27; Aefeso 5:3, 12; Akolose 3:5; ndiponso 1 Atesalonika 4:4, 5.
Mliri wa Dziko wa Nkhani Zolaula,” inatisonyeza mmene tingapeŵere nkhani zowononga khalidwe lauzimu zimenezi. Mneneri Habakuku ananena za Yehova kuti: “Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta.” (Nkhani yotsatira yakuti “Mtendere wa Mulungu Ukusungeni,” inatilimbikitsa kuti pamene nkhaŵa zatifoola tingathe kum’senzetsa Yehova nkhaŵa zathuzo. (Salmo 55:22) Ngati titamuuza Yehova momasuka m’pemphero, iye adzatipatsa “mtendere wa Mulungu,” womwe ndi mtendere wamumtima umene umadza chifukwa cha ubale wamtengo wapatali ndi iye.—Afilipi 4:6, 7.
Tsiku loyamba linatha ndi nkhani yosangalatsa kwambiri yakuti “Yehova Akometsa Anthu Ake ndi Kuunika.” Nkhaniyi inafotokoza za kukwaniritsidwa kwa lemba la Yesaya chaputala 60. M’kati mwa mdima wamakono wa dzikoli, “alendo” omwe ndi khamu lalikulu la anthu onga nkhosa, akusangalala ndi kuunika kwa Yehova pamodzi ndi Akristu odzozedwa. Pokambapo za mavesi 19 ndi 20, wokamba nkhaniyi anati: “Yehova ‘sadzaloŵa’ monga limachitira dzuŵa kapena ‘kupita kumidima’ monga umachitira mwezi. Iye adzapitirizabe kukometsa anthu ake mwa kuwaunikira. Amenewotu ndi mawu okhazika mtima pansi kwambiri kwa ife pamene tikukhala m’masiku otsiriza a dziko lamdimali.” Kumapeto kwa nkhaniyi, wokambayo analengeza kutulutsidwa kwa buku lakuti, Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse, Gawo 2. Kodi mwamaliza kuŵerenga buku latsopano limeneli?
Tsiku lachiŵiri—Okhoza Kuphunzitsa Bwino Ena
Itatha nkhani yokambirana lemba la tsikuli, tinamvetsera mwatcheru nkhani yachiŵiri yosiyirana yakuti, “Atumiki Amene Kudzera Mwa Iwo Ena Amakhala Okhulupirira.” Okamba nkhani yosiyirana ya mbali zitatuyi, anagogomeza masitepe atatu ofunika pothandiza anthu kuti akhale okhulupirira. Masitepe ake ndiwo aŵa: kulalikira uthenga wa Ufumu, kukulitsa chidwi chomwe anthu anasonyeza, ndiponso kuwaphunzitsa anthuwo kuti asunge zinthu zomwe Kristu analamulira. Anthu omwe anafunsidwa kulongosola zomwe zawachitikira, anatithandiza makamaka kuona mmene tingaphunzitsire anthu kuti akhale ophunzira.
Nkhani yotsatira inali ya mutu wakuti “Wonjezerani Kudzipereka Kwaumulungu pa Chipiriro Chanu.” Wokamba nkhaniyi anati, chomwe chili chofunika kwambiri ndicho ‘kupirira kufikira kuchimaliziro.’ (Mateyu 24:13) Tifunika kugwiritsa ntchito zonse zomwe Mulungu akupereka kuti zitithandize kukulitsa kudzipereka kwaumulungu. Zimenezi ndi zinthu monga, pemphero, phunziro la umwini, misonkhano, ndiponso kulalikira. Tifunika kupeŵa zilakolako ndi zochitika za dzikoli kuti zisawononge kudzipereka kwathu kwaumulungu.
Kodi anthu olema ndi othodwa angapeze bwanji mpumulo masiku ano? Nkhani yakuti “Kupeza Mpumulo M’goli la Kristu,” inayankha funso limeneli. Yesu mokoma mtima anapempha otsatira ake kuti aloŵe m’goli lake ndiponso kuphunzira kwa iye. (Mateyu 11:28-30) Titha kuloŵa m’goli la Yesu mwa kutsanzira chitsanzo chake chokhala ndi moyo wosalira zambiri. Mfundo yaikulu ya nkhaniyi inagogomezedwa mwa kufunsa anthu amene akukhala moyo wosalira zambiri.
Chimodzi mwa zochitika zikuluzikulu pa misonkhano yaikulu ya Mboni za Yehova ndi ubatizo wa atumiki a Mulungu omwe adzipatulira kumene. Mbale amene anakamba nkhani ya ubatizo yakuti “Ubatizo Umatsegula Mipata Yaikulu Yophunzitsa,” analandira ndi manja aŵiri anthu onse opita ku ubatizo ndipo anawapempha kuchita nawo utumiki wapadera umenewu. Aphunzitsi a Mawu a Mulungu obatizidwa kumenewo atha kukalamira maudindo osiyanasiyana malinga atakwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba.
“Tsanzirani Mphunzitsi Wamkulu,” ndiwo unali mutu wa nkhani yoyamba masana a tsikulo. Yesu anakhala Mphunzitsi Wamkulu chifukwa chakuti kwa zaka zosaŵerengeka zomwe anakhala kumwamba, ankaonetsetsa ndiponso kutsanzira Atate wake. Ali pano padziko lapansi, ankagwiritsa ntchito njira zophunzitsira zogwira mtima monga, mafunso okhudza mtima, ndiponso mafanizo osavuta kumva koma ochititsa chidwi. Zomwe Yesu anali kuphunzitsa zinali zochokera m’Mawu a Mulungu ndipo anali kuzilankhula mwamphamvu, ndiponso mwachikoka. Kodi sitinakopeke kutsanzira Mphunzitsi Wamkulu ameneyu?
Nkhani ina yosonkhezera yakuti “Kodi Ndinu Wofunitsitsa Kutumikira Ena?,” inatilimbikitsa kutsanzira chitsanzo cha Yesu potumikira ena. (Yohane 13:12-15) Wokamba nkhaniyi analimbikitsa mwachindunji amuna oyenerera kuti azikhala ngati Timoteo pogwiritsa ntchito mipata imene ilipo kuthandiza anthu ena. (Afilipi 2:20, 21) Makolo analimbikitsidwa kutsanzira chitsanzo cha Elikana ndi Hana pothandiza ana awo kuchita utumiki wa nthaŵi zonse. Ndipo achinyamata analangizidwa kutsanzira zitsanzo za Yesu Kristu ndiponso wachinyamata Timoteo mwa kutumikira ndi mtima wonse. (1 Petro 2:21) Tinalimbikitsidwanso kwambiri ndi zomwe analankhula omwe agwiritsa ntchito mwayi wotumikira ena.
Mutu wankhani yachitatu yosiyirana unali wakuti “Pindulani Mokwanira ndi Maphunziro Ateokalase.” Wokamba woyamba anagogomeza kufunika kokulitsa nthaŵi yomwe timakhala ndi chidwi chomvetsera. Kuti tichite zimenezo, titha kuyesera kaye kutero panthaŵi ya phunziro lathu laumwini lalifupi kenako n’kuyesa kulitalikitsa. Wokambayo analimbikitsanso omvera kuŵerenga Malemba ndiponso kulemba notsi pa misonkhano. Wokamba wachiŵiri anatiuza kufunika kogwiritsitsa “mawu a moyo.” (2 Timoteo 1:13, 14) Kuti tidziteteze ku nkhani zosayenera za m’zoulutsira nkhani, mafilosofi a anthu, maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo, ndiponso ziphunzitso za mpatuko, tiyenera kupatula nthaŵi yochita phunziro laumwini ndiponso kupezeka pa misonkhano. (Aefeso 5:15, 16) Wokamba womaliza wa nkhani yosiyiranayi anagogomeza kufunika kochita zomwe tinaphunzira kuti tipindule mokwanira ndi maphunziro ateokalase.—Afilipi 4:9.
Tinali osangalala kwambiri kumvetsera nkhani yakuti “Zinthu Zatsopano Zothandiza Kuti Tipite Patsogolo Mwauzimu.” Tinakondwa kwambiri kumva kuti buku latsopano lakuti Benefit From Theocratic Ministry School Education lidzatulutsidwa posachedwapa. Pamene wokamba nkhaniyi anali kufotokoza zomwe zili m’bukuli, chilakolako chofuna kulilandira chinakula kwambiri. Ponenapo za chigawo cha bukuli chomwe chili
ndi mauphungu akulankhula, wokambayo anati: “Buku lophunzira latsopanoli sanalilembe ngati buku la kumasukulu a kudziko. Mfundo 53 za kuŵerenga bwino, kulankhula bwino, ndi kuphunzitsa bwino azifotokoza mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba.” Bukuli lidzasonyeza mmene aneneri, Yesu, ndiponso ophunzira ake, anasonyezera maluso abwino a kuphunzitsa. Inde, buku lophunzira limeneli ndiponso zinthu zatsopano za m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zidzatithandiza kukhala aphunzitsi abwino a Mawu a Mulungu.Tsiku Lachitatu—Khalani Aphunzitsi Chifukwa cha Nyengoyi
Itatha nkhani yokambirana lemba la tsiku lomalizali, onse anamvetsera mwachidwi nkhani yosiyirana yomaliza ya msonkhanowu yakuti, “Ulosi wa Malaki Ukutikonzekeretsa Tsiku la Yehova.” Malaki analosera zimenezi pafupifupi zaka 100 Ayuda atabwerako ku Babulo. Iwo anali ataloŵereranso kutsatira mpatuko ndi kuchita zoipa, komanso kuchitira chipongwe dzina la Yehova mwa kunyalanyaza malamulo ake olungama ndi kupereka nsembe nyama zakhungu, zopunduka, ndi zodwala. Komanso, iwo anali kusudzula akazi a paubwana wawo mwina chifukwa chofuna kukwatira akazi achikunja.
Chaputala choyamba cha Malaki chimatitsimikizira kuti Yehova amakonda anthu ake. Chimagogomeza kufunika koopa kusam’kondweretsa Mulungu komanso kuyamikira zinthu zopatulika. Yehova amayembekezera kuti tizim’patsa zinthu zabwino koposa, kumulambira chifukwa cha chikondi chathu chopanda dyera. Utumiki wathu wopatulika suyenera kungokhala mwambo chabe ayi, tiyenera kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu.
Pogwirizanitsa chaputala chachiŵiri cha Malaki ndi masiku athu ano, wokamba wachiŵiri anafunsa kuti: “Kodi ife aliyense payekha ndife atcheru kuti ‘chosalungama chisapezeke m’milomo yathu?” (Malaki 2:6) Amene akutsogolera pa ntchito yophunzitsa ayenera kuonetsetsa kuti zomwe akulankhula n’zochokeradi m’Mawu a Mulungu. Tiyenera kudana ndi chinyengo monga kusudzula kosayenera.—Malaki 2:14-16.
Pa nkhani yakuti “Ndani Adzapulumuka Tsiku la Yehova,” wokamba womaliza wa nkhani yosiyiranayi anatithandiza kukonzekera tsiku la Yehova. Wokamba anafuula kuti: “N’kolimbikitsa kwambiri kwa atumiki a Yehova kudziŵa kuti Malaki chaputala 3, vesi 17, akukwaniritsidwa makamaka kwa iwo! Lembali limati: ‘“Ndipo adzakhala anga anga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.”’”
Chochitika china chachikulu pa msonkhano
wachigawo chinali Seŵero la m’nthaŵi zakale la mutu wakuti “Lemekezani Ulamuliro wa Yehova.” Seŵeroli linasonyeza ana a Kora. Ngakhale kuti atate awo anali ndi mtima wopandukira Mose ndi Aroni, anawo anakhalabe okhulupirika kwa Yehova ndiponso kwa omuimira ake. Ana a Kora anapulumuka pamene Kora ndi om’tsatira ake anatha psiti. Nkhani yotsatira yakuti “Gonjerani Ulamuliro wa Mulungu Mokhulupirika,” inafotokoza mmene mfundo za m’Seŵero tingazigwiritsire ntchito pa moyo wa aliyense wa ife. Wokamba nkhaniyo anachenjeza mbali zisanu ndi imodzi zomwe Kora ndi om’tsatira ake anali ofooka: Sanali kuchirikiza ulamuliro wa Yehova mokhulupirika; anali odzikuza, onyada, ndipo nsanje inakula kwambiri mwa iwo. Analinso kungoyang’ana zophophonya za anthu amene Yehova anawasankha; anakulitsa mtima wodandaula; anali osakhutira ndi maudindo amene anali nawo; ndiponso analola kuti chibale kapena banja likhale lofunika kwambiri kuposa kukhala wokhulupirika kwa Yehova.Nkhani ya onse inali ndi mutu wakuti “Kodi Ndani Amene Akuphunzitsa Mitundu Yonse Choonadi?” Choonadi chomwe nkhaniyi inatchula si choonadi wamba, koma choonadi chokhudza chifuno cha Yehova chomwe Yesu Kristu ankachitira umboni. Wokamba nkhaniyi anatchulapo za choonadi chokhudza zikhulupiriro, choonadi chokhudza kalambiridwe, ndiponso choonadi chokhudza kulemekeza khalidwe la munthuwe. Poyerekezera Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino ndi Mboni za Yehova lerolino, kutsimikiza mtima kwathu kuti ‘Mulungu alidi ndi ife’ kunali kolimbikitsa kwambiri.—1 Akorinto 14:25.
Litatha phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda la mlungu umenewo, aphunzitsi onse a mawu a Mulungu omwe anafika pa msonkhanowo anasonkhezeredwa kwambiri kuchitapo kanthu atamva nkhani yomaliza yakuti “Kugwira Mwachangu Ntchito Yathu Yophunzitsa.” Kubwereramo kwachidule kwa pulogalamuyi kunagogomeza kufunika kogwiritsa ntchito Malemba pophunzitsa, kugwiritsa ntchito njira zomwe zingatichititse kukonzeka mokwanira kukhala aphunzitsi, ndiponso kufunika kokhala n’chidaliro ndi choonadi chomwe timaphunzitsa ena. Wokamba nkhaniyi anatilangiza kuti tionetsetse kuti ‘kupita patsogolo kwathu kuonekere’ ndiponso kuti ‘tidzipenyerere tokha, ndi chiphunzitsocho.—1 Timoteo 4:15, 16, NW.
Msonkhano Wachigawo wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu,” unalidi phwando lauzimu lokoma kwambiri! Tiyeni titsanzire Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova, ndiponso Mphunzitsi wathu Wamkulu, Yesu Kristu, pophunzitsa ena mawu a Mulungu.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 28]
Zofalitsa Zatsopano Zothandiza Pa Zofunika Zapadera
Nthumwi za ku Msonkhano Wachigawo wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” zinalandira mokondwera zofalitsa ziŵiri zomwe zili zothandiza kwambiri pophunzitsa choonadi cha m’Malemba kwa anthu a m’madera ena a dziko lapansi. Thirakiti la mutu wakuti Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa? lidzakhala chida chothandiza kuyambitsa kukambirana ndi anthu amene amakhala m’mayiko omwe zinenero za kumeneko sizisiyanitsa pakati pa “mzimu” ndi “moyo.” Thirakiti latsopanoli limanena momveka bwino kuti mphamvu ya mzimu n’njosiyana ndi cholengedwa chauzimu ndipo kuti anthu sasanduka zolengedwa zauzimu akamwalira.
Bulosha lakuti Mmene Mungapezere Moyo Wokhutiritsa linatulutsidwa kumapeto kwa tsiku lachiŵiri la msonkhanowo. Bulosha limeneli linakonzedwa n’cholinga choti tiziyambitsira phunziro la Baibulo ndi anthu amene sadziŵa kuti Mlengi ali ndi makhalidwe ndiponso kuti pali buku lomwe iye analiuzira. Kodi mwagwiritsapo ntchito zofalitsa zatsopano zimenezi mu utumiki wanu?
[Zithunzi patsamba 26]
Ku Milan, Italy, ndiponso pa misonkhano ina padziko lonse, anthu mazanamazana anabatizidwa
[Chithunzi patsamba 29]
Anthu omwe anafika pa msonkhanowu anasonkhezeredwa ndi seŵero lakuti “Lemekezani Ulamuliro wa Yehova”