‘Kulalikira Mawu’ Kumadzetsa Mpumulo
“Idzani Kuno kwa Ine . . . Ndipo Ine Ndidzakupumulitsani Inu”
‘Kulalikira Mawu’ Kumadzetsa Mpumulo
IYE ANALI munthu wangwiro ndipo anali pa ntchito yofunika kwambiri. Njira zomwe ankagwiritsa ntchito pophunzitsa zinali zogwira mtima kwambiri moti “makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Analinso mlaliki wosatopa. Anagwiritsa ntchito nthaŵi yake, mphamvu zake, ndiponso zinthu zomwe anali nazo, makamaka polalikira Ufumu wa Mulungu. Inde, Yesu Kristu anayenda m’madera onse a dziko lakwawo kulalikira ndi kuphunzitsa kuposa wina aliyense.—Mateyu 9:35.
Ntchito ya Yesu yofunika changu inali kulalikira “uthenga wabwino wa Ufumu” kwa anthu a m’nthaŵi yake ndiponso kuphunzitsa ophunzira ake kuti akagwire ntchito yomweyo padziko lonse lapansi. (Mateyu 4:23; 24:14; 28:19, 20) Kodi kuvuta kwa ntchito yolalikira ndi kufunika kwa changu pogwira ntchitoyo komanso kukula kwa gawo lolalikirako kukanawafoola ophunzira ake opanda ungwirowo ndiponso okhala ndi zolepheretsa?
Ayi ndithu! Yesu atawalangiza ophunzira ake kupempha “Mwini zotuta,” Yehova Mulungu, kuti antchito achuluke, anawatumiza kukaphunzitsa anthu. (Mateyu 9:38; 10:1) Kenako anawatsimikizira kuti kukhala otsatira ake ndiponso kugwira ntchito yolalikira kudzawadzetsera mpumulo weniweni. Yesu anati: “Idzani kuno kwa Ine . . . ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.”—Mateyu 11:28.
Gwero la Chimwemwe
Limenelotu ndi pempho lachifundo, lachikondi, ndiponso lokoma mtima bwanji! Likusonyeza nkhaŵa ya Yesu yoganizira otsatira ake. Ophunzira ake amapezadi mpumulo pokwaniritsa ntchito yawo yolalikira “uthenga wabwino” wa Ufumu wa Mulungu. Zimenezi zimawapatsa chimwemwe chenicheni ndipo amakhaladi okhutira.—Yohane 4:36.
Kale kwambiri Yesu asanabwere padziko lapansi, Malemba anatsindika kuti chimwemwe chiyenera kukhala mbali ya utumiki wopatulika kwa Mulungu. Zimenezi zinaonekera bwino kwambiri pamene wamasalmo anaimba kuti: “Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.” (Salmo 100:1, 2) Lerolino, anthu a mitundu yonse akukondwera mwa Yehova ndipo mawu awo otamanda akumveka ngati mfuu ya gulu la nkhondo lopambana. Anthu amene adziperekadi kwa Mulungu amadza pamaso pake ndi “kumuimbira mokondwera.” Ndipo zimenezi n’zoyenereradi chifukwa Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe” amene amafuna kuti atumiki ake akhale achimwemwe pokwaniritsa kudzipatulira kwawo kwa iye.—1 Timoteo 1:11, NW.
Atumiki Opumulitsidwa
Kodi zimatheka bwanji kuti kugwira molimbika ntchito yolalikira sikumatifoola koma mmalo mwake kumatipatsa mpumulo? Eya, kugwira ntchito ya Yehova kunali ngati chakudya chopatsa mphamvu kwa Yesu. Iye anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.”—Yohane 4:34.
N’chimodzimodzinso lerolino, alaliki achikristu achangu amakhala achimwemwe pamene ‘akulalikira mawu.’ (2 Timoteo 4:2) Connie, mkazi wachikristu wazaka zapakati pa 40 ndi 60 amene amathera maola opitirira 70 pa ntchito yolalikira mwezi uliwonse, anati: “Ndikalalikira ndimakhala wokhutira ndiponso wachimwemwe, ngakhale kuti nthaŵi zina pamapeto pa tsikulo ndimakhala wotopa.”
Koma bwanji ngati anthu sakulabadira uthenga wa Ufumu? Connie anapitiriza kuti: “Kaya anthu alabadira kapena ayi, palibe tsiku limene ndinadandaula kuti ndangowononga nthaŵi yanga pachabe muutumiki. Kuwonjezera pa kudziŵa kuti ndikuchita zomwe zimakondweretsa Yehova, ndimaona ulaliki kukhala mwayi wanga chifukwa pamene ndikuuza ena choonadi,
ziyembekezo zosangalatsa za m’Baibulo zimakhazikika mumtima mwanga.”Ena amaona kuti kuthandiza anthu ena kudziŵa zolondola ponena za Mulungu kumachititsa moyo wawo kukhala waphindu. Meloney, mtsikana amene nthaŵi zonse amathera maola opitirira 50 pa ntchito yolalikira mwezi uliwonse, ananena kuti: “Kulalikira n’kosangalatsa chifukwa chakuti kumandiunikira zinthu zofunika kwambiri ndiponso cholinga cha moyo wanga. Mavuto anga ndiponso nkhaŵa za tsiku ndi tsiku zimachepa ndikalalikira.”
Millicent, yemwenso ndi mtumiki wachangu wa Mboni za Yehova ananena kuti: “Tsiku lililonse limakhala lamtengo wapatali ndikalalikira kwa anthu, kuwauza chifuno cha Mulungu kwa anthu ndiponso kuwafotokozera mmene Paradaiso adzabwezeretsedwera padziko lapansi. Zimenezi zimachititsa kuti Yehova azikhala weniweni kwa ine tsiku lililonse ndipo ndimakhala ndi mtendere ndiponso chimwemwe zomwe sizingapezeke mwa njira ina iliyonse.”
Anthu Opumulitsidwa
Olalikira Ufumu mosakayika amapumulitsidwa ndi utumiki wachikristu, ndipo amene amalandira uthenga wopulumutsa moyo umenewu amatonthozedwa. Ngakhale kuti mphunzitsi wina wachikazi wa ku Portugal anali ataphunzitsidwa ndi ansembe ndiponso avirigo, iye anaona kuti tchalitchi chakecho sichinali kukwaniritsa zofuna zake zauzimu. Mafunso ake okhudza Baibulo sanali kuyankhidwa. Phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse lomwe anali kuchita ndi wa Mboni za Yehova linamuthandiza kumvetsa Malemba nthaŵi ndi nthaŵi. Mphunzitsiyo anali wosangalala kwambiri. Iye anati: “Ndinali kuyembekezera mwachidwi kuchita phunziro langa, Lachitatu lililonse chifukwa mafunso anga anali kuyankhidwa limodzi ndi limodzi pogwiritsa ntchito umboni wogwira mtima wa m’Baibulo.” Panopa, mkazi ameneyu ndi mtumiki wodzipatulira wa Yehova ndipo nayenso amapumulitsa ena ndi choonadi cha m’Baibulo.
Ndiyeno, n’zoonekeratu kuti Mboni za Yehova sizigwa mphwayi chifukwa cha kuvuta kwa ntchito yawo yolalikira kapena kukula kwa gawo lolalikira la padziko lonse. Ngakhale anthu atatsutsa kapena kusalabadira uthengawo, iwo sabwerera mmbuyo. Adzipereka ndi mphamvu zawo zonse kuti akwaniritse ntchito yawo yolalikira Ufumu. Amauza anthu uthenga wabwino kulikonse kumene angawapeze—poimika galimoto ku United States (1), pabwalo la ndege ku Korea (2), kumapiri a Andes (3), kapena m’sitolo ku London (4). Otsatira a Yesu amakono amagwira mokondwera ntchito yawo yopindulitsayi padziko lonse. Ndipo Yesu wawapumulitsa monga momwe analonjezera ndiponso akuwagwiritsira ntchito kupumulitsa anthu ena ambiri.—Chivumbulutso 22:17.