Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Dziko Lakale Limenelo Linawonongedwa?

N’chifukwa Chiyani Dziko Lakale Limenelo Linawonongedwa?

N’chifukwa Chiyani Dziko Lakale Limenelo Linawonongedwa?

CHIGUMULA cha dziko lonse sichinali tsoka lachilengedwe ayi. Chinali chiweruzo chochokera kwa Mulungu. Chenjezo linaperekedwa koma linanyalanyazidwa. N’chifukwa chiyani linanyalanyazidwa? Yesu anafotokoza kuti: ‘M’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalawa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.’​—Mateyu 24:38, 39.

Anthu Otukuka Kwambiri

Anthu omwe analiko Chigumula chisanafike anali ndi mwayi m’mbali zina womwe ifeyo tilibe masiku ano. Mwachitsanzo, anthu onse anali kulankhula chinenero chimodzi. (Genesis 11:1) Zimenezi ziyenera kuti zinathandiza kwambiri kuti ntchito zaluso ndiponso zasayansi zomwe zimafuna mgwirizano wa anthu ambiri aluso ziziyenda bwino. Komanso moyo wautali umene anthu ambiri anali nawo unachititsa kuti iwo azipitirizabe kuwonjezera nzeru pa zomwe azidziŵa kale kwa zaka mazana ambiri.

Ena amanena kuti moyo wa anthu kalelo sunali wautali kwambiri ndipo kuti zaka zomwe Baibulo limatchula zinali miyezi chabe. Kodi zimenezi n’zoona? Ayi, taganizirani za Mahalalele. Baibulo limanena kuti: “Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi. . . . Masiku ake onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anayi ndi zisanu; ndipo anamwalira.” (Genesis 5:15-17) Ngati chaka chimodzi chinali mwezi umodzi ndiye kuti Mahalalele anabala mwana wake wamwamunayo ali ndi zaka zisanu zokha basi. Sizinali choncho ayi, anthu m’nthaŵi imeneyo anali adakali ndi mphamvu pang’ono zaungwiro za munthu woyamba Adamu. Iwo analidi kukhala ndi moyo zaka mazana ambiri. Kodi iwo anakwaniritsa kuchita zotani?

Zaka mazana ambiri Chigumula chisanafike, anthu pa dziko lapansi anali atachuluka kwambiri moti mpaka mwana wa Adamu wamwamuna Kaini anamanga mzinda womwe anautcha kuti Enoke. (Genesis 4:17) M’nthaŵi yonseyo Chigumula chisanafike anthu anali kugwira ntchito zosiyanasiyana. Kunali malo a ‘umisiri wonse wa mkuwa ndi wa zitsulo.’ (Genesis 4:22) Mosakayikira zipangizo zimenezi ankazigwiritsa ntchito pa zomangamanga, zokhomakhoma, zosokasoka, ndiponso zaulimi. Ntchito zonsezi zimatchulidwa m’nkhani za anthu oyambirira kukhala pa dziko lapansi.

Nzeru zochuluka zomwe anthuwo anali nazo ziyenera kuti zinatheketsa mbadwo wotsatira kupititsa patsogolo maluso pa ntchito ya zitsulo, kulima mbewu, kuweta nkhosa ndi ng’ombe, zonjambulanjambula, zoimbaimba, ndiponso zosemasema. Mwachitsanzo, Yubala ndiye anali “atate wawo wa iwo oimba zeze ndi chitoliro.” (Genesis 4:21) Chitukuko chinafalikira m’madera ambiri. Komabe, zonsezo zinatha mwadzidzidzi. Kodi chinachitika n’chiyani?

Kodi Chinalakwika N’chiyani?

Ngakhale kuti anthu omwe analiko Chigumula chisanafike anali ndi mwayi m’mbali zambiri, iwo sanayambe bwino. Kholo lawo Adamu anali wopandukira Mulungu. Kaini yemwe anamanga mzinda woyamba kulembedwa, anapha mbale wake. N’zosadabwitsa kuti kuipa kunafala mofulumira kwambiri. Zotsatira za uchimo womwe Adamu anapatsira mbadwa zake zinali kukulabe.​—Aroma 5:12.

Zikuoneka kuti zinthu zinali kuipiraipira pamene Yehova anatsimikiza mtima kuti angolola kuipako kupitiriza kwa zaka 120 zokha basi. (Genesis 6:3) Baibulo limati: “Kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha. . . . Dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.”​—Genesis 6:5, 11.

M’kupita kwa nthaŵi, Nowa anauzidwa mwachindunji kuti Mulungu adzawononga anthu onse ndi chigumula. (Genesis 6:13, 17) Ngakhale kuti Nowa anali “mlaliki wa chilungamo” zinali zoonekeratu kuti anthuwo zinawavuta kukhulupirira kuti zonse zomwe anali kuziona zidzawonongedwa. (2 Petro 2:5) Anthu asanu ndi atatu okha ndiwo anamvera chenjezolo ndipo anapulumutsidwa. (1 Petro 3:20) N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika kwa ife lerolino?

Kodi Zili ndi Phindu Lanji kwa Ife?

Tikukhala m’nthaŵi yofanana ndi ya Nowa. Nthaŵi ndi nthaŵi timamva nkhani za uchigaŵenga zochititsa mantha, kupulula anthu, kupha anthu ambirimbiri popanda zifukwa zenizeni kochitidwa ndi anthu okhala ndi mfuti, ndiponso ziwawa m’banja zikufala mochititsa mantha. Dziko lapansi ladzalanso ndi chiwawa, ndipo monga momwe zinalili kale, anthu akhala akuchenjezedwa za chiweruzo chomwe chikubwera. Yesu mwiniyo ananena kuti adzabwera monga Woweruza woikidwa ndi Mulungu kudzalekanitsa anthu monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Yesu ananena kuti amene adzawapeze ali osayenera, “adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse.” (Mateyu 25:31-33, 46) Komabe panthaŵiyi, Baibulo limati padzakhala opulumuka miyandamiyanda​—khamu lalikulu limene limalambira Mulungu woona yekha. M’dziko lomwe likubweralo, anthu ameneŵa adzasangalala ndi mtendere ndi chitetezo zosatha zomwe sizinaonekepo n’kale lonse.​—Mika 4:3, 4; Chivumbulutso 7:9-17.

Ambiri amaseka mawu a m’Baibulo ngati ameneŵa ndiponso amaseka chenjezo la chiweruzo chomwe chidzasonyeze kuti mawuwo ndi oona. Koma mtumwi Petro anafotokoza kuti anthu okayikira ameneŵa akunyalanyaza zinthu zoona. Iye analemba kuti: “Masiku otsiriza adzafika onyoza . . . ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwake? . . . Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mawu a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka; koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.”​—2 Petro 3:3-7.

Chenjezo la chiweruzo chomwe chikubwera ndiponso uthenga wabwino wonena za mtendere womwe udzatsatira zikulalikidwa mwakhama padziko lonse lerolino motsatira lamulo laulosi la Yesu. (Mateyu 24:14) Chenjezo limeneli siliyenera kuonedwa mwachibwanabwana. Mulungu Wamphamvuyonse amakwaniritsa zomwe walonjeza.

Dziko Lomwe Likubwera

Poganizira za kusintha kofunika kwambiri komwe kukubwera, kodi tsogolo la anthu ndi lotani? M’mawu oyamba a ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu analonjeza kuti: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” Kenako anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kwa Mulungu kuti: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 5:5; 6:10) Inde, Yesu anaphunzitsa kuti anthu okhulupirika adzakhala ndi tsogolo labwino kwambiri pompano pa dziko lapansi. Iye anali kunena za dziko limenelo pamene anati “m’kubadwanso.”​—Mateyu 19:28.

Choncho, pamene mukuganizira za m’tsogolo musalole onyoza kukuchititsani kukayikira chenjezo la Mulungu. N’zoona kuti zinthu zomwe timaziona zingaoneke ngati zidzakhalitsa ndipo dzikoli lakhaladi nthaŵi yaitali. Komabe, tisakhulupirire zimenezi. Anthu aweruzidwa. Choncho, akulimbikitsenitu mawu omwe mtumwi Petro anamaliza nawo kalata yake akuti:

“Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu . . . Popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanga chirema. . . . Kulani m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu.” (2 Petro 3:11, 12, 14, 18) Choncho, tenganipo phunziro pa zimene zinachitika kale m’masiku a Nowa. Yandikirani kwa Mulungu. Wonjezerani kudziŵa kwanu Yesu Kristu. Kulitsani kudzipereka kwanu kwa Mulungu ndipo khalani m’gulu la anthu miyandamiyanda amene asankha kudzapulumuka chimaliziro cha dziko lino ndi kuloŵa m’dziko lamtendere lomwe likubwera.

[Chithunzi patsamba 5]

Ntchito yopanga zinthu ndi zitsulo inali yodziŵika chigumula chisanachitike

[Chithunzi patsamba 7]

Dziko labwino kwambiri likutiyembekezera