Anthu Okhulupirika Analimbana ndi Minga M’matupi Awo
Anthu Okhulupirika Analimbana ndi Minga M’matupi Awo
“Kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze.”—2 AKORINTO 12:7.
1. Kodi ndi mavuto ena ati amene anthu akukumana nawo masiku ano?
KODI mukulimbana ndi mayesero ena ake amene sakutha? Ngati ndi choncho, simuli nokha. Mu “nthaŵi zowawitsa” zino, Akristu okhulupirika akulimbana ndi chitsutso choopsa, mavuto a m’banja, matenda, mavuto a zachuma, kuvutika maganizo, kumwalira kwa anthu amene ankawakonda kwambiri, ndi mavuto enanso. (2 Timoteo 3:1-5) M’madera ena, miyoyo ya anthu ambiri ili pangozi chifukwa chosoŵa zakudya ndiponso nkhondo.
2, 3. Kodi ndi maganizo ofooketsa ati amene tingakhale nawo chifukwa cha mavuto onga munga amene timakumana nawo, ndipo n’chifukwa chiyani maganizo ameneŵa angakhale oopsa?
2 Mavuto ameneŵa angam’chititse munthu kutayiratu chiyembekezo, makamaka ngati mavuto angapo am’gwera nthaŵi imodzi. Taonani zimene Miyambo 24:10 amanena. Amati: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Inde, kulefuka ndi mayesero athu kungatilande mphamvu zimene timafunikira ndipo kungafooketse kutsimikiza mtima kwathu koti tipirire mpaka mapeto. Kodi zili choncho motani?
3 Eya, kulefuka kungatichititse kulephera kuzindikira zinthu mwanzeru. Mwachitsanzo, n’kosavuta kuti tikokomeze mavuto athuwo ndiponso kuyamba kudzimvera chisoni. Ena mwinanso angafuule kwa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mwalola kuti zimenezi zindichitikire?” Ngati maganizo ofooketsa ameneŵa akhazikika mumtima mwa munthu, angam’chotsere munthuyo chimwemwe ndi chidaliro. Mtumiki wa Mulungu angakhumudwe moti mwina angasiye kulimba nayo “nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.”—1 Timoteo 6:12.
4, 5. Kodi nthaŵi zina Satana amachita chiyani ndi mavuto athu, komabe tingakhale ndi chidaliro chotani?
4 Kunena zoona, Yehova Mulungu satiyesa. (Yakobo 1:13) Mayesero ena timakumana nawo chifukwa chakuti tikuyesetsa kukhala okhulupirika kwa iye. Ndipotu, Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wamkulu wa Yehova, amalimbana ndi atumiki Ake. M’nthaŵi yochepa imene yam’tsalira, “mulungu [woipa] wa nthaŵi ino ya pansi pano” ameneyu akuyesetsa kuchititsa aliyense amene amakonda Yehova kusiya kuchita zimene Iye amafuna. (2 Akorinto 4:4) Satana akukantha abale athu onse padziko lapansi ndi mavuto ambiri. (1 Petro 5:9) N’zoona kuti Satana sayambitsa mwachindunji mavuto onse amene timakumana nawo, koma angagwiritse ntchito mavuto amene tikukumana nawo kuti atifooketse kwambiri.
5 Komabe, ngakhale Satana kapena zida zake zikhale zamphamvu motani, tingathe kumugonjetsa. N’chifukwa chiyani tikutsimikiza motero? Chifukwa chakuti Yehova Mulungu amatimenyera nkhondo. Iye waonetsetsa kuti atumiki ake akudziŵa machenjerero a Satana. (2 Akorinto 2:11) Ndipotu, Mawu a Mulungu amatiuza za mayesero ambiri amene Akristu oona amakumana nawo. Posimba za mayesero a mtumwi Paulo, Baibulo linagwiritsa ntchito mawu oti “munga m’thupi.” Chifukwa chiyani? Tiyeni tione mmene Mawu a Mulungu amafotokozera mawu ameneŵa. Ndiyeno tiona kuti si ife tokha amene tikufuna kuti Yehova atithandize kugonjetsa mayesero.
Chifukwa Chake Ziyeso Zili Ngati Minga
6. Kodi Paulo anatanthauza chiyani pamene anati “munga m’thupi,” ndipo munga umenewo uyenera kuti unali chiyani?
6 Paulo atayesedwa kwambiri, anauziridwa kulemba kuti: “Kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.” (2 Akorinto 12:7) Kodi munga umene unali m’thupi la Paulo unali chiyani? Eya, munga umene waloŵa kwambiri m’thupi ungapweteke kwabasi. Motero, fanizoli likusonyeza chinachake chimene chinachititsa Paulo kumva kuwawa—kaya mwakuthupi, mwamaganizo, kapena zonse ziŵiri. Mwina Paulo anadwala maso kapena matenda ena. Kapenanso, mungawo unali anthu amene anatsutsa zoti Paulo anayenerera kukhala mtumwi ndi kukayikira phindu la ntchito yake yolalikira ndi kuphunzitsa. (2 Akorinto 10:10-12; 11:5, 6, 13) Kaya mungawo unali chiyani, uwo unakhalabe mwa Paulo ndipo sakanatha kuuchotsa.
7, 8. (a) Kodi mawu akuti ‘kutundudza’ akusonyeza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani n’kofunika kuti tilimbane ndi minga iliyonse imene ikutivutitsa pakalipano?
7 Onani kuti mungawo unatundudza Paulo. N’zochititsa chidwi kuti verebu la Chigiriki limene Paulo analigwiritsa ntchito pano likuchokera ku liwu lotanthauza “mfundo za zala za m’manja.” Liwu limenelo analigwiritsa ntchito m’tanthauzo lake lenileni pa Mateyu 26:67 ndipo analigwiritsa ntchito mophiphiritsa pa 1 Akorinto 4:11. M’mavesi amenewo, liwuli likupereka tanthauzo la kumenyedwa. Poganizira udani waukulu umene Satana ali nawo kwa Yehova ndi atumiki Ake, tingatsimikize kuti Mdyerekezi ankasangalala kuti munga unali kutundudza Paulo. Lerolinonso, Satana amasangalala chimodzimodzi tikamavutika ndi munga m’thupi.
8 Motero, tifunika kudziŵa mmene tingalimbanire ndi minga imeneyo monga mmene anachitira Paulo. Kuti tikhale ndi moyo tifunika kuchita zimenezi. Kumbukirani kuti Yehova akufuna kuti tidzakhale ndi moyo kosatha m’dziko lake latsopano pamene sitidzavutikanso ndi mavuto onga minga. Pofuna kutithandiza kuti tidzapeze mphoto yabwino kwambiri imeneyi, Mulungu watipatsa zitsanzo zambiri m’Mawu ake opatulika, Baibulo, zosonyeza kuti atumiki ake okhulupirika anakwanitsa bwinobwino kulimbana ndi minga m’matupi awo. Iwo anali anthu wamba opanda ungwiro monga mmenenso ife tilili. Kupenda ena mwa anthu amene akupanga ‘mtambo wa mboni’ waukulu umenewu kungatithandize ‘kuthamanga mwachipiriro makaniwo adatiikira.’ (Ahebri 12:1) Kusinkhasinkha zinthu zimene iwo anapirira kungakulitse chidaliro chathu chakuti tingalimbane ndi minga iliyonse imene Satana angagwiritse ntchito polimbana nafe.
Minga Imene Inavutitsa Mefiboseti
9, 10. (a) Kodi zinatani kuti Mefiboseti akhale ndi munga m’thupi? (b) Kodi Mfumu Davide inam’komera mtima motani Mefiboseti, ndipo tingatsanzire motani Davide?
9 Taganizirani za Mefiboseti, mwana wa bwenzi la Davide, Yonatani. Pamene Mefiboseti anali ndi zaka zisanu, analandira uthenga woti bambo ake, Yonatani pamodzi ndi agogo ake, Mfumu Sauli, anaphedwa. Mlezi wake anagwidwa njakata. “Adam’nyamula nathaŵa; ndipo kunali pofulumira kuthaŵa, iye anagwa nakhala wopunduka.” (2 Samueli 4:4) Kupunduka kumeneku kuyenera kuti kunali ngati munga umene Mefiboseti anafunika kuupirira pamene anali kukula.
10 Patapita zaka, Mfumu Davide anam’komera mtima Mefiboseti chifukwa cha chikondi chachikulu chimene anali nacho kwa Yonatani. Davide anam’patsa Mefiboseti minda yonse ya Sauli ndipo anauza mnyamata wa Sauli, Ziba, kuti azisamalira mindayo. Davide anauzanso Mefiboseti kuti: “Udzadya pa gome langa chikhalire.” (2 Samueli 9:6-10) N’zosakayikitsa kuti kukoma mtima kwa Davide kunatonthoza Mefiboseti ndipo kunathandiza kuchepetsa kuwawa kumene anali kumva chifukwa cha kupunduka kwake. Chitsanzo chabwinotu chimenechi! Ifenso tiziwakomera mtima anthu amene akulimbana ndi munga m’thupi mwawo.
11. Kodi Ziba anam’neneza chiyani Mefiboseti, koma tikudziŵa bwanji kuti linali bodza? (Onani mawu a m’munsi.)
11 Kenaka, Mefiboseti anafunikanso kulimbana ndi munga wina m’thupi lake. Mnyamata wake, Ziba, anam’neneza kwa Mfumu Davide, yemwe panthaŵiyo anali kuthaŵa m’Yerusalemu chifukwa * Davide anakhulupirira bodza la Ziba ndipo anam’patsa munthu wabodzayu zinthu zonse za Mefiboseti.—2 Samueli 16:1-4.
cha kugalukira kwa mwana wake, Abisalomu. Ziba ananena kuti Mefiboseti anatsala ku Yerusalemu n’cholinga chakuti akhale mfumu.12. Kodi Mefiboseti anachita chiyani ndi mavuto ake, ndipo ali chitsanzo chabwino kwa ife motani?
12 Komabe, Mefiboseti atakumana ndi Davide, anaiuza mfumuyi zoona zake za nkhaniyi. Iye anali kukonza zoti atsagane ndi Davide pamene Ziba anamunamiza n’kudzipereka kupita m’malo mwake. Kodi Davide anakonza kulakwika kumene kunachitikaku? Pang’ono chabe. Iye anagaŵa zinthuzo kuti zina zikhale za Mefiboseti, zina za Ziba. Uwu uyeneranso kuti unali munga wina m’thupi la Mefiboseti. Kodi iye anakhumudwa kwambiri? Kodi anatsutsa kugamula kwa Davide, kudandaula kuti sanam’chitire chilungamo? Ayi, iye modzichepetsa anagwirizana ndi zimene mfumu inafuna. Iye anangoika mtima wake pa zimene zinali bwino, kusangalala kuti mfumu yoyenerera ya Israyeli inabwerako ili bwinobwino. Mefiboseti anaperekadi chitsanzo chabwino kwambiri mwa kupirira kupunduka kwake, kum’neneza, ndi kum’khumudwitsa.—2 Samueli 19:24-30.
Nehemiya Analimbana ndi Mayesero Ake
13, 14. Kodi Nehemiya anafunika kupirira minga yotani pamene anabwerera kukamanganso malinga a Yerusalemu?
13 Taganizani za minga yophiphiritsa imene Nehemiya anapirira pamene anabwerera ku mzinda wopanda malinga wa Yerusalemu m’zaka za m’ma 400 B.C.E. Iye anapeza kuti mzindawo unali wosatetezeka ndipo Ayuda amene anabwerera analibe dongosolo labwino, anafooketsedwa, ndiponso anali odetsedwa pamaso pa Yehova. Ngakhale kuti Nehemiya analoledwa ndi Mfumu Aritasasta kuti amangenso linga la Yerusalemu, iye posakhalitsa anapeza kuti akazembe a mayiko oyandikana nawo anaipidwa ndi ntchito imeneyi. “Chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israyeli chokoma.”—Nehemiya 2:10.
14 Anthu otsutsa a mayiko ena amenewo anachita chilichonse pogwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti alepheretse ntchito ya Nehemiya. Kuopseza kwawo ndi mabodza awo, kuphatikizapo kugwiritsa ntchito azondi amene anawatumiza kuti akafooketse Nehemiya, ziyenera kuti zinali ngati minga yosalekeza m’thupi lake. Kodi iye anagonjera machenjerero a adaniŵa? Ayi. Iye anakhulupirira Mulungu kotheratu. Sanafooke. Motero, pamene malinga a Yerusalemu anamangidwanso, anapereka umboni wosatha wakuti Yehova anathandiza Nehemiya mwachikondi.—Nehemiya 4:1-12; 6:1-19.
15. Kodi ndi mavuto ati a Ayuda amene anam’pweteketsa mtima kwambiri Nehemiya?
15 Nehemiya, monga kazembe, analimbananso ndi mavuto ambiri amene anali pakati pa anthu a Mulungu. Mavuto ameneŵa anali ngati minga Nehemiya 5:1-10) Ayuda ambiri anali kuswa Sabata ndipo sanali kuthandiza Alevi ndi kuthandizira pa kachisi. Ndiponso ena anakwatira “akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amoabu.” Zimenezi zinam’pweteketsatu mtima Nehemiya. Koma minga yonseyi sinamuchititse kusiya ntchito yake. Anachirimika mobwerezabwereza monga wotsatira wachangu wa malamulo olungama a Mulungu. Monga Nehemiya, tiyeni tisalole kuti kusakhulupirika kwa anthu ena kutilepheretse kutumikira Yehova mokhulupirika.—Nehemiya 13:10-13, 23-27.
imene inam’vutitsa kwambiri chifukwa anakhudza ubale wa anthuwo ndi Yehova. Anthu olemera anali kukongoletsa pa chiwongoladzanja chachikulu, ndipo abale awo osauka pofuna kubweza ngongoleyo ndiponso kupereka msonkho wa Aperisiya, anali kupereka minda yawo ndiponso ngakhale kugulitsa ana awo kuukapolo. (Anthu Okhulupirika Ena Ambiri Analimbana ndi Minga M’thupi
16-18. Kodi mavuto a m’banja anakantha motani Isake ndi Rebeka, Hana, Davide, ndi Hoseya?
16 M’Baibulo mulinso zitsanzo zina zambiri za anthu amene analimbana ndi zochitika zovutitsa maganizo zimene zinali ngati minga. Gwero lina lofala la minga imeneyo linali mavuto a m’banja. Akazi aŵiri a Esau “anapweteka mtima wa Isake ndi Rebeka,” makolo a Esau. Rebeka anafika ponena kuti analema nawo moyo wake chifukwa cha akazi amenewo. (Genesis 26:34, 35; 27:46) Taganizaninso za Hana ndi mmene mkazi mnzake, Penina, “anam’puta kwakukulu” chifukwa chakuti Hana anali wosabereka. Mwina Hana anali kuvutika ndi chipongwe chimenechi nthaŵi zambiri kunyumba kwawo. Penina analinso kum’puta Hana pagulu—pamaso pa achibale ndi anzawo—banjali likapita kukachita nawo madyerero ku Silo. Kumeneku kunali ngati kukanikizira mungawo mkati kwambiri mwa thupi la Hana.—1 Samueli 1:4-7.
17 Taganizaninso zimene Davide anapirira chifukwa cha njiru yoipa kwambiri ya apongozi ake, Mfumu Sauli. Davide pofuna kupulumutsa moyo wake, anali kukhala m’mapanga ku chipululu cha Engedi, kumene anafunika kudutsa njira za m’miyala yaitali, yotsetsereka ndiponso yoopsa. Kupanda chilungamo kumeneku kuyenera kuti kunam’pweteka kwambiri chifukwa iye sanam’lakwire Sauli. Komabe, kwa zaka zambiri, Davide ankangokhalira kuthaŵathaŵa ndipo zonsezi ankachita chifukwa cha njiru ya Sauli.—1 Samueli 24:14, 15; Miyambo 27:4.
18 Taganizani za mavuto a m’banja amene anakantha mneneri Hoseya. Mkazi wake anali wachigololo. Khalidwe lake loipa liyenera kuti linali ngati munga umene unakanirira mumtima wa Hoseya. Ndiponso ayenera kuti anavutika maganizo kwambiri pamene mkaziyo anam’balira ana aŵiri apathengo chifukwa cha dama lake.—Hoseya 1:2-9.
19. Kodi mneneri Mikaya anazunzidwa motani?
19 Munga wina m’thupi ndiwo chizunzo. Talingalirani zimene mneneri Mikaya anakumana nazo. Kuona kuti Mfumu Ahabu yoipayo inazingidwa ndi aneneri onyenga ndiponso kuti inkakhulupirira mabodza awo am’kunkhuniza, kuyenera kuti kunapweteketsa mtima wolungama wa Mikaya. Ndiyeno, pamene Mikaya anauza Ahabu kuti 1 Mafumu 22:6, 9, 15-17, 23-28) Kumbukiraninso za Yeremiya ndi zimene anam’chitira anthu akupha mozunza.—Yeremiya 20:1-9.
“mzimu wonama” ndi umene unkalankhulitsa aneneri onsewo, kodi mtsogoleri wa aneneri onyengawo anatani? “[A]napanda Mikaya patsaya.” Choipa kwambiri chinali mmene Ahabu anachitira Yehova atam’chenjeza kuti alephera kulanda Ramoti Gileadi. Ahabu analamula kuti Mikaya amuike m’ndende kumene ankam’patsa chakudya ndi madzi zochepa. (20. Kodi ndi minga yotani imene Naomi anapirira, ndipo anafupidwa motani?
20 Kumwalira kwa anthu amene tinali kuwakonda ndi vuto linanso lalikulu limene lingakhale ngati munga m’thupi. Naomi anapirira kuwawa mtima kumene anali nako chifukwa cha kumwalira kwa mwamuna wake ndi ana ake aamuna aŵiri. Iye anabwerera ku Betelehemu mtima wake ukuwawa chifukwa cha imfa zimenezi. Anauza mabwenzi ake kuti asamamutche Naomi koma Mara, dzina limene linasonyeza kuwawidwa mtima chifukwa cha zimene anakumana nazo. Komabe pomaliza, Yehova anafupa kupirira kwake mwa kum’patsa mdzukulu amene anakhala mumzera wa makolo a Mesiya.—Rute 1:3-5, 19-21; 4:13-17; Mateyu 1:1, 5.
21, 22. Kodi Yobu anavutika motani ndi kumwalira kwa ana ake ndi kuwonongeka kwa zinthu zake, nanga anachita bwanji?
21 Taganizani mmene Yobu ayenera kuti anavutikira maganizo atamva za kumwalira kwadzidzidzi ndiponso koipa kwambiri kwa ana ake khumi ndiponso kufa kwa ziweto zake zonse ndiponso antchito ake. Mwadzidzidzi, Yobu anapezeka kuti alibe pogwira. Ndiyeno, pamene anali kulimbana ndi mavuto ameneŵa, Satana anam’kanthanso ndi matenda. Yobu ayenera kuti anaganiza kuti matendawo amene anafalikira thupi lake lonse anali oti amupha. Kuwawa kwake kunali kosapiririka moti anaganiza kuti kunali bwino kufa kuti apumule.—Yobu 1:13-20; 2:7, 8.
22 Ndiyeno ngati kuti mavuto ameneŵa anali osakwanira, mkazi wake, chifukwa cha chisoni chimene anali nacho ndi kuwawa mtima kwake, anauza Yobu kuti: “Chitira Mulungu mwano, ufe.” Umenewutu unali munga m’thupi la Yobu limene linali likupweteka. Kenako, anzake a Yobu atatu, m’malo mom’limbikitsa, anam’pweteketsa mtima ndi mfundo zawo zabodza, kumuimba mlandu kuti anachita machimo amseri ndi kuti machimo ameneŵo ndi amene anachititsa kuti avutike choncho. Tinganene kuti mfundo zolakwika zimenezo zinali kukanikizira munga mkati kwambiri mwa thupi la Yobu. Kumbukiraninso kuti Yobu sankadziŵa chifukwa chake mavuto ameneŵa anamugwera ndiponso sankadziŵa kuti moyo wake wokha unali woti suwonongedwa. Komabe, “mwa ichi chonse Yobu sanachimwa, kapena kunenera Mulungu cholakwa.” (Yobu 1:22; 2:9, 10; 3:3; 14:13; 30:17) Ngakhale kuti anavutika ndi minga yambiri nthaŵi imodzi, iye anakhulupirikabe. Zolimbikitsatu zimenezi!
23. N’chifukwa chiyani anthu okhulupirika amene takambirana m’nkhani ino anatha kupirira minga yosiyanasiyana imene inali m’matupi awo?
23 Pali zitsanzo zambiri za anthu onga amene takambiranaŵa. M’Baibulo muli zitsanzo zinanso zambiri. Atumiki okhulupirika ameneŵa analimbana ndi minga yawoyawo yophiphiritsa. Ndipotu mavuto amene anakumana nawo anali osiyanasiyana. Komabe, anafanana pa chinthu chimodzi. Palibe ndi m’modzi yemwe amene anataya mtima n’kusiya kutumikira Yehova. Ngakhale kuti anakumana ndi mayesero ovutitsa maganizo, iwo anagonjetsa Satana chifukwa cha mphamvu zimene Yehova anawapatsa. Motani? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli ndipo itisonyeza mmene ifenso tingalimbanire ndi chinthu china chilichonse chimene chili ngati munga m’thupi lathu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Mefiboseti yemwe anali woyamikira ndiponso wodzichepetsa sakanakhala ndi maganizo ofuna kulanda ufumu motero. Mosakayika, iye ankadziŵa za kukhulupirika kwa atate wake, Yonatani. Ngakhale kuti anali mwana wa Mfumu Sauli, Yonatani anazindikira modzichepetsa kuti Davide ndi amene Yehova anam’sankha kuti adzakhale mfumu ya Israyeli. (1 Samueli 20:12-17) Yonatani, monga kholo loopa Mulungu la Mefiboseti ndiponso bwenzi lokhulupirika la Davide, sakanaphunzitsa mwana wake kuti azilakalaka kutenga ufumu.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• N’chifukwa chiyani mavuto amene timakumana nawo tingawafanizire ndi minga m’thupi?
• Kodi ndi minga ina iti imene Mefiboseti ndi Nehemiya analimbana nayo?
• Mwa zitsanzo za m’Malemba za amuna ndi akazi amene anapirira minga yosiyanasiyana m’thupi lawo, ndi zitsanzo ziti zimene zakukhudzani mtima kwambiri, ndipo chifukwa chiyani?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 15]
Mefiboseti analimbana ndi kupunduka kwake, kum’neneza, ndi kum’khumudwitsa
[Chithunzi patsamba 16]
Nehemiya anapirira ngakhale anam’tsutsa kwambiri