Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kuchita Zabwino

Pitirizani Kuchita Zabwino

Pitirizani Kuchita Zabwino

“Chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi.”​—AEFESO 5:9.

1. Kodi anthu miyandamiyanda pakalipano akusonyeza bwanji kuti akugwirizana ndi Salmo 31:19?

CHINTHU chabwino kuposa china chilichonse chimene munthu angachite ndicho kulemekeza Yehova. Anthu miyandamiyanda lerolino akuchita zimenezi mwa kutamanda Mulungu chifukwa cha ubwino wake. Ife monga Mboni za Yehova zokhulupirika, timavomereza ndi mtima wonse zimene wamasalmo anaimba kuti: “Ha! kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu.”​—Salmo 31:19.

2, 3. Kodi chingachitike n’chiyani ngati tilibe makhalidwe abwino pamene tigwira ntchito yathu yopanga ophunzira?

2 Kuopa Yehova kom’lemekeza kumatichititsa kum’tamanda chifukwa cha ubwino wake. Kumatichititsanso ‘kuyamika Yehova, kum’lemekeza, ndi kunenera ulemerero wa ufumu wake.’ (Salmo 145:10-13) N’chifukwa chake timagwira ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira mwachangu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Komabe, tifunika kukhala ndi khalidwe labwino pamene tikugwira ntchito yathu yolalikira. Ngati osatero ndiye kuti tidzatonzetsa dzina loyera la Yehova.

3 Anthu ambiri amanena kuti amalambira Mulungu, koma khalidwe lawo siligwirizana ndi miyezo imene ili m’Mawu amene Mulunguyo anawauzira. Mtumwi Paulo pouza anthu amene sanali kuchita zabwino pomwe ankanena kuti amatsatira miyezo yabwino analemba kuti: “Ndiwe . . . wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? . . . Dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.”​—Aroma 2:21, 22, 24.

4. Kodi khalidwe lathu labwino limakhala ndi zotsatirapo zotani?

4 M’malo motonzetsa dzina la Yehova, timayesetsa kulilemekeza mwa makhalidwe athu abwino. Zimenezi zimakhala ndi zotsatirapo zabwino kwa anthu amene sali mumpingo wachikristu. Chimodzi mwa zotsatirapo zimenezi n’chakuti khalidwe lathu labwino limachititsa anthu amene amatitsutsa kusoŵa chonena. (1 Petro 2:15) Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti khalidwe lathu labwino limakokera anthu ku gulu la Yehova. Zimenezi zimawapatsa mwayi woti am’lemekeze ndiponso kupeza moyo wosatha.​—Machitidwe 13:48.

5. Kodi ndi mafunso ati amene tifunika kuwalingalira tsopano?

5 Popeza ndife anthu opanda ungwiro, kodi tingapeŵe bwanji khalidwe limene linganyozetse Yehova ndi kukhumudwitsa anthu ofuna choonadi? Ndipo kodi tingatani kuti tikwanitse kuchita zabwino?

Chipatso cha Kuunika

6. Kodi zina mwa “ntchito za mdima zosabala kanthu” n’ziti, koma kodi ndi chipatso chiti chimene chiyenera kuonekera mwa Akristu?

6 Ife monga Akristu odzipatulira, tili ndi chinachake chimene chimatithandiza kupeŵa “ntchito za mdima zosabala kanthu.” Zina mwa ntchito zonyozetsa Mulungu zimenezi ndi monga kunama, kuba, mawu amwano, kulankhula konyansa pa nkhani za kugonana, khalidwe lonyansa, nthabwala zotukwana ndiponso kuledzera. (Aefeso 4:25, 28, 31; 5:3, 4, 11, 12, 18) M’malo mochita ntchito zimenezi, ‘timayenda monga ana a kuunika.’ Mtumwi Paulo ananena kuti “chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi.” (Aefeso 5:8, 9) Motero, timatha kupitiriza kuchita zabwino chifukwa choyenda m’kuunika. Koma kodi kumeneku n’kuunika kwa mtundu wanji?

7. Kodi titani kuti tipitirizebe kuonetsa chipatso cha ubwino?

7 Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, tingachite zabwino ngati tiyenda m’kuunika kwauzimu. Wamasalmo anaimba kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Ngati tikufuna kupitirizabe kuonetsa “chipatso cha kuunika” kudzera “m’ubwino wonse,” tifunika kugwiritsa ntchito kuunika kwauzimu nthaŵi zonse kumene kumapezeka m’Mawu a Mulungu. Ndipo kuunika kumeneku kumafotokozedwa mosamalitsa m’zofalitsa zachikristu, ndiponso timakukambirana nthaŵi zonse pamisonkhano yathu yolambira. (Luka 12:42; Aroma 15:4; Ahebri 10:24, 25) Tifunikanso kutsanzira kwambiri chitsanzo ndi ziphunzitso za Yesu Kristu yemwe ali “kuunika kwa dziko lapansi” ndiponso “chinyezimiro cha ulemerero [wa Yehova].”​—Yohane 8:12; Ahebri 1:1-3.

Chipatso cha Mzimu

8. N’chifukwa chiyani tingathe kuchita zabwino?

8 Mosakayika, kuunika kwauzimu kumatithandiza kuchita zabwino. Ndiponso, timatha kuonetsa khalidwe limeneli chifukwa chakuti mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, umatitsogolera. Ubwino kapena kuti kukoma mtima ndi mbali ya “chipatso cha Mzimu.” (Agalatiya 5:22, 23) Ngati tilola kuti mzimu woyera wa Yehova utitsogolere, udzabala mwa ife chipatso chake chosangalatsa kwambiri cha ubwino.

9. Kodi tingatsatire motani zimene Yesu ananena zimene zili pa Luka 11:9-13?

9 Kufunitsitsa kwathu kuti tim’sangalatse Yehova mwa kuonetsa chipatso cha mzimu cha ubwino kutichititse kutsatira zimene Yesu ananena kuti: “Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani. Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzam’tsegulira. Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzam’pempha mkate, adzampatsa mwala? kapena nsomba, nadzam’ninkha njoka m’malo mwa nsomba? kapena akadzam’pempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala [opanda ungwiro ndipo motero tingati ndinu] oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye?” (Luka 11:9-13) Tiyeni titsatire langizo la Yesu mwa kupempha mzimu wa Yehova kuti tithe kupitiriza kuonetsa chipatso chake cha ubwino.

‘Pitirizani Kuchita Zabwino’

10. Kodi ndi mbali ziti za ubwino wa Yehova zimene azitchula pa Eksodo 34:6, 7?

10 Pogwiritsa ntchito kuunika kwauzimu kochokera m’Mawu a Mulungu ndi thandizo la mzimu woyera wa Mulungu, tingathe ‘[kupitiriza, NW] kuchita zabwino.’ (Aroma 13:3) Timaphunzira zowonjezereka za mmene tingatsanzirire ubwino wa Yehova mwa kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse. Nkhani yapitayi inafotokoza mbali za ubwino wa Mulungu zimene anazitchula m’mawu amene Mose anamva amene ali pa Eksodo 34:6, 7. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.” Kupenda mosamalitsa mbali za ubwino wa Yehova zimenezi kutithandiza ‘kupitirizabe kuchita zabwino.’

11. Kodi kudziŵa kuti Yehova ndi wachifundo ndiponso wachisomo kuyenera kutikhudza motani?

11 Mawu ameneŵa amene Mulungu ananena amatithandiza kuona kufunika kotsanzira Yehova mwa kukhala wachifundo ndi wachisomo. Yesu anati: “Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.” (Mateyu 5:7; Luka 6:36) Kudziŵa kuti Yehova ndi wachisomo kumatilimbikitsa kukhala achisomo ndiponso abwino pochita ndi anthu ena, kuphatikizapo amene timawalalikira. Zimenezi zimagwirizana ndi zimene Paulo analangiza kuti: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.”​—Akolose 4:6.

12. (a) Popeza Mulungu ndi wosakwiya msanga, kodi tiyenera kuchita motani ndi anthu anzathu? (b) Kodi kukoma mtima kwa Yehova kumatilimbikitsa kuchita chiyani?

12 Popeza Mulungu ndi wosakwiya msanga, kufuna kwathu ‘kupitirizabe kuchita zabwino’ kumatilimbikitsa kulolera zolakwa zazing’ono za okhulupirira anzathu ndi kuika mtima kwambiri pa makhalidwe awo abwino. (Mateyu 7:5; Yakobo 1:19) Kukoma mtima kwa Yehova kumatilimbikitsa kuti tionetse chikondi chokhulupirika, ngakhale pamene tili pachiyeso chachikulu. Mosakayika, zimenezi n’zosiririka kwambiri.​—Miyambo 19:22.

13. Kodi tiyenera kumachita motani posonyeza kuti Yehova ndi ‘wachoonadi chochuluka’?

13 Popeza Atate wathu wakumwamba ndi ‘wachoonadi chochuluka,’ timafuna ‘kudzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu mwa mawu a choonadi.’ (2 Akorinto 6:3-7) Zina mwa zinthu zisanu ndi ziŵiri zimene Yehova zimamunyansa ndizo “lilime lonama” ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza.” (Miyambo 6:16-19) Choncho, kufuna kwathu kusangalatsa Mulungu kwatichititsa ‘kutaya zonama ndi kulankhula zoona.’ (Aefeso 4:25) Tiyenitu tisalephere kuonetsa ubwino mwa njira yofunika kwambiri imeneyi.

14. N’chifukwa chiyani tifunika kumakhululukira ena?

14 Mawu amene Mulungu anamuuza Mose azitichititsanso kukhululukira anthu ena chifukwa Yehova ndi wokonzeka kukhululuka. (Mateyu 6:14, 15) Komabe ngakhale zili choncho, Yehova amalanga ochimwa amene salapa. Motero, tifunika kutsatira miyezo yake ya ubwino pa nkhani yosunga mpingo kukhala woyera mwauzimu.​—Levitiko 5:1; 1 Akorinto 5:11, 12; 1 Timoteo 5:22.

“Penyani Bwino”

15, 16. Kodi malangizo a Paulo amene ali pa Aefeso 5:15-19 angatithandize bwanji kupitiriza kuchita zabwino?

15 Tifunika kudzazidwa ndi mzimu wa Mulungu ndi kupenya bwino umo tiyendera kuti tipitirize kuonetsa ubwino ngakhale kuti tikukhala m’dziko loipa. Mogwirizana ndi zimenezi, Paulo anauza Akristu a ku Efeso kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵitsani chifuniro cha Ambuye n’chiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, mmene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m’malimba Ambuye mumtima mwanu.” (Aefeso 5:15-19) Mosakayika, langizo limeneli ndi loyenereradi kwa ife m’masiku ano otsiriza a nthaŵi zoŵaŵitsa.​—2 Timoteo 3:1.

16 Kuti tipitirize kuchita zabwino, tifunika kupenya bwino kuti tikuyenda ngati anthu oti tikusonyeza nzeru ya Mulungu. (Yakobo 3:17) Tiyenera kupeŵa machimo aakulu ndipo tidzazidwe ndi mzimu woyera ndi kuulola kuti uzititsogolera. (Agalatiya 5:19-25) Tingapitirize kuchita zabwino ngati tigwiritsa ntchito malangizo auzimu amene timalandira pa misonkhano yachikristu, misonkhano yadera ndiponso pa misonkhano yachigawo. Zimene Paulo anawauza Aefeso zingatikumbutsenso kuti nthaŵi zambiri pamene timasonkhana kuti tilambire, timapindula ndi kuimba kwathu kochokera pansi pa mtima “nyimbo zauzimu,” zimene zambiri mwa izo zimatsindika pa makhalidwe auzimu onga ubwino.

17. Kodi Akristu amene akudwala kwambiri angakhulupirire za chiyani ngati matenda awo akuwalepheretsa kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse?

17 Nanga bwanji za olambira anzathu amene sangathe kupezeka pa misonkhano yachikristu nthaŵi zonse chifukwa cha matenda aakulu? Angakhumudwe kwambiri chifukwa sangathe kulambira Yehova nthaŵi zonse mwa kusonkhana ndi abale ndi alongo awo auzimu. Koma angakhulupirire kuti Yehova akumvetsa vuto lawo ndiponso kuti adzawasungabe m’choonadi, adzawapatsa mzimu wake woyera, ndiponso adzawathandiza kupitirizabe kuchita zabwino.​—Yesaya 57:15.

18. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirize kuchita zabwino?

18 Kupitirizabe kuchita zabwino kumafuna kusamala mayanjano athu ndi kupeŵa anthu ‘osakonda zabwino.’ (2 Timoteo 3:2-5; 1 Akorinto 15:33) Kugwiritsa ntchito malangizo ameneŵa kumatithandiza kupeŵa ‘kumvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu’ mwa kuchita zinthu zosiyana ndi zimene umatiuza kuchita. (Aefeso 4:30) Ndiponso, timathandizidwa kuchita zabwino ngati tiyanjana kwambiri ndi anthu amene zochita zawo zimasonyeza kuti amakonda zabwino ndipo mzimu woyera wa Yehova umawatsogolera.​—Amosi 5:15; Aroma 8:14; Agalatiya 5:18.

Ubwino Umabweretsa Zotsatira Zabwino

19-21. Fotokozani zimene zinachitika zomwe zikusonyeza zotsatira za kuchita zabwino.

19 Kuyenda m’kuunika kwauzimu, kutsatira malangizo a mzimu wa Mulungu, ndi kupenya bwino umo tiyendera zidzatithandiza kupeŵa zoipa ndi ‘kupitirizabe kuchita zabwino.’ Ndiyeno zimenezi zingabweretse zotsatira zabwino. Taonani zimene zinam’chitikira Zongezile yemwe ndi wa Mboni za Yehova ku South Africa. Tsiku lina m’maŵa akupita kusukulu, anadzera ku banki kukaona ndalama zake zochepa zimene anasungitsa kumeneko. Pepala limene linatuluka m’makina osonyeza ndalama zimene munthu ali nazo ku banki linalakwitsa mwa kusonyeza kuti Zongezile anali ndi ndalama zokwana R42, 000 ($6,000, U.S.) kuwonjezera pa zimene iye anasungitsa ku bankiyo. Mlonda wa bankiyo pamodzi ndi anthu ena anamuuza kuti atenge ndalamazo ndi kukazisungitsa ku banki ina. Mwamuna ndi mkazi wake amene Zongezile ankakhala nawo omwe ndi Mboni ndi okhawo amene anamuuza kuti asatenge ndalamazo.

20 Tsiku lotsatira, Zongezile anakawauza a ku bankiyo kuti makina awo analakwitsa. Atafufuza anapeza kuti nambala yake ya ku banki inali yofananako ndi ya mponda matiki wina wa bizinesi amene analakwitsa posungitsa ndalama zake mwa kugwiritsa ntchito nambala yomwe sinali yake. Mwamuna wabizinesiyo anadabwa kwambiri kuona kuti Zongezile sanagwiritse ntchito ndalamazo ndipo motero anamufunsa kuti: “Kodi uli m’chipembedzo chanji?” Zongezile ananena kuti anali wa Mboni za Yehova. Akuluakulu a bankiyo anamuyamikira kuchokera pansi pa mtima ndipo anati: “Tikanakonda anthu onse akanakhala oona mtima ngati Mboni za Yehova.” Inde, kuona mtima ndi kuchita zabwino kungachititse ena kulemekeza Yehova.​—Ahebri 13:18.

21 Kuchita zabwino sikuti kumafunikira kukhala kwapamwamba kuti kukhale ndi zotsatira zabwino. Mwachitsanzo, mnyamata wina yemwe ndi Mboni ndiponso mlaliki wa nthaŵi zonse pa chilumba china mwa zilumba za Samoa, anapita ku chipatala cha kumeneko. Anthu anali kuyembekeza kuonana ndi dokotala, ndipo Mboniyo inaona kuti mayi wachikulire amene anali pambuyo pake anali wodwala kwambiri. Iye anauza mayiyo kuti atsogole kuti alandire chithandizo cha mankhwala mwamsanga. Tsiku lina, Mboniyo inakumana ndi mayiyo kumsika. Mayiyo anam’kumbukira mnyamatayo ndi zabwino zimene anam’chitira kuchipatala. Mayiyo anati: “Tsopano ndadziŵa kuti Mboni za Yehova zimakondadi anansi awo.” Kale zimenezi zisanachitike, mayiyo ankakana kumvetsera uthenga wa Ufumu, koma tsopano zabwino zimene Mboniyo inam’chitira zinali ndi zotsatira zabwino. Anavomera kuphunzira naye Baibulo kunyumba kwake ndipo anayamba kudziŵa zambiri za m’Mawu a Mulungu.

22. Kodi njira yaikulu ‘yopitiriza kuchita zabwino’ ndi iti?

22 Mwachidziŵikire, mungasimbe zimene munakumana nazo zimene zikusonyeza phindu la kuchita zabwino. Njira yaikulu ‘yopitiriza kuchita zabwino’ ndiyo kulengeza nawo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu nthaŵi zonse. (Mateyu 24:14) Tiyenitu tipitirize kugwira ntchito yamtengo wapatali imeneyi mwachangu, podziŵa kuti imeneyi ndi njira ina yochitira zabwino, makamaka kwa anthu amene akumvetsera uthengawo. Chofunika kwambiri n’chakuti utumiki wathu ndi khalidwe lathu labwino zimalemekeza Yehova, yemwe ndi gwero la ubwino.​—Mateyu 19:16, 17.

Pitirizani ‘Kuchita Chokoma’

23. N’chifukwa chiyani utumiki wachikristu uli ntchito yabwino kwambiri?

23 Mosakayika, utumiki wathu ndi ntchito yabwino kwambiri. Idzatichititsa kupulumuka komanso kupulumutsa anthu amene akumvera uthenga wa Baibulo ndi kuyamba kuyenda m’njira yopita ku moyo wosatha. (Mateyu 7:13, 14; 1 Timoteo 4:16) Motero, pamene tikufuna kusankha zochita, kufuna kuchita zabwino kudzachititsa kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndasankha kuchita zidzakhudza motani ntchito yanga yolalikira Ufumu? Kodi njira imene ndikuiganizirayi ndi yanzeru? Kodi indichititsa kuthandiza ena kulandira “Uthenga Wabwino wosatha” ndi kukhala pa ubale weniweni ndi Yehova Mulungu?’ (Chivumbulutso 14:6) Tingapeze chimwemwe chachikulu ngati tisankha kuchita zinthu zimene zingapititse patsogolo zinthu za Ufumu.​—Mateyu 6:33; Machitidwe 20:35.

24, 25. Kodi ndi njira zina ziti zochitira zabwino mumpingo, ndipo tingakhale ndi chikhulupiriro chotani ngati tipitiriza kuchita zabwino?

24 Tiyeni tisaone mopepuka zotsatira zopindulitsa za kuchita zabwino. Tingapitirize kuonetsa khalidwe limeneli mwa kuthandizira mpingo wachikristu ndi kuchita zimene tingathe posamalira zofunika za mpingowo. Inde, timachita bwino kupezeka pa misonkhano yachikristu nthaŵi zonse ndi kutenga nawo mbali. Kupezekapo kwathu kumalimbikitsa olambira anzathu, ndipo ndemanga zathu zimene tazikonzekera bwino zimawamangirira mwauzimu. Timachitanso bwino kugwiritsa ntchito zinthu zathu kuti Nyumba ya Ufumu ikhale yabwino nthaŵi zonse ndiponso pamene tithandiza nawo kuisamalira. (2 Mafumu 22:3-7; 2 Akorinto 9:6, 7) Inde, “monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.”​—Agalatiya 6:10.

25 Sitingathe kuoneratu zochitika zonse zimene zingafune kuti tionetse ubwino. Motero, pamene tikumana ndi mavuto atsopano, tiyeni tifufuze kuunika m’Malemba, kupempherera mzimu woyera wa Yehova, ndi kuchita zonse zimene tingathe kuti tichite chifuniro chake chabwino ndiponso changwiro. (Aroma 2:9, 10; 12:2) Tingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova adzatidalitsa kwambiri pamene tikupitiriza kuchita zabwino.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tingachite bwanji chabwino choposa china chilichonse?

• Kodi n’chifukwa chiyani ubwino amautcha ‘chipatso cha kuunika’?

• N’chifukwa chiyani ubwino amautcha ‘chipatso cha mzimu’?

• Kodi khalidwe lathu labwino lili ndi zotsatira zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

Mawu a Mulungu ndi mzimu wake woyera zimatithandiza kuchita zabwino

[Zithunzi patsamba 18]

Kuchita zabwino kumabweretsa zotsatira zabwino