Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chochitika Chofunika Koposa M’mbiri

Chochitika Chofunika Koposa M’mbiri

Chochitika Chofunika Koposa M’mbiri

CHINALI imfa ya Yesu Kristu. N’chifukwa chiyani inali yofunika kwambiri? Pali zifukwa zingapo.

Kukhulupirika kwa Yesu mpaka imfa kunasonyeza kuti munthu atha kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Mulungu.

Imfa ya Kristu inapatsa mwayi anthu ena kuti akakhale olamulira limodzi naye kumwamba. Inatsegulanso njira kwa anthu ena ambiri kuti adzakhale ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso.

Yesu pausiku woti aphedwa mawa, anagwiritsa ntchito mkate wopanda zofufumitsa ndi vinyo wofiira monga zizindikiro zoimira nsembe yachikondi ya thupi lake. Ndipo iye anauza ophunzira ake kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Kodi mudzakumbukira nawo chochitika chofunika kwambirichi?

Mboni za Yehova zikukuitanani kuti mudzakhale nazo pa mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chaka chino mwambo umenewu udzachitika Lachinayi, March 28, dzuŵa litaloŵa. Mutha kudzafika ku Nyumba ya Ufumu yomwe ili kufupi ndi kwanu. Chonde funsani Mboni za Yehova zakwanuko kuti zikuuzeni nthaŵi yeniyeni ndi malo ake.