Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khulupirirani Yehova—Mulungu Weniweni

Khulupirirani Yehova—Mulungu Weniweni

Khulupirirani Yehova​—Mulungu Weniweni

Kodi munayang’anapo kumwamba usiku woti kunalibe mitambo n’kuona nyenyezi zambirimbiri? Kodi mukuganiza kuti zinakhalako bwanji?

MOPHIPHIRITSA tinganene kuti nyenyezi usiku wina zinalankhula kwa Mfumu Davide ya Israyeli wakale, zomwe zinam’chititsa kulemba kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” (Salmo 19:1) Inde, Mlengi ndiye woyenera “kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu” osati zinthu zomwe analenga ayi.​—Chivumbulutso 4:11; Aroma 1:25.

Baibulo limati: “Wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Inde, Mulungu weniweni ‘yemwe dzina lake ndi Yehova ndiye Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.’ (Salmo 83:18) Iye si wonyenga, kapena chizimezime chabe ayi. Yesu Kristu ananena za Atate wake wakumwamba Yehova kuti: ‘Iye wondituma Ine ali woona.’​—Yohane 7:28.

Yehova Amakwaniritsa Zolinga Zake

Dzina la Mulungu lapaderali lakuti Yehova, limapezeka ka 7,000 m’Malemba Achihebri mokha. Dzina lokhali limasonyeza kuti iye ndi Mulungu weniweni. Dzina la Mulungu limeneli kwenikweni limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.” Yehova Mulungu amadzidziŵikitsa yekha kuti ndiye Wokwaniritsa zolinga zake. Mose atam’funsa Mulungu dzina lake, Yehova analongosola tanthauzo la dzinalo motere: “Ndidzakhala chimene ndidzakhala.” (Eksodo 3:14, NW) Baibulo la Rotherham limanena motere: “Ndidzakhala chilichonse chimene ndifuna.” Choncho, Yehova amakhala kapena kuti amasankha kukhala chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse zolinga ndi malonjezo ake olungama. Motero, ali ndi mayina aulemu monga aŵa, Mlengi, Atate, Ambuye Mfumu, Mbusa, Yehova wamakamu, Wakumva pemphero, Woweruza, Mlangizi Wamkulu, Mombolo.​—Oweruza 11:27; Salmo 23:1; 65:2; 73:28; 89:26; Yesaya 8:13; 30:20; 40:28; 41:14.

Mulungu woona yekha ndi amene moyenerera angakhale ndi dzina loti Yehova, chifukwa anthu sangatsimikize kuti zomwe akuganiza kudzachita m’tsogolo zidzachitikadi. (Yakobo 4:13, 14) Yehova yekha ndiye anganene kuti: “Monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbewu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:10, 11.

Yehova amatsimikiza motero pokwaniritsa zolinga zake moti ngakhale zinthu zomwe anthu angazione ngati zosatheka, kwa iye n’zotheka. Patapita nthaŵi yaitali Abrahamu, Isake, ndi Yakobo atamwalira, Yesu ananena za anthu ameneŵa kuti: “Iye [Yehova] sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.” (Luka 20:37, 38) Makolo akale atatuwo anali akufa koma cholinga cha Mulungu chowaukitsa chinali chotsimikizika kuti adzachikwaniritsa moti kwa iye anali ngati amoyo. Kuukitsa atumiki okhulupirika amenewo si chinthu chapatali kwa Mulungu poyerekezera ndi mmene zinalili polenga munthu woyamba kuchokera ku dothi la pansi.​—Genesis 2:7.

Mtumwi Paulo anatchula chitsanzo china cha mfundo yakuti Mulungu amakwaniritsadi zolinga zake. M’Malemba, Abrahamu amatchedwa “kholo la mitundu yambiri ya anthu.” (Aroma 4:16, 17) Abramu asanabale mwana aliyense, Yehova anam’sintha dzina kukhala Abrahamu, dzina lomwe limatanthauza “Tate wa khamu la anthu (Namtindi).” Yehova anachititsa kuti tanthauzo la dzinalo likwaniritsidwe mwa kubwezeretsa mozizwitsa mphamvu zoberekera za Abrahamu ndi mkazi wake, Sara, omwe anali okalamba.​—Ahebri 11:11, 12.

Yesu Kristu analankhula zinthu zotheka zomwe anthu sanazimvetse m’pang’ono pomwe chifukwa cha mphamvu ndiponso ulamuliro zomwe anamupatsa. Ngakhale kuti bwenzi lake lapamtima Lazaro anali atamwalira, Yesu anawauza ophunzira ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” (Yohane 11:11) N’chifukwa chiyani Yesu anatchula munthu wakufa kuti ali m’tulo?

Yesu atafika m’tauni ya kwawo kwa Lazaro ya Bituniya, anapita kumanda ndipo analamula kuti mwala womwe unali pakhomo la mandawo auchotse. Atapemphera mokweza, anafuula kuti: “Lazaro tuluka!” Ndipo pamene anthu oonerera anali kuyang’ana m’mandamo “womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo.” Kenako Yesu anati: “M’masuleni iye, ndipo m’lekeni amuke.” (Yohane 11:43,44) Yesu anaukitsa Lazaro​—kubwezeretsa moyo wa munthu amene anali atamwalira kwa masiku anayi. Choncho, Kristu sanalankhule zosemphana ndi choonadi pamene ananena kuti bwenzi lake anali m’tulo. Kwa Yehova ndi Yesu, Lazaro wakufayo anali ngati ali m’tulo. Inde, Yesu ndi Atate wake wakumwamba amanena zinthu zothekadi.

Yehova Atha Kukwaniritsa Zomwe Tikuyembekezera

Pali kusiyana kwakukuludi pakati pa milungu yonyenga ndi Mulungu weniweni. Olambira mafano amaganiza molakwika kuti zinthu zomwe amazilambirazo zili ndi mphamvu zoposa za anthu. Komabe, kulambira kumeneku sikungachititse mafanowo kukhala ndi mphamvu yochita zozizwitsa ayi. Mosiyana ndi mafano, Yehova Mulungu moyenerera anganene za atumiki ake omwe anamwalira kale ngati kuti ali moyo, popeza atha kuwapatsanso moyo. “Yehova ndiye Mulungu woona,” ndipo sanamiza anthu ake m’pang’ono pomwe.​—Yeremiya 10:10.

N’zotonthoza kwambiri kudziŵa kuti Yehova pa nthaŵi yake yoikika, adzaukitsa akufa amene ali m’chikumbukiro chake. (Machitidwe 24:15) Inde, kuukitsa akufa kumaphatikizapo kubwezeretsa momwe munthuyo analili asanamwalire. Kukumbukira mmene munthu analili sikovuta kwa Mlengi amene ali ndi nzeru ndiponso mphamvu zosatha. (Yobu 12:13; Yesaya 40:26) Popeza kuti Yehova ndiye wachikondi chochuluka, adzagwiritsa ntchito chikumbumtima chake changwiro kubwezeretsa moyo kwa anthu akufa, n’kuwaloŵetsa m’dziko lapansi la paradaiso ndi mikhalidwe yomwe anali nayo asanamwalire.​—1 Yohane 4:8.

Pamene mapeto a dziko la Satanali akuyandikira, anthu okhulupirira Mulungu weniweni akuyembekeza motsimikiza tsogolo labwino kwambiri. (Miyambo 2:21, 22; Danieli 2:44; 1 Yohane 5:19) Wamasalmo amatitsimikizira kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti. . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) Upandu ndi chiwawa zidzakhala zinthu zakale. Chilungamo chidzakhala ponseponse ndipo mavuto azachuma kudzakhala kulibe. (Salmo 37:6; 72:12, 13; Yesaya 65:21-23) Zizindikiro zonse za kusankhana magulu, mitundu, ndiponso mafuko, zidzachotsedwa. (Machitidwe 10:34, 35) Nkhondo ndiponso zida za nkhondo sizidzakhalakonso. (Salmo 46:9) Panthaŵiyo, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Aliyense adzasangalala ndi moyo wangwiro ndiponso wathanzi. (Chivumbulutso 21:3, 4) Dziko lapansi lidzakhala Paradaiso posachedwapa. Cholinga cha Yehova n’chimenecho.

Inde, zonse zomwe tikuyembekeza zochokera m’Baibulo zidzakwaniritsidwa posachedwapa. Ndiyeno n’kuloleranji kunyengedwa ndi zinthu zimene anthu akulambira padziko lapansi pano, pamene tikhoza kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse? Iye akufuna “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:3, 4) M’malo mowonongera nthaŵi yathu ndi chuma chathu pa zinthu zonyenga za dzikoli ndiponso mafano ake, tiyeni tiwonjezere kudziŵa Mulungu amene ali weniweni ndiponso kumukhulupirira ndi mtima wathu wonse.​—Miyambo 3:1-6; Yohane 17:3.

[Chithunzi patsamba 6]

Kwa Yehova ndi Yesu, Lazaro anali m’tulo

[Zithunzi patsamba 7]

Dziko lapansi lidzakhala paradaiso posachedwapa.