Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbana ndi “Munga M’thupi”

Kulimbana ndi “Munga M’thupi”

Kulimbana ndi “Munga M’thupi”

“Chisomo changa chikukwanira.”​—2 AKORINTO 12:9.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani sitifunika kudabwa kuti tikukumana ndi mayesero ndi mavuto? (b) N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chidaliro ngakhale tikukumana ndi mayesero?

“ONSE akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12) N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti Satana amalimbikira kunena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera basi, ndipo akuyesetsa mwa njira iliyonse imene angathe kuti atsimikize mfundo yakeyi. Yesu nthaŵi ina anachenjeza atumwi ake kuti: “Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu.” (Luka 22:31) Yesu anadziŵa bwino kuti Mulungu amalola Satana kutiyesa pogwiritsa ntchito mavuto oŵaŵa kwambiri. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti vuto lililonse limene tingakumane nalo limachokera kwa Satana kapena ziwanda zake. (Mlaliki 9:11) Koma Satana ndi wokonzeka kugwiritsa ntchito njira iliyonse imene angathe kuti aswe kukhulupirika kwathu.

2 Baibulo limatiuza kuti tisadabwe ndi mayesero athu. Vuto lililonse limene lingatigwere silachilendo kapena losayembekezeka. (1 Petro 4:12) Ndipotu, “zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale [athu] ali m’dziko.” (1 Petro 5:9) Lerolino, Satana akuvutitsa modetsa nkhaŵa mtumiki aliyense wa Mulungu. Mdyerekezi amasangalala kutiona tikuvutika ndi mavuto ambiri onga minga. Pofuna kukwaniritsa zimenezo, iye amagwiritsa ntchito dongosolo lake la zinthu mwa njira yoti liwonjezere kapena kukulitsa ‘minga iliyonse imene ili m’thupi lathu.’ (2 Akorinto 12:7) Komabe, mavuto amene Satana amabweretsa asaswe kukhulupirika kwathu. Monga mmene zilili kuti Yehova “adzaikanso populumukirapo” kuti tipirire mayesero, adzachitanso chimodzimodzi tikakumana ndi mavuto onga minga m’thupi lathu.​—1 Akorinto 10:13.

Mmene Tingalimbanire ndi Munga

3. Kodi Yehova anayankha motani pamene Paulo anapempha kuti am’chotse munga umene unali m’thupi lake?

3 Mtumwi Paulo anapempha Mulungu kuti achotse munga umene unali m’thupi lake. “Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.” Kodi Yehova anayankha motani pempho la Paulo lochokera pansi pa mtima? “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa [“imakhala yangwiro,” NW] m’ufoko.” (2 Akorinto 12:8, 9) Tiyeni tipende yankho limeneli ndi kuona mmene lingatithandizire kulimbana ndi mavuto alionse onga munga amene akutipweteka.

4. Kodi Paulo anapindula ndi chifundo cha Yehova m’njira zotani?

4 Onani kuti Mulungu analimbikitsa Paulo kuti aziyamikira chifundo chimene anali atalandira kale kudzera mwa Kristu. Zoonadi, Paulo anadalitsidwa m’njira zambiri. Yehova anam’patsa mwachikondi mwayi wapadera wokhala wophunzira wa Yesu ngakhale kuti iye ankatsutsa kwambiri otsatira a Yesu. (Machitidwe 7:58; 8:3; 9:1-4) Kenako, Yehova mwachifundo anam’patsa Paulo mautumiki ena abwino kwambiri. Phunziro limene tikutengapo pamenepa n’loonekeratu. Ngakhale pamene tili m’mavuto aakulu, tidakali ndi madalitso ambiri amene tingayamikire. Tisaloletu kuti mayesero amene tikukumana nawo atiiwalitse zabwino zambiri zimene Yehova amatichitira.​—Salmo 31:19.

5, 6. (a) Kodi Yehova anaphunzitsa motani Paulo kuti mphamvu ya Mulungu “imakhala yangwiro m’ufoko”? (b) Kodi chitsanzo cha Paulo chinatsimikizira motani kuti Satana ndi wabodza?

5 Chifundo cha Yehova n’chokwanira m’njira inanso. Mphamvu ya Yehova ndi yokwanira kutithandiza m’mayesero athu. (Aefeso 3:20) Yehova anaphunzitsa Paulo kuti mphamvu ya Mulungu “imakhala yangwiro m’ufoko.” Motani? Iye anam’patsa Paulo mphamvu zonse zimene anafunikira kuti alimbane ndi mayesero ake. Ndiyeno, kupirira kwa Paulo ndi kukhulupirira kwake Yehova kotheratu, kunavumbula kwa Akristu onse kuti mphamvu ya Mulungu inagwira ntchito mwachipambano mwa munthu wofooka ndi wochimwa ameneyu. Tsono taganizani mmene zimenezi zinakhudzira Mdyerekezi, amene amanena kuti anthu amatumikira Mulungu akakhala kuti zinthu zikuwayendera bwino m’moyo wawo ndipo alibe mavuto alionse. Kukhulupirika kwa Paulo kunam’pweteka mtima woneneza ameneyu.

6 Pauloyu kale anali kuthandizira Satana kulimbana ndi Mulungu, anali kuzunza mwankhanza Akristu, anali Mfarisi wachangu amene mosakayika anali ndi moyo wapamwamba chifukwa chakuti anabadwira ku banja lolemera. Paulo tsopano anali kutumikira Yehova ndi Kristu monga “wamng’ono wa atumwi.” (1 Akorinto 15:9) Motero, iye ankagonjera ulamuliro wa bungwe lolamulira lachikristu la m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Ndipo anali kupirira mokhulupirika ngakhale kuti anali ndi munga m’thupi. Satana anakhumudwa kwambiri kuona kuti mayesero amene Paulo anakumana nawo sanabwezere m’mbuyo changu chake. Paulo sanaiwale chiyembekezo chake choti akalamulira nawo mu Ufumu wakumwamba wa Kristu. (2 Timoteo 2:12; 4:18) Palibe munga umene ukanachepetsa changu chake ngakhale ukanakhala wopweteka bwanji. Tiyenitu nafenso changu chathu chikhalebe champhamvu. Mwa kutithandiza m’mayesero athu, Yehova akutikweza potipatsa mwayi wothandiza kutsimikiza kuti Satana ndi wabodza.​—Miyambo 27:11.

Zimene Yehova Amapereka N’zofunika Kwambiri

7, 8. (a) Kodi Yehova amapatsa mphamvu atumiki ake lerolino mwa njira ziti? (b) N’chifukwa chiyani kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kuliphunzira kuli kofunika kwambiri kuti tilimbane ndi munga m’thupi lathu?

7 Lerolino, Yehova amapereka mphamvu kwa Akristu okhulupirika mwa mzimu wake woyera, Mawu ake, ndi ubale wathu wachikristu. Monga mmene anachitira mtumwi Paulo, tingatule nkhaŵa zathu kwa Yehova m’pemphero. (Salmo 55:22) Ngakhale kuti Mulungu mwina sangachotse mayesero athu, iye angatipatse nzeru zoti tithe kulimbana nawo, ngakhale atakhala ovuta kwambiri kuwapirira. Yehova angatipatsenso mphamvu, “mphamvu yoposa yachibadwa,” kuti itithandize kupirira.​—2 Akorinto 4:7, NW.

8 Kodi timalandira motani thandizo limenelo? Tiyenera kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu chifukwa m’menemo ndi mmene tingapeze chilimbikitso chake chotsimikizika. (Salmo 94:19) M’Baibulo, timaŵerenga mawu okhudza mtima a atumiki a Mulungu pamene anali kupempherera kuti awathandize. Mayankho a Yehova amene nthaŵi zambiri anaphatikizapo mawu olimbikitsa, ndi ofunika kuti tiwasinkhesinkhe. Kuphunzira Mawu a Mulungu kudzatilimbitsa kuti “mphamvu yoposa yachibadwa ikhale ya Mulungu ndipo osati yochokera mwa ife eni.” Monga mmene timafunikira kudya chakudya chakuthupi tsiku lililonse kuti tikhale ndi mphamvu ndiponso thanzi labwino, tiyeneranso kudya mawu a Mulungu nthaŵi zonse. Kodi timachita zimenezi? Ngati timatero, ndiye kuti tidzaona kuti kulandira kwathu “mphamvu yoposa yachibadwa” kumatithandiza kupirira minga iliyonse yophiphiritsa imene tingamavutike nayo.

9. Kodi akulu angathandize bwanji anthu amene akulimbana ndi mavuto?

9 Akulu achikristu oopa Mulungu angakhale “pobisalira mphepo” ya kuvutika maganizo, “pousira chimphepo” cha mavuto. Akulu, amene amafuna kufanana ndi mmene mawu ouziridwaŵa akufotokozera, amapempha Yehova modzichepetsa ndiponso moona mtima kuti awapatse “lilime la ophunzira” n’cholinga choti adziŵe mmene angayankhire anthu ovutika pogwiritsa ntchito mawu oyenera. Mawu a akulu angakhale ngati mvula yowaza imene ingaziziritse ndi kutonthoza mitima yathu pamene tili ndi mavuto. Mwa ‘kulimbikitsa amantha [“opwetekedwa,” NW] mtima,’ akulu amathandizadi abale ndi alongo awo auzimu amene angakhale akufooka kapena kutaya mtima chifukwa cha minga imene ili m’thupi lawo.​—Yesaya 32:2; 50:4; 1 Atesalonika 5:14.

10, 11. Kodi atumiki a Mulungu angalimbikitse bwanji anzawo amene akuvutika ndi mayesero aakulu?

10 Atumiki onse a Yehova ali mbali ya banja lake lachikristu logwirizana. Inde, ndife “ziŵalo zinzake, wina ndi wina,” ndipo “tiyenera kukondana wina ndi mnzake.” (Aroma 12:5; 1 Yohane 4:11) Kodi timakwaniritsa bwanji kukondana kumeneku? Malinga ndi 1 Petro 3:8 timachita zimenezo mwakukhala “ochitirana chifundo, okondana ndi abale, [ndiponso mwakukhala] achisoni” kwa Akristu anzathu. Kwa amene akulimbana ndi minga inayake yopweteka m’thupi mwawo, kaya ndi ana kapena achikulire, tonsefe tingawaganizire mwapadera. Motani?

11 Tiyenera kuyesetsa kudera nkhaŵa mavuto awo. Tingakulitse vuto lawolo mosadziŵa ngati sitiwamvera chisoni, kusawadera nkhaŵa, ndiponso kusonyeza ngati sizikutikhudza. Kudziŵa kwathu za mayesero awo kuyenera kutichititsa kusamala zimene tingalankhule, mmene tingalankhulire, ndiponso mmene tikuchitira. Kukhala ndi chiyembekezo chakuti zinthu zidzakhala bwino ndiponso kuwalimbikitsa kungathandize kuchepetsa kuwawa kwambiri kwa munga umene ukuwavutitsa. Mwakuchita zimenezi tingakhale owatonthoza mtima.​—Akolose 4:11.

Mmene Okhulupirika Ena Apambanira Polimbana ndi Mayesero

12-14. (a) Kodi Mkristu wina anachita chiyani kuti apirire matenda ake a kansa? (b) Kodi abale ndi alongo auzimu a mkaziyu anam’thandiza ndi kum’limbikitsa motani?

12 Pamene tikuyandikira mapeto a masiku otsiriza ano, “zowawa” zikuwonjezereka tsiku lililonse. (Mateyu 24:8) Motero, mayesero angagwere munthu wina aliyense padziko lapansi, makamaka atumiki okhulupirira a Yehova amene akuyesetsa kuchita zimene iye amafuna. Mwachitsanzo, taganizani za mlongo wachikristu wina amene ankachita utumiki wa nthaŵi zonse. Iye anadwala kansa ndipo anafunika kum’chita opaleshoni kuti am’chotse kachiŵalo kamene kamapanga malovu ndiponso kuti am’chotse anabere. Iye ndi mwamuna wake atadziŵa kuti ali ndi matenda ameneŵa, nthaŵi yomweyo anapemphera kwa Yehova pemphero lalitali lochokera pansi pa mtima. Patapita nthaŵi iye ananena kuti anapeza mtendere womwe sankaganiza kuti angakhale nawo. Komabe, iye anapirira ndi kusinthasintha kwa thanzi lake, koma makamaka zotsatirapo za opaleshoniyo.

13 Mlongoyu polimbana ndi matenda akeŵa, anayesetsa kudziŵa zambiri za kansa. Anali kufunsa madokotala ake. Mu Nsanja ya Olonda, Galamukani!, ndi zofalitsa zachikristu zonga zimenezi, anapeza mbiri ya miyoyo ya anthu ena yosonyeza mmene analimbanira ndi matenda ameneŵa. Anapezanso ndime zina za m’Baibulo zogwirizana ndi nkhani imeneyi zosonyeza kuti Yehova amathandiza anthu ake m’nthaŵi za mavuto, ndiponso nkhani zina zothandiza.

14 Nkhani ina yonena za kulimbana ndi kutaya mtima inagwira mawu mfundo yanzeru yakuti: “Wopanduka afunafuna chifuniro chake.” (Miyambo 18:1) Motero, nkhaniyo inalangiza kuti: ‘Pewani kukhala panokha.’ * Mlongoyu anasimba kuti: “Ambiri anandiuza kuti anali kundipempherera. Ena ankandiimbira mafoni. Akulu aŵiri ankandiimbira foni nthaŵi zonse kuti adziŵe mmene ndinalili. Ndinali kulandira maluŵa ndi makadi a mafuno abwino ambirimbiri. Ena mpaka ankandikonzera chakudya. Ndiponso ambiri ankadzipereka kunditenga kupita nane kuchipatala.”

15-17. (a) Kodi mlongo wina wachikristu analimbana bwanji ndi mavuto amene anabwera chifukwa chochita ngozi? (b) Kodi anthu a mumpingo anam’thandiza motani?

15 Mtumiki wina wa Yehova wamkazi ku New Mexico, U.S.A., amene anatumikira kwa nthaŵi yaitali, anachita ngozi ya galimoto kaŵiri konse. Anavulala khosi ndi mapewa zimene zinawonjezera matenda a nyamakazi amene anakhala akuvutika nawo kwa zaka 25. Iye anasimba kuti: “Ndimavutika kutukula mutu wanga ndi kunyamula chinthu chilichonse cholemera makilogalamu aŵiri. Koma kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kwandithandiza kwambiri. Nkhani zimene taphunzira mu Nsanja ya Olonda zandithandizanso kwambiri. Wina anapereka ndemanga pa Mika 6:8, ndipo anafotokoza kuti kudzichepetsa poyenda ndi Mulungu kumatanthauza kuzindikira kuti mphamvu kapena nzeru zathu zili ndi malire. Zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti ngakhale ndinali kudwala, sindinayenera kukhumudwa, ngakhale kuti nthaŵi imene ndinkathera mu utumiki inali yochepa kwambiri kusiyana ndi mmene ndinkafunira. Chofunika kwambiri ndicho kum’tumikira ndi zolinga zabwino.”

16 Iye anasimbanso kuti: “Akulu ankandiyamikira nthaŵi zonse chifukwa choyesetsa kupezeka pa misonkhano ndi kuloŵa nawo muutumiki wakumunda. Achinyamata anali kundikumbatira pondipatsa moni. Apainiya anali kuleza nane mtima ndipo nthaŵi zambiri anali kusintha ndandanda yawo pamene ndinali kudwala kwambiri kwakuti sindikanatha kuloŵa m’munda. Pamene nyengo sinali bwino, iwo mwachifundo ankapita nane ku maulendo obwereza kapena kundipempha kuti ndikhale nawo pa maphunziro awo a Baibulo. Ndiponso popeza sindinkatha kunyamula chikwama cha mabuku, ofalitsa ena ankaika mabuku anga m’zikwama zawo ndikamapita kolalikira.”

17 Onani mmene akulu mumpingo ndi okhulupirira anzawo anathandizira alongo aŵiriŵa ndi matenda awo omwe anali ngati minga. Anawathandiza mwachifundo pofuna kukwaniritsa zosoŵa zenizeni zauzimu, zakuthupi ndiponso zamaganizo. Kodi zimenezi sizikukulimbikitsani kuti muthandize abale ndi alongo ena amene akuvutika? Inunso achinyamata mungathandize anthu a mumpingo wanu amene akuvutika ndi minga m’thupi lawo.​—Miyambo 20:29.

18. Kodi nkhani zosimba miyoyo ya anthu ena zimene zimafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zingatilimbikitse motani?

18 Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! afalitsa nkhani zosimba miyoyo ndi zokumana nazo za Mboni zimene zalimbana ndipo zikulimbanabe ndi mavuto m’moyo wawo. Mukamaŵerenga nkhani zimenezi kaŵirikaŵiri, mudzaona kuti abale ndi alongo anu auzimu ambiri padziko lonse apirira mavuto a zachuma, kumwalira kwa okondedwa awo panthaŵi ya tsoka, ndiponso nkhondo zoopsa. Ena akuvutika ndi matenda amene akuwalepheretsa kuchita zinthu zina. Ambiri sangathe kuchita ntchito zina zing’onozing’ono zimene anthu amene ali bwino amaziona kuti n’zosavuta. Matenda awowo amawayesa kwambiri, makamaka akamalephera kuchita nawo ntchito zachikristu monga mmene ankafunira. Amayamikiratu kwambiri zimene abale ndi alongo awo, ana ndiponso achikulire, amachita powathandiza ndi kuwalimbikitsa.

Kupirira Kumabweretsa Chimwemwe

19. N’chifukwa chiyani Paulo anasangalala ngakhale kuti anakumana ndi mayesero onga minga ndiponso anali ndi zofooka?

19 Paulo anasangalala kuona mmene Mulungu anamulimbitsira. Iye anati: “Makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m’maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine. Chifukwa chake ndisangalala m’maufoko, m’ziwawa, m’zikakamizo, m’mazunzo, m’zipsinjiko, chifukwa cha Kristu; pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:9, 10) Paulo, chifukwa cha zimene anakumana nazo, ananena mtima uli m’malo kuti: “Si kuti ndinena monga mwa chipereŵero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. Ndadziŵa ngakhale kupeputsidwa, ndadziŵanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:11-13.

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani tingapeze chimwemwe posinkhasinkha “zinthu zosaoneka”? (b) Kodi ndi “zinthu zosaoneka” zina ziti zimene mukuyembekeza kudzaziona m’paradaiso padziko lapansi?

20 Ndiyetu, mwakupirira munga wophiphiritsa uliwonse umene ungakhale m’thupi lathu, tingapeze chimwemwe chochuluka posonyeza aliyense kuti mphamvu za Yehova zikukhala zangwiro m’ufoko wathu. Paulo analemba kuti: “Sitifoka . . . Umunthu wathu . . . wa m’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthaŵi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; popeza tipenyerera . . . zinthu zosaoneka; pakuti . . . zinthu zosaoneka zili zosatha.”​—2 Akorinto 4:16-18.

21 Anthu a Yehova ambiri lerolino akuyembekeza kudzakhala m’Paradaiso padziko lapansi ndi kudzasangalala ndi madalitso amene iye walonjeza. Tinganene kuti madalitso amenewo ‘sitikuwaona’ lerolino. Komabe, nthaŵi ikuyandikira kwambiri pamene tidzaona madalitso amenewo ndi maso athu, inde, kudzasangalala nawo kosatha. Limodzi mwa madalitso amenewo lidzakhala lakuti sitidzakhalanso ndi vuto lililonse longa munga. Mwana wa Mulungu ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi’ ndi ‘kuwononga iye amene ali nayo mphamvu ya imfa.’​—1 Yohane 3:8; Ahebri 2:14.

22. Kodi tifunika kukhala ndi chikhulupiriro ndi kutsimikiza mtima kotani?

22 Motero, kaya ndi munga wotani m’thupi lathu umene ukutivutitsa lerolino, tiyeni tipitirizebe kulimbana nawo. Monga Paulo, tidzapeza mphamvu zochitira zimenezo kwa Yehova, amene amatipatsa mphamvu mooloŵa manja. Nthaŵi imene tidzakhala m’paradaiso padziko lapansi, tidzalemekeza Yehova Mulungu wathu tsiku lililonse chifukwa cha ntchito zazikulu zimene amatichitira.​—Salmo 103:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: Njira Yogonjetsera Kutaya Mtima,” mu Galamukani! ya May 8, 2000.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani Mdyerekezi amayesa kuswa kukhulupirika kwathu, ndipo amachita zimenezo motani?

• Kodi mphamvu ya Yehova “imakhala yangwiro m’ufoko” motani?

• Kodi akulu ndi anthu ena angalimbikitse motani anthu amene akulimbana ndi mavuto?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Paulo anapempha Mulungu katatu konse kuti am’chotse munga m’thupi lake