Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungapulumuke Bwanji Mapeto a Dziko Lino?

Kodi Mungapulumuke Bwanji Mapeto a Dziko Lino?

Kodi Mungapulumuke Bwanji Mapeto a Dziko Lino?

BAIBULO limafotokoza kutha kwa dongosolo la zinthu limene lilipoli kukhala “tsiku la mkwiyo, tsiku la masauko ndi lopsinja, tsiku la bwinja ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii.” (Zefaniya 1:15) Mosakayika, inu simungakonde kuyembekezera tsiku ngati limeneli. Komatu, mtumwi Petro analangiza Akristu anzake kuti akhale “akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m’menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu. Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.”​—2 Petro 3:12, 13.

Petro panopa sanali kunena kuti kumwamba kwenikweni ndi dziko lapansi lenilenili zidzawonongedwa. “Miyamba” ndi “dziko lapansi” zimene Petro anali kunena m’nkhani imeneyi zikuimira maboma a anthu a chinyengo ndiponso anthu osaopa Mulungu amene alipo pakalipano. “Tsiku la Yehova” silidzawononga dziko lenilenili koma ‘lidzawonongamo akuchimwa psiti.’ (Yesaya 13:9) Kwa amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse” zimene anthu oipa akuchita masiku ano, tsiku la Yehova lidzakhala tsiku la chipulumutso.​—Ezekieli 9:4.

Ndiyeno, kodi anthu angapulumuke bwanji pa “tsiku la Yehova lalikulu loopsa”? “Mawu a Yehova” amene anawavumbula kwa m’modzi mwa aneneri ake amayankha funso limeneli. Mawuwo amati: “Kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.” (Yoweli 1:1; 2:31, 32) Mboni za Yehova n’zokondwa kukuthandizani kuphunzira zimene kuitanira pa dzina la Yehova kumatanthauza.