Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwalandira “Mzimu wa Choonadi”?

Kodi Mwalandira “Mzimu wa Choonadi”?

Kodi Mwalandira “Mzimu wa Choonadi”?

“Atate . . . adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi.”​—YOHANE 14:16, 17.

1. Kodi ndi nkhani yofunika yotani yomwe Yesu anauza ophunzira ake panthaŵi yomaliza yomwe anali nawo m’chipinda chapamwamba?

“AMBUYE, mumuka kuti?” Limenelo linali lina mwa mafunso omwe atumwi a Yesu anamufunsa panthaŵi yomaliza yomwe iye anali nawo m’chipinda chapamwamba mu Yerusalemu. (Yohane 13:36) Zokambirana zili m’kati, Yesu anawauza kuti tsopano anali pafupi kuwasiya ndi kubwerera kwa Atate wake. (Yohane 14:28; 16:28) Iye sakanakhala nawonso pamodzi mwakuthupi kuti awaphunzitse ndiponso kuyankha mafunso awo. Komabe, iye anawatsimikizira kuti: “Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe [“mthandizi,” kapena “wotonthoza,” NW mawu am’munsi] ina, kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse.”​—Yohane 14:16.

2. Kodi Yesu analonjeza kuti akachoka adzawatumizira chiyani ophunzira ake?

2 Yesu anatchula mthandizi ameneyo ndipo anafotokoza mmene adzawathandizira ophunzira akewo. Iye anawauza kuti: “Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu. Koma tsopano ndimuka kwa Iye wondituma Ine . . . Kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzam’tuma Iye kwa inu. . . . Atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m’choonadi chonse.”​—Yohane 16:4, 5, 7, 13.

3. (a) Kodi Akristu oyambirira anawatumizira liti “Mzimu wa choonadi”? (b) Kodi ndi njira imodzi yofunika iti yomwe mzimuwo unalili “mthandizi” kwa iwo?

3 Lonjezo limeneli linakwaniritsidwa pa Pentekoste wa 33 C.E., monga momwe mtumwi Petro anatsimikizira kuti: “Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.” (Machitidwe 2:32, 33) Monga momwe tionere kutsogoloku, mzimu woyera womwe unatsanuliridwa pa Pentekoste unathandiza Akristu oyambirira kukwaniritsa zinthu zambiri. Koma Yesu analonjeza kuti “Mzimu wa choonadi” ‘udzakumbutsa iwo zinthu zonse zimene iye ananena kwa iwo.’ (Yohane 14:26) Mzimu umenewu ukawakumbutsa utumiki wa Yesu ndiponso zomwe anaphunzitsa ngakhalenso mawu enieni omwe analankhula, ndipo ukawathandiza kulemba zimenezi. Izi makamaka zinathandiza kwambiri mtumwi Yohane yemwe anali wokalamba pamene anayamba kulemba Uthenga wake Wabwino kumapeto kwa zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Nkhani yakeyo imaphatikizapo uphungu wamtengo wapatali womwe Yesu anapereka pamene anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake.​—Yohane, machaputala 13-17.

4. Kodi “Mzimu wa choonadi” unathandiza motani Akristu odzozedwa oyambirira?

4 Yesu analonjezanso ophunzira oyambirirawo kuti mzimuwo ‘udzawaphunzitsa zinthu zonse’ ndi ‘kuwatsogolera ku choonadi chonse.’ Mzimuwo ukawathandiza kumvetsa zinthu zozama za m’Malemba ndiponso kusungabe umodzi wawo wamaganizo, kuzindikira kwawo, ndi cholinga chawo. (1 Akorinto 2:10; Aefeso 4:3) Chotero, mzimu woyera unapatsa mphamvu Akristu oyambirirawo kuti onse monga gulu agwire ntchito monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kupatsa Mkristu wodzozedwa aliyense chakudya chauzimu “panthaŵi yake.”​—Mateyu 24:45.

Mzimu Uchitira Umboni

5. (a) Kodi ndi chiyembekezo chatsopano chotani chomwe Yesu anapatsa ophunzira ake usiku wa pa Nisani 14, 33 C.E.? (b) Kodi ndi ntchito yanji yomwe mzimu ukachita pokwaniritsa lonjezo la Yesu limenelo?

5 Usiku wa pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu anauza ophunzira ake kuti nthaŵi ina, iye adzalandira iwo ndi kukhala nawo kumwamba pamodzi ndi Atate wake. Iye anawauza kuti: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.” (Yohane 13:36; 14:2, 3) Iwo akalamulira pamodzi ndi iye mu Ufumu wake. (Luka 22:28-30) Ndipo kuti akhale ndi chiyembekezo chakumwamba chimenechi, iwo anayenera ‘kubadwa mwa mzimu’ monga ana auzimu a Mulungu ndiponso kudzozedwa kuti akatumikire monga mafumu ndi ansembe pamodzi ndi Kristu kumwamba.​—Yohane 3:5-8; 2 Akorinto 1:21, 22; Tito 3:5-7; 1 Petro 1:3, 4; Chivumbulutso 20:6.

6. (a) Kodi maitanidwe akumwamba anayamba liti, ndipo ndi angati amene analandira maitanidwe ameneŵa? (b)  Kodi oitanidwawo anabatizidwa kuloŵa chiyani?

6 “Maitanidwe akumwamba” amenewo anayamba pa Pentekoste wa 33 C.E. ndipo mbali yaikulu ikuoneka kuti inatha m’ma 1930. (Ahebri 3:1) Chiŵerengero cha osindikizidwa chizindikiro ndi mzimu woyera kukhala mbali ya Israyeli wauzimu ndi 144,000, “ogulidwa mwa anthu.” (Chivumbulutso 7:4; 14:1-4) Ameneŵa anabatizidwa kuloŵa m’thupi lauzimu la Kristu, kuloŵa mumpingo wake, ndiponso mu imfa yake. (Aroma 6:3; 1 Akorinto 12:12, 13, 27; Aefeso 1:22, 23.) Iwo akabatizidwa m’madzi ndiponso kudzozedwa ndi mzimu woyera, amayamba moyo wodzipereka, kutanthauza kukhala wokhulupirika mpaka imfa yawo.​—Aroma 6:4, 5.

7. N’chifukwa chiyani Akristu odzozedwa okha ndiwo moyenerera amadya zizindikiro pa Chikumbutso?

7 Monga Israyeli wauzimu, Akristu odzozedwa ameneŵa anali mbali ya pangano latsopano lomwe Yehova anapangana ndi “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Yeremiya 31:31-34) Pangano latsopanolo linatsimikizidwa ndi mwazi umene Kristu anakhetsa. Yesu anatchula zimenezi pamene ankayambitsa Chikumbutso cha imfa yake. Luka analemba kuti: “Mmene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa. Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.” (Luka 22:19, 20) Otsalira a kagulu ka 144,000 amene adakali padziko lapansi, ndiwo moyenerera amadya mkate ndi vinyo zomwe zili ndi tanthauzo lophiphiritsira pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu.

8. Kodi odzozedwa amadziŵa bwanji kuti aitanidwa kumwamba?

8 Kodi odzozedwa amadziŵa bwanji kuti analandira maitanidwe akumwamba? Iwo amalandira molondola umboni wa mzimu woyera. Mtumwi Paulo analemba za anthu ngati ameneŵa kuti: “Onse amene atsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Mzimu wokha uchita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.” (Aroma 8:14-17) Umboni wa mzimu umenewu ndi wamphamvu kwambiri moti amene akukayikira pang’ono chabe kuti analandira maitanidwe akumwamba angadziŵiretu kuti sanaitanidwe, motero adzapeŵa kudya zizindikiro pa Chikumbutso.

Mzimu ndi Nkhosa Zina

9. Kodi ndi magulu aŵiri osiyana ati omwe amatchulidwa m’Mauthenga Abwino ndiponso m’buku la Chivumbulutso?

9 Yesu podziŵa kuti Akristu oitanidwa kupanga Israyeli wauzimu ndi oŵerengeka, iye anawatcha kuti “kagulu kankhosa.” Iwo amaloŵa ‘m’khola’ la pangano latsopano mosiyana ndi gulu losaŵerengeka la “nkhosa zina” zomwe Yesu anati ayeneranso kuzitenga. (Luka 12:32; Yohane 10:16) A nkhosa zina omwe akusonkhanitsidwa m’masiku otsiriza, adzakhala ‘khamu lalikulu” lomwe lidzapulumuka “chisautso chachikulu,” ndi kukhala ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso. N’zochititsa chidwi kuti masomphenya omwe Yohane anaona kumapeto kwa zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, amasiyanitsa khamu lalikulu ndi mamembala 144,000 a Israyeli wauzimu. (Chivumbulutso 7:4, 9, 14) Kodi nkhosa zina zimalandiranso mzimu woyera, ndipo ngati zimatero, umasintha motani miyoyo yawo?

10. Kodi nkhosa zina zimabatizidwa motani “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera”?

10 Mzimu woyera umachitadi mbali yofunika kwambiri m’miyoyo ya a nkhosa zina. Iwo amasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova mwa kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” (Mateyu 28:19) Amazindikira uchifumu wa Yehova, amamvera Kristu monga Mfumu ndiponso Momboli, ndipo amavomereza mzimu wa Mulungu kapena kuti mphamvu yogwira ntchito, kuti izigwira ntchito m’miyoyo yawo. Tsiku ndi tsiku amayesetsa kusonyeza “chipatso cha mzimu” m’miyoyo yawo. Chipatso cha mzimuchi ndicho: “Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”​—Agalatiya 5:22, 23.

11, 12. (a) Kodi odzozedwa amayeretsedwa motani m’njira yapadera? (b) Kodi a nkhosa zina amayeretsedwa m’njira yotani?

11 A nkhosa zina ayeneranso kulola Mawu a Mulungu ndi mzimu wake woyera kuti ziwayeretse. Odzozedwa anayeretsedwa kale m’njira yapadera kwambiri, ndipo anayesedwa olungama ndi oyera monga mkwatibwi wa Kristu. (Yohane 17:17; 1 Akorinto 6:11; Aefeso 5:23-27) Mneneri Danieli anawatcha kuti “opatulika a Wam’mwambamwamba” omwe amalandira Ufumu mu ulamuliro wa “mwana wa munthu,” Kristu Yesu. (Danieli 7:13, 14, 18, 27) Mmbuyomo, Yehova anauza mtundu wa Israyeli kudzera mwa Mose ndi Aroni kuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, [“dziyeretseni,” NW] ndipo muzikhala oyera; pakuti ine ndine woyera.”​—Levitiko 11:44.

12 Mawu akuti “kuyeretsa” makamaka amatanthauza “kuchititsa kuyera, kupatulika, kapena kudzipatula kuchita utumiki kapena kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova Mulungu; kukhala woyera, wopatulika, kapena wosadetsedwa.” Mu 1938, Nsanja ya Olonda inanena kuti Ayonadabu, kapena kuti a nkhosa zina, “ayenera kudziŵa kuti kudzipatulira ndiponso kudziyeretsa n’kofunika kwambiri kwa aliyense amene adzakhale m’gulu la khamu lalikulu ndi kukhala padziko lapansi.” M’masomphenya olembedwa m’buku la Chivumbulutso, a khamu lalikulu amanenedwa kuti “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa,” ndipo kuti akuchitira Yehova ‘utumiki wopatulika usana ndi usiku m’Kachisi mwake.’ (Chivumbulutso 7:9, 14, 15) A nkhosa zina mothandizidwa ndi mzimu woyera amachita zonse zomwe angathe kukhalabe mogwirizana ndi miyezo ya Yehova ya chiyero.​—2 Akorinto 7:1.

Kuchitira Zabwino Abale a Kristu

13, 14. (a) Malinga ndi fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi, kodi chipulumutso cha a nkhosa zina chimadalira pa kuchita chiyani? (b) M’nthaŵi za mapeto zino, kodi a nkhosa zina achitira motani zabwino abale a Kristu?

13 Yesu anatsindika mgwirizano wolimba womwe ulipo pakati pa nkhosa zina ndi kagulu ka nkhosa m’fanizo lake la nkhosa ndi mbuzi lomwe analinena pamodzi ndi ulosi wake wa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” M’fanizo limenelo, Kristu anasonyeza mosapita m’mbali kuti chipulumutso cha a nkhosa zina chikudalira kwambiri zomwe iwo amachitira odzozedwa omwe iye anawatcha kuti “abale anga.” Iye anati: “Mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi. . . . Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono awa, munandichitira ichi Ine.”​—Mateyu 24:3; 25:31-34, 40.

14 Mawu akuti “chifukwa munachitira ichi” akutanthauza ntchito yochirikiza mwachikondi abale odzozedwa ndi mzimu a Kristu, omwe dziko la Satana lawachitira monga alendo, ngakhale kuika ena mwa iwo m’ndende. Iwo akhala akufuna chakudya, zovala zokwanira ndiponso chithandizo chamankhwala. (Mateyu 25:35, 36, NW, mawu am’munsi) M’nthaŵi yamapeto ino, kuyambira mu 1914, odzozedwa ambiri zawachitikira zimenezi. Mbiri yamakono ya Mboni za Yehova imatsimikizira kuti odzozedwa athandizidwa ndi anzawo okhulupirika a nkhosa zina chifukwa mzimu umawalimbikitsa kutero.

15, 16. (a) Kodi nkhosa zina zathandiza abale odzozedwa a Kristu padziko lapansi makamaka pa ntchito yanji? (b) Kodi odzozedwa asonyeza motani kuyamikira kwawo a nkhosa zina?

15 Abale odzozedwa a Kristu padziko lapansi m’masiku otsiriza ano athandizidwa kwambiri ndi a nkhosa zina makamaka pogwira ntchito yomwe Mulungu anapereka ‘yolalikira uthenga uwu wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi, kuti ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 24:14; Yohane 14:12) Pamene chiŵerengero cha odzozedwa padziko lapansi chikuchepabe m’kupita kwa zaka, chiŵerengero cha a nkhosa zina chikuwonjezeka kufika mamiliyoni. Ambiri mwa ameneŵa atumikira monga alaliki a nthaŵi zonse​—apainiya ndiponso amishonale​—kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu “kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Ena amachita nawo ntchito yolalikira imeneyi mmene angathere ndipo amathandiza mosangalala ntchito yofunikayi ndi ndalama.

16 Abale odzozedwa a Kristu amayamikira kwambiri kuthandiza kosalekeza kumeneku komwe a nkhosa zina akuchita. M’buku lakuti Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga Wamtendere” lomwe gulu la kapolo linatulutsa mu 1986, muli mawu osonyeza mmene iwo amamvera. Bukuli limati: “Chiyambire Nkhondo Yadziko II, kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wa ‘mapeto a dongosolo la zinthu,’ kwakukulukulu kukuchitika chifukwa cha mbali imene ‘khamu lalikulu’ la ‘nkhosa zina’ likuchita. . . . Chifukwa chake, tikuyamikira kwambiri, ‘khamu lalikulu’ lochokera m’mitundu yonse, m’zilankhulidwe zonse, chifukwa cha mbali yaikulu imene iwo akhala nayo m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa [Yesu] pa Mateyu 24:14!”

‘Asayesedwe Angwiro Opanda Ife’

17. Kodi anthu okhulupirika akale omwe adzaukitsidwe padziko lapansi ‘sadzayesedwa angwiro popanda’ odzozedwa m’njira yotani?

17 Polankhula za amuna ndi akazi okhulupirika omwe anakhalako Kristu asanabwere, mtumwi Paulo monga wodzozedwa analemba kuti: “Iwo onse adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro, sanalandira lonjezanolo, popeza Mulungu adatikonzera ife [odzozedwa] kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu [“angwiro,” NW] opanda ife.” (Ahebri 11:35, 39, 40) Panthaŵi ya Zaka Chikwi, Kristu ndi abale ake odzozedwa a 144,000 kumwamba, adzakhala mafumu ndi ansembe ndipo adzagaŵa phindu la nsembe ya dipo ya Kristu padziko lapansi. Akadzatero, m’pamene a nkhosa zina ‘adzayesedwe angwiro’ m’thupi ndiponso m’maganizo.​—Chivumbulutso 22:1, 2.

18. (a) Kodi mfundo za m’Baibulo ziyenera kuthandiza a nkhosa zina kuzindikira chiyani? (b) Kodi a nkhosa zina amadikira “vumbulutso la ana a Mulungu” ndi chiyembekezo chotani?

18 Zonsezi ziyenera kuwazindikiritsa a nkhosa zina chifukwa chomwe Malemba Achigiriki Achikristu amagogomeza kwambiri za Kristu ndi abale ake odzozedwa ndiponso ntchito yofunika kwambiri yomwe iwo amachita pokwaniritsa zolinga za Yehova. Choncho, a nkhosa zina amaona kuti ndi mwayi wapadera kuthandiza kagulu ka odzozedwa m’njira iliyonse yomwe angathe pamene akudikira “vumbulutso la ana a Mulungu” pa Armagedo ndiponso m’Zaka Chikwi. Iwo angayembekezere ‘kudzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’​—Aroma 8:19-21.

Ogwirizana mu Mzimu pa Chikumbutso

19. Kodi “Mzimu wa choonadi” wachita chiyani kwa odzozedwa ndi anzawo a nkhosa zina, ndipo kodi iwo adzagwirizana motani makamaka usiku wa pa March 28?

19 Yesu m’pemphero lake lomaliza usiku wa pa Nisani 14, 33 C.E., anati: ‘Ndipempherera kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupire kuti Inu munandituma Ine.’ (Yohane 17:20, 21) Mulungu chifukwa cha chikondi chake, anatumiza Mwana wake kudzapereka moyo wake kuti odzozedwa ndiponso anthu omvera padziko lapansi apulumuke. (1 Yohane 2:2) “Mzimu wa choonadi” wagwirizanitsa abale a Kristu ndi anzawo a nkhosa zina. Usiku wa pa March 28, dzuŵa likuloŵa, magulu onse aŵiri adzasonkhana pamodzi kukumbukira imfa ya Kristu ndiponso zinthu zonse zomwe Yehova wawachitira kudzera m’nsembe ya Mwana wake wokondedwa Kristu Yesu. Kupezekapo kwawo pamwambo wofunika kwambiri umenewo kulimbikitsetu mgwirizano wawo ndiponso kutsimikiza mtima kwawo kupitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu, mwakutero akumapereka umboni wakuti amanyadira kukhala pakati pa anthu amene Yehova amawakonda.

Kubwereramo

• Kodi “Mzimu wa choonadi” unatumizidwa liti kwa Akristu oyambirira, ndipo kodi wakhaladi “mthandizi” motani?

• Kodi odzozedwa amadziŵa bwanji kuti alandira maitanidwe akumwamba?

• Kodi mzimu wa Mulungu umagwira ntchito kwa nkhosa zina m’njira zotani?

• Kodi a nkhosa zina achitira motani zabwino abale a Kristu, ndipo n’chifukwa chiyani iwo ‘sadzayesedwa angwiro’ opanda odzozedwa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

“Mzimu wa choonadi” unatsanuliridwa pa ophunzira pa Pentekoste wa 33 C.E.

[Zithunzi patsamba 23]

Nkhosa zina zachitira zabwino abale a Kristu mwa kuwathandiza kukwaniritsa ntchito yolalikira yomwe Mulungu anapereka