Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mudzi Wokhala Pamwamba pa Phiri

Mudzi Wokhala Pamwamba pa Phiri

Mudzi Wokhala Pamwamba pa Phiri

“INU ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika,” Yesu anawauza motero ophunzira ake pa ulaliki wake wotchuka wa pa phiri.​—Mateyu 5:14.

Midzi yambiri ya ku Galileya ndi ku Yudeya inkakhala pamwamba pa mapiri m’malo mokhala m’zigwa zimene zinali m’munsi mwa mapiriwo. Chifukwa chachikulu chimene ankasankhira pamwamba pa phiri chinali chakuti ankafuna kukhala otetezeka. Kuwonjezera pa adani amene akanatha kulanda midziyo, magulu a chifwamba ankakonda kuwononga midzi ya Aisrayeli. (2 Mafumu 5:2; 24:2) Anthu olimba mtima a m’midziyo, ankatha kuteteza mosavuta nyumba zoyandikana zimene zinali pamwamba pa phiri kusiyana ndi zimene zinali m’munsi. Midzi imene inali m’munsi mwa phiri, inkafunika kukhala ndi khoma lalikulu lotetezera.

Popeza nthaŵi zambiri makoma a nyumba za Ayuda ankawapaka laimu, nyumba zonse zoyandikana zopakidwa laimuzi zomwe zinkaunjikana pamodzi pamwamba pa phiri, zinkaoneka mosavuta pa mtunda wautali. (Machitidwe 23:3) Masiku oti dzuŵa likuwala bwinobwino ku Palestina, midzi ya pamwamba pa phiriyi inkawala ngati muuni, monganso mmene lerolino midzi ya ku Mediterranean yofanana ndi imeneyi ikuwalira.

Yesu anagwiritsa ntchito mbali zapadera zimenezi za midzi ya ku Galileya ndi ku Yudeya pophunzitsa otsatira ake zimene Mkristu woona amafunika kuchita. Anawauza kuti: “Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:16) Ngakhale kuti Akristu sachita ntchito zabwino n’cholinga choti anthu awatame, anthu amaonabe khalidwe lawo labwino.​—Mateyu 6:1.

Khalidwe labwino lotero limaonekera kwambiri pa misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova. Nyuzipepala ina ku Spain pofotokoza za msonkhano wachigawo umene unali utangochitika kumene, inati: “Pamene kukonda ziphunzitso za chipembedzo kukucheperachepera m’zipembedzo zina, sizili choncho kwa Mboni za Yehova. Popeza safuna kuti Baibulo lithe mphamvu, amachita zimene Mawu a Mulungu amanena.”

Thomas, yemwe ankasamalira bwalo la maseŵero la kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Spain limene Mboni zinkagwiritsa ntchito nthaŵi zambiri, ankasangalala kukhala ndi anthu amene ankachita zimene Mawu a Mulungu amanena. Anasintha nthaŵi yake yopuma pantchito kuti adzatero milungu ingapo m’tsogolo n’cholinga choti adzakhale nawo pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Msonkhano utatha, nthumwi zambiri, kuphatikizapo achinyamata, zinamuyandikira kuti zim’thokoze chifukwa chakuti anathandiza Mboni kugwiritsa ntchito malowo kwa zaka zambiri ndiponso kum’funira zabwino zonse pamene akukapuma pantchito. Pamene anali kumuuza zimenezi, misozi inagwa m’maso mwake. Iye anati: “Kukhala ndi anthu inu chinali chimodzi mwa zinthu zabwino kwambiri zimene ndakumana nazo pa moyo wanga.”

Mudzi umene uli pamwamba pa phiri, anthu amatha kuuona bwinobwino chifukwa umaonekera mosavuta ndiponso chifukwa chakuti nyumba zopaka laimu za m’mudzimo zimabweza kuwala kwa dzuŵa. N’chimodzimodzinso Akristu oona amaonekera kuti ndi osiyana ndi anthu ena chifukwa amayesetsa kutsatira miyezo yapamwamba ya m’Malemba monga kuona mtima, makhalidwe abwino, ndi chifundo.

Ndiponso, Akristu amasonyeza kuwala kwa choonadi mwa ntchito yawo yolalikira. Mtumwi Paulo ponena za Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anati: “Popeza tili nawo utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifoka; . . . koma ndi maonekedwe a choonadi tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.” (2 Akorinto 4:1, 2) Ngakhale kuti kulikonse kumene analalikira anthu anawatsutsa, Yehova anadalitsa utumiki wawo moti pomafika cha m’ma 60 C.E., Paulo anatha kulemba kuti uthenga wabwino unali kulalikidwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”​—Akolose 1:23.

Lerolino, Mboni za Yehova zimachitanso ntchito yawo mwakhama kuti ‘ziwalitse kuunika kwawo pamaso pa anthu,’ monga mmene Yesu ananenera. Mboni za Yehova zikufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu mwa kulankhula ndi anthu ndiponso mwa kugaŵira mabuku, magazini ndi zina zimene amafalitsa. Akuchita zimenezi m’mayiko okwana 235 padziko lonse. Mboni zikufalitsa mabuku ndi magazini awo m’zinenero zokwana 370 n’cholinga choti anthu ambiri alandire kuwala kwa choonadi cha Baibulo.​—Mateyu 24:14; Chivumbulutso 14:6, 7.

M’madera ambiri, Mboni zikuchita ntchito yovuta kwambiri yophunzira zinenero za anthu amene afika m’dziko lawo kuchokera ku mayiko amene ntchito yolalikira anailetsa. Mwachitsanzo, m’mizinda yambiri yaikulu ya ku North America, mwafika anthu ambiri ochokera ku China ndi ku Russia. Mboni za m’mizinda imeneyi zachita khama kuphunzira Chitchaina, Chirasha ndi zinenero zina n’cholinga choti zilalikire uthenga wabwino kwa alendowo. Ndipotu, maphunziro othandiza kuti afulumize ntchito yophunzira zinenero zimenezi akuchititsidwa kuti uthenga wabwino ulalikidwe ndithu kwa ena pamene munda ukadali ‘woyera kufikira kumweta.’​—Yohane 4:35.

Mneneri Yesaya analosera kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.” Mwa makhalidwe awo ndi utumiki wawo, Mboni za Yehova zikuthandiza anthu kulikonse kuti apite ku “phiri la nyumba ya Yehova” kuti akalangizidwe njira za Mulungu ndi kuphunzira kuyenda m’njira yake. (Yesaya 2:2, 3) Zotsatira zake zosangalatsa n’zakuti, monga mmene Yesu ananenera, onse ‘amalemekeza Atate wawo wakumwamba,’ Yehova Mulungu.​—Mateyu 5:16; 1 Petro 2:12.