Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kusungabe Chikumbumtima Chabwino Tingakuvutikire Mpaka Pati?

Kodi Kusungabe Chikumbumtima Chabwino Tingakuvutikire Mpaka Pati?

Kodi Kusungabe Chikumbumtima Chabwino Tingakuvutikire Mpaka Pati?

“BOMA Analilamula Kuti Lilandire Ndalama Zokwana R$ 20,000.” Umenewu ndi mutu wankhani wodabwitsa kwambiri umene unalembedwa posachedwapa m’nyuzipepala ina ya ku Brazil ya Correio do Povo. Nkhaniyo inasimba za mwamuna wina dzina lake Luiz Alvo de Araújo, yemwe anagulitsa malo ku boma. Iye amagwira ntchito yotenga ndi kupereka makalata m’dera lakumeneko. Atapereka malowo, Luiz anadabwa kuona kuti walandira ndalama zochuluka kuposa zomwe anagwirizana. Ndalama zowonjezerazo zinali zokwanira R$20,000, (pafupifupi madola 8,000 a ku United States).

Kubweza ndalama zowonjezerazo kunavuta kwambiri. Atapita ku madipatimenti a boma ambirimbiri koma wosaphula kanthu, Luiz analangizidwa kugula loya kuti akathetse nkhaniyi ku khoti. Woweruza amene analamula kuti boma lilandire ndalama zowonjezerazo ndi kulipira ndalama zomwe zinawonongedwa pamlanduwo anati: “Zikuoneka kuti wina wake anaphonyetsa penapake, ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mafomu ndiponso ndondomeko zovuta kuzitsatira, palibe ankadziŵa mmene angathetsere nkhaniyo. Mlandu wotere sindinauonepo n’kale lonse.”

Luiz, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, anafotokoza kuti: “Chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo sichingandilole kutenga chinthu chomwe sichili changa. Ndinayenera kuyesetsa kuti ndibweze ndalamazo.”

Ena angaone kuti mtima ngati umenewu ndi wodabwitsa kapena wovuta kuumvetsa. Koma Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Akristu oona amaona kusungabe chikumbumtima chabwino kukhala nkhani yofunika kwambiri akamachita zinthu ndi maboma. (Aroma 13:5) Mboni za Yehova zili zotsimikiza mtima kusungabe ‘chikumbumtima chokoma ndiponso kukhala oona mtima m’zinthu zonse.’​—Ahebri 13:18, NW.