Nawonso Ali ndi Nzeru Zawo
Nawonso Ali ndi Nzeru Zawo
“ACHIKULIRE ali ndi nzeru, koma ana nawonso ali ndi nzeru zawo,” umatero mwambi wina wa ku Nigeria. Edwin, yemwe ndi mkulu wachikristu, anatsimikiza kuti zimenezi n’zoona.
Tsiku lina, Edwin anapeza bokosi lachitsulo kunsi kwa desiki yake kunyumba.
“Kodi bokosili n’landani?” Edwin anawafunsa motero ana ake atatu.
“Ndi langa,” anayankha motero Emmanuel, wa zaka zisanu ndi zitatu. Anapitiriza kunena kuti bokosi lachitsulolo lomwe linali ndi dzimbiri ndipo lalikulu masentimita 12 komanso la kachibowo pamwamba pake linali loti aziponyamo zopereka za ntchito ya Mboni za Yehova ya padziko lonse. Iye anati: “Popeza sindipita ku Nyumba ya Ufumu tsiku lililonse, ndinaganiza zopanga bokosi kuti ngati ndalama zanga zogulira zokhwasulakhwasula sindinazigwiritse ntchito, ndiziponya m’bokosi limeneli.”
Bambo a Emmanuel anali ndi bokosi kunyumba kwawo limene ankasungamo ndalama zoti ziziwathandiza kukapezeka pa msonkhano wachigawo umene umachitika kamodzi pachaka. Koma chifukwa cha mavuto ena amene anagwa mwadzidzidzi m’banjamo, ndalamazo anazigwiritsa ntchito. Pofuna kuonetsetsa kuti ndalama zake za choperekazo zisagwire ntchito ina, Emmanuel anatenga chitini chakale n’kupititsa kwa wowotcherera zitsulo kuti akatseke pamwamba pake. Wowotcherera zitsuloyo atamva mmene akagwiritsire ntchito chitinicho, anam’konzera Emmanuel bokosi pogwiritsa ntchito zidutswa za zitsulo zakale. Nayenso Michael, mng’ono wake wa Emmanuel, anapempha bokosi lake.
Edwin podabwa ndi zimene anaŵa anachita, anawafunsa chifukwa chake anakakonzetsa mabokosiwo. Michael anayankha kuti: “Ndikufuna ndizipereka nawo!”
Emmanuel, Michael, ndi Uchei, yemwe ndi mlongo wawo wa zaka zisanu ndi zinayi, ankasunga ndalama zina zogulira zokhwasulakhwasula ndi kuziika m’mabokosiwo. Ankachita zimenezi makolo awo osadziŵa. Kodi nzeru imeneyi anaipeza kuti? Anaŵa atangoyamba kuyenda ndi kutha kusunga ndalama m’manja, makolo awo anawaphunzitsa kuponya ndalama m’bokosi la zopereka ku Nyumba ya Ufumu. Mwachionekere, anaŵa anagwiritsadi ntchito zimene anaphunzira.
Mabokosiwo atadzaza, anawatsegula. Ndalama zimene zinalimo zonse pamodzi zinakwana $3.13 (U.S.) zomwe ndi ndalama zambiri. Tikutero chifukwa chakuti m’dzikolo anthu achikulire ambiri amangopeza ndalama zokwana madola pafupifupi 300 okha basi pachaka. Zopereka zaufulu zimenezo zimathandizira ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova imene pakalipano ikuchitika m’mayiko okwana 235 padziko lonse.