‘Chikondi Chathu Chalimbikitsidwa’
‘Chikondi Chathu Chalimbikitsidwa’
LACHISANU pa March 31, 2000, Phiri la Usu ku Hokkaido, Japan, linaphulika litakhala zaka 23 lisanachitepo zimenezo. Anthu zikwizikwi anathaŵa m’dera la ngozi limenelo. Nyumba za anthu ambiri zinawonongeka ndiponso ntchito zawo zinatha, koma mwamwayi palibe amene anafa. Mboni za Yehova zokwana 46 zinali m’gulu la anthu othaŵawo, koma sizinasiyidwe popanda thandizo.
Mothandizidwa ndi mtumiki woyendayenda wachikristu wa m’deralo, tsiku lomwelo lomwe phirilo linaphulika, njira zothandizira anthu ovutikawo zinakonzedwa. Posapita nthaŵi, katundu wothandizira anthuwo anayamba kufika kuchokera m’mipingo yoyandikana nayo. Komiti yopereka chithandizo inakhazikitsidwa mwamsanga motsogozedwa ndi nthambi ya ku Japan ndipo zinthu zambiri zothandizira ovutikawo zinaperekedwa ndi Mboni za Yehova m’dziko lonse la Japan. Pofuna kuthandiza pa zinthu zauzimu, atumiki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova anatumizidwa ku mipingo yomwe inakhudzidwa kwambiri. Woyang’anira dera anayendera deralo mobwerezabwereza kulimbitsa mitima abale ndiponso kuwalimbikitsa mwauzimu.
Mboni zomwe zinkakhala m’dera lomwe linakhudzidwa ndi vutolo zinapitirizabe kuchita misonkhano yachikristu panthaŵi yovutayo mwa kugwiritsa ntchito nyumba za anthu zomwe zinali m’dera lomwe silinakhudzidwe ndi vutolo. Atalamula kuti anthu atha kubwereranso m’dera lokhudzidwalo komwe kunali Nyumba ya Ufumu, abale anabwerera ndipo anapeza kuti nyumbayo inali yoŵerama ndiponso yogumuka. Pafupi ndi Nyumba ya Ufumuyo, phiri lina linali litangophulika kumene ndipo utsi wakuda unali kutulukabe. Mbonizo zinadzifunsa kuti, ‘Kodi n’kwanzeru kupitiriza kusonkhana m’dera lino? Kodi Nyumba ya Ufumuyi titha kuikonzanso?’
Anagwirizana kuti ndi bwino kumanga Nyumba ya Ufumu yatsopano m’dera lina komwe sikungachitike ngozi zoterozo. Komiti Yamanga Yachigawo inapereka thandizo lofunika pa ntchitoyo. Ndalama zomwe Mboni m’dziko lonselo zinapereka zinagwiritsidwa ntchito kumanga nyumbayo. Malo anapezeka mofulumira, ndipo chifukwa cha anthu ambiri odzipereka, ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu yatsopanoyo inatha mofulumira. Lamlungu, pa July 23, 2000, anthu okwanira 75 anafika pa msonkhano woyamba kuchitikira m’Nyumba ya Ufumu yatsopanoyo. Ambiri amene anafika pa msonkhanowo anali kugwetsa misozi chifukwa cha chimwemwe. Nyumba ya Ufumuyo itapatulidwa mu October chaka chomwecho, mmodzi mwa akulu a mpingowo anati: “Kuphulika kwa phiri kunadzetsa mavuto osaneneka. Koma kumangidwa kwa Nyumba ya Ufumuyi kwasanduliza mantha athu kukhala chimwemwe. Chikondi chathu kwa Yehova ndiponso kwa abale athu achikristu chalimbikitsidwa.”
[Mawu a Chithunzi patsamba 19]
Kuphulika kwa Phiri la Usu: AP Photo/Koji Sasahara