Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino

Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino

Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino

“M’yamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino.”​—YEREMIYA 33:11.

1. N’chifukwa chiyani timafuna kulemekeza Mulungu chifukwa cha ubwino wake?

YEHOVA MULUNGU ndi wabwino mwangwiro. Mneneri Zekariya anati: “Ukoma wake ndi waukulu ndithu.” (Zekariya 9:17) Inde, ubwino wa Mulungu ukuonekera m’zonse zimene iye anachita pokonza dziko lapansili kuti tizikhalamo. (Genesis 1:31) Sitidzatha kudziŵa malamulo onse osamvetsetseka amene Mulungu anawaika kuti azigwira ntchito pamene anali kulenga zinthu zonse. (Mlaliki 3:11; 8:17) Koma zochepa zimene tikudziŵa za chilengedwe zimatichititsa kulemekeza Mulungu chifukwa cha ubwino wake.

2. Kodi ubwino umatanthauzanji?

2 Kodi ubwino n’chiyani? Ubwino ndiwo khalidwe labwino kopambana, kapena kuganiza ndi kuchita zabwino ndi kupeŵa zoipa. Komabe, ubwino umatanthauza zambiri osati kungopeŵa zoipa chabe. Kukoma mtima, komwe ndi mbali ya chipatso cha mzimu, kumasonyezedwa mwa kuchita zinthu zabwino ndiponso zopindulitsa. (Agalatiya 5:22, 23) Timaonetsa ubwino pamene tichitira anthu ena zabwino ndiponso zoti apindule nazo. M’dziko limene tikukhala lino, zimene anthu ena amati n’zabwino, ena amati n’zoipa. Komabe, kuti tipeze mtendere ndi chimwemwe, payenera kukhala muyezo umodzi wa ubwino. Kodi ndani amene ali woyenera kukhazikitsa muyezo umenewo?

3. Kodi Genesis 2:16, 17 amasonyeza chiyani za muyezo wa ubwino?

3 Mulungu amaika muyezo wa ubwino. Pachiyambi pa mbiri ya anthu, Yehova ndi amene analamulira munthu woyamba kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Inde, anthu afunika kuyang’ana kwa Mlengi wawo kuti awadziŵitse zabwino ndi zoipa.

Kusonyeza Ubwino Waukulu

4. Kodi Mulungu wachitira anthu chiyani kuyambira pamene Adamu anachimwa?

4 Mwayi woti anthu akhale achimwemwe kosatha ali angwiro unasokonezeka pamene Adamu anachimwa ndi kusavomereza kuti Mulungu anali woyenera kukhazikitsa miyezo ya ubwino. (Genesis 3:1-6) Komabe, ana a Adamu asanabadwe monga oloŵa uchimo ndi imfa, Mulungu analosera kuti Mbewu yangwiro idzafika. Ndipotu polankhula ndi “njoka yokalambayo,” Satana Mdyerekezi, Yehova anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:15) Yehova anali ndi cholinga chowombola anthu ochimwa. Posonyeza kukoma mtima kwakukulu, Yehova anachitadi zimenezo kuti apulumutse anthu amene akukhulupirira nsembe ya dipo ya Mwana wake wokondedwa.​—Mateyu 20:28; Aroma 5:8, 12.

5. Ngakhale kuti tinatengera mtima woipa, n’chifukwa chiyani tingachite zabwino pa mlingo winawake?

5 Inde, anthufe tinatengera mtima woipa chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu. (Genesis 8:21) Komabe chosangalatsa n’chakuti Yehova amatithandiza kuchita zabwino pa mlingo winawake. Kutsatirabe zinthu zimene tinaphunzira m’malemba ake opatulika a mtengo wapatali, ‘kumatipatsa nzeru kufikira chipulumutso’ ndi ‘kutikonzekeretsa kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ Ndiponso kumatithandiza kuchita zabwino pamaso pake. (2 Timoteo 3:14-17) Komabe, kuti tipindule ndi malangizo a m’Malemba ndiponso kuti tichite zabwino, tikhale ndi maganizo a wamasalmo amene anaimba kuti: “Inu [Yehova] ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino; mundiphunzitse malemba anu.”​—Salmo 119:68.

Ubwino wa Yehova Umatamandidwa Kwambiri

6. Kodi Alevi anaimba nyimbo imene inali ndi mawu otani pamene Mfumu Davide anabweretsa likasa la chipangano ku Yerusalemu?

6 Mfumu Davide ya Israyeli wakale inadziŵa za ubwino wa Mulungu ndipo inafuna chitsogozo Chake. Davide anati: “Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima: chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira.” (Salmo 25:8) Malangizo a Mulungu amene anapatsa Aisrayeli anaphatikizapo Malamulo Khumi omwe anali ofunika kwambiri ndipo anawalemba pa miyala iŵiri ndi kuwasunga m’bokosi lopatulika lotchedwa likasa la chipangano. Davide atabweretsa Likasa ku mzinda waukulu wa Israyeli, Yerusalemu, Alevi anaimba nyimbo imene mawu ake ena anali akuti: “Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake n’chosatha.” (1 Mbiri 16:34, 37-41) Ziyeneratu kuti zinali zosangalatsa kumva mawu amene Aleviŵa anali kuimba.

7. Kodi n’chiyani chinachitika ataika Likasa m’Malo Opatulikitsa ndiponso litatha pemphero la Solomo lopatulira kachisi?

7 Mawu olemekeza ameneŵa anawatsindikanso pamene anali kupatulira kachisi wa Yehova amene mwana wa Davide, Solomo, anamanga. Ataika likasa la chipangano m’Malo Opatulikitsa a kachisi watsopanoyo, Alevi anayamba kulemekeza Yehova ndi kuti: “Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.” Patsiku limenelo, mtambo unadzaza kachisiyo mozizwitsa kusonyeza kuti Yehova anafika muulemerero pakachisiyo. (2 Mbiri 5:13, 14) Solomo atamaliza kupereka pemphero lopatulira, “moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera.” Ataona zimenezi, “ana onse a Israyeli . . . [a]nawerama nkhope zawo pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.” (2 Mbiri 7:1-3) Litatha phwando la masiku 14, Aisrayeli anabwerera ku nyumba zawo “akusekera ndi kukondwera m’mtima mwawo chifukwa cha zokoma Yehova adachitira Davide, ndi Solomo, ndi Aisrayeli anthu ake.”​—2 Mbiri 7:10.

8, 9. (a) Ngakhale kuti Aisrayeli analemekeza Yehova chifukwa cha ubwino wake, kodi m’kupita kwa nthaŵi anachita zotani? (b) Kodi Yehova analosera chiyani zokhudza Yerusalemu kudzera mwa Yeremiya, ndipo ulosi umenewo unakwaniritsidwa motani?

8 N’zomvetsa chisoni kuti Aisrayeli sanapitirize kutsatira zimene anaimba polemekeza Mulungu. Patapita nthaŵi, Ayuda ‘analemekeza Yehova ndi milomo yawo chabe.’ (Yesaya 29:13, NW) Iwo anayamba kuchita zoipa m’malo motsatira miyezo ya Mulungu ya ubwino. Kodi ndi zoipa ziti zimene anachita? Iwo analitu kulambira mafano, kuchita chiwerewere, kupondereza osauka ndi kuchita machimo ena aakulu. Zotsatira zake zinali zakuti Yerusalemu anawonongedwa ndipo anthu a mu Yuda anawatenga ukapolo ku Babulo mu 607 B.C.E.

9 Motero, Mulungu analanga anthu ake. Komabe, iye ananeneratu kudzera mwa mneneri Yeremiya kuti mu Yerusalemu mudzamvekanso mawu a iwo akuti: “M’yamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake n’chosatha.” (Yeremiya 33:10, 11) Ndipo n’zimene zinachitikadi. Ayuda otsala anabwerera ku Yerusalemu mu 537 B.C.E., dzikolo litakhala bwinja kwa zaka 70. (Yeremiya 25:11; Danieli 9:1, 2) Anamanga guwa la nsembe pa kachisi paphiri la Moriya ndipo anayamba kupereka nsembe. Maziko a kachisi anawamanga m’chaka chachiŵiri atabwerako ku ukapolo. Inali nthaŵi yosangalatsatu kwambiri! Ezara anati: “Ndipo pomanga maziko a Kachisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe ovala zovala zawo ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israyeli. Ndipo anathirirana mang’ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake n’chosalekeza pa Israyeli.”​—Ezara 3:1-11.

10. Kodi Salmo 118 limayamba ndi kutsiriza ndi mawu ofunika otani?

10 Mawu olemekeza ubwino wa Yehova ofanana ndi ameneŵa amapezeka m’masalmo ambiri. Limodzi mwa masalmo ameneŵa ndi Salmo 118, limene Aisrayeli anaimba pomaliza phwando la Paskha. Salmo limeneli limayamba ndiponso kutsiriza ndi mawu akuti: “Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake n’chosatha.” (Salmo 118:1, 29) N’zothekanso kuti ameneŵa anali mawu otamanda omaliza amene Yesu Kristu ndi ophunzira ake okhulupirika anaimba usiku woti iye aphedwa m’maŵa wake mu 33 C.E.​—Mateyu 26:30.

“Ndionetsenitu Ulemerero Wanu”

11, 12. Kodi Mose anamva mawu otani ataona mwachimbuuzi ulemerero wa Mulungu?

11 Kugwirizana kwa ubwino wa Yehova ndi kukoma mtima kwake kunaoneka zaka mazana ambiri Ezara asanabadwe. Aisrayeli atangomaliza kumene kulambira mwana wa ng’ombe wa golide m’chipululu ndiponso ochita zoipawo ataphedwa, Mose anapempha Yehova kuti: “Ndionetsenitu ulemerero wanu.” Yehova pozindikira kuti Mose sakanatha kuona nkhope Yake ndi kukhala ndi moyo, anati: “Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako.”​—Eksodo 33:13-20.

12 M’maŵa wake, ukoma wa Yehova unadutsa pamaso pa Mose pa Phiri la Sinai. Panthaŵi imeneyo, Mose anaona mwachimbuuzi ulemerero wa Mulungu ndipo anamva mawu akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza [“wosakwiya msanga,” NW], ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo [“kukoma mtima,” NW], wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi.” (Eksodo 34:6, 7) Mawu ameneŵa akusonyeza kuti ubwino wa Yehova ndi wogwirizana ndi kukoma mtima kwake pamodzinso ndi makhalidwe ake ena. Kupenda zimenezi kutithandiza kuchita zabwino. Tiyeni choyamba tipende khalidwe limene alitchula kaŵiri m’mawu ochititsa chidwi a Mulungu ameneŵa.

“Mulungu . . . wa Ukoma Mtima Wochuluka”

13. Kodi ndi khalidwe liti limene alitchula kaŵiri m’mawu onena za ubwino wa Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zoyenerera?

13 “Yehova [ndi] Mulungu . . . wa ukoma mtima wochuluka . . . wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo [“kukoma mtima,” NW].” Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “ukoma mtima” limatanthauzanso “chikondi chokhulupirika.” Ndi khalidwe lokhali limene alitchula kaŵiri m’mawu amene Mulungu anamuuza Mose. Zimenezi n’zoyenereratu kwambiri popeza khalidwe lalikulu la Yehova ndilo chikondi. (1 Yohane 4:8) Mawu odziŵika bwino otamanda Yehova akuti, “pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo [“kukoma mtima,”NW] chake chikhala chikhalire,” akutsindika khalidwe limeneli.

14. Kodi ndi ndani makamaka amene Mulungu amawasonyeza ubwino ndi kukoma mtima kwake?

14 Mbali ina ya ubwino wa Yehova ndi yakuti iye ndi wa ‘kukoma mtima kochuluka.’ Zimenezi makamaka zimaonekera pa mmene amasamalirira bwino atumiki ake okhulupirika amene adzipatulira kwa iye. (1 Petro 5:6, 7) Iye ‘amasungira ukoma mtima’ anthu amene amamukonda ndi kumutumikira ndipo Mboni za Yehova zingachitire umboni zimenezi. (Eksodo 20:6) Mtundu wa Israyeli wakuthupi unasiya kulandira ukoma mtima kapena chikondi chokhulupirika cha Yehova chifukwa unakana Mwana wake. Koma ubwino wa Mulungu ndi chikondi chake chokhulupirika adzazisonyeza kwa Akristu okhulupirika a mitundu yonse ku nthaŵi yosatha.​—Yohane 3:36.

Yehova​—Wachifundo ndi Wachisomo

15. (a) Kodi mawu amene Mose anamva pa Phiri la Sinai anayamba ndi kuti chiyani? (b) Kodi chifundo chimaphatikizapo chiyani?

15 Mawu amene Mose anamva pa Phiri la Sinai anayamba ndi kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo.” Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “chifundo” lingatanthauze “matumbo” ndipo ndi logwirizana kwambiri ndi liwu lotanthauza “chibelekero.” Choncho, chifundo chimaphatikizapo kumva chisoni kochokera m’kati mwenimweni mwa munthu. Koma chifundo chimaphatikizapo zambiri osati kungomvera chisoni munthu kokha ayi. Chiyenera kutilimbikitsa kuchitapo kanthu kuti tichepetse mavuto a anthu ena. Mwachitsanzo, akulu achikristu achikondi amaona kuti n’kofunika kuchitira chifundo okhulupirira anzawo, ‘kuchitira chifundo ndi kukondwera mtima’ ngati kuli koyenera kutero.​—Aroma 12:8; Yakobo 2:13; Yuda 22, 23.

16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi wachisomo?

16 Mbali ina ya ubwino wa Mulungu ndiyo chisomo chake. Munthu wachisomo “amaganizira mmene anthu ena akumvera mumtima mwawo” ndipo ‘amaonetsa kukoma mtima makamaka kwa anthu otsika.’ Yehova ndiye chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu wachisomo pochita ndi atumiki ake okhulupirika. Mwachitsanzo, Mulungu kudzera mwa angelo analimbikitsa mwachifundo mneneri wokalamba Danieli ndiponso anadziŵitsa namwali Maria kuti adzabereka Yesu womwe unali mwayi waukulu. (Danieli 10:19; Luka 1:26-38) Ife monga anthu a Yehova, timayamikira zedi chisomo chake potiphunzitsa kudzera m’Baibulo. Timam’lemekeza chifukwa chosonyeza ubwino ndipo timafuna kukhala a chisomo pochita ndi anthu ena. Amene ali oyenerera mwauzimu akamabweza wokhulupirira mnzawo “mu mzimu wa chifatso,” amayesetsa kukhala ofatsa, achisomo.​—Agalatiya 6:1.

Mulungu Wosakwiya Msanga

17. N’chifukwa chiyani tikuyamikira kuti Yehova ndi “wosakwiya msanga”?

17 “Mulungu . . . wosakwiya msanga.” Mawu amenewo akutsindika mbali ina ya ubwino wa Yehova. Iye amalolera zolakwa zathu moleza mtima ndipo amatipatsa nthaŵi yoti tigonjetse zolakwa zathu zazikulu ndi kupita patsogolo mwauzimu. (Ahebri 5:12–6:3; Yakobo 5:14, 15) Kuleza mtima kwa Mulungu kukupindulitsanso anthu amene sanayambebe kumulambira. Adakali ndi nthaŵi ya kulabadira uthenga wa Ufumu ndi kulapa. (Aroma 2:4) Komabe, ngakhale kuti Yehova ndi woleza mtima, nthaŵi zina ubwino wake umam’chititsa kusonyeza mkwiyo wake, monga mmene anachitira pamene Aisrayeli analambira mwana wang’ombe wagolidi pa Phiri la Sinai. Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake waukulu posachedwapa pamene adzathetsa dongosolo loipa la Satana.​—Ezekieli 38:19, 21-23.

18. Pankhani ya choonadi, kodi Yehova amasiyana motani ndi atsogoleri a anthu?

18 “Yehova [ndi] Mulungu . . . wachoonadi chochuluka.” Yehova amasiyanatu kwambiri ndi atsogoleri a anthu amene amalonjeza zinthu zambiri koma n’kulephera kuzikwaniritsa. Mosiyana ndi amenewo, olambira Yehova angadalire zonse zimene zinalembedwa m’Mawu ake ouziridwa. Popeza Mulungu ndi wachoonadi chochuluka, tingakhulupirire malonjezo ake nthaŵi zonse. Chifukwa cha ubwino wake, Atate wathu wakumwamba salephera kuyankha mapemphero athu opempha choonadi chauzimu ndipo amatero mwakupereka choonadi chochuluka.​—Salmo 43:3; 65:2.

19. Kodi Yehova wasonyeza motani ubwino waukulu kwa anthu ochimwa amene alapa?

19 “Yehova [ndi] Mulungu . . . wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.” Ubwino umam’chititsa Yehova kukhala wokonzeka kukhululukira ochimwa amene alapa. Mosakayika, timayamikira kuti Atate wathu wachikondi wakumwamba wakonza zotikhululukira kudzera mu nsembe ya Yesu. (1 Yohane 2:1, 2) Inde, ndife okondwa kuti onse amene angakhulupirire dipo angakhale paubale wabwino ndi Yehova, ndi kuyembekezera kudzakhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano limene iye walonjeza. N’zifukwa zabwinotu zimenezi zolemekezera Yehova chifukwa chosonyeza ubwino wake kwa anthu.​—2 Petro 3:13.

20. Kodi tili ndi umboni wotani woti Yehova samalekerera zoipa?

20 [Yehova ndi] wosamasula wopalamula.” Chimenechitu ndi chifukwa china cholemekezera Yehova chifukwa cha ubwino wake. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mbali yofunika kwambiri ya ubwino ndi yakuti sumalekerera zoipa. Ndipotu, “pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,” adzabwezera chilango “iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino.” Iwo “adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.” (2 Atesalonika 1:6-9) Ndiyeno olambira Yehova amene adzapulumuka adzasangalala kwambiri ndi moyo popanda kusokonezedwa ndi anthu osadziŵa Mulungu, omwe ‘sakonda zabwino.’​—2 Timoteo 3:1-3.

Tsanzirani Ubwino wa Yehova

21. N’chifukwa chiyani tifunika kuchita zabwino?

21 Mosakayika, tili ndi zifukwa zambiri zolemekezera ndi kuthokoza Yehova chifukwa cha ubwino wake. Kodi ife monga atumiki ake sitingachite zonse zimene tingathe kuti tisonyeze khalidwe limeneli? Tiyeneradi kutero, pakuti mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Atate wathu wakumwamba amachita zabwino nthaŵi zonse ndipo ifenso tifunika kutero.

22. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani yotsatirayi?

22 Ngati tadzipatulira kwa Yehova ndi mtima wonse, mosakayika timafunitsitsa kutsanzira ubwino wake. Popeza ndife ana a Adamu wochimwa, zimativuta kuti tichite zabwino. Komabe, m’nkhani yotsatirayi tiona chifukwa chake tingathe kuchita zabwino. Tikambirana njira zosiyanasiyana mmene tingatsanzirire Yehova yemwe ndi chitsanzo chachikulu pankhani yosonyeza ubwino.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ubwino n’chiyani?

• Kodi ndi mawu a m’Malemba ati amene amaonetsa ubwino wa Mulungu?

• Kodi mbali zina za ubwino wa Yehova ndi ziti?

• N’chifukwa chiyani tifunika kutsanzira chitsanzo cha Yehova pankhani yosonyeza ubwino?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 12]

Yehova analanga anthu ake akale chifukwa chakuti sanatsatire mawu awo om’lemekeza

[Chithunzi patsamba 12]

Otsalira amene anali okhulupirika anabwerera ku Yerusalemu

[Chithunzi patsamba 13]

Mose anamva mawu ochititsa chidwi onena za ubwino wa Yehova

[Chithunzi patsamba 15]

Ubwino wa Yehova umaonekera pa mmene amatiphunzitsira kudzera m’Baibulo