Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Konzekerani Kumva Kuwawa”

“Konzekerani Kumva Kuwawa”

“Konzekerani Kumva Kuwawa”

KODI munamvapo mawu ameneŵa? Mwina dokotala kapena nesi anakuuzanipo mawuŵa asanapereke chithandizo choyenera chamankhwala.

Mwachionekere, simunakane kulandira mankhwalawo kuti mupewe kuwawa komwe mudzamva. M’malo mwake, munapirira kuwawako kuti mupeza bwino. Nthaŵi zina zinthu zikafika poipa, kuvomera kapena kukana chithandizo chosasangalatsa kungakhale kusankha moyo kapena imfa.

Ngakhale kuti nthaŵi zonse sitingafunikire chithandizo cha dokotala, tonsefe monga anthu opanda ungwiro timafunikira chilango, kapena kuwongoleredwa, ngakhale kuti zimenezo nthaŵi zina zingakhale zopweteka. (Yeremiya 10:23) Potsindika kufunika kwa chilango kwa ana, Baibulo limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yom’langira idzauingitsira kutali.”​—Miyambo 22:15.

Nthyole panopa ikuimira malangizo a makolo. N’zoona kuti ndi ana oŵerengeka chabe amene amakonda malangizo. Ana angakwiye ndi malangizo ngati akuphatikizapo chilango chamtundu wina wake. Komabe, makolo anzeru ndiponso achikondi amaona ubwino wa chilangocho kuposa kuwawidwa mtima komwe mwanayo angakhale nako. Makolo achikristu amadziŵa kuti Mawu a Mulungu ndi oona pamene amati: “Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”​—Ahebri 12:11; Miyambo 13:24.

N’zoona kuti si ana okha amene amafunika chilango. Achikulire nawonso amafunika chilango. Baibulo limalankhula ndi achikulire pamene limati: “Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.” (Miyambo 4:13) Inde, anthu anzeru​—ana ndi achikulire omwe​—adzalandira chilango chochokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo, chifukwa chakuti kutero kudzapulumutsa moyo wawo m’tsogolo.