Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Peŵani Kudzikuza

Peŵani Kudzikuza

Peŵani Kudzikuza

MUNTHU wodzikuza amadziona ngati wofunika kwambiri, wapamwamba kuposa anthu ena onse. Zotsatira zake zimakhala zakuti munthu wotero nthaŵi zambiri amafuna kuti anthu azim’lemekeza ndi kum’tama mopitirira muyeso ndipo iye salemekeza anthu ena.

Kudzikuza n’kotsutsana ndi kudzichepetsa. Mawu a Chigiriki ndi Chihebri amene anawamasulira kuti “wodzikuza” ndiponso “kudzikuza,” kwenikweni amatanthauza kudzionetsera kukhala “wapamwamba,” “wokwezeka,” “wofunika kwambiri,” “wotchuka.”

Khalidwe la Mumtima

Kudzikuza ndi khalidwe loipa lomwe n’lozama kuposa zimene munthu akuganiza chabe. Yesu Kristu anatchula kudzikuza pamodzi ndi kupha, kuba, mwano, ndi zoipa zina ndipo anati “mkati mwake mwa mitima ya anthu,” ndi mmene mumatuluka zinthu ngati zimenezi. (Marko 7:21, 22) Mayi ake a Yesu a padziko lapansi, Mariya, ananena za Yehova kuti: ‘Iye anabalalitsa odzitama [“odzikuza,” NW] ndi m’lingaliro wa mtima wawo.’ (Luka 1:51) Davide anauza Yehova kuti: “Mtima wanga sunadzikuza.”​—Salmo 131:1.

Ngakhale munthu amene mtima wake unali wodzichepetsa potumikira Mulungu angakhale wodzikuza chifukwa cholemera kapena kukhala ndi ulamuliro kapena chifukwa chakuti ndi wokongola, zinthu zimamuyendera bwino, ndi wanzeru, kapena chifukwa chakuti ena amam’tama. Mfumu Uziya ya Yuda inachita zimenezi. Anali kulamulira bwino ndipo analandira madalitso a Yehova kwa zaka zambiri.​—2 Mbiri 26:3-5.

Koma Baibulo likuti: “Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuwononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analoŵa m’Kachisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la chofukiza.” (2 Mbiri 26:16) Uziya anadzikuza n’kuchita ntchito ya ansembe. Mulungu sanapatse mafumu a Israyeli ntchito imeneyi, zimene zinachititsa kuti ufumu ndi unsembe zikhale zinthu zosiyana.

Nthaŵi ina Mfumu yabwino Hezekiya, kwakanthaŵi kochepa, anakhala ndi mtima wodzikuza, ndipo mosakayika kudzikuza kwake kunafalikira kwa anthu amene anali kuwalamulira. Ulamuliro wake unali utakwezedwa chifukwa cha madalitso a Yehova, koma analephera kuzindikira kuti Mulungu ndi amene anayenera kulandira ulemu wonse. Wolemba mbiri ananena za iye kuti: “Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa chokoma anam’chitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unam’dzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.”

N’zosangalatsa kuti anasiya mtima wachabewu. Nkhaniyo ikupitiriza kuti: “Koma Hezekiya anadzichepetsa m’kudzikuza kwa mtima wake, iye ndi okhala m’Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.”​—2 Mbiri 32:25, 26.

Mulungu Amadana ndi Kudzikuza

Anthu oona mtima amanyansidwa ndi anthu odzikuza ndipo koposa amenewo, Yehova Mulungu amada odzikuzawo. (Yakobo 4:6) Kudzikuza n’kupusa ndiponso n’kuchimwa, ndipo Yehova amadana ndi odzikuza ndi kuwachepetsa.​—Miyambo 14:3; 2 Samueli 22:28; Yobu 40:11.

Ngati munthu sasiya kudzikuza, khalidwe lakelo lidzamuwononga. Mtundu wakale wa Moabu umene unadzikuza kulimbana ndi Mulungu ndi anthu ake, unawonongedwa. (Yesaya 16:6; 25:10, 11) Ngakhale Ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi sanaulekerere pamene unayamba kudzikuza ndi kuchita mwano.​—Yesaya 9:8-12.

Kupeŵa Kudzikuza

Motero, munthu afunika kusamala kuti asakhale ndi mtima wodzikuza. Afunika kusamala makamaka akakhala kuti zimene akuchita zikumuyendera bwino kapena akapatsidwa maudindo aakulu. Afunika kukumbukira kuti ‘kunyada kutsogolera kukuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.’​—Miyambo 16:18.

Ngati alekerera kuti kudzikuza kukule, kudzayamba kum’lamulira kufika poti Yehova adzamuika m’gulu la anthu amene Iye amawada, ndiponso amene akuyenerera kuphedwa. (Aroma 1:28, 30, 32) Chenjezo limeneli n’lofunika kwambiri makamaka mu “masiku otsiriza,” pamene kudzikuza kudzakhala chimodzi mwa zizindikiro za nthaŵi zowawitsa zimenezo, monga mmene mtumwi Paulo anachenjezera.​—2 Timoteo 3:1, 2.

Ndiponso, munthu amene akufuna kuti Mulungu amuyanje afunika kupeŵa kusyasyalika, kumene kumapangitsa kuti ena azidzikuza. Mwambi wina umati: “Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde.”​—Miyambo 29:5.

Kuphatikiza pa kuwononga mnzake, munthu wosyasyalika sayanjidwa ndi Mulungu. (Miyambo 26:28) Mtumwi Paulo anali wosamala kuti apewe kusyasyalika ndiponso kudzikuza. (1 Atesalonika 2:5, 6) Ifenso tifunika kupitirizabe kupeŵa khalidwe loipa limeneli.