Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira ndi Mzimu Wodzimana

Kutumikira ndi Mzimu Wodzimana

Mbiri ya Moyo Wanga

Kutumikira ndi Mzimu Wodzimana

YOSIMBIDWA NDI DON RENDELL

Mayi anga anamwalira ndili ndi zaka zisanu zokha mu 1927. Komabe, chikhulupiriro chawo chinakhudza kwambiri moyo wanga. Kodi zimenezo zinatheka bwanji?

MAYI anga anali a Tchalitchi cha England pamene ankakwatiwa ndi bambo anga omwe anali msilikali. Zimenezo zinachitika nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanayambe. Nkhondoyo itaulika mu 1914, Mayi sanagwirizane ndi mbusa wa tchalitchi chifukwa chogwiritsa ntchito gome lake monga tebulo lolembetserapo asilikali. Kodi akuluakulu a tchalitchilo anati chiyani? Anati: “Bwerera kunyumba, usavutike ndi mafunso ngati amenewo!” Izi sizinawagwire mtima amayi.

Mu 1917, nkhondoyo itafika pachimake, Mayi anapita kukaonerera “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe.” Atakhutira kuti apeza choonadi, iwo nthaŵi yomweyo analeka kupita ku tchalitchi chawo n’kugwirizana ndi Ophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinkadziŵika nalo panthaŵiyo. Iwo ankasonkhana ndi mpingo wa ku Yeovil, tauni yapafupi ndi mudzi wathu wa West Coker, m’chigawo cha Somerset, ku England.

Mayi mwamsanga anauza akulu awo aŵiri ndi mng’ono wawo za chipembedzo chomwe anali atachipeza kumenecho. Anthu akale mumpingo wa Yeovil anandiuza mmene mayi ndi mng’ono wawo Millie ankazungulira gawo lakumudzi lalikululo panjinga kugaŵira buku lothandizira kuphunzira Baibulo lakuti Studies in the Scriptures. Komabe mwatsoka, miyezi 18 yotsiriza ya moyo wawo, Mayi anadwala kwambiri chifuwa cha TB chomwe chinalibe mankhwala panthaŵiyo.

Kusonyeza Mzimu Wodzimana

Mayi aang’ono a Millie omwe tinkakhala nawo panthaŵiyo, anadwazika Mayi ndiponso kusamalira ine ndi mlongo wanga Joan yemwe anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Mayi atamwalira, iwo nthaŵi yomweyo anadzipereka kuti atilera. Bambo chifukwa chofuna kumasuka ku udindo wolera ana, anavomera mosavuta kuti tizikhala ndi Mayi aang’ono a Millie.

Tinkawakonda kwambiri mayi aang’ono ndipo tinali osangalala kuti apitiriza kukhala nafe. Koma n’chifukwa chiyani anaganiza zotilera? Patapita zaka zambiri, iwo anatiuza kuti anadziŵa kuti ali ndi udindo wophunzitsa Joan ndi ine choonadi cha m’Baibulo chomwe Mayi anali atayala kale maziko ake, zomwe ankadziŵa kuti bambo sakanatha kuchita chifukwa analibe chidwi ndi chipembedzo.

Kenaka, tinadziŵanso kuti Mayi aang’onowa anali atasankhanso chinthu china. Pofuna kutisamalira mokwanira, iwo anasankha kusakwatiwa. Kunalitu kudzimana zedi! Joan ndi ine tikuwathokoza kwambiri. Zonse zomwe anatiphunzitsa ndiponso chitsanzo chawo chabwino sitidzaziiŵala.

Nthaŵi Yosankha Zochita

Joan ndi ine tinkapita ku sukulu ya Tchalitchi cha England ya m’mudzimo komwe Mayi aang’ono sanagonje kwa mphunzitsi wamkulu wapasukulupo pankhani ya maphunziro athu achipembedzo. Pamene ana ena ankapita ku tchalitchi, ife tinkapita kunyumba ndipo mbusa wa tchalitchi ankati akabwera kusukuluko kudzapereka malangizo achipembedzo, ife tinkakhala kwatokha ndipo ankatipatsa ndime za m’Malemba kuti tiloweze. Zimenezi zinadzandithandiza kwambiri m’tsogolo chifukwa chakuti ndime zimenezo sizinachoke m’maganizo mwanga.

Ndinasiya sukulu ndili ndi zaka 14 ndipo ndinayamba kosi ya zaka zinayi ku kampani ina yopanga tchizi. Ndinaphunziranso kuimba piyano, nyimbo, ndiponso ndinkakonda kuvina. Ngakhale kuti choonadi cha m’Baibulo chinazika mizu mumtima mwanga, chinali chisanandilimbikitsepo kuchita zinthu. Kenako tsiku lina mu March 1940, Mboni ina yachikazi yachikulire inandipempha kuti tipite limodzi ku msonkhano waukulu ku Swindon, mtunda wa makilomita pafupifupi 110. Albert D. Schroeder yemwe anali mtumiki woimira Mboni za Yehova ku Britain ndiye anakamba nkhani yaikulu. Moyo wanga unasinthiratu pa msonkhano umenewo.

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inali mkati. Kodi ndinali kuchita chiyani chaphindu ndi moyo wanga? Ndinaganiza zobwerera ku Nyumba ya Ufumu ya ku Yeovil. Pa msonkhano woyamba womwe ndinapezekapo, ntchito yolalikira munsewu inayamba. Ngakhale kuti ndinkadziŵa zochepa, ndinadzipereka kuchita nawo ntchitoyo. Zimenezi zinadabwitsa kwambiri amene ndinkati ndi anzanga ndipo ankandiseka akamadutsa.

Mu June 1940, ndinabatizidwa mumzinda wa Bristol. Mwezi umodzi usanathe ndinalembetsa upainiya wanthaŵi zonse​—dzina la wolalikira wa nthaŵi zonse. Kenako patapita nthaŵi pang’ono, ndinali wosangalala kwambiri pamene mlongo wanga nayenso anasonyeza kudzipatulira kwake mwa kubatizidwa.

Kuchita Upainiya Nthaŵi ya Nkhondo

Patatha chaka chimodzi nkhondo itayamba, ndinalandira kalata yondiitana kukayamba usilikali. Popeza ndinali n’talembetsa ku Yeovil monga munthu wosaloŵa usilikali pazifukwa za chipembedzo, ndinayenera kupita ku khoti ku Bristol. Ndinali n’tagwira ntchito yaupainiya ndi John Wynn ku Cinderford, Gloucestershire, Haverfordwest ndiponso Carmarthen, ku Wales. * Kenako, pamene khoti linkazenga mlandu wanga ku Carmarthen, ndinalamulidwa kukakhala m’ndende ya ku Swansea kwa miyezi itatu ndiponso kuti ndilipire ndalama zokwana mapaundi 25, zomwe zinali ndalama zambiri ndithu nthaŵi imeneyo. Kenako, anandilamula kuti ndikhale miyezi ina itatu m’ndende chifukwa cholephera kupereka ndalamazo.

Panthaŵi yachitatu yozenga mlandu wanga, ndinafunsidwa kuti: “Kodi umadziŵa kuti Baibulo limanena kuti, ‘Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara’?” “Inde ndimadziŵa,” ndinayankha motero, “koma ndifuna ndimalize zomwe vesilo limanena. Limati: ‘ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.’ N’zimene ndikuchita ine.” (Mateyu 22:21) Patapita milungu yoŵerengeka, ndinalandira kalata yondiuza kuti ndili womasuka kusaloŵa usilikali.

Kumayambiriro kwa 1945, ndinaitanidwa ku Beteli ya ku London. M’nyengo yozizira yotsatira, Nathan H. Knorr yemwe ankatsogolera ntchito yolalikira yapadziko lonse, pamodzi ndi mlembi wake Milton G. Henschel, anabwera kudzacheza ku London. Abale achinyamata asanu ndi atatu a ku Britain analembetsa kuti akakhale m’kalasi yachisanu ndi chitatu ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, ndipo ine ndinali mmodzi mwa iwo.

Ntchito Yaumishonale

Pa May 23, 1946, tinayamba ulendo pa sitima yapamadzi yoyenda panthaŵi ya nkhondo yotchedwa Liberty kuchokera pa doko laling’ono la Cornish ku Fowey. Wamkulu wa pa dokolo dzina lake Captain Collins anali wa Mboni za Yehova ndipo pamene tinkanyamuka, analiza belu. Mwachibadwa, tonsefe tinali ndi mantha pamene gombe lonse la ku England sitinali kulionanso. Ulendo wodutsa nyanja ya Atlantic umenewo unali wovuta kwambiri, koma patatha masiku 13, tinafika bwinobwino ku United States.

Kuchita nawo Msonkhano Wateokalase wamayiko wakuti Mitundu Yokondwa ku Cleveland, Ohio, kuyambira pa August 4 mpaka pa 11, 1946, chinali chochitika chosaiŵalika. Nthumwi zokwana 8,000 kuphatikizapo 302 zochokera m’mayiko 32 zinachita nawo msonkhanowo. Pamsonkhanowo magazini a Galamukani! * ndiponso buku lothandizira kuphunzira Baibulo lakuti Mulungu Akhale Woona zinatulutsidwa kwa khamu lachimwemwelo.

Tinamaliza maphunziro a ku Gileadi mu 1947 ndipo Bill Copson ndi ine anatitumiza ku Egypt. Koma tisananyamuke, ndinali n’taphunzira ntchito ya muofesi kuchokera kwa Richard Abrahamson ku Beteli ya ku Brooklyn. Tinafikira ku Alexandria ndipo posakhalitsa ndinazoloŵera moyo wa ku Middle-East. Komabe, kuphunzira Chiarabu kunali kovuta kwambiri moti ndinkachita kugwiritsa ntchito makadi aulaliki a m’zinenero zinayi.

Bill Copson anakhala m’dzikolo kwa zaka zisanu ndi ziŵiri koma ine chitatha chaka chimodzi sizinatheke kukonzetsanso viza yanga, choncho ndinayenera kuchoka m’dzikolo. Chaka chimodzi chautumiki wa umishonale chimenecho ndicho ndimachiona kukhala chopindulitsa kwambiri pa moyo wanga. Ndinali ndi mwayi wochititsa maphunziro a Baibulo apanyumba opitirira 20 mlungu uliwonse, ndipo ena amene anaphunzira choonadi nthaŵi imeneyo akupitirizabe kutamanda Yehova mwachangu. N’tachoka ku Egypt, ananditumiza ku Cyprus.

Ku Cyprus Ndiponso ku Israel

Ndinayamba kuphunzira Chigiriki chomwe chinali chinenero chachilendo ndiponso zinenero zina za m’deralo. Patapita nthaŵi pang’ono, pamene Anthony Sideris anapemphedwa kusamukira ku Greece, ine anandisankha kukhala woyang’anira ntchito ku Cyprus. Panthaŵiyo n’kuti ofesi ya nthambi ya ku Cyprus ikusamaliranso ntchito ya m’dziko la Israel. Ine pamodzi ndi abale ena tinali ndi mwayi wokacheza ndi Mboni zoŵerengeka zomwe zinali m’dzikolo mwa apo ndi apo.

Paulendo wanga woyamba wa ku Israel, tinachita msonkhano waung’ono m’nyumba ina yodyeramo ku Haifa, ndipo anthu okwanira 50 kapena 60 anafika pamsonkhanowo. Mwa kupatula magulu a m’dzikolo, tinachita pulogalamu yonse ya msonkhanowo m’zinenero zisanu ndi chimodzi. Nthaŵi ina, ndinasonyeza filimu yopangidwa ndi Mboni za Yehova mumzinda wa Yerusalemu, ndiponso ndinakamba nkhani ya onse yomwe nyuzipepala ina yachingelezi inalemba zabwino zokhudza nkhaniyo.

Panthaŵiyo ku Cyprus kunali Mboni pafupifupi 100 ndipo zinali kumenya nkhondo yachikhulupiriro chawo mwamphamvu. Magulu achiwembu otsogozedwa ndi ansembe a Tchalitchi cha Greek Orthodox ankasokoneza misonkhano yathu. Kugendedwa ndi miyala pamene ndinkalalikira m’madera akumidzi kunali chinthu chomwe chinali chisanandichitikirepo. Ndinaphunzira kuthaŵa mofulumira zinthu zikathina. M’mavuto ngati amenewo, kunali kolimbikitsa chikhulupiriro kuona amishonale ambiri akutumizidwa pa chilumbacho. Dennis ndi Mavis Matthews pamodzi ndi Joan Hulley ndi Beryl Heywood anafika kudzagwira nane ntchito ku Famagusta, pamene Tom ndi Mary Goulden ndi Nina Constanti wa ku Cyprus, yemwe anabadwira ku London, anapita ku Limassol. Panthaŵi imodzimodziyo, Bill Copson anatumizidwa ku Cyprus, ndipo patapita nthaŵi Bert ndi Beryl Vaisey anafikanso kudzagwira nawo ntchito limodzi.

Kuzoloŵera Kusintha kwa Zinthu

Kumapeto kwa chaka cha 1957, ndinadwala ndipo sindikanapitiriza ntchito yanga ya umishonale. Kuti ndipezenso bwino, ndinaganiza zobwerera ku England koma ndikudandaula. Kumeneko, ndinakapitiriza kuchita upainiya mpaka mu 1960. Mlongo wanga ndi mwamuna wake anali kundisunga m’nyumba yawo koma zinthu zinali zitasintha. Zinthu zinali kumvuta Joan mowonjezereka. Kuwonjezera pa kusamalira mwamuna wake ndi mwana wake wamkazi wamng’ono, zaka zonse 17 zomwe ine kunalibe, iye wakhala akusamaliranso mwachikondi bambo athu ndi Mayi aang’ono a Millie omwe onse panthaŵiyo anali atakalamba ndiponso asakupeza bwino. Kufunika kotsatira chitsanzo cha mayi aang’ono chosonyeza mzimu wodzimana kunali koonekeratu. Choncho, ndinakhala ndi mlongo wanga mpaka pamene mayi aang’ono ndi bambo anamwalira.

Zinali zosavuta kukhazikika ku England, koma n’tapuma kwakanthaŵi kochepa ndinaona kuti ndi bwino kubwereranso ku ntchito yanga ya umishonale. Ndiponsotu, kodi gulu la Yehova silinawononge ndalama zambiri pondiphunzitsa? Motero, mu 1972 ndinadzilipirira ulendo wobwerera ku Cyprus kukachitanso upainiya kumeneko.

Nathan H. Knorr anafika kudzakonza za msonkhano womwe unali kudzachitika chaka chotsatira. Atadziŵa kuti ndinabweranso, anavomereza kuti andiike kukhala woyang’anira dera lonse la chilumbacho, mwayi wamtengo wapatali womwe ndinakhala nawo kwa zaka zinayi. Komabe inali ntchito yochititsa mantha chifukwa ndinkafunikira kulankhula Chigiriki nthaŵi zambiri.

Nthaŵi ya Mavuto

Ndinali kukhala ndi Paul Andreou, Mboni yolankhula Chigiriki ya ku Cyprus, m’nyumba ina yomwe inali m’mudzi wa Karakoumi, kummaŵa kwa Kyrenia, ku gombe lakumpoto la chilumbacho. Ofesi ya nthambi ya ku Cyprus inali ku Nicosia kumwera kwa mapiri a Kyrenia. Kumayambiriro kwa July 1974, ndinali ku Nicosia pamene chiwembu chofuna kuchotsa pulezidenti Makarios paudindo wake chinachitika ndipo ndinaona ndi maso anga nyumba yake ikuyaka moto ndi kugwa. Ziwawazo zitachepa moti munthu n’kutha kuyenda, ndinachoka mwamsanga kupita ku Kyrenia komwe tinkakonzekera kuchita msonkhano. Patangopita masiku aŵiri ndinamva bomba loyamba litaponyedwa pa doko. Ndipo ndinaona ndege za mtundu wa helokoputa zambirimbiri zikubweretsa magulu ankhondo odzalanda dzikolo kuchokera ku Turkey.

Popeza ndinali nzika ya ku Britain, magulu ankhondo a ku Turkey ananditenga kupita nane kunja kwa mzinda wa Nicosia komwe ndinakafunsidwa mafunso ndi wogwira ntchito m’bungwe la United Nations yemwe analankhulana ndi a ku ofesi ya nthambi. Kenako ndinali ndi vuto lodutsa m’dera la ngozi lomwe nthambo za matelefoni ndiponso za magetsi za m’nyumba zomwe anthu anathawamo zinali zokolanakolana. Ndinali wokondwa kwambiri kuti njira yanga yolankhulirana ndi Yehova Mulungu siikanasokonezeka. Mapemphero anga anandilimbikitsa kugonjetsa vuto lalikulu kwambiri limeneli pa moyo wanga.

Katundu wanga yense anali atawonongedwa, koma ndinali wokondwa kuti ofesi ya nthambi inali kunditeteza. Komabe, mavutowo sanatenge nthaŵi yaitali. Patangopita masiku angapo, magulu odzalanda dzikolo anali atayamba kulamulira chimodzi mwa zigawo zitatu zakumpoto za chilumbacho. Zitatero, tinayenera kuchoka ku Beteli, ndipo tinasamukira ku Limassol. Ndinali wosangalala kugwira ntchito ndi komiti yomwe inapangidwa kuti isamalire abale 300 amene anakhudzidwa ndi tsokalo, omwe ambiri mwa iwo nyumba zawo zinali zitawonongedwa.

Kusinthanso Utumiki

Mu January 1981, Bungwe Lolamulira linandipempha kusamukira ku Greece kukakhala pa Beteli ku Athens, koma kumapeto kwa chaka chimenecho, ndinabwereranso ku Cyprus ndipo anandiika kukhala wotsogolera Komiti ya Nthambi. Andreas Kontoyiorgis ndi mkazi wake Maro a ku Cyprus omwe anawatumiza kuchokera ku London, analidi “akundikhalira ine chonditonthoza mtima.”​—Akolose 4:11.

Theodore Jaracz atatha kuchezera nthambi mu 1984, ndinalandira kalata kuchokera ku Bungwe Lolamulira yomwe inangonena kuti: “Mbale Jaracz, akamaliza kuchezera nthambi, tikufuna kuti mutsagane naye popita ku Greece.” Sanatchule chifukwa chilichonse, koma titafika ku Greece, kalata ina yochokera ku Bungwe Lolamulira yondiika kukhala wotsogolera Komiti ya Nthambi inaŵerengedwa kwa mamembala a Komiti ya Nthambi.

Panthaŵiyo ku Greece, kunabuka magulu ambiri ampatuko. Kunalinso milandu yambiri yokhudza kutembenuza anthu koletsedwa. Tsiku ndi tsiku, anthu a Yehova anali kumangidwa ndi kuweruzidwa m’makhoti. Unali mwayi wapadera kwambiri kudziŵana ndi abale ndi alongo omwe anapirira ndi kukhalabe okhulupirika panthaŵi ya mavutowo. Ina mwa milandu yawo inazengedwa ndi khoti la ufulu wachibadwidwe wa anthu la ku Ulaya lotchedwa European Court of Human Rights ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwambiri moti zinachititsa kuti ntchito yolalikira izichitika mosavuta ku Greece. *

Ndikutumikira ku Greece, ndinali ndi mwayi wokachita nawo msonkhano wosaiwalika ku Athens, ku Thessalonica ndiponso pa zilumba za Rhodes ndi Crete. Zinali zaka zinayi zosangalatsa ndiponso zopindulitsa kwambiri, koma kusintha kwina kunali kubwera​—kubwereranso ku Cyprus mu 1988.

Ku Cyprus Ndiponso Kubwerera ku Greece

Panthaŵi yomwe sindinali ku Cyprus, abale kumeneko anapeza malo ndi nyumba za nthambi yatsopano ku Nissou, makilomita oŵerengeka kuchokera ku Nicosia, ndipo Carey Barber wochokera ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn ndiye anakamba nkhani yopatulira nthambiyo. Tsopano pa chilumbacho panali bata ndipo ndinali wokondwa kuti ndinabwereranso. Koma bata limenelo silinakhalitse.

Bungwe Lolamulira linali litavomereza kumangidwa kwa nyumba ya Beteli ku Greece, makilomita angapo kumpoto kwa mzinda wa Athens. Popeza ndinkatha kulankhula Chingelezi ndi Chigiriki, anandipempha kupita ku malo omanga atsopanowo mu 1990 kuti ndikakhale womasulira wa antchito a m’mayiko ena omwe ankagwira ntchito kumeneko. Ndimakumbukirabe chimwemwe chomwe ndinkakhala nacho mmamaŵa pamene ndinali kulandira abale ndi alongo achigiriki ambirimbiri omwe anadzipereka kugwira ntchito limodzi ndi gulu lomanga Beteliyo. Sindidzaiwala chimwemwe chawo ndi changu chawo.

Ansembe a tchalitchi cha Greek Orthodox ndi owatsatira awo anayesetsa kufuna kuloŵa ku malo komwe tinkamanga Beteliyo kuti asokoneza ntchito yathu, koma Yehova anamva mapemphero athu ndipo tinatetezedwa. Ndinakhalabe komweko mpaka ndinaonerera nyumba ya Beteli yatsopanoyo ikupatulidwa pa April 13, 1991.

Kuthandiza Mlongo Wanga Wokondedwa

Chaka chotsatira, ndinapita kutchuti ku England komwe ndinakakhala ndi mlongo wanga ndi mwamuna wake. Mwatsoka ndili komweko, matenda a mtima anamugwira mlamu wanga kaŵiri konse ndipo anamwalira. Joan wakhala akundithandiza mowolowa manja pamene ndinali kutumikira monga mmishonale. Mlungu umodzi sunali kutha asanandilembere kalata yondilimbikitsa. Kulemberedwa makalata kotero kumakhalatu dalitso kwa mmishonale aliyense. Tsopano iye anali mkazi wamasiye, wofooka ndipo ankafunika thandizo. Kodi ndikanatani?

Mwana wamkazi wa Joan, dzina lake Thelma ndi mwamuna wake ankasamaliranso mkazi wina wamasiye wokhulupirika wa mumpingo wawo yemwe anali wodwala kwambiri. Mkazi wamasiye ameneyo anali mmodzi wa asuwani athu. Nditapemphera kwambiri, ndinaganiza kuti ndiyenera kukhala kuti ndisamalire Joan. Ndinavutika kwambiri kusintha moyo wanga. Komabe, ndili ndi mwayi wotumikira monga mkulu pa mpingo wa Pen Mill womwe ndi umodzi mwa mipingo iŵiri ya ku Yeovil.

Abale amene ndinatumikira nawo kumayiko ena akupitiriza kundilembera makalata ndi kundiimbira mafoni ndipo ndikuthokoza kwambiri zimenezi. Nditafuna kubwereranso ku Greece kapena ku Cyprus, ndikudziŵa kuti abale adzakhala okonzeka kunditumizira tikiti ya ndege. Koma tsopano ndili ndi zaka 80 ndipo maso anga ndi thupi langa zilibe mphamvu monga momwe zinalili kale. N’zokhumudwitsa kuti sindikuchitanso zinthu mwachangu monga kale, koma zaka zomwe ndinatumikira pa Beteli zinandithandiza kukhala ndi zizoloŵezi zomwe zikundithandiza tsopano. Mwachitsanzo, nthaŵi zonse ndimaŵerenga lemba la tsiku ndisanadye chakudya chammaŵa. Ndinaphunziranso kukhala bwino ndi anthu ndiponso kuwakonda, chomwe ndicho chinsinsi choti ntchito ya umishonale iyende bwino.

Ndikamakumbukira zaka pafupifupi 60 zomwe ndakhala ndikutumikira Yehova, ndimadziŵa kuti utumiki wanthaŵi zonse ndiwo chitetezo chachikulu kwambiri ndiponso ndiwo maphunziro abwino koposa. Nditha kunena ndi mtima wonse mawu a Davide kwa Yehova akuti: “Pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.”​—Salmo 59:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Nkhani yosimba za moyo wa John Wynn ili mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1997, masamba 25-8 ndipo ili ndi mutu wakuti “Mtima Wanga Wadzaza Chiyamiko Chosaneneka.”

^ ndime 23 Kale ankatchedwa Consolation.

^ ndime 41 Onani Nsanja ya Olonda ya December 1, 1998, masamba 20-1, ndiponso ya September 1, 1993, masamba 27-31; Galamukani! ya January 8, 1998, masamba 28-31, ndi yachingelezi ya March 22, 1997, masamba 14-15.

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

GREECE

Athens

CYPRUS

Nicosia

Kyrenia

Famagusta

Limassol

[Chithunzi patsamba 21]

Mayi mu 1915

[Chithunzi patsamba 22]

Pamwamba pa denga la nyumba ya Beteli ya ku Brooklyn mu 1946, ine (wachinayi kuchokera kumanzere) ndi abale ena a m’kalasi ya chisanu ndi chitatu ya Gileadi

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi Mayi aang’ono a Millie paulendo wanga woyamba n’tabwerera ku England